Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w90 4/15 tsamba 26-28
  • “Chirimikani”—Musakhumudwe

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Chirimikani”—Musakhumudwe
  • Nsanja ya Olonda​—1990
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Chizunzo Chingatikhumudwitse
  • Zogwiritsa Mwala Zingafooketse Chikhulupiriro
  • Kudzitsutsa Kungawononge
  • Musakhalebe Wokhumudwa
  • Kodi Muli Pati?
  • Okonda Chilungamo Palibe Chowakhumudwitsa
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2021
  • Kodi Mudzakhumudwa N’kusiya Kutsatira Yesu?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2021
  • Tizipewa Kuchita Zinthu Zimene Zingakhumudwitse Ena
    Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2018
  • Anthu Okonda Yehova ‘Alibe Chowakhumudwitsa’
    Nsanja ya Olonda—2013
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda​—1990
w90 4/15 tsamba 26-28

“Chirimikani”​—Musakhumudwe

NKHANI yaikulu koposa imene ikuyang’aniza mtundu wa anthu lerolino ndiyo ya ulamuliro wa chilengedwe chonse. Yehova akutiitana kuti titenge kaimidwe kathu ndi kuŵerengeredwa m’nkhaniyi mwakugonjera kwa Mfumu yake yoikidwa, Kristu Yesu. Pali kufunika kofulumira kwa kuvomereza ku chiitanochi, ndipo kwa zaka zisanu zokha zapitazi, anthu oposa miliyoni imodzi achita zimenezo. Komatu ameneŵa apeza kuti zambiri zikuloŵetsedwamo m’kutenga kaimidwe osati chosankha wamba cha nthaŵi imodzi cha kutumikira Yehova. Payenera kukhala kudzipatulira kwa moyo wonse. Kodi tidzasungabe kaimidwe kathu pamene zinthu zavuta? Kapena kodi tidzafooka pang’onopang’ono, pambuyo ‘pochirimika’ kwa nthaŵi yoyamba?​—1 Akorinto 16:13; Ahebri 2:1.

Ngati mwapeza njira Yachikristu kukhala yovuta, tonthozedwani mwakudziŵa kuti mmenemo ndi mmene zinaliri ndi Yesu Kristu. Inde, ngakhale Mwana wobadwa yekha wa Mulungu anayenera kupempherera nyonga kuti asungebe kaimidwe kake, makamaka pamene chiyeso chake chachikulu chinkayandikira. Tangomulingalirani ali m’munda wa Getsemane, akupemphera mwamphamphu: “Abba, Atate, zinthu zonse zitheka ndi Inu; mundichotsere chikho ichi; komatu si chimene ndifuna Ine, koma chimene mufuna Inu.” (Marko 14:36) Iye anadziŵa kuti njira yakutsogoloko inali yovuta. Anali wozindikira mwapadera kuti dzina la Atate wake likayambukiridwa. Chotero, munthu wangwiro yekha pa dziko lapansi sanachite manyazi kupempha thandizo.

Pamene zinthu zitivutira, tiri ndi magwero ofananawo a nyonga amene Yesu anali nawo. Tingapemphere kwa Yehova kaamba ka thandizo kotero kuti tisakhumudwe kapena kugwa. Koma kodi ndi mtundu wanji wa zovuta zimene tingakumane nazo zimene zingatikhumudwitse? Kudziŵa zimenezi ndi kukonzekera pasadakhale mwinamwake kungatithandize kupeŵa kukhumudwa.

Chizunzo Chingatikhumudwitse

Baibulo likuchenjeza kuti: “Onse akufuna kukhala opembedza m’moyo mwa Kristu Yesu, adzamva mazunzo.” (2 Timoteo 3:12) Chizunzo chingatikhumudwitse, ndipo chimabwera m’mitundu yosiyanasiyana. (Marko 4:17) Chingakhale chiletso chalamulo​—chobweretsa ngozi ya kuikidwa m’ndende ndipo ngakhale imfa​—chiwawa cha gulu, chitsutso cha tsiku ndi tsiku chophwetsa chikhulupiriro chochokera kwa wa muukwati wogamulapo, wotsutsa, kapena kusekedwa kwa nthaŵi zonse ndi anzanu a kusukulu.

Chizunzo nchovuta kuchipirira, koma tikuchenjezedwa kuti chidzabwera mu mtundu umodzi kapena unzake. Chotero, tingakulitse chikhulupiriro chathu tsopano ndi kuphunzira kudalira pa nyonga ya Yehova kotero kuti pamene nthaŵiyo ifika, tidzapirira ndi nyonga imeneyo. (1 Petro 4:13, 14; 5:6-11) Komabe, kaŵirikaŵiri zokhumudwitsa zimakhala zamachenjera kuposa kuwukira kwachiwawa kwa chizunzo.

Zogwiritsa Mwala Zingafooketse Chikhulupiriro

Kodi ndani amene sakumbukira kudzimva koswa maganizo kumene kunadza pamene tinali ana ndi kudzimva okhumudwa? Kodi mumakumbukira nthaŵi imene Atate analonjeza chinthu chapadera kwa banja ndipo chifukwa cha zinazake nkusintha maganizo awo? Kapena nthaŵi imene anayenera kupita nanu ku malo osungira zinyama ndipo kenaka pomalizira nkusintha? Mudali wogwiritsidwa mwala chotani nanga!

Akristu achikulire angagwiritsidwenso mwala, ndipo m’zochitika zina, zimenezi zatsogoza ku ngozi yauzimu. Ena anayedzamitsa chiyembekezo chawo pa deti limene anali otsimikiza kuti Armagedo idzafika. Pamene sikunachitike chirichonse pa tsikulo, anakhumudwa. Ena anagwiritsidwa mwala pamene mwaŵi woyembekezeredwa sunakwaniritsidwe. Kuwonjezerapo, anthu angagwiritse mwala. Msungwana wa zaka 18 zakubadwa anauza makolo ake kuti anakhumudwitsidwa kwambiri ndi mkhalidwe wa amuna achichepere ena mu mpingo​—ndi kulephera kwa makolo awo kupereka chilango​—kotero kuti anafuna kuleka chowonadi.

Pamene kuli kwakuti kugwiritsidwa mwala kwa m’mikhalidwe yonseyi nkomveka, kodi ogwiritsidwa mwalawo ayenera kukhumudwitsidwa mu unansi wawo ndi Yehova? Tangolingalirani kugwiritsidwa mwala kwa Yesu pamene atumwi ake anaumirira pa kukangana kuti ndani anali wamkulu pakati pawo, mwakutero kusonyeza zikhumbo zamkati. (Luka 9:46; 22:24) Tangolingaliraninso, kugwiritsidwa mwala kwa Yobu pamene mabwenzi ake atatu amene anayenera kudzamuthandiza anamuwukira ndi kuyamba kukaikira kukhulupirika kwake! (Yobu 22:5-10) Komabe, Yesu ndi Yobu sanakhumudwe.

Anthu onse ngwofooka, chotero kukakhala kupanda nzeru kulola kulephera kwa ena kuyambukira unansi wathu ndi Yehova. (Salmo 51:5) Kupanda ungwiro kwa ena sikuyenera kutichititsa khungu ku ntchito yosangalatsa imene Yehova akuchita pamene akusonkhanitsa “pamodzi zonse mwa Kristu.” (Aefeso 1:9, 10) Kumbukirani kuti ali anthu opanda ungwiro, ofooka onga ife amene Yehova akusonkhanitsa, anthu amene akufunikira chilango ndi kuyenga kotero kuti akhale olimba. (Salmo 130:3) Mdani wathu si mbale wathu Wachikristu wopanda ungwiro koma Satana, amene amafuna kutilikwira ngati angathe. Sadzapambana ngati ‘tidzisungira, okhazikika m’chikhulupiriro.’ (1 Petro 5:8, 9) Ngati tiri ndi chikhulupiriro choterocho, ‘sitidzachita manyazi’ konse.​—Aroma 9:33.

Kudzitsutsa Kungawononge

Ena ataya unansi wawo ndi Yehova Mulungu chifukwa cha kudzimva kukhala osayenerera. Akumazindikira za zofooka zawo ndi zophophonya, amamaliza kuti Yehova sadzalandira konse utumiki wawo. Iwo amaganiza kuti kudzinenera kwawo kukhala mmodzi wa Mboni za Yehova kuli chinyengo. Kodi munadziumirapo mtima motero? Ngati ndi choncho, muyenera kulimbana ndi maganizo oterowo.

Kodi mumadzimva kukhala wosayenera kutumikira Yehova? Pamenepa dzifunseni kuti, ‘Kodi ndani amene ali woyeneretsedwa kaamba ka mwaŵi umenewu?’ Akristu onse ali ndi nkhondo yosalekeza yolimbana ndi kupanda ungwiro kwawo. Ngakhale mtumwi Paulo anadandaula kuti: “Pamene ndifuna chabwino, choipa chiriko.” (Aroma 7:21) Kodi Paulo anali wonyenga chifukwa chakuti nthaŵi zina anachita zinthu zimene zinali zolakwa? Ayi. Wonyenga ali munthu amene amanamizira kukhala amene sali. Ngati tiyesetsa kuchita zabwino koma tilephera kamodzikamodzi mosafuna, kodi kumeneko nkunamizira kukhala chinachake? Ndithudi ayi.

Baibulo likutichenjeza ‘kuvala umunthu watsopano.’ (Aefeso 4:24) Komabe, kodi zimenezo zimatanthauza kuti timataya zikhoterero zonse za umunthu wakale? Ayi. M’kalata yake kwa Akolose, Paulo anati umunthu watsopano ‘ulikukonzeka watsopano’ mwa chidziŵitso cholongosoka. (Akolose 3:9, 10) Mawu akuti ‘ulikukonzeka watsopano’ amasonyeza kachitidwe kopitiriza. Chotero kusintha umunthu kuli kachitidwe kopitiriza. Pamenepa, nzosadabwitsa kuti nthaŵi zina timapeza zophophonya mwa ife eni.

Ndithudi, uku sikuli kuchepetsa kuwopsya kwa chimo, sikukutanthauzanso kuti tiyenera kugonjera ku chiyeso popanda kuyesera kulimbana nacho, tikumalingalira kuti Yehova adzangotikhululukira. Koma zimatithandiza kusakhala wodzisuliza mopambanitsa. Ndipo zimatipangitsa kumkonda Yehova mowonjezereka chifukwa anapereka nsembe ya dipo ya Kristu kotero kuti tingamtumikire Iye mosasamala kanthu za mkhalidwe wathu wacholoŵa wochimwa.

Mtumwi Yohane anapereka kawonedwe kolinganizika ka nkhaniyo pamene anati: “Ndikulemberani, kuti musachimwe.” Koma kenaka anawonjezera kuti: “Ndipo akachimwa wina [chifukwa cha kupanda ungwiro kwaumunthu], Nkhoswe tiri naye kwa Atate, ndiye Yesu Kristu.” (1 Yohane 2:1) M’malo modzitsutsa mopambanitsa, chidziŵitso chimenechi cha mkhalidwe wathu ndi thandizo limene Yehova wapereka zimatitsogoza kufuula mawu a Paulo akuti: “Ndiyamika Mulungu, mwa Yesu Kristu Ambuye wathu.”​—Aroma 7:25.

Musakhalebe Wokhumudwa

Yesu anapereka chenjezo lamphamvu kwa aliyense amene angakhale wokhumudwitsa: “Koma yense amene adzakhumudwitsa kamodzi ka tiana iti, takukhulupirira Ine, kumuyenera iye kuti mphero yaikulu ikolowekedwe m’khosi mwake, namizidwe poya pa nyanja.” (Mateyu 18:6) Koma bwanji ponena za wokhumudwayo? Ngati takhumudwitsidwa ndi winawake kapena mkhalidwe, kodi tiyenera kudzikhululukira ndi kuti, “Ayi, sikulakwa kwanga, chotero sindidzatumikiranso Yehova”?

Lingalirani fanizoli. Kodi munayamba mwaterereka pa chidutswa cha madzi owundana kapena kugwa pa sitepe? Mwinamwake ngoziyo inakudzidzimutsani. Nzomveka kuti munangodzipeza mutagwa pansi. Koma kodi potsatira munachitanji? Kodi munati: “Sicholakwa changa kuti ndagona pano. Ncholakwa cha madzi owundana [kapena sitepe]. Choncho sindidzukanso”? Mothekera kwenikweni, munaimirira ndi kuchoka pa malo ochititsa manyaziwo mwamsanga monga mmene munathera.

Kodi siziyenera kukhala tero mu nkhani zauzimu? Ngati talakwiridwa ndi mkhalidwe wina kapena Mkristu mnzathu, limenelo ndi vuto lalikulu limene liyenera kusamaliridwa. Komabe, ngati tikhalabe okhumudwa, tikumaumirira kupatsa liŵongo winawake chifukwa cha vuto lathu, kodi sizowona kuti mkhalidwe wathu mowonjezereka umakhala cholakwa chathu?

Mosangalatsa, ngati takhumudwa, akulu ndi ena achikulire mu mpingo amakhala ofunitsitsa kupereka thandizo. (Agalatiya 6:1) Ndipo Yehova iyemwini amapereka nyonga kwa awo amene akukhumba kumtumikira mosasamala kanthu za mavuto. (Afilipi 4:13) Chotero nthaŵi zonse tiyenera kukhala okonzeka kupempha thandizo ngati zikuwoneka kuti chinachake chikufuna kusokoneza kaimidwe kathu kochirimika kaamba ka Yehova ndi Ufumu wake. Pamenepo sitidzampatsa Satana chilakiko mwakukhumudwa ndi kukhalabe wokhumudwa.

Kodi Muli Pati?

Tsiku lirilonse, atumiki odzipatulira a Mulungu amakumana ndi nkhani zimene zimayesa kudzipereka kwawo kwa Yehova. Mosasamala kanthu za zimene ayenera kulimbana nazo, ayenera kuima ndi kuŵerengedwa kumbali ya Mfumu Yaumesiya ya Yehova. Olamulira amphamvu a dziko lino atenga kaimidwe kawo “kutsutsana naye Yehova ndi wodzozedwa wake.” Tiri ndi mwaŵi wotani nanga kuima kaamba ka iye!​—Salmo 2:2.

Komabe, sitingalimbane ndi chisonkhezero cha dongosolo la dzikoli ndi mphamvu yathu yokha, chotero timatonthozedwa ndi lonjezo la Yesu la kukhala ndi mpingo wake “kufikira chimaliziro cha nthaŵi ya pansi pano.” (Mateyu 28:20) Iye adzatichilikiza. Kuwonjezerapo, thandizo lalikulu limadza pamene timamatira kwa Yehova ndi kufuna chilikizo kuchokera kwa iye. Kutembenukira ku Mawu ake kungatipatse nyonga. Pamene tidzimva kukhala osakhoza kupirira, Salmo 55:22 likutiitana ‘kumsenza Yehova nkhaŵa zathu, ndipo iye adzatigwiriziza. Nthaŵi zonse sadzalola wolungama agwedezeke.’ Inde, Baibulo likufulumiza anthu a Mulungu onse “kuchirimika m’chikhulupiriro”​—ndipo osati kukhumudwa.​—1 Akorinto 16:13.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena