-
Kuukitsidwa kwa Yesu Kudzapangitsa Anthu Kupeza Moyo WosathaNsanja ya Olonda—2013 | March 1
-
-
KUUKITSIDWA kwa Yesu kuli ndi phindu lalikulu kwa ife. Mtumwi Paulo anafotokoza kufunika kwa nkhani imeneyi pamene analemba kuti: “Khristu anaukitsidwa kwa akufa, n’kukhala chipatso choyambirira cha amene akugona mu imfa. Popeza imfa inafika kudzera mwa munthu mmodzi, kuuka kwa akufa kunafikanso kudzera mwa munthu mmodzi. Pakuti monga mwa Adamu onse akufa, momwemonso mwa Khristu onse adzapatsidwa moyo.”—1 Akorinto 15:20-22.
-
-
Kuukitsidwa kwa Yesu Kudzapangitsa Anthu Kupeza Moyo WosathaNsanja ya Olonda—2013 | March 1
-
-
Kenako Paulo anatchula chinthu chimene chinatheka chifukwa cha kuukitsidwa kwa Yesu. Iye anati: “Popeza imfa inafika kudzera mwa munthu mmodzi, kuuka kwa akufa kunafikanso kudzera mwa munthu mmodzi.” Anthufe timafa chifukwa cha uchimo ndi kupanda ungwiro zimene tinatengera kwa Adamu. Komabe pamene Yesu anapereka moyo wake wangwiro n’kuukitsidwa, anachititsa kuti anthu adzamasulidwe ku ukapolo wa uchimo ndi imfa. Pomveketsa mfundoyi, pa Aroma 6:23, Paulo analemba kuti: “Malipiro a uchimo ndi imfa, koma mphatso imene Mulungu amapereka ndi moyo wosatha kudzera mwa Khristu Yesu Ambuye wathu.”
-