-
Amuna, Kodi Mumagonjera Khristu Monga Mutu Wanu?Nsanja ya Olonda—2010 | May 15
-
-
Amuna, Kodi Mumagonjera Khristu Monga Mutu Wanu?
“Mutu wa mwamuna aliyense ndi Khristu.”—1 AKOR. 11:3.
1. Perekani umboni wakuti Yehova ndi Mulungu wa dongosolo.
LEMBA la Chivumbulutso 4:11 limati: “Ndinu woyenera, inu Yehova Mulungu wathu, kulandira ulemerero, ndi ulemu, ndi mphamvu, chifukwa munalenga zinthu zonse, ndipo chifukwa cha chifuniro chanu, zinakhalapo, inde zinalengedwa.” Chifukwa chakuti analenga zonse, Yehova Mulungu ndi Mfumu yaikulu m’chilengedwe chonse ndipo ndi wolamulira wa zonse zimene analenga. Umboni wakuti Yehova “si Mulungu wa chisokonezo, koma wa mtendere,” umaoneka ndi mmene iye walinganizira angelo ake.—1 Akor. 14:33; Yes. 6:1-3; Aheb. 12:22, 23.
2, 3. (a) Kodi poyambirira Yehova analenga ndani? (b) Kodi Mwana woyamba kubadwa ali ndi udindo wotani poyerekeza ndi Atate?
2 Zinthu zonse zisanalengedwe, Mulungu analiko yekhayekha kwa zaka zosawerengeka. Poyambirira penipeni, iye analenga munthu wauzimu wotchedwa “Mawu” chifukwa anali Wolankhulira Yehova. Zinthu zina zonse zinalengedwa pogwiritsa ntchito Mawuyo. Kenako iye anabwera padziko lapansi ngati munthu ndipo anatchedwa Yesu Khristu.—Werengani Yohane 1:1-3, 14.
3 Kodi Malemba amati chiyani pa nkhani ya udindo umene Mulungu ndiponso Mwana wake woyamba ali nawo? Polemba mouziridwa ndi Mulungu mtumwi Paulo anati: “Ndikufuna mudziwe kuti mutu wa mwamuna aliyense ndi Khristu; ndi mutu wa mkazi ndi mwamuna; ndi mutu wa Khristu ndiye Mulungu.” (1 Akor. 11:3) Khristu amagonjera Atate monga mutu wake. Mfundo ya umutu ndiponso kugonjera n’zofunika kuti pakati pa angelo komanso anthu pakhale mtendere ndiponso kuti zinthu zizichitika mwadongosolo. Ngakhale Yesu amene “kudzera mwa iye zinthu zina zonse zinalengedwa,” amafunika kugonjera Mulungu yemwe ndi mutu wake.—Akol. 1:16.
4, 5. Kodi Yesu ankaona bwanji udindo wake poyerekezera ndi wa Yehova?
4 Kodi Yesu anamva bwanji ndi mfundo yoti ayenera kugonjera Yehova ndiponso kubwera padziko lapansi? Malemba amati: ‘Khristu Yesu ngakhale kuti anali ndi maonekedwe a Mulungu, kukhala wolingana ndi Mulungu sanakuganizirepo ngati chinthu choti angalande. Sanatero ayi, koma anakhuthula zonse za mwa iye n’kukhala ngati kapolo, nakhala wofanana ndi anthu. Kuposanso pamenepo, atakhala munthu, anadzichepetsa nakhala womvera mpaka imfa, inde, imfa ya pa mtengo wozunzikirapo.’—Afil. 2:5-8.
5 Nthawi zonse Yesu ankagonjera modzichepetsa chifuniro cha Atate wake. Iye anati: “Ine sindingachite chilichonse chongoganiza ndekha; . . . ndipo chiweruzo chimene ndimapereka n’cholungama, chifukwa sinditsatira chifuniro changa, koma chifuniro cha amene anandituma ine.” (Yoh. 5:30) Pa nthawi ina iye ananenanso kuti: “Ndimachita zinthu zom’kondweretsa [Atate] nthawi zonse.” (Yoh. 8:29) Chakumapeto kwa moyo wake padziko lapansi Yesu popemphera kwa Atate wake anati: “Ndakulemekezani padziko lapansi, popeza ndatsiriza kugwira ntchito imene munandipatsa.” (Yoh. 17:4) N’zoonekeratu kuti Yesu ankazindikira ndiponso kuvomereza kuti Mulungu ndiye mutu wake.
Mwana Amapindula Chifukwa Chogonjera Atate
6. Kodi Yesu anasonyeza makhalidwe abwino ati?
6 Yesu ali padziko lapansi anasonyeza makhalidwe abwino ambiri. Khalidwe lina linali chikondi chachikulu chimene anasonyeza Atate wake. Iye anati: “Ndimakonda Atate.” (Yoh. 14:31) Iye ankakondanso kwambiri anthu. (Werengani Mateyo 22:35-40.) Yesu anali wokoma mtima ndi wachifundo, osati wankhanza kapena wopondereza. Iye anati: “Bwerani kwa ine, nonsenu ogwira ntchito yolemetsa ndi olemedwa, ndipo ndidzakutsitsimutsani. Senzani goli langa ndipo phunzirani kwa ine, pakuti ndine wofatsa ndi wodzichepetsa, ndipo mudzapeza chitsitsimutso cha miyoyo yanu. Pakuti goli langa ndi lofewa ndipo katundu wanga ndi wopepuka.” (Mat. 11:28-30) Anthu onse onga nkhosa amisinkhu yonse makamaka amene ankaponderezedwa anatsitsimulidwa ndi Yesu ndiponso uthenga wake wolimbikitsa.
7, 8. Malinga ndi Chilamulo, kodi mayi amene ankadwala matenda otaya magazi sanayenere kutani, koma Yesu anamuthandiza bwanji mayiyu?
7 Taganizirani mmene Yesu ankachitira zinthu ndi akazi. Kuyambira kale amuna ambiri amachitira nkhanza akazi. N’chimodzimodzinso ndi atsogoleri a zipembedzo mu nthawi ya Isiraeli. Koma Yesu ankalemekeza akazi. Umboni wa zimenezi, ndi mmene anachitira ndi mayi amene ankadwala matenda otaya magazi kwa zaka 12. Ochiritsa ambiri “anam’chititsa kumva zopweteka zambiri” ndipo iye anawononga chuma chake chonse kuti achire. Ngakhale kuti anayesetsa, “matendawo anangokulirakulira.” Malinga ndi Chilamulo, iye anali wodetsedwa ndipo aliyense amene akanamukhudza akanakhalanso wodetsedwa.—Lev. 15:19, 25.
8 Mayiyu atamva kuti Yesu akuchiritsa odwala, iyenso anakhala nawo pagulu la anthu omwe anazungulira Yesu. Mumtima mwake ankati: “Ndikangogwira malaya ake akunja okhawo, ndichira ndithu.” Iye anagwiradi Yesu, ndipo nthawi yomweyo anachira. Yesu ankadziwa kuti mayiyu sanayenera kugwira malaya ake. Koma sanamukalipire. M’malomwake anamukomera mtima. Yesu ankadziwa mmene mayiyu anamvera pazaka zonse zimene ankadwala ndipo anazindikira kuti ankafuna thandizo. Mwachifundo anamuuza kuti: “Mwanawe, chikhulupiriro chako chakuchiritsa. Pita mu mtendere, matenda ako aakuluwo atheretu.”—Maliko 5:25-34.
9. Kodi Yesu anatani ophunzira ake ataletsa ana kuti asabwere kwa iye?
9 Ngakhale ana ankakhala omasuka akakhala ndi Yesu. Panthawi ina anthu atabweretsa ana kwa Yesu, ophunzira ake anawakalipira poganiza kuti Yesu sangafune kuti ana amusokoneze. Koma umu si mmene Yesu ankaonera zinthu. Baibulo limati: “Ataona zimenezi Yesu anakwiya ndi kuwauza [ophunzira ake] kuti: “Alekeni ana aang’onowo abwere kwa ine; musawaletse iyayi, pakuti ufumu wa Mulungu ndi wa onga amenewa.” Ndipo iye “anatenga anawo m’manja mwake ndi kuyamba kuwadalitsa, mwa kuwaika manja.” Yesu sanali kungolola ana kubwera kwa iye, koma ankawalandiranso mwachikondi.—Maliko 10:13-16.
10. Kodi Yesu anaphunzira kuti makhalidwe amene ankasonyeza?
10 Kodi Yesu anaphunzira kuti makhalidwe amene ankasonyeza ali padziko lapansi? Iye asanakhale munthu, anakhala ndi Atate wake wa kumwamba kwa nthawi yaitali zedi. Iye ankaona mmene ankachitira zinthu ndipo anatengera zimenezi. (Werengani Miyambo 8:22, 23, 30.) Ali kumwamba ankaona mmene Yehova ankachitira umutu wake mwachifundo pa zolengedwa zake zonse ndipo anatengera kwambiri zochita za Atate wake. Kodi Yesu akanatha kuchita zimenezi akanakhala kuti sanali wogonjera? Iye ankasangalala kugonjera Atate wake ndipo Yehova ankasangalalanso kukhala ndi Mwana wotereyu. Ali padziko lapansi, Yesu anasonyeza bwino kwambiri makhalidwe ochititsa chidwi a Atate wake wa kumwamba. Ndi mwayi wapadera kugonjera Khristu yemwe ndi Wolamulira wa Ufumu wakumwamba amene Mulungu wamusankha.
Tsanzirani Makhalidwe a Khristu
11. (a) Kodi tiyenera kuyesetsa kutsanzira ndani? (b) Mumpingo wachikhristu, n’chifukwa chiyani makamaka amuna ayenera kuyesetsa kutsanzira Yesu?
11 Anthu onse mumpingo wachikhristu, makamaka amuna, ayenera kupitirizabe kuyesetsa kutsanzira makhalidwe a Khristu. Monga taonera kale, Baibulo limati: “Mutu wa mwamuna aliyense ndi Khristu.” Khristu amatsanzira Mutu wake yemwe ndi Yehova Mulungu, choncho amuna achikhristu ayeneranso kutsanzira Khristu mutu wawo. Atakhala Mkhristu, mtumwi Paulo nayenso ankatsanzira Yesu. Iye analimbikitsa Akhristu anzake kuti: “Khalani otsanzira ine, monga inenso ndili wotsanzira Khristu.” (1 Akor. 11:1) Ndipo mtumwi Petulo anati: “Anakuitanirani ku moyo umenewu, pakuti ngakhale Khristu anavutika chifukwa cha inu, kukusiyirani chitsanzo kuti mutsatire mapazi ake mosamalitsa.” (1 Pet. 2:21) Malangizo onena kuti tiyenera kutsanzira Khristu ndi ofunikanso makamaka kwa amuna pa chifukwa china. Iwo ndi amene amakhala akulu ndi atumiki othandiza. Popeza Yesu ankasangalala kutsanzira Yehova, amuna achikhristu nawonso ayenera kusangalala kutsanzira Khristu ndiponso makhalidwe ake.
12, 13. Kodi akulu ayenera kuchita zinthu motani ndi nkhosa zimene apatsidwa kuti aziyang’anire?
12 Akulu mumpingo wachikhristu ayenera kuyesetsa kukhala ngati Khristu. Petulo analangiza akulu kuti: “Wetani gulu la nkhosa za Mulungu lomwe anakuikizani, osati mokakamizika, koma mwaufulu; osatinso chifukwa chofuna kupindulapo, koma ndi mtima wonse; osati mochita ufumu pa aja ali cholowa chochokera kwa Mulungu, koma kukhala zitsanzo kwa gulu la nkhosa.” (1 Pet. 5:1-3) Akulu sayenera kukhala opondereza kapena ankhanza. Potsanzira Khristu, ayenera kuyesetsa kukhala achikondi, achifundo, odzichepetsa ndiponso okoma mtima akamachita zinthu ndi nkhosa zimene apatsidwa kuti azisamalire.
13 Anthu amene akutsogolera mumpingo ndi opanda ungwiro ndipo nthawi zonse ayenera kukumbukira zimenezi. (Aroma 3:23) Choncho ayenera kuyesetsa kuphunzira za Yesu ndi kutsanzira chikondi chake. Ayenera kuganizira mmene Mulungu ndi Khristu amachitira zinthu ndi anthu n’kumatsanzira zimenezo. Petulo akutilangiza kuti: “Nonsenu khalani odzichepetsa kwa wina ndi mnzake, chifukwa Mulungu amatsutsa odzikweza, koma odzichepetsa amawasonyeza kukoma mtima kwa m’chisomo chake.”—1 Pet. 5:5.
14. Kodi akulu ayenera kuchita chiyani posonyeza kulemekeza ena?
14 Pochita zinthu ndi nkhosa za Mulungu akulu mumpingo afunika kusonyeza makhalidwe abwino. Lemba la Aroma 12:10 limati: “Posonyezana chikondi chaubale khalani ndi chikondi chenicheni kwa wina ndi mnzake. Posonyezana ulemu wina ndi mnzake, khalani patsogolo.” Akulu ndi atumiki othandiza ayenera kulemekeza ena. Mofanana ndi Akhristu onse, amuna amenewa sayenera kuchita ‘kanthu kalikonse ndi mzimu wandewu kapena wodzikuza, koma modzichepetsa, ndipo ayenera kuona ena kukhala owaposa.’ (Afil. 2:3) Oyang’anira ayenera kuona ena kukhala owaposa. Akamachita zimenezi, akulu amatsatira malangizo a Paulo akuti: “Ife olimba tiyenera kunyamula zofooka za osalimba, osati kumadzikondweretsa tokha. Aliyense wa ife azikondweretsa mnzake pa zinthu zabwino zomulimbikitsa. Pakuti ngakhale Khristu sanadzikondweretse yekha.”—Aroma 15:1-3.
Kulemekeza Akazi
15. Kodi amuna ayenera kuchita zinthu motani ndi akazi awo?
15 Tsopano taganizirani malangizo a Petulo kwa amuna okwatira. Iye analemba kuti: “Inunso amuna pitirizani kukhala nawo [akazi anu] mowadziwa bwino, kupatsa ulemu mkazi monga chiwiya chosalimba.” (1 Pet. 3:7) Kupatsa ulemu munthu kumatanthauza kuona munthuyo kuti ndi wofunika. Motero mumaganizira zofuna ndiponso maganizo a munthuyo ndipo mumakhala ololera ngati mukuona kuti palibe vuto kuchita zimene wanena. Izi n’zimene mwamuna ayenera kuchitira mkazi wake.
16. Kodi ndi chenjezo lotani limene Mawu a Mulungu amapereka kwa amuna pa nkhani yolemekeza akazi awo?
16 Pouza amuna kuti azilemekeza akazi awo, Petulo anachenjeza kuti: “Kuti mapemphero anu asatsekerezedwe.” (1 Pet. 3:7) Zimenezi zikusonyeza kuti mmene mwamuna amachitira ndi mkazi wake ndi nkhani yaikulu kwa Yehova. Kulephera kulemekeza mkazi kungachititse kuti mapemphero a mwamunayo atsekerezedwe. Ndipotu mwachibadwa akazi ambiri samavutika kugonjera ngati amalemekezedwa ndi amuna awo.
17. Kodi mwamuna ayenera kukonda mkazi wake mpaka pati?
17 Pa nkhani ya kukonda mkazi, Mawu a Mulungu amati: “Amuna akonde akazi awo monga matupi awoawo. . . . Pakuti palibe munthu anadapo thupi la iye mwini; koma amalidyetsa ndi kulisamala, mmenenso Khristu amachitira ndi mpingo, . . . aliyense wa inu akonde mkazi wake monga adzikonda iye mwini.” (Aef. 5:28, 29, 33) Kodi amuna ayenera kukonda akazi awo mpaka pati? Paulo analemba kuti: “Amuna inu, pitirizani kukonda akazi anu, monga Khristu anakonda mpingo nadzipereka yekha chifukwa cha mpingowo.” (Aef. 5:25) Choncho mwamuna ayenera kukhala wokonzeka kufera mkazi wake ngati mmene Khristu anachitira pofera anthu ena. Mwamuna wachikhristu akamachita zinthu ndi mkazi wake mwachikondi, mwachifundo, momuganizira ndiponso mopanda dyera, mkaziyo savutika kugonjera umutu wake.
18. Kodi n’chiyani chingathandize amuna kukwaniritsa udindo wawo mu ukwati?
18 Kodi kulangiza amuna kuti azilemekeza akazi awo mwa njira imeneyi, n’kuwapempha kuchita zimene sangathe? Ayi. Yehova sangawapemphe kuchita zinthu zimene sangakwanitse. Ndiponso atumiki a Yehova onse ali ndi mwayi woti atha kulandira mzimu woyera wa Mulungu womwe ndi wamphamvu koposa m’chilengedwe chonse. Yesu anati: “Ngati inu, ngakhale muli oipa, mumadziwa kupatsa ana anu mphatso zabwino, kuli bwanji Atate wakumwamba! Iye adzapereka mowolowa manja mzimu woyera kwa amene akum’pempha.” (Luka 11:13) Akamapemphera, amuna angapemphe Yehova kuti awapatse mzimu wake woyera kuti uwathandize pochita zinthu ndi ena kuphatikizapo akazi awo.—Werengani Machitidwe 5:32.
19. Kodi tikambirana chiyani m’nkhani yotsatira?
19 Ndithudi, amuna ali ndi udindo waukulu wophunzira kugonjera Khristu ndiponso kutsanzira umutu wake. Nanga bwanji akazi, makamaka okwatiwa? Nkhani yotsatira ifotokoza mmene ayenera kuonera udindo wawo m’makonzedwe a Yehova.
-
-
Akazi, N’chifukwa Chiyani Muyenera Kugonjera Amuna Monga Mutu?Nsanja ya Olonda—2010 | May 15
-
-
Akazi, N’chifukwa Chiyani Muyenera Kugonjera Amuna Monga Mutu?
“Mutu wa mkazi ndi mwamuna.”—1 AKOR. 11:3.
1, 2. (a) Kodi mtumwi Paulo analemba zotani pa nkhani yokhudza dongosolo la Yehova la umutu ndiponso kugonjera? (b) Kodi tikambirana mafunso ati m’nkhani ino?
YEHOVA anakhazikitsa dongosolo labwino limene mtumwi Paulo anatchula pamene analemba kuti: “Mutu wa mwamuna aliyense ndi Khristu; ndi mutu wa mkazi ndi mwamuna” ndipo “mutu wa Khristu ndiye Mulungu.” (1 Akor. 11:3) Nkhani yapitayi inanena kuti Yesu ankaona kuti ndi mwayi kugonjera Mutu wake, Yehova Mulungu, ndipo ankasangalala kuchita zimenezi. Inanenanso kuti mutu wa amuna achikhristu ndi Khristu. Khristu anali wokoma mtima, wodekha, wachifundo ndiponso wopanda dyera pochita zinthu ndi anthu. Amuna mumpingo ayeneranso kusonyeza makhalidwe amenewa pochita zinthu ndi anthu ena makamaka akazi awo.
2 Nanga bwanji akazi? Kodi mutu wawo ndi ndani? Paulo analemba kuti: “Mutu wa mkazi ndi mwamuna.” Kodi akazi ayenera kuona bwanji mawu ouziridwa amenewa? Kodi mfundo imeneyi imagwiranso ntchito ngati mwamuna ali wosakhulupirira? Kodi kugonjera mwamuna monga mutu kumatanthauza kuti mkazi azingokhala chete osanena maganizo ake pamene zosankha zikupangidwa m’banja? Nanga mkazi angatani kuti azitamandidwa?
“Ndidzam’pangira Wom’thangatira”
3, 4. N’chifukwa chiyani dongosolo la umutu n’lothandiza m’banja?
3 Mulungu ndi amene anakhazikitsa dongosolo la umutu. Adamu atalengedwa, Yehova Mulungu anati: “Si kwabwino kuti munthu akhale yekha; ndidzam’pangira wom’thangatira iye.” Hava atalengedwa, Adamu anasangalala kwambiri kuona kuti ali ndi mnzake woti azimuthandiza moti ananena kuti: “Uyu tsopano ndiye fupa la mafupa anga, ndi mnofu wa mnofu wanga.” (Gen. 2:18-24) Adamu ndi Hava anali ndi mwayi wapadera wokhala atate ndi amayi a anthu angwiro omwe akanakhala mosangalala m’paradaiso kosatha padziko lonse.
4 Chifukwa cha kupanduka kwa makolo athu oyambirira, anthu sanalinso angwiro ngati mmene zinalili poyamba m’munda wa Edene. (Werengani Aroma 5:12.) Koma dongosolo la umutu silinasinthe. Mwamuna ndi mkazi akamatsatira dongosolo limeneli amapindula kwambiri ndipo banja lawo limakhala losangalala. Zotsatira zake zimakhala zofanana ndi mmene Yesu ankamvera pa nkhani yogonjera Yehova monga mutu wake. Asanakhale munthu, Yesu ‘ankakondwera pamaso pa Yehova nthawi zonse.’ (Miy. 8:30) Chifukwa cha kupanda ungwiro amuna amavutika kukhala mutu wabwino ndipo akazi zimawavutanso kugonjera bwinobwino. Koma amuna ndi akazi akamayesetsa kuchita zonse zimene angathe, dongosolo la umutu limeneli limathandiza kuti akhale ndi banja losangalatsa.
5. N’chifukwa chiyani anthu okwatirana ayenera kutsatira malangizo opezeka pa Aroma 12:10?
5 Chofunika kwambiri kuti banja likhale losangalala ndi kutsatira malangizo a m’Malemba opita kwa Akhristu onse akuti: “Posonyezana chikondi chaubale khalani ndi chikondi chenicheni kwa wina ndi mnzake. Posonyezana ulemu wina ndi mnzake, khalani patsogolo.” (Aroma 12:10) Mwamuna ndi mkazi ayeneranso kuyesetsa ‘kukhala okomerana mtima wina ndi mnzake, a chifundo chachikulu, okhululukirana ndi mtima wonse.’—Aef. 4:32.
Ngati Mwamuna Wanu Ali Wosakhulupirira
6, 7. Kodi chingachitike n’chiyani ngati mkazi wachikhristu akhalabe wogonjera mwamuna wake wosakhulupirira?
6 Bwanji ngati mwamuna kapena mkazi wanu satumikira Yehova? Nthawi zambiri amuna ndi amene amakhala osakhulupirira. Zikatere, kodi mkazi ayenera kuona bwanji mwamuna wake? Baibulo limayankha kuti “Inu akazi, muzigonjera amuna anu, kuti ngati ali osamvera mawu akopeke, osati ndi mawu, koma ndi khalidwe lanu, poona okha ndi maso awo khalidwe lanu loyera ndi ulemu wanu waukulu.”—1 Pet. 3:1, 2.
7 Mawu a Mulungu amalimbikitsa akazi kukhalabe ogonjera amuna awo osakhulupirira. Khalidwe labwino la mkazi lingachititse mwamuna kuti aganizire za zimene zimapangitsa mkazi kukhala ndi khalidwe labwinolo. Zotsatira zake n’zakuti mwamunayo angayambe kukhala ndi chidwi ndi zimene mkazi wake yemwe ndi Mkhristu amakhulupirira, ndipo m’kupita kwanthawi angaphunzire choonadi.
8, 9. Kodi mkazi wachikhristu angatani ngati mwamuna wake wosakhulupirira sakulabadira khalidwe lake labwino?
8 Bwanji ngati mwamuna wosakhulupirirayo salabadira zimene mkazi wake amachita? Malemba amalimbikitsa mkazi wokhulupirirayo kusonyeza makhalidwe achikhristu nthawi zonse ngakhale kuti zimenezi zingakhale zovuta. Mwachitsanzo, lemba la 1 Akorinto 13:4 limati: “Chikondi n’choleza mtima.” Choncho mkazi wachikhristu ayenera kupitirizabe kuchita zinthu “modzichepetsa kotheratu ndi mofatsa, moleza mtima” ndipo azilolera mwachikondi zimene zikumuchitikira. (Aef. 4:2) Mzimu woyera, womwe ndi mphamvu ya Mulungu yogwira ntchito, ungakuthandizeni kukhalabe ndi makhalidwe abwino ngakhale pamene zinthu zili zovuta.
9 Paulo analemba kuti: “Pa zinthu zonse, ndimapeza mphamvu kwa iye amene amandipatsa mphamvu.” (Afil. 4:13) Mzimu wa Mulungu umathandiza mwamuna kapena mkazi wachikhristu kuchita zinthu zambiri zomwe sakanazikwanitsa payekha. Mwachitsanzo, munthu akamachitiridwa nkhanza ndi mwamuna kapena mkazi wake angakhale ndi maganizo ofuna kubwezera. Koma Baibulo limalangiza Akhristu onse kuti: “Musabwezere choipa pa choipa; . . . pakuti Malemba amati: ‘Kubwezera ndi kwanga; ndidzawabwezera ndine, atero Yehova.’” (Aroma 12:17-19) Nalonso lemba la 1 Atesalonika 5:15 limatilangiza kuti: “Onetsetsani kuti wina asabwezere choipa pa choipa kwa wina aliyense, koma nthawi zonse yesetsani kuchita chabwino kwa wina ndi mnzake ndi kwa ena onse.” Mothandizidwa ndi mzimu woyera wa Yehova tingakwanitse kuchita zinthu zimene sizingatheke mwa mphamvu yathu. Choncho ndi bwino kupempha mzimu woyera wa Mulungu kuti utithandize pa zimene tikulephera kuchita.
10. Kodi Yesu ankatani anthu ena akamunenera kapena kumuchitira zinthu zoipa?
10 Yesu anapereka chitsanzo chabwino pa zimene tiyenera kuchita anthu akamatinenera kapena kutichitira zinthu zoipa. Lemba la 1 Petulo 2:23 limati: “Pamene anali kunenedwa zachipongwe, sanabwezere zachipongwe. Pamene anali kuvutika, sanawopseze, koma anali kudzipereka kwa iye amene amaweruza molungama.” Tikulimbikitsidwa kutengera chitsanzo chake chabwino. Musamakhumudwe chifukwa cha khalidwe loipa la anthu ena. Monga mmene Akhristu onse akulangizidwira, muzikhala “a chifundo chachikulu, a maganizo odzichepetsa. Osabwezera choipa pa choipa kapena chipongwe pa chipongwe.”—1 Pet. 3:8, 9.
Kodi Akazi Ayenera Kungokhala Chete?
11. Kodi ndi mwayi wapadera uti umene akazi ena achikhristu apatsidwa?
11 Kodi kugonjera amuna monga mutu kumatanthauza kuti akazi safunika kulankhula chilichonse pa nkhani za m’banja kapena nkhani zina? Ayi si choncho. Yehova wapatsa akazi ndi amuna zinthu zambiri zoti achite. Tangoganizani za mwayi wapadera umene anthu a 144,000 ali nawo wokhala mafumu ndi ansembe kumwamba motsogoleredwa ndi Khristu pamene azidzalamulira dziko lapansi. M’gulu limeneli mulinso akazi. (Agal. 3:26-29) Apatu n’zoonekeratu kuti Yehova wapatsa akazi ntchito yaikulu m’gulu lake.
12, 13. Perekani chitsanzo chosonyeza kuti akazi ankanenera.
12 Mwachitsanzo, m’nthawi za Baibulo akazi ena ankanenera. Pa lemba la Yoweli 2:28, 29 pali ulosi wakuti: “Ndidzatsanulira mzimu wanga pa anthu onse, ndi ana anu aamuna ndi aakazi adzanenera, . . . ndi pa akapolo ndi adzakazi omwe ndidzatsanulira mzimu wanga masiku awo.”
13 Ophunzira a Yesu okwana 120 amene anasonkhana m’chipinda chapamwamba ku Yerusalemu pa tsiku la Pentekosite mu 33 C.E. anali akazi ndi amuna. Mzimu wa Mulungu unatsanulidwa pa anthu onsewo. Choncho Petulo anagwira mawu a ulosi wa mneneri Yoweli ndipo anasonyeza kuti zimene ankachita amuna ndi akazi amenewa, kunali kukwaniritsidwa kwa ulosiwo. Iye anati: “Izi ndi zimene zinanenedwa kudzera mwa mneneri Yoweli kuti: ‘Ndipo m’masiku otsiriza,’ akutero Mulungu, ‘ndidzatsanulira mbali ya mzimu wanga pa anthu osiyanasiyana. Pamenepo ana anu aamuna ndi aakazi adzanenera. . . . Ndidzatsanuliranso mbali ya mzimu wanga ngakhale pa akapolo ndi adzakazi anga m’masiku amenewo, ndipo iwo adzanenera.’”—Mac. 2:16-18.
14. Kodi akazi anachita zotani pothandiza kuti Chikhristu choyambirira chifalikire?
14 M’nthawi ya atumwi akazi anathandiza kwambiri kufalitsa Chikhristu. Iwo ankalalikira za Ufumu wa Mulungu ndipo anachita zinthu zina zothandiza pa ntchito yolalikira. (Luka 8:1-3) Mwachitsanzo, mtumwi Paulo anatchula za Febe ‘amene ankatumikira mumpingo wa ku Kenkereya.’ Popereka moni kwa antchito anzake, Paulo anatchula akazi okhulupirika angapo kuphatikizapo “Turufena ndi Turufosa, akazi ogwira ntchito mwakhama potumikira Ambuye.” Iye ananenanso kuti, ‘Peresida, wokondedwa wathu anachita ntchito zambiri potumikira Ambuye.’—Aroma 16:1, 12.
15. Masiku ano, kodi akazi amachita zotani pothandiza kuti Chikhristu chifalikire?
15 Masiku ano, ambiri mwa anthu oposa 7 miliyoni amene akulalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu padziko lonse, ndi akazi a misinkhu yonse. (Mat. 24:14) Ambiri mwa akazi amenewa akuchita utumiki wanthawi zonse. Ena ndi amishonale pomwe ena akutumikira pa Beteli. Wamasalmo Davide anaimba kuti: “Ambuye anapatsa mawu: Akazi akulalikira uthengawo ndiwo khamu lalikulu.” (Sal. 68:11) Mawu amenewa akukwaniritsidwa masiku ano. Yehova amayamikira kwambiri ntchito imene akazi amagwira polengeza uthenga wabwino ndiponso pokwaniritsa zolinga zake. Choncho mfundo yakuti akazi achikhristu azigonjera siitanthauza kuti azingokhala chete.
Akazi Awiri Amene Sanangokhala Chete
16, 17. Kodi chitsanzo cha Sara chikusonyeza bwanji kuti akazi sayenera kungokhala chete m’banja?
16 Ngati Yehova wapatsa akazi zinthu zambiri zoti achite, ndiye kuti amuna ayenera kufunsira maganizo kwa akazi awo asanapange zosankha zikuluzikulu. Akamachita zimenezi ndiye kuti akusonyeza nzeru. Malemba amatchula zochitika zingapo pamene akazi analankhula kapena kuchita zinthu ngakhale kuti amuna awo sanalabadire zonena kapena zochita zawo. Taganizirani zitsanzo ziwiri izi.
17 Sara ankauza mobwerezabwereza mwamuna wake Abulahamu kuti achotse mkazi wake wachiwiri limodzi ndi mwana wake chifukwa chakuti sanali kusonyeza ulemu. “Mawuwo anaipira Abulahamu,” koma osati Mulungu. Ndipo Yehova anauza Abulahamu kuti: “Usaipidwe nawo, chifukwa cha mnyamatayo, ndi chifukwa cha mdzakazi wako; momwe monse akunenera iwe Sara umvere iwe mawu ake.” (Gen. 21:8-12) Abulahamu anamvera Yehova ndipo anachita zimene Sara ananena.
18. Kodi Abigayeli anachita chiyani?
18 Taganiziraninso za Abigayeli, mkazi wa Nabala. Pamene Davide ankathawa mfumu ya nsanje, Sauli, anakakhala pafupi ndi ziweto za Nabala. Davide ndi anyamata ake sanatenge chilichonse pa katundu wochuluka wa Nabala yemwe anali wolemera koma m’malo mwake iwo ankateteza katundu wakeyu. Koma Nabala “anali waphunzo ndi woipa machitidwe ake,” ndipo ‘anakalipira’ anyamata a Davide. Nabala anali ‘munthu woipa’ ndiponso ‘wopusa.’ Pamene anyamata a Davide mwaulemu anam’pempha Nabala kuti awapatseko zinthu, iye anakana. Kodi Abigayeli anatani atamva zimene zinachitikazi? Popanda kuuza Nabala iye “anafulumira, natenga mikate mazana awiri, ndi zikopa ziwiri za vinyo, nkhosa zisanu zowotchawotcha, ndi miyeso isanu ya tirigu wokazinga, ndi nchinchi za mphesa zouma zana limodzi, ndi nchinchi za nkhuyu mazana awiri,” ndipo anazipereka kwa Davide ndi anyamata ake. Kodi pamenepa, Abigayeli anachita zolondola? Inde, chifukwa chakuti Baibulo limati: “Yehova anam’kantha Nabala, nafa.” Ndipo kenako Davide anakwatira Abigayeli.—1 Sam. 25:3, 14-19, 23-25, 38-42.
‘Mkazi Amene Amatamandidwa’
19, 20. Kodi n’chiyani chimachititsa kuti mkazi azitamandidwa?
19 Malemba amayamikira akazi okwatiwa amene amachita zinthu mmene Yehova amafunira. Buku la Miyambo limatamanda “mkazi wangwiro,” ndipo limati: “Mtengo wake uposa ngale. Mtima wa mwamuna wake um’khulupirira, sadzasowa phindu. Mkaziyo am’chitira zabwino, si zoipa, masiku onse a moyo wake.” Limatinso, “Atsegula pakamwa pake ndi nzeru, ndipo chilangizo cha chifundo chili pa lilime lake. Ayang’anira mayendedwe a banja lake, sadya zakudya za ulesi. Ana ake adzanyamuka, nadzamutcha wodala; mwamuna wake nam’tama.”—Miy. 31:10-12, 26-28.
20 Kodi n’chiyani chimachititsa kuti mkazi azitamandidwa? Lemba la Miyambo 31:30 limati: “Kukongola kungonyenga, maonekedwe okoma ndi chabe; koma mkazi woopa Yehova adzatamandidwa.” Kuopa Yehova kumaphatikizapo kugonjera mofunitsitsa dongosolo la umutu limene Mulungu anakhazikitsa. Baibulo limati: “Mutu wa mkazi ndi mwamuna,” monga zililinso kuti “mutu wa mwamuna aliyense ndi Khristu” ndipo “mutu wa Khristu ndiye Mulungu.”—1 Akor. 11:3.
Yamikirani Mulungu Chifukwa cha Mphatso Imene Wakupatsani
21, 22. (a) Kodi Akhristu okwatirana ali ndi zifukwa zotani zoyamikira Mulungu chifukwa cha mphatso ya ukwati? (b) N’chifukwa chiyani tiyenera kulemekeza dongosolo la Yehova la ulamuliro ndiponso umutu? (Onani bokosi pa tsamba 17.)
21 Akhristu okwatirana ali ndi zifukwa zambiri zoyamikira Mulungu. Iwo angamayende mosangalala atagwirana manja. Iwo makamaka ayenera kuthokoza Mulungu chifukwa cha mphatso ya ukwati. Ndipo ukwati umawapatsa mwayi wochitira limodzi zinthu ndiponso kuyenda ndi Yehova. (Rute 1:9; Mika 6:8) Popeza Mulungu ndi amene anayambitsa ukwati, amadziwa bwino zimene zimafunika kuti okwatirana akhale osangalala. Nthawi zonse, chitani zinthu mogwirizana ndi zimene amafuna, ndipo ngakhale kuti tili m’dziko la mavuto ‘chimwemwe cha Yehova chidzakhala mphamvu yanu.’—Neh. 8:10.
22 Mwamuna wachikhristu amene amakonda mkazi wake ngati mmene amadzikondera, amachita umutu wake mwachikondi ndiponso mwachifundo. Amakonda kwambiri mkazi wake woopa Mulungu popeza mkaziyo amam’thandiza ndiponso amam’lemekeza kwambiri. Ndipo chofunika kwambiri n’chakuti, ukwati wawo wachitsanzo chabwino umalemekeza Yehova Mulungu wathu yemwe ndi woyenera kutamandidwa.
-