Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w94 8/15 tsamba 11-15
  • Mbiri Yabwino Imeneyi Iyenera Kulalikidwa Choyamba

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mbiri Yabwino Imeneyi Iyenera Kulalikidwa Choyamba
  • Nsanja ya Olonda—1994
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kusiyana ndi Atsogoleri Achipembedzo a Dziko Lachikristu
  • Kodi Nchifukwa Ninji Mbiri Yabwino Iyenera Kulalikidwa Choyamba?
  • Mbiri Yabwino ndi Chikondi cha Yehova
  • Mbiri Yabwino ndi Mphamvu ya Yehova
  • Mbiri Yabwino ndi Nzeru za Yehova
  • Mbiri Yabwino ndi Chilungamo cha Mulungu
  • Kodi Dziko Lalalikiridwa Mofalikira Chotani?
  • Kodi Nchiyani Chimene Chimasonkhezera Mbonizo Kupitirizabe?
  • “Mbiri Yabwino Iyenera Kulalikidwa Choyamba”
    Nsanja ya Olonda—1988
  • “Pitani Mukaphunzitse Anthu a Mitundu Yonse”
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2016
  • Yehova Akugwiritsira Ntchito “Chopusa” Kupulumutsa Okhulupirirawo
    Nsanja ya Olonda—1992
  • Kufalitsa “Uthenga Wabwino wa Zinthu Zabwino”
    Nsanja ya Olonda—2005
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1994
w94 8/15 tsamba 11-15

Mbiri Yabwino Imeneyi Iyenera Kulalikidwa Choyamba

“M’mitundu yonse mbiri yabwino iyenera kulalikidwa choyamba.”​—MARKO 13:10, NW.

1, 2. Kodi chizindikiro cha Mboni nchiyani, ndipo chifukwa ninji?

KODI nchifukwa ninji Mboni za Yehova zimalalikira mwakhama chotero? Ndithudi ndife odziŵika padziko lonse chifukwa cha utumiki wathu wapoyera, kaya ukhale wa kunyumba ndi nyumba, m’makwalala, kapena pa kukambitsirana kwa mwamwaŵi. Panthaŵi iliyonse yoyenera, timadzidziŵikitsa ife eni kukhala Mboni ndipo timayesa mwaluso kuuza ena mbiri yabwino imene timaiona kukhala yamtengo wake. Kwenikweni, tinganene kuti utumikiwu ndiwo chizindikiro chathu!​—Akolose 4:6.

2 Tangozilingalirani​—nthaŵi iliyonse pamene anthu aona m’malo awo okhala gulu la amuna, akazi, ndi ana ovala bwino ali ndi zikwama, kodi nchiyani chimene kaŵirikaŵiri amaganiza poyamba? Kodi amati, ‘Oo, abweranso Akatolika (kapena a Orthodox) aja!’ kapena, ‘Si awa abweranso a Pentecostal (kapena a Baptist) aja!’ Ayi. Anthu amadziŵa kuti zipembedzo zimenezo zilibe mabanja athunthu amene amachita utumiki wakunyumba ndi nyumba. Mwinamwake magulu ena azipembedzo amatumiza “amishonale” kwa nyengo ya zaka ziŵiri m’madera ena, koma ziŵalo zawo zina sizimatenga mbali muutumiki uliwonse wotero. Mboni za Yehova zokha zimazindikiridwa padziko lonse chifukwa cha changu chawo m’kuuza ena uthenga wawo pa nthaŵi iliyonse yoyenera. Ndipo zimadziŵika chifukwa cha magazini awo, Nsanja ya Olonda ndi Galamukani!​—Yesaya 43:10-12; Machitidwe 1:8.

Kusiyana ndi Atsogoleri Achipembedzo a Dziko Lachikristu

3, 4. Kodi atsogoleri achipembedzo a Dziko Lachikristu amasonyezedwa motani kaŵirikaŵiri m’zoulutsira nkhani?

3 Mosiyana kwambiri, malipoti anyuzi mobwerezabwereza avumbula atsogoleri achipembedzo ambiri a maiko ena kukhala ogona ana, mbala zoipa, ndi onyenga. Ntchito zawo zathupi ndi moyo wawo wapamwamba kopambana zimaonekera kuti onse azione. Wolemba nyimbo wina wotchuka analongosola bwino m’nyimbo yake yotchedwa kuti “Kodi Yesu Akadavala Rolex [wotchi yodula kwambiri yagolidi] pa Chiwonetsero Chake Chapawailesi Yakanema?” Iye akufunsa funso lakuti: “Kodi Yesu angakhale wandale zadziko Iye atabweranso Padziko Lapansi? Kodi angakhale ndi nyumba Yake yachiŵiri ku Palm Springs [malo a anthu olemera mu California] ndi kuyesa kubisa chuma Chake?” Ali oyenerera chotani nanga mawu a Yakobo akuti: “Mwadyerera padziko, ndipo mwachita zokukondweretsani; mwadyetsa mitima yanu m’tsiku lakupha.”​—Yakobo 5:5; Agalatiya 5:19-21.

4 Kuyanjana kwa atsogoleri achipembedzo ndi andale zadziko ndipo ngakhale kuima kwawo m’masankho azandale kumawasonyeza kukhala alembi ndi Afarisi amakono. Panthaŵi imodzimodziyo, m’maiko onga ngati United States ndi Canada, milandu ndi ziweruzo zotsutsa atsogoleri achipembedzo chifukwa cha khalidwe lawo lachiwerewere kwa ana ndi achikulire, zimawonongetsa ndalama zambiri zachipembedzo zoperekedwa.​—Mateyu 23:1-3.

5. Kodi nchifukwa ninji atsogoleri achipembedzo a Dziko Lachikristu sanatsimikiziridwe kukhala “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru”?

5 Molondola, Yesu anakhoza kunena kwa atsogoleri achipembedzo a tsiku lake kuti: “Tsoka inu, alembi ndi Afarisi, onyenga! chifukwa mufanafana ndi manda opaka njereza, amene aonekera okoma kunja kwake, koma adzala mkatimo ndi mafupa a anthu akufa ndi zonyansa zonse. Chomwecho inunso muonekera olungama pamaso pa anthu, koma mkati muli odzala ndi chinyengo ndi kusayeruzika.” Motero, Mulungu sanapatse atsogoleri achipembedzo a Dziko Lachikristu, kaya Achikatolika, Achiprotesitanti, a Orthodox, kapena opanda chipembedzo, ntchito ya kulalikira mbiri yabwino. Iwo sanatsimikizire kukhala “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” wonenedweratuyo.​—Mateyu 23:27, 28; 24:45-47.

Kodi Nchifukwa Ninji Mbiri Yabwino Iyenera Kulalikidwa Choyamba?

6. Kodi ndi zochitika zotani zimene zidzachitika posachedwapa?

6 M’malongosoledwe ake atsatanetsatane a lamulo la Yesu la kulalikira mbiri yabwino m’mitundu yonse, Marko yekha akugwiritsira ntchito liwu lakuti “choyamba.” (Marko 13:10; yerekezerani ndi Mateyu 24:14.) Matembenuzidwe a J. B. Phillips amati: “Popeza kuti mapeto asanafike uthenga wabwino uyenera kulengezedwa ku mitundu yonse.” Kugwiritsira ntchito liwu lakuti “choyamba” monga muonjezi kumatanthauza kuti zochitika zina zidzatsatira ntchito yolengeza yapadziko lonse. Zochitika zimenezo zidzaphatikizapo chisautso chachikulu ndi ulamuliro wolungama wa Kristu pa dziko lapansi latsopano zolonjezedwazo.​—Mateyu 24:21-31; Chivumbulutso 16:14-16; 21:1-4.

7. Kodi nchifukwa ninji Mulungu amafuna kuti mbiri yabwino ilalikidwe choyamba?

7 Chotero kodi nchifukwa ninji Mulungu akufuna kuti mbiri yabwino ilalikidwe choyamba? Chifukwa chimodzi nchakuti iye ali Mulungu wa chikondi, chilungamo, nzeru, ndi mphamvu. Pokwaniritsa ndemanga za Yesu zolembedwa pa Mateyu 24:14 ndi Marko 13:10, tingapeze kusonyezedwa kokhutiritsa maganizo kwa mikhalidwe imeneyi ya Yehova. Tiyeni tiipende mwachidule umodziumodzi ndi kuona mmene imagwirizanirana ndi kulalikira mbiri yabwino.

Mbiri Yabwino ndi Chikondi cha Yehova

8. Kodi ndimotani mmene kulalikidwa kwa mbiri yabwino kulili chisonyezero cha chikondi cha Mulungu? (1 Yohane 4:7-16)

8 Kodi kulalikira mbiri yabwino kumasonyeza motani chikondi cha Mulungu? Choyamba, chifukwa chakuti suli uthenga wopita ku fuko kapena ku gulu limodzi lokha. Ndi mbiri yabwino ya “mitundu yonse.” Mulungu amakonda kwambiri banja la anthu kwakuti anatumiza Mwana wake wobadwa yekha kudziko lapansi kudzakhala nsembe yadipo kaamba ka machimo a mtundu wonse wa anthu, osati fuko limodzi lokha. Mtumwi Yohane analemba kuti: “Mulungu anakonda dziko lapansi kotero, kuti anapatsa Mwana wake wobadwa yekha, kuti yense wakukhulupirira Iye asatayike, koma akhale nawo moyo wosatha. Pakuti Mulungu sanatuma Mwana wake ku dziko lapansi, kuti akaweruze dziko lapansi, koma kuti dziko lapansi likapulumutsidwe ndi Iye.” (Yohane 3:16, 17) Ndithudi mbiri yabwino, uthenga wolonjeza dziko latsopano la mtendere, kugwirizana, ndi chilungamo, ili umboni wa chikondi cha Mulungu.​—2 Petro 3:13.

Mbiri Yabwino ndi Mphamvu ya Yehova

9. Kodi nchifukwa ninji Yehova sanagwiritsire ntchito zipembedzo zamphamvu za Dziko Lachikristu kulalikira mbiri yabwino?

9 Kodi mphamvu ya Yehova imasonyezedwa motani mwa kulalikira mbiri yabwino? Talingalirani izi, kodi iye wagwiritsira ntchito yani kuchita ntchito imeneyi? Kodi ndi magulu azipembedzo amphamvu koposa a Dziko Lachikristu, monga ngati Tchalitchi cha Roma Katolika kapena mipingo yotchuka ya Chiprotesitanti? Ayi, kuloŵa kwawo m’ndale zadziko kumawalepheretsa kuchita ntchitoyi. (Yohane 15:19; 17:14; Yakobo 4:4) Chuma chawo chochuluka ndi migwirizano yawo ndi chisonkhezero chawo pa kagulu kolamulira kamphamvu sizinakondweretse Yehova Mulungu, ndiponso maphunziro awo azaumulungu ogwirizana ndi mwambo sanatero. Mphamvu yaumunthu sinafunikire kuti chifuniro cha Mulungu chichitidwe.​—Zekariya 4:6.

10. Kodi Mulungu wasankha yani kuti alalikire?

10 Zili monga momwe mtumwi Paulo ananenera m’kalata yake yopita ku mpingo wa Akorinto kuti: “Penyani maitanidwe anu, abale, kuti saitanidwa ambiri anzeru, monga mwa thupi; ambiri amphamvu, mfulu zambiri, iyayi; koma Mulungu anasankhula zopusa za dziko lapansi, kuti akachititse manyazi anzeru; ndipo zofooka za dziko lapansi Mulungu anazisankhula, kuti akachititse manyazi zamphamvu; ndipo zopanda pake za dziko lapansi, ndi zonyozeka, anazisankhula Mulungu, ndi zinthu zoti kulibe; kuti akathere zinthu zoti ziliko; kuti thupi lililonse lisadzitamande pamaso pa Mulungu.”​—1 Akorinto 1:26-29.

11. Kodi ndi mfundo zotani zonena za Mboni zimene zimazichititsa kukhala zapadera?

11 Mboni za Yehova zili ndi ziŵalo zochepa zolemera m’gulu lawo ndipo palibiretu amphamvu m’zandale zadziko. Uchete wawo wamphamvu m’nkhani zandale zadziko umatanthauza kuti alibe chisonkhezero m’zandale zadziko. Mosiyana ndi zimenezo, iwo kaŵirikaŵiri amakhala mikhole ya chizunzo chonyansa chosonkhezeredwa ndi atsogoleri achipembedzo ndi andale zadziko m’zaka za zana lino la 20. Komabe, mosasamala kanthu za chitsutso chowopsa chosonkhezeredwa pa iwo ndi ophunzira a Chinazi, Chifascism, Chikomyunizimu, utundu, ndi chipembedzo chonyenga, Mboni sizikulalikira kokha mbiri yabwino m’dziko lonse komanso zawonjezereka m’chiŵerengero modabwitsa.​—Yesaya 60:22.

12. Kodi nchifukwa ninji Mboni zakhala zachipambano?

12 Kodi Mboni zimatamanda yani kaamba ka chipambano chawo? Yesu analonjeza ophunzira ake kuti: “Mudzalandira mphamvu, Mzimu Woyera atadza pa inu: ndipo mudzakhala mboni zanga m’Yerusalemu, ndi m’Yudeya lonse, ndi m’Samariya, ndi kufikira malekezero ake a dziko.” Chotero, kodi nchiyani kwenikweni chimene chingakhale magwero a chipambano chawo? Yesu anati: “Mudzalandira mphamvu, Mzimu Woyera atadza pa inu.” Mofananamo lerolino, mphamvu yochokera kwa Mulungu, osati luso la anthu, yakhala mfungulo ya chipambano cha Mboni muutumiki wawo wapadziko lonse. Akumagwiritsira ntchito anthu ooneka ofooka kopambana, Mulungu akukwaniritsa ntchito yophunzitsa yaikulu koposa m’mbiri.​—Machitidwe 1:8; Yesaya 54:13.

Mbiri Yabwino ndi Nzeru za Yehova

13. (a) Kodi nchifukwa ninji Mboni zimatumikira modzifunira ndipo popanda malipiro? (b) Kodi Yehova wayankha motani chitonzo cha Satana?

13 Mbiri yabwino ikulalikidwa ndi odzipereka modzifunira. Yesu anati: “Munalandira kwaulere, patsani kwaulere.” (Mateyu 10:8) Chotero, palibe aliyense wa Mboni za Yehova amene amalandira malipiro chifukwa chotumikira Mulungu, ndipo samafuna malipiro. Kwenikweni, iwo samasonkhetsa konse ndalama pamisonkhano yawo. Iwo amakhala achimwemwe, kupereka kwa Mulungu yankho kwa womtonza wake, Satana Mdyerekezi, mwa utumiki wawo wodzipereka popanda dyera. Wotsutsa wauzimu wa Mulungu ameneyu kwenikweni wanena kuti anthu sangatumikire Mulungu ndi cholinga chopanda dyera. Mu nzeru zake Yehova watulutsa yankho losatsutsika ku chitonzo cha Satana​—mamiliyoni a Mboni Zachikristu zokhulupirika zikumalalikira mbiri yabwino kunyumba ndi nyumba, m’makwalala, ndi mwamwaŵi.​—Yobu 1:8-11; 2:3-5; Miyambo 27:11.

14. Kodi ‘nzeru yobisika’ imene Paulo anatchula nchiyani?

14 Umboni wina wa nzeru za Mulungu m’kuchititsa kulalikidwa kwa mbiri yabwino ndi wakuti lonjezo la Ufumu lenilenilo lili chisonyezero cha nzeru za Mulungu. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Koma tilankhula nzeru mwa angwiro; koma si nzeru ya nthaŵi yino ya pansi pano, kapena ya akulu a nthaŵi yino ya pansi pano, amene alinkuthedwa; koma tilankhula nzeru ya Mulungu m’chinsinsi, yobisikayo, imene Mulungu anaikiratu, pasanakhale nyengo za pansi pano, ku ulemerero wathu.” ‘Nzeru yobisika’ imeneyo ikutanthauza njira yanzeru ya Mulungu yothetsera chipanduko choyambidwa m’Edeni. Nzeru ya chinsinsi chopatulika chimenecho inavumbulidwa mwa Yesu Kristu, amene ali phata la mbiri yabwino ya Ufumu wa Mulungu.a​—1 Akorinto 2:6, 7; Akolose 1:26-28.

Mbiri Yabwino ndi Chilungamo cha Mulungu

15. Kodi timadziŵa motani kuti Yehova ali Mulungu wa chilungamo? (Deuteronomo 32:4; Salmo 33:5)

15 Timaona kufunika kwa liwu lakuti “choyamba” pa Marko 13:10 makamaka mogwirizana ndi chilungamo. Yehova ali Mulungu wa chilungamo chimene chimaphatikizidwa ndi kukoma mtima. Iye akunena kupyolera mwa mneneri wake Yeremiya kuti: “Wakudzitamandira adzitamandire adzikweze umo, kuti ali wakuzindikira, ndi kundidziŵa Ine, kuti ndine Yehova wakuchita zokoma mtima, chiweruziro, ndi chilungamo m’dziko lapansi, pakuti mmenemo ndikondwerera, ati Yehova.”​—Yeremiya 9:24.

16. Kodi kungachitiridwe chitsanzo motani kuti chilungamo chimafunikira kupereka chenjezo poyamba?

16 Kodi chilungamo cha Yehova chimasonyezedwa motani m’nkhani ya kulalikira mbiri yabwino? Tiyeni tiyerekezere nkhaniyi ndi mayi amene waphika keke yabwino ya chocolate imene iyenera kudyedwa pambuyo pake atafika alendo. Ngati aisiya pathebulo ya m’khitchini popanda kuuza ana ake kuti idzadyedwa liti, kodi nchiyani chimene chingakhale chikhoterero chachibadwa cha anawo? Tonsefe tinali ana panthaŵi ina! Kachala kakang’ono kadzafuna kulaŵa kekeyo! Tsopano ngati mayiyo walephera kupereka chenjezo pasadakhale, sadzakhala ndi maziko amphamvu operekera chilango. Komano, ngati anena momvekera bwino kuti kekeyo idzadyedwa pambuyo pake alendo atafika ndipo chotero siiyenera kukhudzidwa, pamenepo ndiye kuti wapereka chenjezo lomvekera bwino. Ngati pali kusamvera, iye ali ndi kuyenera kwa kuchitapo kanthu mwamphamvu ndi molungama.​—Miyambo 29:15.

17. Kodi Yehova wasonyeza motani chilungamo m’njira yapadera kuyambira 1919?

17 Yehova, m’chilungamo chake, sadzabweretsa chilango pa dongosolo ili loipa la zinthu popanda kupereka poyamba chenjezo lofunika. Nchifukwa chake, makamaka kuyambira 1919, pambuyo pakuti nkhondo yadziko yoyamba yabweretsa “zowawa,” Yehova wachititsa Mboni zake kutulukira padziko lonse lapansi zikumalalikira mwachangu mbiri yabwino. (Mateyu 24:7, 8, 14) Mitundu yonse singanene moyenerera kuti sikudziŵa za chenjezo lapadera limeneli.

Kodi Dziko Lalalikiridwa Mofalikira Chotani?

18. (a) Kodi pali umboni wotani wakuti ntchito ya Mboni yafika m’madera akutali? (b) Kodi ndi zitsanzo zina zotani zimene mumadziŵa?

18 Chisonyezero cha kugwira mtima kwa ntchito yophunzitsa yapadziko lonse imeneyi chingaonedwe m’buku lakuti Last Places​—A Journey in the North. Mlembi wake akusimba kuti pamene anafufuza pa matchati a nyanja a chisumbu chakutali cha Foula, chimodzi cha zisumbu za Shetland kumpoto kwa Scotland, matchatiwo anasonyeza kuti “kuzungulira pa chisumbu chonsecho panali WKS (wrecks [zidutswa za zophwanyika]), RKS (rocks [matanthwe]), LDGS (ledges [nsolomondo]), ndi OBS (obstructions [zopinga]).” Zimenezi “zinachenjeza woyembekezera kukhala malinyero kusayandikirako. Madzi a Foula anali malo a zida zotcheredwa onyezimira, amene anachititsa chisumbucho kukhala chosafikirika kwa amalinyero, alendo a tsiku limodzi, ndipo ngakhale gulu logwira ntchito za boma la Wolemekezeka Mfumukazi, ngakhale kuti zimenezi​—ndinadziŵa masiku angapo pambuyo pake​—sizinaletse Mboni za Yehova.” Iye anapitiriza kuti: “Monga momwe zafufuzira mosamalitsa m’matauni a mizinda yaikulu ndi Maiko Osauka kufunafuna owatembenuza, motero izo zinalalikiranso za chikhulupiriro chawo ku Foula wakutaliyo.” Iye anavomereza kuti nzika yakumaloko, Andrew, anasiyiridwa kope la Nsanja ya Olonda pakhomo pake miyezi ingapo kumbuyoko. Ndiyeno anawonjezera kuti: “Mlungu umodzi pambuyo pake ndinatha kuona kope la [Galamukani! m’Chidanishi] pa Faeroes [zisumbu za ku North Sea] ndipo miyezi iŵiri pambuyo pake kope la [Nsanja ya Olonda m’Chidanishi] ku Nuuq, ku Greenland.” Ndi umboni wolongosoka wotani nanga wa ntchito yachangu ya Mboni za Yehova m’zigawo zakumpoto zimenezo!

Kodi Nchiyani Chimene Chimasonkhezera Mbonizo Kupitirizabe?

19, 20. (a) Kodi nchiyani chimene chimasonkhezera Mboni za Yehova kupitiriza kulalikira? (b) Kodi ndi mafunso otani amene adzayankhidwa kenako?

19 Ndithudi, kulalikira kunyumba ndi nyumba kwa osawadziŵa si nkhani yokhweka, mosasamala kanthu kuti munthu wakhala Mboni kwa zaka zochuluka motani. Nangano nchiyani chimene chimasonkhezera Akristu ameneŵa kupitirizabe? Kudzipereka kwawo Kwachikristu ndi lingaliro la thayo. Paulo analemba kuti: “Pakuti ngati ndilalikira Uthenga Wabwino ndilibe kanthu kakudzitamandira; pakuti chondikakamiza ndigwidwa nacho; pakuti tsoka ine ngati sindilalikira Uthenga Wabwino.” Akristu oona ali ndi uthenga umene umatanthauza moyo, chotero kodi iwo angathe motani kuusunga osauza ena? Lamulo la mkhalidwe lenileni la liwongo la mwazi chifukwa cha kulephera kupereka chenjezo m’nthaŵi ya ngozi ndilo chifukwa champhamvu cha kulalikirira mbiri yabwino.​—1 Akorinto 9:16; Ezekieli 3:17-21.

20 Pamenepo, kodi mbiri yabwino ikulalikidwa motani? Kodi nchiyani chimene chili mfungulo ya chipambano cha Mboni? Kodi ndi mbali zotani za utumiki wawo ndi gulu zimene zimathandiza kuzizindikiritsa kukhala chipembedzo choona? Nkhani yathu yotsatira idzayankha mafunso amenewo.

[Mawu a M’munsi]

a Kuti mupeze malongosoledwe owonjezereka a nzeru za Mulungu ndi “chinsinsi chopatulika,” onani Insight on the Scriptures, Voliyumu II, tsamba 1190, yofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.

Kodi Mukukumbukira?

◻ Kodi nchiyani chimene chimasiyanitsa Mboni za Yehova ndi atsogoleri achipembedzo?

◻ Kodi kulalikira kumasonyeza motani chikondi, mphamvu, ndi nzeru za Mulungu?

◻ Kodi kulalikira mbiri yabwino kumasonyeza motani chilungamo cha Mulungu?

◻ Kodi nchiyani chimene chimasonkhezera Mboni za Yehova kupitirizabe muutumiki wawo?

[Zithunzi patsamba 15]

Mosasamala kanthu kuti anthu angakhale kutali motani, Mboni za Yehova zimafuna kuwafikira

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena