Yendani mwa Chikhulupiriro
1 Anthu mamiliyoni ambiri amasumika moyo wawo pa chuma chakuthupi, akumadalira mopanda nzeru mphamvu yonyenga ya chuma. (Mat. 13:22) Pamene chuma chawo chitayika kapena kubedwa kapena kukhala chosapindula kwenikweni, iwo amapezapo phunziro loŵaŵa. Tikulimbikitsidwa kulondola njira yanzeru, tikumakalimira chuma chauzimu. (Mat. 6:19, 20) Zimenezi zimaphatikizapo ‘kuyenda mwa chikhulupiriro.’—2 Akor. 5:7.
2 Liwulo “chikhulupiriro” latembenuzidwa kuchokera ku liwu lachigiriki limene limapereka lingaliro la chidaliro, kukhulupirira, kutsimikiza mtima mwamphamvu. Kuyenda mwa chikhulupiriro kumatanthauza kuyang’anizana ndi mikhalidwe yovuta ndi chidaliro mwa Mulungu, kukhulupirira mphamvu yake ya kutsogoza mapazi athu ndi kufunitsitsa kwake kusamalira zofunika zathu. Yesu anapereka chitsanzo changwiro; anasumika maganizo ake pa chimene chinalidi chofunika. (Aheb. 12:2) Mofananamo, tifunikira kusumika mitima yathu pa zinthu zosaoneka zauzimu. (2 Akor. 4:18) Nthaŵi zonse tiyenera kuzindikira kuti moyo wathu wamakono ngwosatsimikizirika ndi kuvomereza kuti timadalira kotheratu pa Yehova.
3 Tiyeneranso kukhala otsimikiza mtima kwambiri kuti Yehova akutitsogolera kupyolera m’gulu lake looneka lotsogozedwa ndi “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.” (Mat. 24:45-47) Timasonyeza chikhulupiriro chathu pamene ‘timvera atsogoleri’ mumpingo. (Aheb. 13:17) Kugwira ntchito modzichepetsa mogwirizana ndi makonzedwe ateokrase kumasonyeza kukhulupirira kwathu Yehova. (1 Pet. 5:6) Tiyenera kusonkhezeredwa kuchirikiza ndi mtima wonse ntchito imene gulu lapatsidwa kuchita. Zimenezi zidzatiyandikizitsa kwa abale athu m’chomangira cholimba cha chikondi ndi umodzi.—1 Akor. 1:10.
4 Mmene Tingalimbitsire Chikhulupiriro: Sitiyenera kulola chikhulupiriro chathu kupinimbira. Tifunikira kulimbikira kuti chiwonjezeke. Phunziro la nthaŵi zonse, pemphero, ndi kupezeka pamisonkhano kudzatithandiza kulimbitsa chikhulupiriro chathu kotero kuti, ndi thandizo la Yehova, chingalake chiyeso chilichonse. (Aef. 6:16) Kodi mwakhazikitsa ndandanda yabwino ya kuŵerenga Baibulo tsiku ndi tsiku ndi kukonzekera misonkhano? Kodi nthaŵi zambiri mumasinkhasinkha pa zimene mumaphunzira, ndipo kodi mumafikira Yehova m’pemphero? Kodi muli ndi chizoloŵezi cha kupezeka pamisonkhano yonse ndi kutengamo mbali mpata utapezeka?—Aheb. 10:23-25.
5 Chikhulupiriro cholimba chimasonyezedwa ndi ntchito zabwino. (Yak. 2:26) Imodzi ya njira zabwino koposa zosonyezera chikhulupiriro chathu ndiyo kulengeza chiyembekezo chathu kwa ena. Kodi mumafunafuna mipata youzira ena uthenga wabwino? Kodi mungasinthe mikhalidwe yanu kuti mukhoze kuchita zambiri mu utumiki? Kodi mumagwiritsira ntchito malingaliro amene timalandira owongolera mkhalidwe wa utumiki wathu ndi kugwira mtima kwake? Kodi mumadziikira zonulirapo zauzimu zaumwini ndi kulimbikira kuti muzifikire?
6 Yesu anachenjeza za kukhala otanganitsidwa mopambanitsa ndi zinthu za moyo wa tsiku ndi tsiku ndi kulola zikhumbo za chuma kapena zadyera kuphimba maso athu auzimu. (Luka 21:34-36) Tiyenera kupenya bwino umo tiyendera kuti tipeŵe kutayika kwa chikhulupiriro chathu. (Aef. 5:15; 1 Tim. 1:19) Tonsefe tikuyembekezera kuti pomalizira pake tidzakhoze kunena kuti ‘talimbana nako kulimbana kwabwino, tatsiriza njirayo, tasunga chikhulupiriro.’—2 Tim. 4:7.