Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • “Akufa Adzaukitsidwa”
    Nsanja ya Olonda—1998 | July 1
    • 7. (a) Kodi ndi nkhani yaikulu iti imene Paulo anasumikapo maganizo? (b) Kodi ndani amene anaona Yesu ataukitsidwa?

      7 M’mavesi aŵiri oyambirira a 1 Akorinto chaputala 15, Paulo akutchula cholinga cha nkhani yake kuti: “Ndikudziŵitsani, abale, Uthenga Wabwino umene ndinakulalikirani inu, umenenso munalandira, umenenso muimamo, umenenso mupulumutsidwa nawo . . . ngati simunakhulupira chabe.” Ngati Akorinto analephera kuchirimika pauthenga wabwino, ndiye kuti kulandira kwawo choonadi kunali kwachabe. Paulo anapitiriza kuti: “Ndinapereka kwa inu poyamba, chimenenso ndinalandira, kuti Kristu anafera zoipa zathu, monga mwa malembo; ndi kuti anaikidwa; ndi kuti anaukitsidwa tsiku lachitatu, monga mwa malembo; ndi kuti anaonekera kwa Kefa; pamenepo kwa khumi ndi aŵiriwo; pomwepo anaoneka panthaŵi imodzi kwa abale oposa mazana asanu, amene ochuluka a iwo akhala kufikira tsopano, koma ena agona; pomwepo anaonekera kwa Yakobo; pamenepo kwa atumwi onse; ndipo potsiriza pake pa onse, anaoneka kwa inenso monga mtayo.”​—1 Akorinto 15:3-8.

  • “Akufa Adzaukitsidwa”
    Nsanja ya Olonda—1998 | July 1
    • 9 Kristu anaonekeranso kwa gulu lina lalikulu, “abale oposa mazana asanu.” Popeza kuti ndi ku Galileya kokha kumene anali ndi otsatira ambiri motero, mwina pamenepa panali pachochitika chofotokozedwa pa Mateyu 28:16-20, pamene Yesu anapereka lamulo lopanga ophunzira. Ndiyetu anthu ameneŵa anapereka umboni wamphamvu! Ena anali adakali moyo mu 55 C.E. pamene Paulo analemba kalata yake yoyamba imeneyi kwa Akorinto. Komano, taonani kuti amene anali atamwalira anati iwo “agona.” Anali asanaukitsidwebe kuti alandire mphotho yawo yakumwamba.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena