Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Sonyezani Mtima wa Kristu
    Nsanja ya Olonda—2000 | September 1
    • 4, 5. Ndi mbali iti ya mtima wa Yesu yomwe ikutchulidwa pa Aroma 15:1-3, ndipo kodi Akristu angam’tsanzire motani?

      4 Kodi chofunika n’chiyani kuti tikhale ndi mtima ngati wa Kristu Yesu? Chaputala 15 cha kalata ya Paulo yomwe analembera Aroma chimatithandiza kuyankha funso limenelo. M’mavesi oyambirira angapo a chaputala chimenechi, Paulo ananena za mkhalidwe wapadera wa Yesu pamene anati: “Ndipo ife amene tili olimba tiyenera kunyamula zofooka za opanda mphamvu, ndi kusadzikondweretsa tokha. Yense wa ife akondweretse mnzake, kum’chitira zabwino, zakum’limbikitsa. Pakuti Kristunso sanadzikondweretsa yekha; koma monga kwalembedwa: Minyozo ya iwo amene anakunyoza iwe inagwa pa ine.”​—Aroma 15:1-3.

  • Sonyezani Mtima wa Kristu
    Nsanja ya Olonda—2000 | September 1
    • 6. Kodi tingatsanzire zochita za Yesu m’njira iti pamene titsutsidwa ndi kunyozedwa?

      6 Mkhalidwe winanso wabwino umene Yesu anasonyeza unakhudza kulingalira kwake ndi zochita zake zomwe nthaŵi zonse zinali zolimbikitsa. Iye sanalole konse mtima woipa wa anthu ena kusonkhezera mtima wake wabwinowo pa kutumikira Mulungu; nafenso tisalole. Pamene anali kunyozedwa ndi kuzunzidwa chifukwa cha kulambira Mulungu mokhulupirika, Yesu moleza mtima anapirira popanda kudandaula. Iye anadziŵa kuti awo amene akuyesa kusangalatsa mnzawo mwa “kum’chitira zabwino, zakum’limbikitsa,” ayenera kuyembekezera chitsutso chochokera m’dziko losakhulupirira ndi losazindikirali.

      7. Kodi Yesu anasonyeza motani kuleza mtima, ndipo n’chifukwa chiyani ifeyo tiyenera kuchita chimodzimodzi?

      7 Yesu anasonyeza mtima wabwino m’njira zinanso. Sanasonyeze konse kusaleza mtima ndi Yehova koma moleza mtima anayembekezera kukwaniritsidwa kwa zifuno Zake. (Salmo 110:1; Mateyu 24:36; Machitidwe 2:32-36; Ahebri 10:12, 13) Komanso, Yesu sanachitepo mosaleza mtima ndi om’tsatira ake. Iye anawauza kuti: “Phunzirani kwa Ine”; popeza kuti anali “wofatsa,” malangizo akewo anali olimbikitsa ndi otsitsimula. Ndipo chifukwa chakuti anali “wodzichepetsa mtima,” sanali wodzitukumula kapena wodzikuza. (Mateyu 11:29) Paulo akutilimbikitsa kutsanzira mikhalidwe imeneyi ya mtima wa Yesu pamene akunena kuti: “Mukhale nawo mtima m’kati mwanu umene unalinso mwa Kristu Yesu, ameneyo, pokhala nawo maonekedwe a Mulungu, sanachiyesa cholanda kukhala wofanana ndi Mulungu, koma anadzikhuthula yekha, natenga maonekedwe a kapolo, nakhala m’mafanizidwe a anthu.”​—Afilipi 2:5-7.

      8, 9. (a) N’chifukwa chiyani tifunikira kuchita khama kuti tikulitse mtima wopanda dyera? (b) N’chifukwa chiyani sitiyenera kukhumudwa ngati tilephera kutsatira bwino lomwe chitsanzo chomwe Yesu anatisiyira, ndipo Paulo anali chitsanzo chabwino motani pambali imeneyi?

      8 N’chapafupi kunena kuti tikufuna kutumikira ena ndi kuti tikufuna kuika zosoŵa zawo patsogolo pa zathu. Koma kupenda moona mtima mkhalidwe wathu wa maganizo kungavumbule kuti mitima yathu siilidi yofunitsitsa kuchita zimenezo. Chifukwa chiyani? Choyamba, chifukwa chakuti tinatengera mikhalidwe yadyera kuchokera kwa Adamu ndi Hava; chachiŵiri, chifukwa chakuti tikukhala m’dziko lomwe limachirikiza dyera. (Aefeso 4:17, 18) Kuti tikhale ndi mtima wopanda dyera kaŵirikaŵiri zimatanthauza kukulitsa kalingaliridwe kosiyana kotheratu ndi chibadwa chathu chopanda ungwirochi. Kuchita zimenezo kumafunatu kutsimikiza mtima ndi khama.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena