Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Kodi Ufumu wa Mulungu N’chiyani?
    Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
    • 7. Ufumu wa Mulungu uli ndi malamulo abwino kwambiri

      Maboma a anthu amapanga malamulo omwe amayenera kuthandiza ndi kuteteza nzika zawo. Nawonso Ufumu wa Mulungu uli ndi malamulo amene nzika zake zimayenera kuwatsatira. Werengani 1 Akorinto 6:9-11, kenako mukambirane mafunso awa:

      • Kodi mukuganiza kuti zinthu zidzakhala bwanji padzikoli aliyense akamadzatsatira malamulo a Mulungu?a

      • Yehova amayembekezera kuti nzika za Ufumu wake zizitsatira malamulo ake, kodi mukuganiza kuti zimene Yehova amafunazi n’zoyenera? N’chifukwa chiyani mukutero?

      • Ndi mfundo iti imene ikusonyeza kuti anthu amene satsatira malamulo amenewa atha kusintha?​—Onani vesi 11.

      Wathirafiki akuimitsa magalimoto pamphambano ya msewu wodutsa anthu ambiri. Anthu amisinkhu yosiyanasiyana akuwoloka msewu.

      Maboma amakhazikitsa malamulo n’cholinga chofuna kuthandiza ndi kuteteza nzika zawo. Ufumu wa Mulungu uli ndi malamulo abwino kwambiri omwe amathandiza ndi kuteteza nzika zake

  • Kodi Baibulo Limanena Zotani pa Nkhani ya Kugonana?
    Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
    • Phunziro 41. Mwamuna ndi mkazi agwirana manja.

      PHUNZIRO 41

      Kodi Baibulo Limanena Zotani pa Nkhani ya Kugonana?

      Anthu ambiri amaona kuti nkhani zokhudza kugonana ndi zoumitsa pakamwa. Komabe, Baibulo likamanena zokhudza kugonana, limanena zinthu mosapita m’mbali, koma mwaulemu. Ndipo zimene limanena n’zothandiza kwambiri. Zimenezi ndi zomveka chifukwa Yehova ndi amene anatilenga. Choncho amadziwa bwino zimene zingatithandize kuti tizikhala ndi moyo wabwino. Iye amatiuza zimene tiyenera kuchita kuti tizimusangalatsa ndiponso zimene zingatithandize kuti tizisangalala ndi moyo kuyambira panopa mpaka kalekale.

      1. Kodi maganizo a Yehova ndi otani pa nkhani ya kugonana?

      Kugonana ndi mphatso yochokera kwa Yehova yomwe anapereka kwa anthu okwatirana kuti azisangalala nayo. Mphatsoyi simangothandiza anthu kuti azibereka ana basi, koma imawathandizanso kuti azisonyezana chikondi n’kumasangalala. N’chifukwa chake Mawu a Mulungu amati: “Usangalale ndi mkazi wapaunyamata wako.” (Miyambo 5:​18, 19) Yehova amayembekezera kuti Akhristu okwatirana azikhala okhulupirika m’banja, choncho sangachite chigololo.​​​—Werengani Aheberi 13:4.

      2. Kodi chiwerewere n’chiyani?

      Baibulo limatiuza kuti “adama [achiwerewere] . . . sadzalowa mu ufumu wa Mulungu.” (1 Akorinto 6:9, 10) Olemba Baibulo ena amene analilemba m’Chigiriki anagwiritsa ntchito mawu akuti por·neiʹa ponena za chiwerewere. Mawuwa amanena za (1) kugonanaa kwa anthu amene sali pabanja, (2) kugonana kwa amuna kapena akazi okhaokha, komanso (3) kugonana ndi nyama. Timasangalatsa Yehova komanso timakhala ndi moyo wabwino tikamayesetsa “kupewa dama” kapena kuti chiwerewere.​—1 Atesalonika 4:3.

      FUFUZANI MOZAMA

      Onani zimene mungachite kuti mupewe chiwerewere komanso phindu limene mungapeze ngati mutayesetsa kukhalabe ndi makhalidwe oyera.

      Yosefe akuthawa mkazi wa Potifara. Mkaziyo wagwira malaya a Yosefe.

      3. Muziyesetsa kupewa chiwerewere

      Yosefe, yemwe anali munthu wokhulupirika, anakana kugonana ndi mzimayi yemwe ankamunyengerera kuti achite naye zachiwerewere. Werengani Genesis 39:1-12, kenako mukambirane mafunso awa:

      • N’chifukwa chiyani Yosefe anakana kuchita chiwerewere?​—Onani vesi 9.

      • Kodi mukuganiza kuti Yosefe anachita zinthu mwanzeru? N’chifukwa chiyani mukutero?

      Kodi masiku ano achinyamata angatsanzire bwanji Yosefe pa nkhani yokana kuchita chiwerewere? Onerani VIDIYO.

      VIDIYO: Thawani Dama (5:06)

      Yehova amafuna kuti tonsefe tiziyesetsa kupewa chiwerewere. Werengani 1 Akorinto 6:18, kenako mukambirane mafunso awa:

      • Kodi ndi zinthu ziti zomwe zingapangitse munthu kuchita chiwerewere?

      • Kodi mungatani kuti mupewe kuchita chiwerewere?

      4. Yesetsani kuti musagonje pa mayesero

      N’chiyani chingapangitse kuti munthu agonje mosavuta akamayesedwa kuti achite chiwerewere? Onerani VIDIYO, kenako mukambirane mafunso otsatirawa.

      VIDIYO: Muziwerenga Baibulo Kuti Musagonje pa Mayesero (3:02)

      • Kodi m’bale wamuvidiyoyi anachita chiyani atazindikira kuti zinthu zina zimene amaganiza ndi kuchita zikanachititsa kuti asiye kukhala wokhulupirika kwa mkazi wake?

      Ngakhale Akhristu okhulupirika amafunika kuchita khama kuti asamaganizire zinthu zoipa. Kodi mungatani kuti musamaganizire zinthu zachiwerewere? Werengani Afilipi 4:8, kenako mukambirane mafunso awa:

      • Kodi ndi zinthu ziti zimene tiyenera kumaziganizira?

      • Kodi kuwerenga Baibulo komanso kukhala ndi zochita zambiri potumikira Yehova kungatithandize bwanji kuti tipewe mayesero?

      5. Mfundo za Yehova zimatithandiza kukhala ndi moyo wabwino

      Yehova amafuna kuti zinthu zizitiyendera bwino. Iye amatiuza zimene tingachite kuti tikhale ndi makhalidwe oyera komanso ubwino wochita zimenezi. Werengani Miyambo 7:7-27 kapena onerani VIDIYO, kenako mukambirane mafunso otsatirawa.

      VIDIYO: Wopanda Nzeru Mumtima (9:31)

      • Kodi mnyamatayu anachita chiyani chomwe chikanatha kumulowetsa m’mayesero?​—Onani Miyambo 7:8, 9.

      • Lemba la Miyambo 7:23, 26, limasonyeza kuti kuchita chiwerewere kukhoza kutibweretsera mavuto aakulu. Ndiye kodi tingapewe mavuto ati tikamayesetsa kukhala ndi makhalidwe oyera?

      • Kodi kukhala ndi makhalidwe oyera kungatithandize bwanji kuti tizisangalala ndi moyo panopa mpaka kalekale?

      Anthu ena amaona kuti zimene Baibulo limanena pa nkhani ya kugonana kwa amuna komanso akazi okhaokha, ndi kukhwimitsa zinthu. Koma zimenezi si zoona chifukwa Yehova amatikonda ndipo amafuna kuti tonse tizisangalala ndi moyo panopa mpaka kalekale. Kuti zimenezi zitheke, tiziyesetsa kutsatira mfundo zake. Werengani 1 Akorinto 6:9-11, kenako mukambirane funso ili:

      • Kodi kugonana kwa amuna kapena akazi okhaokha ndi khalidwe lokhalo limene Mulungu amadana nalo?

      Kuti tizisangalatsa Mulungu, tonsefe tiyenera kuyesetsa kusintha moyo wathu. Kodi kuchita zimenezi n’kothandizadi? Werengani Salimo 19:8, 11, kenako mukambirane mafunso awa:

      • Kodi Yehova anachita bwino kutipatsa mfundo zamakhalidwe abwino kapena anangokhwimitsa zinthu? N’chifukwa chiyani mukutero?

      Zithunzi: 1. Mtsikana wakhala pafupi ndi chibwenzi chake ndipo akuoneka wosasangalala. Iye akumwa mowa komanso kusuta limodzi ndi anzake kumalo ena azisangalalo. 2. Mtsikana yemwe uja akucheza mosangalala ndi alongo ku Nyumba ya Ufumu.

      Yehova wathandiza anthu ambiri kuti asiye makhalidwe oipa. Inunso angakuthandizeni

      ZIMENE ENA AMANENA: “Palibe vuto kugonana ndi wina aliyense amene ukufuna, bola ngati mukukondana.”

      • Kodi inuyo mungamuuze zotani munthu wotereyu?

      ZOMWE TAPHUNZIRA

      Kugonana ndi mphatso yochokera kwa Yehova ndipo imathandiza kuti mwamuna ndi mkazi wake azisangalala.

      Kubwereza

      • Kodi kuchita chiwerewere kumaphatikizaponso kuchita zinthu ziti?

      • N’chiyani chingatithandize kuti tipewe kuchita chiwerewere?

      • Kodi timapindula bwanji tikamatsatira mfundo za Yehova zamakhalidwe abwino?

      Zolinga

      ONANI ZINANSO

      Onani chifukwa chake Yehova amafuna kuti mwamuna ndi mkazi azimanga kaye banja lawo asanatengane.

      “Kodi Baibulo Limavomereza Kuti Mwamuna ndi Mkazi Azikhalira Limodzi Asanakwatirane?” (Nkhani yapawebusaiti)

      Onani chifukwa chimene Baibulo likamaphunzitsa kuti kugonana kwa amuna kapena akazi okhaokha n’kolakwika, silitanthauza kuti tizidana ndi anthu amene amachita zimenezi.

      “Kodi Kugonana Kwa Amuna Kapena Akazi Okhaokha N’kolakwika?” (Nkhani yapawebusaiti)

      Onani mmene malamulo a Mulungu pa nkhani zokhudza kugonana amatitetezera.

      “Kodi Kugonana M’kamwa Kumakhaladi Kugonana?” (Nkhani yapawebusaiti)

      Munkhani yakuti, “Anandilandira Mwaulemu Kwambiri,” onani zimene zinathandiza munthu wina kusiya khalidwe logonana ndi amuna anzake n’cholinga choti azisangalatsa Mulungu.

      “Baibulo Limasintha Anthu” (Nsanja ya Olonda, April 1, 2011)

      a Zimenezi zikuphatikizapo kuchita zinthu monga chiwerewere, kugonana m’kamwa, kugonana kobibira komanso kuseweretsa maliseche a munthu wina ndi cholinga chofuna kudzutsa kapena kukhutiritsa chilakolako cha kugonana.

  • Kodi Mukachita Tchimo Lalikulu Muyenera Kutani?
    Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
    • Ngakhale kuti mumakonda kwambiri Yehova ndiponso mumayesetsa kupewa kuchita zinthu zomwe zingamukhumudwitse, nthawi zina mukhoza kulakwitsa zinazake. Komabe machimo ena amakhala aakulu kuposa ena. (1 Akorinto 6:9, 10) Ngati mwachita tchimo lalikulu musataye mtima ndipo musaiwale kuti Yehova sanasiye kukukondani. Iye ndi wofunitsitsa kukukhululukirani komanso kukuthandizani kuti musinthe.

      1. Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti Yehova atikhululukire?

      Anthu amene amakonda Yehova amadzimvera chisoni kwambiri akazindikira kuti achita tchimo lalikulu. Komabe Yehova amawatonthoza ndi lonjezo lakuti: “Ngakhale machimo anu atakhala ofiira kwambiri, adzayera kwambiri.” (Yesaya 1:18) Tikalapa mochokera pansi pa mtima, Yehova sakumbukiranso machimo athu ndipo amatikhululukira ndi mtima wonse. Ndiye timasonyeza bwanji kuti talapa? Timadzimvera chisoni kwambiri chifukwa cha zimene tachitazo, sitimazibwerezanso, kenako timapempha Yehova kuti atikhululukire. Komanso timachita khama kuti tisiye kuchita kapena kuganizira zinthu zoipa zimene zinachititsa kuti tichite tchimo. Kuonjezera pamenepa, timayesetsa kutsatira mfundo za Yehova za makhalidwe abwino pa moyo wathu.​—Werengani Yesaya 55:6, 7.

      2. Kodi Yehova amagwiritsa ntchito bwanji akulu kuti atithandize tikachimwa?

      Tikachita tchimo lalikulu Yehova amatiuza kuti ‘tiitane akulu a mpingo.’ (Werengani Yakobo 5:14, 15.) Akuluwa amakonda Yehova ndi nkhosa zake. Iwo anaphunzitsidwa bwino mmene angatithandizire n’cholinga choti tikhalenso pa ubwenzi wabwino ndi Yehova.​—Agalatiya 6:1.

      Kodi akulu amatithandiza bwanji tikachita tchimo lalikulu? Akulu awiri kapena atatu amagwiritsa ntchito mfundo za m’Malemba potithandiza kuzindikira kuti zomwe tachitazo ndi zolakwika. Iwo amatipatsa malangizo ndi kutilimbikitsa n’cholinga chotithandiza kuti tipewe kudzachitanso tchimolo. Pofuna kuteteza mpingo kuti ukhalebe woyera, akulu amachotsa mumpingo munthu yemwe wachita tchimo lalikulu koma sanasonyeze mtima wolapa kuti munthuyo asasokoneze ena.

      FUFUZANI MOZAMA

      Onani zimene mungachite kuti muziyamikira zimene Yehova amachita potithandiza tikachita tchimo lalikulu.

      3. Kuulula machimo athu kumatithandiza kuti tikhalenso pa ubwenzi ndi Yehova

      Tikachita tchimo lililonse Yehova amakhumudwa. Choncho tingachite bwino kuulula kwa iyeyo. Werengani Salimo 32:1-5, kenako mukambirane funso ili:

      • N’chifukwa chiyani tiyenera kuulula machimo athu kwa Yehova m’malo momubisira?

      Tikaulula machimo athu kwa Yehova tiyeneranso kuuza akulu ndipo kuchita zimenezi kumathandiza kuti zinthu ziyambirenso kutiyendera bwino. Onerani VIDIYO, kenako mukambirane funso lotsatirali.

      VIDIYO: “Yehova Amalanga Aliyense Amene Iye Amamukonda” (3:01)

      • Muvidiyoyi, kodi akulu anathandiza bwanji Canon kuti abwerere kwa Yehova?

      Tizimasuka pofotokozera akulu za tchimo lathu ndipo tiziwauza zoona zokhazokha. Iwo amafuna kutithandiza. Werengani Yakobo 5:16, kenako mukambirane funso ili:

      • N’chifukwa chiyani akulu savutika kutithandiza tikawauza zoona zokhazokha zokhudza tchimo lathu?

      Zithunzi: 1. M’bale akudzimvera chisoni chifukwa cha tchimo limene wachita. 2. Akupemphera kwa Yehova. 3. Akulankhula ndi mkulu pafoni. 4. Wakumana ndi akulu atatu. 5. Akumwetulira chifukwa sakudziimbanso mlandu.

      Muziulula machimo anu kwa Yehova, muziuza akulu zoona zokhazokha komanso muzivomereza chilango chochokera kwa Yehova chomwe amachipereka mwachikondi

      4. Yehova amasonyeza chifundo kwa anthu ochimwa

      Ngati munthu amene wachita tchimo lalikulu sakufuna kulapa komanso kutsatira mfundo za m’Malemba amachotsedwa mumpingo ndipo sitiyenera kumacheza naye. Werengani 1 Akorinto 5:6, 11, kenako mukambirane funso ili:

      • Monga mmene chofufumitsa chimafufumitsira mtanda wonse, kodi kucheza ndi munthu wochimwa yemwe sanalape kungakhudze bwanji mpingo wonse?

      Potsanzira mmene Yehova amasonyezera chifundo kwa anthu ochimwa, akulu amayesetsa kuthandiza anthu amene amachotsedwa mumpingo. Anthu ambiri omwe anachotsedwa mumpingo anabwerera chifukwa cha chilango chomwe anapatsidwa. Ngakhale kuti kuchotsedwa mumpingo ndi kowawa, kunawathandiza kuzindikira kuti zomwe anachita zinali zolakwika.​—Salimo 141:5.

      Kodi mmene Yehova amachitira zinthu ndi anthu ochimwa zimasonyeza bwanji kuti amawamvetsa, ndi wachifundo ndiponso ndi wachikondi?

      5. Yehova amakhululukira munthu amene walapa

      Yesu anagwiritsa ntchito fanizo lomwe limatithandiza kumvetsa mmene Yehova amamvera munthu wochimwa akalapa. Werengani Luka 15:1-7, kenako mukambirane funso ili:

      • Kodi fanizoli likukuphunzitsani chiyani zokhudza Yehova?

      Werengani Ezekieli 33:11, kenako mukambirane funso ili:

      • Kodi munthu ayenera kuchita chiyani posonyeza kuti walapadi?

      M’busa akumanga mwendo wa nkhosa yovulala.

      Mofanana ndi m’busa, Yehova amasamalira mwachikondi nkhosa zake

      ZIMENE ENA AMANENA: “Ndikuopa kuti ndikaulula tchimo langa kwa akulu andichotsa mumpingo.”

      • Kodi munthu amene ali ndi maganizo amenewa mungamuuze zotani?

      ZOMWE TAPHUNZIRA

      Ngati munthu wachita tchimo lalikulu n’kulapa mochokera pansi pa mtima komanso watsimikiza mtima kuti sadzachitanso tchimolo, Yehova amamukhululukira.

      Kubwereza

      • N’chifukwa chiyani tiyenera kuulula machimo athu kwa Yehova?

      • Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti Yehova atikhululukire machimo athu?

      • Ngati tachita tchimo lalikulu, n’chifukwa chiyani tiyenera kupempha akulu kuti atithandize?

      Zolinga

      ONANI ZINANSO

      Onani mmene Yehova anasonyezera munthu wina chifundo chotchulidwa pa Yesaya 1:18.

      Musamakayikire Kuti Yehova ndi Wachifundo (5:02)

      Kodi akulu amathandiza bwanji munthu amene wachita tchimo lalikulu?

      “Mmene Tingasonyezere Chikondi ndi Chifundo Wina Akachita Tchimo” (Nsanja ya Olonda, August, 2024)

      Onani mmene anthu osalapa amasonyezedwera chikondi komanso chifundo.

      “Kodi Akulu Angathandize Bwanji Anthu Amene Achotsedwa Mumpingo?” (Nsanja ya Olonda, August, 2024)

      Munkhani yakuti, “Ndinazindikira Kuti Ndiyenera Kubwerera kwa Yehova,” onani chifukwa chake munthu wina anaona kuti Yehova wamuthandiza kubwerera kwa iye.

      “Baibulo Limasintha Anthu” (Nsanja ya Olonda, April 1, 2012)

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena