-
Kodi Baibulo Limanena Zotani pa Nkhani ya Mowa?Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
-
-
Kodi Baibulo Limanena Zotani pa Nkhani ya Mowa?
Anthu padzikoli amakhala ndi maganizo osiyanasiyana pa nkhani ya mowa. Ena amasankha kumwa mowa ndi anzawo akamacheza. Pomwe ena amasankha kuti asamamwe mowa. Anthu enanso amamwa mowa n’kufika poledzera. Ndiye kodi Baibulo limanena zotani pa nkhani ya mowa?
1. Kodi kumwa mowa n’kulakwa?
Baibulo silinena kuti kumwa mowa n’kulakwa. M’malomwake, likamanena za zinthu zabwino zambiri zimene Mulungu watipatsa, limatchulanso za “vinyo amene amasangalatsa mtima wa munthu.” (Salimo 104:14, 15) Ndipotu, amuna ndi akazi ena okhulupirika otchulidwa m’Baibulo ankamwa mowa.—1 Timoteyo 5:23.
2. Kodi Baibulo limapereka malangizo otani kwa amene asankha kumwa mowa?
Yehova amaletsa kumwa mowa mwauchidakwa komanso kuledzera. (Agalatiya 5:21) Mawu ake amati: “Usakhale pakati pa anthu omwa vinyo kwambiri.” (Miyambo 23:20) Choncho tikasankha kumwa mowa, ngakhale tili patokha, sitiyenera kumwa wambiri mpaka kufika polephera kuganiza bwino, kulephera kulankhula ndi kuchita zinthu zanzeru kapenanso kufika powononga thanzi lathu. Komabe, ngati zikutivuta kumwa mowa modziletsa, tingachite bwino kungosiyiratu.
3. Kodi tingasonyeze bwanji kuti timalemekeza zimene anthu ena anasankha pa nkhani ya mowa?
Munthu aliyense ayenera kusankha yekha ngati akufuna kumamwa mowa kapena ayi. Munthu wina akasankha kumwa mowa mosapitirira malire, tisamamuweruze. Komanso ngati wina wasankha kusamwa mowa, tisamamukakamize kuti ayambe kumwa. (Aroma 14:10) Komabe, tingasankhe kusamwa mowa ngati ena angakhumudwe kapena ngati kumwa mowa kungabweretse mavuto kwa anthu ena. (Werengani Aroma 14:21.) Timayesetsa kupewa kuchita zinthu ‘zopindulitsa ife tokha basi,’ koma timachita ‘zopindulitsanso anthu ena.’—Werengani 1 Akorinto 10:23, 24.
FUFUZANI MOZAMA
Onani mfundo za m’Baibulo zimene zingakuthandizeni kusankha kumwa mowa kapena ayi komanso kuchuluka kwa mowa womwe mungamamwe. Onaninso zomwe mungachite ngati muli ndi vuto lomwa mowa mosadziletsa.
4. Mungasankhe kumwa mowa kapena ayi
Kodi maganizo a Yesu anali otani pa nkhani ya mowa? Kuti tiyankhe funsoli, tiyeni tione chozizwitsa choyamba chimene Yesu anachita. Werengani Yohane 2:1-11, kenako mukambirane mafunso awa:
Malinga ndi zimene tawerengazi, kodi maganizo a Yesu ndi otani pa nkhani ya mowa, nanga amawaona bwanji anthu amene amasankha kumwa mowa?
Popeza Yesu saona kuti kumwa mowa n’kulakwa, kodi Mkhristu ayenera kumuona bwanji munthu amene wasankha kumwa mowa?
Ngakhale kuti Mkhristu ali ndi ufulu wosankha kumwa mowa, pa nthawi zina, singakhale nzeru kuchita zimenezi. Werengani Miyambo 22:3, kenako onani mmene mfundo zotsatirazi zingakuthandizireni kudziwa ngati muyenera kumwa mowa kapena ayi:
Ngati mukufunika kuyendetsa galimoto kapena kugwiritsa ntchito mashini enaake.
Ngati ndinu woyembekezera.
Ngati dokotala wakuuzani kuti musamwe mowa.
Ngati mumamwa mowa mosadziletsa.
Ngati lamulo lam’dziko lanu likukuletsani kumwa mowa.
Ngati muli ndi munthu amene wasankha kusamwa mowa chifukwa chakuti m’mbuyomo ankamwa mowa mosadziletsa.
Kodi n’chiyani chingakuthandizeni kudziwa ngati ndi zoyenera kukhala ndi mowa paphwando la ukwati kapena pa zochitika zina? Kuti mudziwe zoyenera kuchita, onerani VIDIYO.
Werengani Aroma 13:13 ndi 1 Akorinto 10:31, 32. Pambuyo powerenga lemba lililonse, mukambirane funso ili:
Kodi kugwiritsa ntchito mfundo yamulembali kungakuthandizeni bwanji kusankha zinthu zimene zingasangalatse Yehova?
Mkhristu aliyense amasankha yekha kumwa mowa kapena ayi. Ngakhale mkhristu yemwe amamwa mowa, nthawi zina angasankhe kusamwa
5. Ganizirani kuchuluka kwa mowa womwe mungamwe
Ngati mwasankha kumwa mowa, muzikumbukira mfundo iyi: Ngakhale kuti Yehova saletsa kumwa mowa, koma amaletsa kumwa mowa mwauchidakwa. N’chifukwa chiyani zimenezi zili choncho? Werengani Hoseya 4:11, 18, kenako mukambirane funso ili:
N’chiyani chingachitike ngati munthu atamwa mowa wambiri?
N’chiyani chingatithandize kuti tisamwe mowa wambiri? Tiyenera kuzindikira malire athu n’kupewa kumwa mowa mopitirira muyezo. Werengani Miyambo 11:2, kenako mukambirane funso ili:
N’chifukwa chiyani muyenera kudziikira malire a mowa womwe muyenera kumamwa?
6. N’chiyani chimene chingathandize munthu kusiya kumwa mowa mopitirira malire?
Onani zomwe zinathandiza munthu wina kusiya kumwa mowa mopitirira malire. Onerani VIDIYO, kenako mukambirane mafunso awa:
Kodi Dmitry ankatani akaledzera?
Kodi anakwanitsa kusiya kumwa mowa kamodzin’kamodzi?
N’chiyani chinamuthandiza kuti asiyiretu kumwa mowa mwauchidakwa?
Werengani 1 Akorinto 6:10, 11, kenako mukambirane mafunso awa:
Kodi Baibulo limanena zotani pa nkhani ya kumwa mowa mwauchidakwa?
N’chiyani chikusonyeza kuti munthu yemwe amamwa mowa mopitirira malire akhoza kusintha?
Werengani Mateyu 5:30, kenako mukambirane funso ili:
Pamene Yesu amanena za kudula dzanja ankatanthauza kuti tiyenera kulolera kusiya kuchita zinazake ndi cholinga choti tisangalatse Yehova. Kodi mungatani ngati zikukuvutani kusiya kumwa mowa mwauchidakwa?a
Werengani 1 Akorinto 15:33, kenako mukambirane funso ili:
Kodi n’chiyani chimene chingakuchitikireni ngati mumacheza ndi anthu omwe amakonda kumwa mowa wambiri?
MUNTHU WINA ANGAKUFUNSENI KUTI: “Kodi kumwa mowa n’kulakwa?”
Kodi mungamuyankhe bwanji?
ZOMWE TAPHUNZIRA
Mowa ndi mphatso imene Yehova anatipatsa kuti tizisangalala. Koma iye safuna kuti tizimwa mowa wambiri kapena kuledzera.
Kubwereza
Kodi Baibulo limanena zotani pa nkhani ya mowa?
Kodi kumwa mowa wambiri kumabweretsa mavuto otani?
Kodi tingasonyeze bwanji kuti timalemekeza zimene anthu ena anasankha pa nkhani ya mowa?
ONANI ZINANSO
Kodi achinyamata angasankhe bwanji zinthu mwanzeru pa nkhani ya mowa?
Onani njira zimene muyenera kutsatira kuti muthane ndi vuto lomwa mowa mosadziletsa.
“Khalani ndi Maganizo Oyenera Pankhani ya Kumwa Mowa” (Nsanja ya Olonda, January 1, 2010)
Kodi Mkhristu ayenera kuchita nawo mwambo wowombanitsa mabotolo kapena matambula azakumwa?
“Mafunso Ochokera kwa Owerenga” (Nsanja ya Olonda, February 15, 2007)
Munkhani yakuti, “Ndinali Mbiyang’ambe,” onani zimene zinathandiza munthu wina kuti asiye kumwa mowa mwauchidakwa.
a Anthu amene mowa unawalowerera kwambiri angafunike thandizo lachipatala kuti akwanitse kusiya. Ndipotu madokotala ambiri amanena kuti anthu amene anali ndi vuto limeneli sayenera kumwa mowa n’komwe.
-
-
Tizivala Ndi Kudzikongoletsa MoyeneraMungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
-
-
PHUNZIRO 52
Tizivala Ndi Kudzikongoletsa Moyenera
Tonsefe timasankha zimene tikufuna kuvala komanso mmene tikufuna kudzikongoletsera. Komabe, tikamatsatira mfundo za m’Baibulo zokhudza nkhaniyi, tingamavale zovala zimene timakonda koma zomwe sizingakhumudwitse Yehova. Tiyeni tione zina mwa mfundo zimenezi.
1. Ndi mfundo ziti zimene zingatithandize kuti tizisankha kuvala ndi kudzikongoletsa moyenera?
Tiyenera kusankha “zovala zoyenera, povala mwaulemu ndi mwanzeru” ndipo nthawi zonse tizioneka bwino kuti anthu ena aziona kuti ndife anthu amene “amalemekeza Mulungu.” (1 Timoteyo 2:9, 10) Tiyeni tione mfundo 4 izi: (1) Zovala zathu zizikhala “zoyenera.” Mwina munaona kuti pamisonkhano yathu timavala mosiyanasiyana. Komabe, zomwe timavala komanso mmene timametera kapena kukonzera tsitsi lathu, zimasonyeza kuti timalemekeza Mulungu amene timamulambira. (2) Kuvala “mwaulemu” kumatanthauza kupewa kuvala zovala zimene zingachititse anthu kuganizira zachiwerewere, kapenanso kuti azingoganizira za ifeyo basi. (3) Timasonyezanso kuti timavala “mwanzeru” tikamapewa kumangotengera sitayiro iliyonse yatsopano yakavalidwe ndi kudzikongoletsa. (4) Timayesetsa kuti nthawi zonse tizioneka monga anthu amene “amalemekeza Mulungu” moti anthu ena sangavutike kuzindikira kuti timalambira Mulungu woona.—1 Akorinto 10:31.
2. N’chifukwa chiyani tiyenera kuganizira abale ndi alongo athu tikamasankha zomwe tikufuna kuvala?
N’zoona kuti tili ndi ufulu wosankha zimene tikufuna kuvala, komabe ndi bwino kuganizira mmene kavalidwe kathu kangakhudzire anthu ena. Timapewa kukhumudwitsa ena ndipo timayesetsa “kuwakondweretsa pa zinthu zabwino zowalimbikitsa.”—Werengani Aroma 15:1, 2.
3. Kodi kavalidwe kathu kangathandize bwanji anthu ena kuti ayambe kuphunzira za Yehova?
Ngakhale kuti nthawi zonse timavala bwino, koma timayesetsa kuvala bwino kwambiri tikamapezeka pamisonkhano yampingo komanso tikamalalikira uthenga wabwino. Sitimafuna kuti anthu ena alephere kumvetsera uthenga wabwino chifukwa cha mmene tavalira. M’malomwake, timafuna kuti kaonekedwe kathu kazithandiza anthu ena kukopeka ndi uthenga wabwino ndiponso ‘kuti kazikometsera chiphunzitso cha Mpulumutsi wathu.’—Tito 2:10.
FUFUZANI MOZAMA
Onani zimene tingachite kuti anthu ena asamavutike kuzindikira kuti ndife Akhristu akamaona mmene timavalira ndi kudzikongoletsera.
Zomwe timavala zingasonyeze ngati timalemekeza kapena sitilemekeza anthu omwe ali ndi udindo. Ngakhale kuti Yehova amaona zimene zili mumtima, tingasonyeze kuti timamulemekeza povala ndi kudzikongoletsa moyenera
4. Tikamaoneka bwino timalemekeza Yehova
Kodi ndi chifukwa chachikulu chiti chimene chiyenera kutipangitsa kuti tizisamala ndi mmene timaonekera? Werengani Salimo 47:2, kenako mukambirane mafunso awa:
Kodi kukumbukira kuti timaimira Yehova kungatithandize bwanji tikamasankha zomwe tikufuna kuvala?
Kodi mukuona kuti ndi nzeru kuganizira mmene timaonekera tikakhala pamisonkhano komanso tikamalalikira? N’chifukwa chiyani mukutero?
5. Zimene tingachite kuti tizivala ndi kudzikongoletsa moyenera
Zovala zathu zizikhala zoyera ndiponso zoyenera malo amene tili, kaya zikhale zodula kapena zotchipa. Werengani 1 Akorinto 10:24 ndi 1 Timoteyo 2:9, 10. Kenako, mukambirane chifukwa chake tiyenera kupewa kuvala zovala . . .
zakuda kapena zosalongosoka.
zothina, zoonekera mkati kapenanso zomwe zingachititse anthu ena kuganizira zachiwerewere.
Ngakhale kuti Akhristu masiku ano satsatira chilamulo cha Mose, angadziwe maganizo a Yehova pa nkhani yakavalidwe kuchokera m’Chilamulochi. Werengani Deuteronomo 22:5, kenako mukambirane funso ili:
N’chifukwa chiyani tiyenera kupewa kuvala ndi kudzikongoletsa m’njira imene imachititsa kuti amuna azioneka ngati akazi kapenanso akazi azioneka ngati amuna?
Werengani 1 Akorinto 10:32, 33 ndi 1 Yohane 2:15, 16, kenako mukambirane mafunso awa:
N’chifukwa chiyani ndi bwino kuganizira mmene kaonekedwe kathu kangakhudzire anthu am’dera lathu kapenanso amumpingo wathu?
Kodi kumene mumakhala, anthu amakonda kuvala ndi kudzikongoletsa m’njira yotani?
Kodi mumaona kuti ena mwa masitayilowo sangakhale oyenera kwa Mkhristu? N’chifukwa chiyani mukutero?
Tikhoza kuvala komanso kudzikongoletsa m’njira zosiyanasiyana n’kumasangalatsabe Yehova
ZIMENE ENA AMANENA: “Ndi ufulu wanga kuvala chilichonse chomwe ndikufuna.”
Kodi nanunso mumaona choncho? N’chifukwa chiyani mukutero?
ZOMWE TAPHUNZIRA
Tikamasankha bwino zomwe tikufuna kuvala komanso mmene tingadzikongoletsere, timasonyeza kuti timalemekeza Yehova ndi anthu ena.
Kubwereza
N’chifukwa chiyani Yehova amafuna kuti tizivala komanso kudzikongoletsa moyenera?
Kodi ndi mfundo ziti zimene zingatithandize kuti tizisankha mwanzeru zimene tikufuna kuvala komanso mmene tingadzikongoletsere?
Kodi mmene timavalira ndi kudzikongoletsera zingachititse kuti anthu ena aziona bwanji kulambira kwathu?
ONANI ZINANSO
Werengani nkhaniyi kuti mudziwe zomwe ena angaganize akaona zimene mumavala.
“Kodi Ndimakonda Kuvala Zovala Zotani?” (Nkhani yapawebusaiti)
Onani chifukwa chake muyenera kumaganiza kaye musanasankhe kukhala ndi matatuu.
“Kodi Baibulo Limati Chiyani pa Nkhani Yodzilemba Matatuu?” (Nkhani yapawebusaiti)
Onani mfundo zinanso zomwe zingatithandize posankha zochita.
“Kodi Mavalidwe Anu Amalemekeza Mulungu?” (Nsanja ya Olonda, September 2016)
-