Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • ‘Valani Kuleza Mtima’
    Nsanja ya Olonda—2001 | November 1
    • “Chikondi Chikhala Chilezere”

      9. Kodi Paulo ayenera kuti anauza Akorinto kuti “chikondi chikhala chilezere” pa chifukwa chiti?

      9 Paulo anasonyeza kuti pali kugwirizana kwapadera pakati pa chikondi ndi kuleza mtima pamene ananena kuti: “Chikondi chikhala chilezere.” (1 Akorinto 13:4) Albert Barnes, wa maphunziro apamwamba a Baibulo, anapereka ganizo lakuti Paulo anatsindika zimenezi chifukwa cha kulimbana ndi mikangano imene inali mumpingo wachikristu wa ku Korinto. (1 Akorinto 1:11, 12) Barnes anati: “Liwu limene analigwiritsa ntchito pano [lotanthauza kuleza mtima] limatsutsana ndi kuchita zinthu mopupuluma. Limatsutsananso ndi kulankhula kapena kulingalira moipidwa ndiponso kupsa mtima msanga. Limasonyeza KULOLERA KWA NTHAŴI YAITALI munthu akavutitsidwa kapena kuputidwa.” Lerolinonso, chikondi ndi kuleza mtima zimathandiza kwambiri kuti mumpingo wachikristu mukhale mtendere.

      10. (a) Kodi chikondi chimatithandiza motani kuti tikhale oleza mtima, ndipo mtumwi Paulo analangiza motani pankhani imeneyi? (b) Kodi munthu wina wa maphunziro apamwamba a Baibulo anapereka ndemanga yotani pa kuleza mtima ndi chifundo cha Mulungu? (Onani mawu a m’munsi.)

      10 “Chikondi chikhala chilezere, chili chokoma mtima. Chikondi . . . sichitsata za mwini yekha, sichipsa mtima.” Motero, chikondi chimatithandiza m’njira zambiri kuti tikhale oleza mtima.a (1 Akorinto 13:4, 5) Chikondi chimatithandiza kuti tilolerane wina ndi mnzake moleza mtima ndi kukumbukira kuti tonse ndife opanda ungwiro ndipo timalakwa. Chimatithandiza kuti tikhale oganizira ena ndi okhululuka. Mtumwi Paulo akutilimbikitsa kuti tiyende koyenera “ndi kuonetsera kudzichepetsa konse, ndi chifatso, ndi kuonetsera chipiriro, ndi kulolerana wina ndi mnzake, mwa chikondi; ndi kusamalitsa kusunga umodzi wa Mzimu mwa chimangiriro cha mtendere.”​—Aefeso 4:1-3.

  • ‘Valani Kuleza Mtima’
    Nsanja ya Olonda—2001 | November 1
    • a Pothirira ndemanga zimene Paulo ananena kuti “chikondi chikhala chilezere, chili chokoma mtima,” Gordon D. Fee yemwe ndi wa maphunziro apamwamba a Baibulo analemba kuti: “Malinga ndi zimene Paulo anaphunzitsa, mawu ameneŵa [kuleza mtima ndi kukoma mtima] akuimira mbali ziŵiri za maganizo a Mulungu kwa anthu (yerekezerani ndi Aroma 2:4). Kulolera kwachikondi kwa Mulungu kukuonekera m’kuletsa kwake ukali pa kupanduka kwa anthu ndiponso kukoma mtima kwake kumene kumaonekera m’nthaŵi zambirimbiri zimene wasonyeza chifundo. Motero Paulo analongosola za chikondi mwa kuyamba kufotokoza mbali ziŵiri zimenezi za Mulungu amene kudzera mwa Kristu analolera ndi kuwachitira chifundo anthu amene anayenera kuwalanga.”

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena