-
Zimene Tingaphunzire Kuchokera kwa Mng’ono Wake wa YesuNsanja ya Olonda (Yophunzira)—2022 | January
-
-
MUZIKHALA ODZICHEPETSA NGATI YAKOBO
Yakobo anadzichepetsa Yesu ataonekera kwa iye ndipo kuchokera pamenepo anakhala wophunzira wake wokhulupirika (Onani ndime 5-7)
5. Kodi Yakobo anatani Yesu ataonekera kwa iye pambuyo poukitsidwa?
5 Kodi ndi liti pamene Yakobo anakhala wotsatira wokhulupirika wa Yesu? Yesu ataukitsidwa “anaonekera kwa Yakobo, kenakonso kwa atumwi onse.”(1 Akor. 15:7) Kukumana kumeneku kunachititsa kuti Yakobo akhale wophunzira wa Yesu. Iye analipo pamene atumwi ankayembekezera kulandira mzimu woyera m’chipinda cha m’mwamba ku Yerusalemu. (Mac. 1:13, 14) Pambuyo pake iye anali ndi mwayi wotumikira m’bungwe lolamulira la mu nthawi ya atumwi. (Mac. 15:6, 13-22; Agal. 2:9) Ndipo pa nthawi ina chisanafike chaka cha 62 C.E., iye anauziridwa kulembera kalata Akhristu odzozedwa. Malangizo a m’kalatayo angatithandizenso masiku ano, kaya tikuyembekezera kudzapita kumwamba kapena kudzakhala padzikoli. (Yak. 1:1) Malinga ndi zimene ananena Josephus, wolemba mbiri wa munthawi ya atumwi, Yakobo anaphedwa, Hananiya wamng’ono yemwe anali mkulu wa ansembe wa Chiyuda atalamula. Yakobo anakhalabe wokhulupirika, mpaka pamene anamaliza moyo wake wapadzikoli.
-