-
Akazi Achikristu—Kusunga Umphumphu Mmalo AntchitoNsanja ya Olonda—1987
-
-
Mkazi wolingalira wotchedwa Betty amatenga chinjirizo lina lake. Iye akuti: “Ndimakhala wochenjera ponena za kuyanjana ndi anzanga ogwira nawo ntchito chifukwa makhalidwe awo siali ofanana ndi anga.” (1 Akorinto 15:33) Ichi sichikutanthauza kuti muyenera kudzipatula kapena kukhala waukali kwa ogwira nawo ntchito. Koma pamene iwo akakamira pa kukambitsirana nkhani zomwe ziri zonyansa kwa Mkristu, musachedwe kudzichotsapo inu eni. (Aefeso 5:3, 4) Kumvetsera kwanu ku nkhani yoipa imeneyo kungapereke kwa amuna apantchito chikhutiritso chakuti mungakhale wovomereza ku kukufikirani kwawo.
-
-
Akazi Achikristu—Kusunga Umphumphu Mmalo AntchitoNsanja ya Olonda—1987
-
-
Pomalizira, mkazi wolingalira amapewa mkhalidwe yogonjera. Kuitanidwa kumwa chakumwa choledzeretsa kapena kutsalira kuntchito pambuyo pa nthaŵi ya ntchito popanda chifukwa chenicheni kungakhale msampha. (Yerekezani ndi 2 Samueli 13:1-14. ) “Wochenjera awona zoipa nabisala,” umatero mwambo wanzeru.—Miyambo 22:3.
-