Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • “Akufa Adzaukitsidwa”
    Nsanja ya Olonda—1998 | July 1
    • 7. (a) Kodi ndi nkhani yaikulu iti imene Paulo anasumikapo maganizo? (b) Kodi ndani amene anaona Yesu ataukitsidwa?

      7 M’mavesi aŵiri oyambirira a 1 Akorinto chaputala 15, Paulo akutchula cholinga cha nkhani yake kuti: “Ndikudziŵitsani, abale, Uthenga Wabwino umene ndinakulalikirani inu, umenenso munalandira, umenenso muimamo, umenenso mupulumutsidwa nawo . . . ngati simunakhulupira chabe.” Ngati Akorinto analephera kuchirimika pauthenga wabwino, ndiye kuti kulandira kwawo choonadi kunali kwachabe. Paulo anapitiriza kuti: “Ndinapereka kwa inu poyamba, chimenenso ndinalandira, kuti Kristu anafera zoipa zathu, monga mwa malembo; ndi kuti anaikidwa; ndi kuti anaukitsidwa tsiku lachitatu, monga mwa malembo; ndi kuti anaonekera kwa Kefa; pamenepo kwa khumi ndi aŵiriwo; pomwepo anaoneka panthaŵi imodzi kwa abale oposa mazana asanu, amene ochuluka a iwo akhala kufikira tsopano, koma ena agona; pomwepo anaonekera kwa Yakobo; pamenepo kwa atumwi onse; ndipo potsiriza pake pa onse, anaoneka kwa inenso monga mtayo.”​—1 Akorinto 15:3-8.

  • “Akufa Adzaukitsidwa”
    Nsanja ya Olonda—1998 | July 1
    • 10. (a) Kodi msonkhano womaliza wa Yesu ndi ophunzira ake unawasonkhezera motani? (b) Kodi Yesu anaonekera motani kwa Paulo “monga mtayo”?

      10 Mboni ina yodziŵika kwambiri ya kuukitsidwa kwa Yesu anali Yakobo, mwana wa Yosefe ndi amayi wa Yesu, Mariya. Yesu asanaukitsidwe, Yakobo mwachionekere sanali wokhulupirira. (Yohane 7:5) Koma Yesu ataonekera kwa iye, Yakobo anakhala wokhulupirira ndiponso mwina anathandizira kuti abale ake enawo atembenuke. (Machitidwe 1:13, 14) Pamsonkhano wake womaliza ndi ophunzira ake, nthaŵi imene anakwera kumwamba, Yesu anawalamula ‘kukhala mboni . . . kufikira malekezero ake a dziko.’ (Machitidwe 1:6-11) Pambuyo pake, anaonekera kwa Saulo wa ku Tariso, wozunza Akristu. (Machitidwe 22:6-8) Yesu anaonekera kwa Saulo “monga mtayo.” Zinali monga kuti Saulo waukitsidwira kale kumoyo wauzimu ndipo akuona Ambuye waulemerero zaka mazana ambiri kuukitsidwa kumeneku kusanachitike. Chokumana nacho chimenechi chinachititsa Saulo kupotoloka mwadzidzidzi pacholinga chake cha kutsutsa ndi kupha a mumpingo wachikristu ndipo chinamsinthiratu. (Machitidwe 9:3-9, 17-19) Saulo anakhala mtumwi Paulo, mmodzi mwa ochirikiza chikhulupiriro chachikristu achangu koposa.​—1 Akorinto 15:9, 10.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena