-
“Pitirizani Kugonjetsa Choipa” mwa Kupewa Kupsa MtimaNsanja ya Olonda—2010 | June 15
-
-
10. Kodi Akhristu ayenera kuiona bwanji nkhani yobwezera?
10 Nkhani ya Simeoni ndi Levi komanso ya Davide ndi Abigayeli imasonyeza kuti Yehova sasangalala ndi kukwiya mosadziletsa ndiponso kuchita chiwawa. Nkhanizi zikusonyezanso kuti iye amatidalitsa tikamayesetsa kukhazikitsa mtendere. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Ngati ndi kotheka, khalani mwa mtendere ndi anthu onse, monga mmene mungathere. Okondedwa, musabwezere choipa, koma siyirani malo mkwiyo wa Mulungu; pakuti Malemba amati: ‘Kubwezera ndi kwanga; ndidzawabwezera ndine, atero Yehova.’ Koma, ‘ngati mdani wako ali ndi njala, m’patse chakudya; ngati ali ndi ludzu, m’patse chakumwa; pakuti mwakutero udzamuunjikira makala a moto pamutu pake.’ Musalole kuti choipa chikugonjetseni, koma pitirizani kugonjetsa choipa mwa kuchita chabwino.”—Aroma 12:18-21.a
-
-
“Pitirizani Kugonjetsa Choipa” mwa Kupewa Kupsa MtimaNsanja ya Olonda—2010 | June 15
-
-
a Mawu akuti “makala a moto” amanena za njira imene anthu ankagwiritsa ntchito poyenga zitsulo. Anthuwo ankaika makala a moto pamwamba ndi pansi pa chitsulo chimene akufuna kuyengacho. Tikamakomera mtima anthu amene atichitira zoipa, timafewetsa mtima wawo n’kuwathandiza kuti azisonyeza makhalidwe awo abwino.
-