Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Chimene Tingaphunzirepo pa Mbiri ya Aroma
    Nsanja ya Olonda—2002 | June 15
    • Chimene Tingaphunzirepo pa Mbiri ya Aroma

      “NGATI ndinalimbana ndi zilombo ku Efeso monga mwa munthu.” Ena amaganiza kuti mawu ameneŵa, a pa 1 Akorinto 15:32, amatanthauza kuti mtumwi Paulo anam’patsa chilango chomenyana ndi munthu wina m’bwalo la maseŵera la Aroma. Kaya anamenyanadi kapena ayi, chodziŵika n’chakuti m’mabwalo amaseŵera panthaŵiyo sichinali chachilendo anthu kumenyana mpaka wina atafa. Kodi mbiri imatiuza chiyani za m’mabwalo a maseŵera ameneŵa ndiponso zimene zinkachitika kumeneko?

  • Chimene Tingaphunzirepo pa Mbiri ya Aroma
    Nsanja ya Olonda—2002 | June 15
    • Mungafunse kuti, ‘Kodi ankamenyanawo ndani?’ Anali akapolo, anthu olakwa amene awaweruza kuti aphedwe, asilikali amene agwidwa ukapolo, kapena anthu wamba ongofuna kusangalala kapena kutchuka ndiponso chuma. Onse ankawaphunzitsa m’sukulu zangati ndende. Buku lakuti Giochi e spettacoli (Maseŵera ndi Zionetsero) limanena kuti anthu omenyanaŵa akamaphunzira “alonda ankawayang’anira nthaŵi zonse ndipo ankalandira chilango chokhwima, malamulo oipa kwambiri, ndipo makamaka zilango zinali zankhanza . . . Kaŵirikaŵiri zimenezi zinkapangitsa anthuŵa kudzipha, kupanduka, ndi kuukira.” Sukulu yaikulu ya Aroma yophunzitsa anthu kumenya inali ndi tizipinda ta munthu mmodzimmodzi tokwana pafupifupi 1000. Munthu aliyense ankamuphunzitsa kukhala katswiri pa mbali inayake. Ena ankamenya pogwiritsa ntchito zida zodzitetezera, zishango, ndi malupanga. Ena ankagwiritsa ntchito ukonde ndiponso mikondo ya mano atatu. Komabe ena ankaphunzira kumenyana ndi nyama m’maseŵera ena otchuka, otchedwa kusaka. Kapena kodi Paulo anali kunena za maseŵera ameneŵa?

  • Chimene Tingaphunzirepo pa Mbiri ya Aroma
    Nsanja ya Olonda—2002 | June 15
    • Nthaŵi ya m’maŵa ku bwalo la maseŵera inali nthaŵi ya maseŵera otchedwa kusaka. Nyama za kuthengo za mitundu yonse ankazikakamiza kuloŵa m’bwalomo. Anthu oonerera ankasangalala ng’ombe ikamamenyana ndi chimbalangondo. Nthaŵi zambiri ankazimanga pamodzi nyamazi kuti zimenyane mpaka ina ife, ndiyeno yotsalayo ankaipha ndi mlenje. Maseŵera ena otchuka ankamenyanitsa mikango ndi njuzi, kapena njobvu ndi chimbalangondo. Alenje ankasonyeza luso lawo pa kupha nyama zakunja zomwe ankazibweretsa m’dziko lawolo, mosasamala kanthu kuti amawononga ndalama zochuluka motani. Nyamazi zinali monga akambuku, zipembere, mvuwu, akadyamsonga, afisi, ngamila, mimbulu, nkhumba, ndi agwape.

      Zimene zinkachitika pamaseŵera osakawo zinkasangalatsa anthu kwambiri. M’bwalomo ankaikamo miyala, madzi, ndi mitengo kuti muoneke ngati m’nkhalango. M’mabwalo ena, nyama zinkaoneka ngati zabwera mwamatsenga kuchokera pansi ndiponso kumwamba. Khalidwe lachilendo la nyama linkawonjezera kuti zinthu zikhale zosangalatsa, koma zimene zinapangitsa maseŵera a kusaka kukhala osangalatsa kwambiri zinali nkhanza zimene anthu ankachita.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena