-
Aroma Amva Mbiri Yabwino KoposaNsanja ya Olonda—1990 | August 1
-
-
Roma anali malo apakati amphamvu a ndale zadziko m’tsiku la Paulo. Chotero, Paulo akulangiza Akristu mwanzeru kuti: ‘Anthu onse amvere maulamuliro aakulu; pakuti palibe ulamuliro wina koma wochokera kwa Mulungu.’ (Aroma 13:1) Zochita za Akristu kwa wina ndi mnzake zirinso mbali yakukhala ndi moyo mogwirizana ndi chilungamo. “Musakhale ndi mangawa kwa munthu ali yense,” akutero Paulo, ‘koma kukondana ndiko; pakuti iye amene akondana ndi mnzake wakwanitsa lamulo.’—Aroma 13:8.
-
-
Aroma Amva Mbiri Yabwino KoposaNsanja ya Olonda—1990 | August 1
-
-
[Bokosi/Chithunzi patsamba 24]
‘Palibe ulamuliro [wakudziko] wina koma wochokera kwa Mulungu.’ Ichi sichimatanthauza kuti Mulungu amaika wolamulira aliyense m’malo. M’malomwake, olamulira akudziko amakhalapo kokha mwa kuloledwa ndi Mulungu. Kaŵirikaŵiri, olamulira aumunthu anaonedwa ndi kunenedweratu ndi Mulungu ndipo mwakutero iwo “a[na]ikidwa ndi Mulungu.”—Aroma 13:1.
[Mawu a Chithunzi]
Museo della Civiltà Romana, Roma
-