Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w91 12/15 tsamba 5-7
  • Krisimasi—kodi Ndiyo Njira Yolandirira Yesu?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Krisimasi—kodi Ndiyo Njira Yolandirira Yesu?
  • Nsanja ya Olonda—1991
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • ‘Ngati Lipenga Lipereka Mawu Osazindikirika’
  • ‘Kupindula Anthu’
  • “Akristu Obisika” Sanabwezeretsedwe
  • Kubwezeretsedwa ku Chikristu Chowona
  • Chiyambi cha Krisimasi Yamakono
    Nsanja ya Olonda—1997
  • N’chifukwa Chiyani a Mboni za Yehova Sakondwerera Khirisimasi?
    Mafunso Ofunsidwa Kawirikawiri
  • Krisimasi—kodi Nchifukwa Ninji Iri Yotchuka Kwambiri M’japani?
    Nsanja ya Olonda—1991
  • N’chifukwa Chiyani Anthu Ena Sachita Nawo Khirisimasi?
    Nsanja ya Olonda—2012
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1991
w91 12/15 tsamba 5-7

Krisimasi​—kodi Ndiyo Njira Yolandirira Yesu?

KUBADWA kwa Mpulumutsi, Mesiya woyembekezeredwa kwa nthaŵi yaitali, kunalidi nthaŵi yachisangalalo. Mngelo analengeza kwa abusa pafupi ndi Betelehemu kuti: ‘Onani, ndikuuzani inu uthenga wabwino wa chikondwero chachikulu, chimene chidzakhala kwa anthu onse; pakuti wakubadwirani inu lero, m’mudzi wa Davide, Mpulumutsi, amene ali Kristu Ambuye.’ Ndipo khamu la angelo linagwirizana naye, kutamanda Mulungu: ‘Ulemerero ukhale kwa Mulungu kumwambamwamba, ndi mtendere pansi pano mwa anthu amene akondwera nawo.’ (Luka 2:10-14) Ena angagamule kuti Akristu ayenera kutsanzira angelowo m’kusonyeza chimwemwe chawo pa kudza kwa Kristu ku dziko lapansi pa nthaŵiyo.

Ichi sichinali cholembedwa choyamba cha Baibulo cha kuimba mokondwera nyimbo za chitamando kwa angelo. Pamene maziko a dziko lapansi anayalidwa, ‘nyenyezi za m’maŵa zinaimba limodzi mokondwera, ndi ana onse a Mulungu anafuula ndi chimwemwe.’ (Yobu 38:4-7) Deti lenileni la chochitika chimenechi silinalembedwe m’Baibulo. (Genesis 1:1, 14-18) Mosasamala kanthu kuti chochitikacho chinali chosangalatsa, Akristu sananene kuti popeza kuti angelo anakondwera, iwo ayenera kukondwerera kulengedwa kwa dziko lapansi chaka ndi chaka ndipo mwinamwake kutengera phwando lachikunja kukumbukira chochitikacho.

Komabe zimenezo ndizo zomwe anthu amene amakondwerera Krisimasi akuchita ndi kubadwa kwa Yesu Kristu. Kupenda mabuku anazonse ambiri odalirika pansi pamutu wakuti “Krisimasi” kumatsimikizira kuti deti la kubadwa kwa Yesu nlosadziŵika. Baibulo silimanena kalikonse za detilo.

‘Ngati Lipenga Lipereka Mawu Osazindikirika’

‘Mulungu sali Mulungu wa chisokonezo koma wa mtendere,’ analemba motero mtumwi Paulo, powongolera chisokonezeko cha mpingo m’Korinto wakale. M’mawu amodzimodziwo, iye anafunsa kuti: ‘Ngati lipenga lipereka mawu osazindikirika, adzadzikonzera ndani kunkhondo?’ (1 Akorinto 14:8, 33) Tsopano, ngati Mulungu wadongosolo anafuna kuti Akristu adzikondwerera kubadwa kwa Mwana wake padziko lapansi, kodi Iye akanasiira anthu opanda ungwiro kusankha mwadala deti lotengedwa kumapwando achikunja ndi kutengera machitachita opanda umulungu?

Kusanthula zitsanzo zoŵerengeka Zabaibulo kumamveketsa kuti Yehova Mulungu samachita ndi anthu ake mwanjira imeneyo. Pamene anafuna kuti Aisrayeli adzisunga zikondwerero zapachaka pansi pa Chilamulo cha Mose, Mulungu anapereka madeti akutiakuti ndi kuwauza mmene akachitira mapwando amenewo. (Eksodo 23:14-17; Levitiko 23:34-43) Yesu Kristu, ngakhale kuti sanalamule konse kuti kubadwa kwake kukumbukiridwe, analamula otsatira ake kusunga deti limodzi lokha. “Usiku uja anaperekedwa,” Nisani 14, 33 C.E., Yesu anayambitsa chikondwerero cha Mgonero wa Ambuye, akumagwiritsira ntchito mkate wopanda chotupitsa ndi vinyo. Iye analamula kuti: ‘Chitani ichi chikhale chikumbukiro changa.’ (1 Akorinto 11:23, 24) Lipenga lopereka mawu onena za nthaŵi ndi mmene Mgonero wa Ambuye uyenera kuchitidwira linali lomveka ndi losakaikirika. Pamenepo bwanji nanga za Krisimasi? Palibe paliponse m’Baibulo pamene timapeza lamulo lirilonse lakukondwerera kubadwa kwa Kristu, ndiponso silimatiuza nthaŵi ndi mmene chikondwererocho chingachitidwire.

‘Kupindula Anthu’

“Inde ndithu, ndimadziŵa kuti Krisimasi ili ndi chiyambi chachikunja,” anatero mtsogoleri wina wachipembedzo wa Tchalitchi cha Ziyoni ku Tokyo, “koma malinga ngati anthu wamba ali osangalatsidwa m’Chikristu pa December 25 ndipo amabwera kudzaphunzira ziphunzitso za Yesu Wolemekezekayo, Krisimasi ili ndi malo ake m’Chikristu.” Ambiri amagwirizana ndi kulingalira kwake. Kodi mumakhulupirira kuti kulolera molakwa koteroko kuli koyenera?

Ena amapereka chigomeko chakuti ngakhale Paulo analolera molakwa kuti apindule okhulupirira. Analemba kuti: “Ndimadzipanga kukhala kapolo wa munthu aliyense, kuti ndipindule anthu ochuluka monga momwe kungathekere . . . Pamene ndiri ndi Amitundu, ndimakhala ngati Wamitundu, wokhala kunja kwa Chilamulo Chachiyuda, kuti ndipindule Amitundu. . . . Zonsezi ndimachita kaamba ka uthenga wabwino, kuti ndilandireko madalitso ake.” (1 Akorinto 9:19-23, Today’s English Version) Kodi mawu ameneŵa amapereka chifukwa chotengera phwando lachikunja kuti tikope Amitundu kubwera m’Chikristu?

Talingalirani mosamalitsa za mawu apatsogolo ndi apambuyo a ndemanga ya Paulo. M’vesi 21, iye anati: “Izi sizikutanthauza kuti sindimvera lamulo la Mulungu; ndiridi pansi pa lamulo la Kristu.” (TEV) Chotero sanalolere molakwa pankhani zimene zinalumpha lamulo la Kristu, koma ‘anakhala ngati Wamitundu’ mwakulemekeza miyambo yakumaloko ndi zizoloŵezi malinga ngati izi sizinali zosemphana ndi malamulo Achikristu.a

Mukumakumbukira zimenezi, talingalirani mmene kutengera mapwando achikunja kuloŵa “m’Chikristu” m’dzina la Krisimasi kukawonekera pamene tikulingalira moyerekezera ndi lamulo la Baibulo lotsatirali: ‘Musakhale omangidwa m’goli ndi osakhulupira osiyana; pakuti chilungamo chigawana bwanji ndi chosalungama? . . . Kapena wokhulupira ali nalo gawo lanji pamodzi ndi wosakhulupira? . . . Chifukwa chake, Tulukani pakati pawo, ndipo patukani, ati [Yehova, NW], ndipo musakhudza kanthu kosakonzeka; ndipo ine ndidzalandira inu.’ (2 Akorinto 6:14-17) Mosasamala kanthu za chodzikhululukira chimene chingaperekedwe, kusukulutsa Chikristu ndi mapwando achikunja sikuli njira yolandirira Yesu monga Mpulumutsi. Kukanakhala kosayenera m’zaka za zana loyamba pamene Yesu anadza m’thupi, ndipo nkosayenera lerolino kapena mtsogolo, pamene Kristu adzadza monga Mfumu kudzapereka ziweruzo za Mulungu. (Chibvumbulutso 19:11-16) Kwenikwenidi, awo amene amakonda kukondwerera mapwando achikunja mwakuwabisa “m’Chikristu” amakanadi Yesu Kristu.

“Akristu Obisika” Sanabwezeretsedwe

Phunzirani kanthu ku zimene zinachitikira Akatolika m’Japani m’nyengo ya ulamuliro wa akazembe ankhondo. Pamene kutsendereza kwa Chikatolika kunayamba mu 1614, Akatolika a ku Japani okwanira 300,000 anali ndi zosankha zitatu: kukhala ofera chikhulupiriro, kusiya chikhulupiriro chawo, kapena kuchita zinthu mobisa. Awo amene anachita zinthu mobisa anatchedwa Akristu obisika. Kuti aphimbe chikhulupiriro chawo, anagwirizana ndi miyambo yosiyanasiyana Yachibuda ndi Chishinto. M’mapemphero awo, anagwiritsira ntchito Maria Kannon, amene anali Mariya wobisidwa monga bodhisattva Wachibuda mumpangidwe wa mayi wonyamula mwana. Mapwando awo anasakaniza miyambo ya chipembedzo ya Chibuda, Chikatolika ndi chipembedzo chamwambo. Komabe, pamene anakakamizidwa kufika pamaliro Achibuda, iwo anapereka mapemphero Achikristu ndi kupanga mwambo wa modoshi, dzoma lothetsera utumiki Wachibuda. Kodi nchiyani chimene chachitika kwa “Akristu” amenewo?

“Malinga ndi kunena kwa a Kirishitans [Akristu] ambiri, kugwirizana kwachipembedzo kunakula mwa iwo kukupanga kukhala kovuta kusiya kulambira milungu Yachishinto ndi Chibuda,” likufotokoza motero bukhu la The Hidden Christians. Pamene chiletsocho chinachotsedwa ndipo amishonale Achikatolika anabwerera ku Japani, ambiri a “Akristu obisika” amenewo anamamatira ku mtundu wawo wa chipembedzo cha zikhulupiriro zosakaniza.

Komabe, kodi Tchalitchi cha Katolika chingasulizedi “Akristu obisika” amenewo amene anakana kubwezeretsedwa ku Roma Katolika? Mofananamo Tchalitchi cha Katolika chatengera ziphunzitso zambiri ndi mapwando achikunja, kuphatikizapo Krisimasi. Ngati Akatolika ndi Aprotesitanti, ngakhale kuti amadzitcha kukhala Akristu, apanga “Chikristu” chawo kukhala chachikunja ndi mapwando achikunja, kodi nawonso sakukana Yesu Kristu?

Kubwezeretsedwa ku Chikristu Chowona

Setsuko, Mkatolika wodzipereka kwa zaka 36, pomalizira pake anazindikira zimenezo. Pambuyo pa Nkhondo Yadziko ya II, anayesa kudzaza mbali yake yauzimu yopanda kanthu mwakuyanjana ndi tchalitchi cha Katolika. Pamene anafika pa Misa ya Krisimasi ndikuwona mitengo ya Krisimasi yokongola kunja ndi mkati mwa tchalitchi chake iye analingalira kuti ‘Nzokhutiritsa motani nanga!’ “Ndinanyadira zokometsera zathu zokongola, zomwe zinaposa za matchalitchi oyandikana nawo,” iye anatero. Chikhalirechobe, Setsuko sanamvetsetse kwenikweni ziphunzitso za Katolika, ngakhale kuti anaphunzitsa pa sukulu ya Sande kwa kanthaŵi ndithu. Chotero pamene anafuna kudziloŵetsa kwambiri m’ntchito ya tchalitchi, anafunsa wansembe wake mafunso oŵerengeka. M’malo moyankha mafunso ake, wansembeyo anamnyoza. Atakhumudwa, analingalira zoliphunzira yekha Baibulo. Milungu iŵiri pambuyo pake, Mboni za Yehova zinamchezera, ndipo anavomera phunziro Labaibulo lapanyumba.

Iye akulongosola kuti: “Zinali zopweteka kuyang’anizana ndi zowonadi za Baibulo zimene zinatsutsa zikhulupiriro zanga zakale. Ndinafikira pa kudwala alopecia neurotica, kuthothoka kwa tsitsi chifukwa cha kukhumudwa. Komabe, mwapang’onopang’ono, kuunika kwa chowonadi kunaŵala mumtima mwanga. Ndinadabwa kuphunzira kuti Yesu sakanabadwa m’mwezi wozizira, wamvula wa December, pamene abusa sangamaŵete nkhosa zawo pabwalo usiku. (Luka 2:8-12) Kuzindikira zimenezo kunasintha lingaliro langa la kubadwako, popeza kuti tinali kugwiritsira ntchito thonje monga chipale chofeŵa kukongoletsa zithunzithunzi za nkhosa ndi abusa.”

Pamene anatsimikizira iyemwini zimene Baibulo limaphunzitsadi, Setsuko anasankha kuleka kukondwerera Krisimasi. Iye samakhalanso ndi “mzimu wa Krisimasi” kamodzi pachaka koma amasonyeza mzimu wa kupatsa Kwachikristu tsiku lirilonse.

Ngati mumakhulupirira Kristu mowona mtima, musakwiye pamene muwona akunja akuipitsa Krisimasi. Iwo akungobwereza chimene inali poyambirira​—phwando lachikunja. Krisimasi simatsogolera aliyense kulandira Yesu Kristu, amene anabwerera mosawoneka monga Mfumu yakumwamba. (Mateyu, mitu 24 ndi 25; Marko, mutu 13; Luka, mutu 21) M’malomwake, Akristu owona amasonyeza mzimu wonga wa Kristu chaka chonse, ndipo amalengeza mbiri yabwino ya Ufumu, umene Yesu anakhala Mfumu. Mmenemo ndimmene Mulungu amafunira kuti tilandirire Yesu Kristu monga Mpulumutsi wathu ndi Mfumu ya Ufumuwo.​—Salmo 2:6-12.

[Mawu a M’munsi]

a Yerekezerani njira ziŵiri zimene Paulo anachitira pankhani ya mdulidwe. Ngakhale kuti anadziŵa kuti “mdulidwe ulibe kanthu,” anamdula mnzake woyenda naye Timoteo, amene anali Myuda kumbali ya amake. (1 Akorinto 7:19; Machitidwe 16:3) M’nkhani ya Tito, mtumwi Paulo anapeŵa kumdula chifukwa cholimbana ndi Ayuda. (Agalatiya 2:3) Tito anali Mgiriki ndipo chotero, mosiyana ndi Timoteo, analibe chifukwa chenicheni chodulidwira. Ngati iye, Wamitundu, akanati adulidwe, ‘Kristu sakanapindula naye kanthu.’​—Agalatiya 5:2-4.

[Chithunzi patsamba 7]

Akristu owona amalemekeza Yesu chaka chonse

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena