Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • “Ndili ndi Chiyembekezo mwa Mulungu”
    Nsanja ya Olonda (Yophunzira)—2017 | December
    • 15. Kodi mawu oti Yesu ndi “chipatso choyambirira” akutanthauza chiyani?

      15 Yesu anali woyamba kuukitsidwa m’njira imeneyi ndipo kuuka kwake ndi kofunika kwambiri kuposa kuuka kwa munthu wina aliyense. (Mac. 26:23) Koma Baibulo linanena za anthu enanso amene adzaukitsidwe kupita kumwamba n’kukhala ndi matupi auzimu. Paja Yesu anauza atumwi ake okhulupirika kuti adzakalamulira limodzi naye kumwamba. (Luka 22:28-30) Koma kuti alandire mphoto imeneyi, anafunika kufa kaye kenako n’kuukitsidwa ndi thupi lauzimu. Pa nkhani imeneyi, Paulo analemba kuti: “Khristu anaukitsidwa kwa akufa, n’kukhala chipatso choyambirira cha amene akugona mu imfa.” Kenako anasonyeza kuti padzakhala anthu enanso amene adzaukitsidwe n’kupita kumwamba. Iye anati: “Aliyense pamalo pake: Choyamba Khristu, amene ndi chipatso choyambirira, kenako ake a Khristu pa nthawi ya kukhalapo kwake.”​—1 Akor. 15:20, 23.

      16. Kodi ndi mawu ati amene angatithandize kudziwa nthawi ya kuukitsidwa kwa opita kumwamba?

      16 Mawu oti “pa nthawi ya kukhalapo kwake” angatithandize kudziwa nthawi ya kuukitsidwa kwa anthu opita kumwamba. Kwa zaka zambiri, a Mboni za Yehova akhala akufotokoza kuchokera m’Malemba kuti nthawi ya “kukhalapo” kwa Yesu inayamba mu 1914. Nthawiyi ikupitirira ndipo mapeto a dziko loipali ali pafupi kwambiri.

      17, 18. N’chiyani chidzachitikire odzozedwa ena pa nthawi ya kukhalapo kwa Khristu?

      17 Pa nkhani ya oukitsidwa kupita kumwamba, Baibulo limanenanso kuti: “Sitikufuna kuti mukhale osadziwa za amene akugona mu imfa . . . Pakuti ngati timakhulupirira kuti Yesu anafa ndi kuukanso, ndiye kuti amenenso agona mu imfa kudzera mwa Yesu, Mulungu adzawasonkhanitsa kuti akhale naye limodzi . . . Ife amoyofe amene tidzakhalapo pa nthawi ya kukhalapo kwa Ambuye, sitidzakhala patsogolo pa amene agona mu imfa. Chifukwa Ambuye mwini adzatsika kumwamba, ndi mfuu yolamula . . . Ndipo amene anafa mwa Khristu adzauka choyamba. Pambuyo pake ife amoyo otsalafe, limodzi ndi iwowo, tidzatengedwa m’mitambo kukakumana ndi Ambuye m’mlengalenga, ndipo tizikakhala ndi Ambuye nthawi zonse.”​—1 Ates. 4:13-17.

      18 Malinga ndi lembali, kuuka koyamba kunayenera kuchitika pambuyo poti nthawi ya “kukhalapo” kwa Khristu yayamba. Odzozedwa amene adzakhalebe moyo pa nthawi ya chisautso chachikulu ‘adzatengedwa m’mitambo.’ (Mat. 24:31) Tinganene kuti anthu amene ‘adzatengedwewo’ ‘sadzagona mu imfa’ chifukwa chakuti sipadzadutsa nthawi yaitali ali akufa. Iwo ‘adzasandulika, m’kamphindi, m’kuphethira kwa diso, pa kulira kwa lipenga lomaliza.’​—1 Akor. 15:51, 52.

  • “Ndili ndi Chiyembekezo mwa Mulungu”
    Nsanja ya Olonda (Yophunzira)—2017 | December
    • 20. N’chifukwa chiyani sitikayikira zoti anthu adzauka mwadongosolo m’dziko latsopano?

      20 Ponena za anthu amene adzapite kumwamba, Baibulo limanena kuti iwo adzauka mwadongosolo, “aliyense pamalo ake.” (1 Akor. 15:23) Sitikukayikira kuti anthu ouka padzikoli adzaukanso mwadongosolo. Mfundo imeneyi ndi yochititsa chidwi koma imabweretsa mafunso ambiri. Kodi anthu amene adzafe Ulamuliro wa Zaka 1,000 wa Khristu utatsala pang’ono kuyamba, ndi amene adzayambe kuuka n’cholinga choti adzalandiridwe ndi anthu amene akuwadziwa? Nanga kodi atumiki okhulupirika akale amene ali ndi luso lotha kutsogolera anthu adzauka msanga n’cholinga choti adzathandize anthu a Mulungu kukhala mwadongosolo m’dziko latsopano? Kodi anthu amene sanatumikirepo Yehova adzauka pa nthawi iti, nanga adzaukira kuti? Koma kodi pali chifukwa choti tiziswa mitu kuganizira kwambiri mafunso amenewa? Kunena zoona ndi bwino kungoyembekezera n’kudzaona zonse pa nthawiyo. Zidzakhalatu zochititsa chidwi kwambiri kuona mmene Yehova adzayendetsere zinthu pa nthawi imeneyo.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena