Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Kodi Akristu Ayenera Kuchita Nawo Chikondwerero cha Chaka Chatsopano?
    Galamukani!—2002 | January 8
    • Baibulo limalimbikitsa Akristu kuti “Tiyendeyende koyenera, monga usana; si m’madyerero ndi kuledzera ayi.”a (Aroma 13:12-14; Agalatiya 5:19-21; 1 Petro 4:3) Akristu sachita nawo chikondwerero cha chaka chatsopano pakuti nthaŵi zambiri anthu amatayirira kuchita zinthu zenizenizo zimene Baibulo limatsutsa. Apa si ndiye kuti Akristu amaletsa anthu kusangalala. Zimenezi si zoona, pakuti iwo amadziŵa kuti Baibulo limalangiza mobwerezabwereza anthu olambira Mulungu woona kuti azisangalala, ndipo limapereka zifukwa zingapo ndithu zoyenera kukondwera nazo. (Deuteronomo 26:10, 11; Salmo 32:11; Miyambo 5:15-19; Mlaliki 3:22; 11:9) Baibulo limanenanso kuti pachikondwerero nthaŵi zambiri pamakhalanso zakudya ndi zakumwa.—Salmo 104:15; Mlaliki 9:7a.

  • Kodi Akristu Ayenera Kuchita Nawo Chikondwerero cha Chaka Chatsopano?
    Galamukani!—2002 | January 8
    • a Ponena kuti “madyerero ndi kuledzera” n’kutheka kuti Paulo amatanthauzanso zinthu zimene zinkachitika pa chikondwerero cha chaka chatsopano, chifukwa anthu ambiri ku Roma ankachita zimenezi m’zaka zapakati pa 1 mpakana 100 C.E.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena