Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w87 8/15 tsamba 10-15
  • Achichepere Kodi Mudzachitanji ndi Moyo wanu?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Achichepere Kodi Mudzachitanji ndi Moyo wanu?
  • Nsanja ya Olonda—1987
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Zitsanzo Zofala
  • Chenjezo Lofunika Kulitsatira
  • Zitsanzo Zoyenera Kuyang’anira
  • Khalani ndi Moyo Kaamba ka Dziko Latsopano la Mulungu
  • Timoteo—‘Mwana Weniweni m’Chikhulupiriro’
    Nsanja ya Olonda—1999
  • Timoteyo Anali Wokonzeka Komanso Wofunitsitsa Kutumikira
    Nsanja ya Olonda—2008
  • Achinyamata—khalani ndi Zolinga Zolemekeza Mulungu
    Nsanja ya Olonda—2007
  • “Mwana Wanga Wokondedwa Ndi Wokhulupirika Mwa Ambuye”
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1987
w87 8/15 tsamba 10-15

Achichepere Kodi Mudzachitanji ndi Moyo wanu?

“Kuti akukhala ndi moyo asakhalenso ndi moyo kwa iwo okha, koma kwa iye amene adawafera iwo.”​—2 AKORINTO 5:15.

1. Kodi ndi chisonyezero cha chiyamikiro chotani chimene anthu ena apanga, ndipo nchifukwa ninji?

ZIKOmo! Moyo wanga uli mungongole kwa inu!’ Anthu opulumutsidwa kuchokera kunyumba yakupsya kapena kumira m’madzi ananenapo zoterozo kwa apulumutsi awo. Ndipo Akristu achichepere oyamikira amakamba mawu oterowo kwa makolo awo. Iwo anali kulozera osati kokha ku moyo wa kuthupi wolandiridwa kuchokera kwa makolo awo komanso makamaka ku chisamaliro chachikondi ndi malangizo amene amaika achichepere panjira ya kulandira “lonjezano iye anatilonjezera ife, ndiwo moyo wosatha.”​—1 Yohane 2:25.

2. Kodi ndi m’chiwunikiro chachidziwitso chiti chimene inu muyenera kulingalira pa funsoli, Nchiyani chimene mudzachita ndi moyo wanu?

2 Chinali chikondi chomwe chinafulumiza Yehova Mulungu kupanga moyo wosatha “moyo weniweni,” wokhalapo kwa aliyense wa ife. “Anatikonda ife, ndipo anatuma Mwana wake akhale chiwombolo chifukwa cha machimo athu.” (1 Timoteo 6:19; 1 Yohane 4:10) Tangolingalirani, kachiwirinso, za chikondi chimene Mwana wake Yesu anasonyeza mwa kufa imfa yowawa kotero kuti tingapeze moyo wosatha! (Yohane 15:13) M’chiwunikiro cha zochitikazi, Nchiyani chimene mudzachita ndi moyo wanu?

3. Kodi nchiyani chimene kawirikawiri chimatsimikizira chimene anthu amachita ndi miyoyo yawo?

3 Achichepere kawirikawiri amafunsidwa funso iri, mu njira imodzi kapena inzake, ndi phungu wa ophunzira pa sukulu kapena ena omwe ali okondweretsedwa ndi mtsogolo mwawo. Kodi nchiyani chimene chidzatsimikizira yankho lanu? Kodi ilo lidzatsimikiziridwa ndi zokonda zaumwini? Kodi nsonga ya kugamulapo kwanu idzakhala umboni kwa awo amene amafuna kuti inu mupeze malo achisungiko mu ntchito ya kudziko? Kapena kodi chimene mudzachita ndi moyo wanu chidzatsimikiziridwa ndi zolingalirapo zapamwamba? Chokumbutsa chouziridwa chimanena kuti: “Koma adafera onse, kuti iwo akukhala ndi moyo asakhalenso ndi moyo kwa iwo okha, koma kwa iye amene adawafera iwo, nauka.” (2 Akorinto 5:15) Inde, chiri chabwino chotani nanga pamene njira imene tigwiritsira ntchito miyoyo yathu iwunikira chiyamikiro kaamba ka zimene Yesu Kristu ndi Atate wake wakumwamba anachita kaamba ka ife!

Zitsanzo Zofala

4. Kodi ndani amene ali zitsanzo zotsanziridwa zofala za lerolino?

4 Komabe, kodi ndi anthu otani amene ali ofala lerolino, awo amene achichepere ambiri mwachisawawa amatsanzira zitsanzo zawo?Kodi iwo sali anthu olemera otchuka a m’dziko, mosasamala kanthu za kaimidwe ka makhalidwe awo abwino? Pamene muyang’ana mu zipinda za achichepere ambiri, kodi ndi zithunzithunzi za ndani zimene mumaziwona zopachikidwa mu makoma? Kawirikawiri ziri zija za anthu oimba, owoneka pa kanema, ndi odziwa za masewera. Achichepere mofala amalota za tsiku lina kufikira chipambano chofananacho cha kudziko kapena ngakhale kukwatira wina wake wokhala ndi mawonekedwe akuthupi a anthu amenewa. Bwanji ponena za inu? Kodi nchiyani chimene mumafuna m’moyo?

5, 6. (a) Kodi nchifukwa ninji chinganenedwe kuti chipambano chadziko chimalephera kubweretsa chikhutiritso chenicheni? b) Kodi nchiyani chimene chiri magwero a chikhutiritso chenicheni?

5 Ngati inu munafikira chipambano cha ku dziko cha anthu okumbukiridwa okhumbidwa, kodi inu kwenikwenidi mudzakhala achimwemwe ndi okhutiritsidwa? Mmodzi wa osewera achipambano kwambiri a Hollywood ananena kuti: “Ndalawa kale kukhala wolemera ndi zinthu zina zonse za kuthupi. Izo sizitanthauza chirichonse. Pali kusokonezeka maganizo kumene kumapita ndi dziwe losambiramo liri lonse pano, osatchula kutha kwa maukwati ndi ana amene ainada makolo awo.”​—Mlaliki 5:10; 1 Timoted 6:10.

6 Wophunzira wothamanga wotchuka kwambiri, wopeza mphoto ya gulu la akazi la liwiro la makilomita 10 wa mu 1981 mu New York, anakhala wosokonezeka maganizo kotero kuti anafuna kudzipha. “Ndaphunzira chowonadi chambiri ponena za moyo mu miyezi yochepa yapita,” iye analemba pambuyo pake. “Chimodzi cha icho chiri chakuti chikhutiritso chowona sichimapezedwa mu njira zimene anthu ambiri amakalamira kaamba ka ungwiro ndi zofikiritsa. Chikhutiritso kwa ine sichinabwere kuchokera ku kukhala wophunzira wa mu gulu A, ngwazi yodziwa kuthamanga ya mu boma kapena kukhala msungi wa chiwerengero chokongola kwambiri.” Inde, anthu amafunikira kuphunzira kuti chikhutiritso chowona chimachokera kokha mwa kukhala ndi unansi waumwini ndi Mulungu, amene kokha angapereke mtendere weniweni ndi chimwemwe.​—Masalmo 23:1, 6; 16:11.

7. Ponena za kuzindikira chikwaniritso chenicheni, kodi maphunziro a pa koleji ndi chipambano cha dziko ziri zofunika motani?

7 Mwachiwonekere, ndiyeno, simukafunikira kufuna kutsanzira awo amene amalimbana kokha kuti apeze kutchuka ndi chuma. Ngakhale olemba a kudziko amadziwa kulephera kwa kubweretsa chikhutiritso chenicheni kwa chipambano cha kudziko. Wolemba nkhani mu danga la nyuzipepala Bill Reel analemba kuti: “Mumamaliza maphunziro a pa koleji ndi maloto a mtsogolo. Mwachisoni, zambiri za zolingalira zanu zikatembenukira ku phulusa. Sindikufuna kukunyazitsani inu, koma chingakhale bwino kuti mumve chowonadi: Pamene mupeza chuma chimene muchikhumba, ngati mungachipeze icho, ndipo kenaka mupeza zipambano zimene mulondola, ngati mungazipeze izo, sizidzakukhutiritsani, m malo mwake, panthawi imodzimodziyo pamene mudzayembekezera kukhala mukupambana m’chipambano, mudzadzimva kukhala wopanda kanthu m’malo mwa kudzimva kukhala wokwaniritsidwa, wopsyinjika m’malo mwa kusangalatsidwa, wokwiyitsidwa m’malo mokhala wa mtendere.”​—New York Daily News, May 26, 1983.

8. Kodi ndi chifukwa chiti champhamvu chimene chiripo cha kusalondolera ntchito ya kudziko?

8 Koma kwa ife amene tiri ogalamuka pa kufunika kwa zochitika za dziko m’chiwunikiro cha ulosi wa Baibulo, pali zifukwa zambiri zamphamvu za kusaikira ntchito ya kudziko kukhala yofunika kwambiri m’moyo. (Mateyu 24: 3-14) Tingadziyerekezere ife eni ndi munthu amene amawona nyumba yokhala ndi chizindikiro: “Kampani iyi Ikutha Ntchito.” Kodi tingapite kukafuna ntchito kumeneko? Ndithudi ayi! Ndipo ngati ife timagwira ntchito kukampani imeneyo, mwanzeru tingafune ntchito kwmakwake. Chabwino, chizindikiro chiri chowonekera kuli konse pa malo ophunzirira ntchito a dziko iri, “Likutha Ntchito​—Mapeto ali Pafupi!” Inde, “Dziko lapansi lipita,” Baibulo limatitsimikizira ife. (1 Yohane 2:17) Chotero, mwanzeru, sitidzatsanzira monga zitsanzo zabwino awo amene mozama ali okhudzidwa ndiilo.

Chenjezo Lofunika Kulitsatira

9. Kodi ndi thandizo la kudziko lotani limene awo amene amawoneka kukhala akufuna zabwino koposa kaamba ka inu angapereke?

9 Moyo wanu umawongoleredwa osati kokha ndi awo amene mumawakonda, koma kawirikawirinso ndi achibale ndi mabwenzi amene, monga mmene anachiikira icho,‘amafuna zabwino kwambiri kaamba ka inu.’ ‘Muyenera kumadzipezera ndalama,’ iwo angatero. Chotero angakuthandizeni inu kupeza maphunziro a ku koleji kapena yuniversite kudzikonzekeretsa inumwini kaamba ka ntchito yokhala ndi malipiro abwino. ‘Wolemba Baibulo Luka anali sing’anga,’ iwo angadziwitse tero, ‘ndipo mtumwi Paulo analangizidwa ndi mphunzitsi wa Lamulo Gamaliyeli.’ (Akolose 4:14; Machitidwe 5:34; 22:3) Koma, santhulani mosamalitsa thandizo loterolo.

10. Kodi ndi thandizo lotani limene Luka ndi Paulo anapereka, ndipo nchiyani chimene chinganenedwe ponena za ntchito yawo asanakhale Akristu?

10 Sing’anga Luka sanawalimbikitse konse Akristu kutsatira chitsanzo cha ntchito yake yoyamba mwa kukhala adokotala; m’malo mwake Luka anasunga moyo wa Yesu ndi atumwi ake kaamba ka kuwutsanzira. Mwachidziwikire Luka anakhala sing’anga asanaphunzire ponena za Kristu koma pambuyo pake anaika utumiki wake Wachikristu kukhala woyamba m’moyo. Mkhalidwewo unali wofanana ndi Paulo. M’malo mwa kulimbikitsa ena kumutsanzira iye monga mmene anatsanzirira Gamaliyeli, Paulo analemba: “Khalani onditsanza ine, monga inenso nditsanza Kristu.” Paulo anawona chidziwitso cha Kristu kukhala chamtengo wapatali kotero kuti iye ananena kuti mwakuyerekeza iye analingalira zolondola zake zakale kukhala “zapadzala.”​—1 Akorinto 11:1; Afilipi 3:8.

11. (a) Kodi nchiyani chimene Petro anamuuza Yesu, ndipo kodi nchifukwa ninji? (b) Kodi ndimotani mmene Yesu anayankhira?

11 Kumbukirani, kawonedwe ka zinthu kangapangitse ngakhale awo amene amakukondani inu kupereka thandizo loipa. Mwachitsanzo, pamene Yesu analankhula za zimene zinali kumuyembekezera iye mkati mwa utumiki wake mu Yerusalemu, mtumwi Petro anayankha: “Dzichitireni chifundo, Ambuye; sichidzatero kwa inu ayi.” Petro anamkonda kwambiri Yesu ndipo sanafune kuwona iye akuvutika. Koma Yesu anamdzudzula Petro chifukwa iye anazindikira kuti kuti akwaniritse chifuno cha Mulungu chikaphatikizapo ponse pawiri kuvutika ndi kuphedwa ndi otsutsa.​—Mateyu 16:21-23.

12. Kodi ndi thandizo lotani limene anthu akawonedwe kabwino angapereke kwa achichepere, ndipo nchifukwa ninji?

12 Mofananamo, makolo ena kapena mabwenzi angakukwatuleni inu kuchoka ku njira ya kudzipereka kwanu. Chifukwa chakawonedwe kochenjezedwa molakwa, iwo angasinkhesinkhe kukulimbikitsani inu kutenga ntchito mu utumiki wa upainiya wa nthawi zonse, kutumikira monga mishonale, kapena kuchita ntchito yodzipereka pa ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova. Iwo anganene kuti: ‘M’malo mwake, bwanji osakwatira ndi kukhala kufupi ndi ife?’ Kapena, ‘Ukudziwa, ntchito iri yovuta ku Beteli. Mwinamwake chiri chabwino kuti iwe ukhale ndi ife?’ Mu mawu ena, monga mmene Petro anachiikira icho, “Dzichitireni chifundo.”

13. (a) Kodi ndi kayang’anidwe kowongolera kotani kamene Petro anakasonyeza? (b) Kodi nchiyani chimene chikuphatikizidwamo mu kukhala Mkristu wowona?

13 Ngakhale atumiki a Yehova nthawi zina amafunikira kuwongolera kalingaliridwe kawo. Petro anafunikira kutero, ndipo ndi kawonedwe kowongoleredwa, iye analemba: “Pakuti kudzachita ichi mwaitanidwa; pakutinso Kristu anamva zowawa m’malo mwanu, nakusiyirani chitsanzo kuti mukalondole mapazi ake.” (1 Petro 2:21) Kukhala moyo ndi moyo Wachikristu wowona kumaphatikizapo kudzipereka kwaumwini, inde, ngakhale kuvutika. Iyo sindiyo njira yokhweka, koma iri imodzi ku imene tinaitanidwa monga Akristu. Kuilandira iyo kumaphatikizapo ‘kusakhalanso ndi moyo kwa ife eni, koma kwa iye amene anatifera ife.’ (2 Akorinto 5:15) Kusunga m’chiyang’aniro zitsanzo zabwino zoyenera kuzitsanzira chidzatithandiza ife kusunga miyoyo yathu mu njira imeneyi ya kudzipereka kwaumwini.

Zitsanzo Zoyenera Kuyang’anira

14. Kodi ndi chitsanzo chotani chimene Yesu anachipereka?

14 Chitsanzo chimene mwapadera muyenera kuchiyang’ana chiri chimene Yesu anapereka. Monga munthu wangwiro, iye akanakhala wothamanga wopambana koposa, woyimba, sing’anga, kapena loya amene dziko lapansi likadamudziwa. Koma chisamaliro chake chinalunjikitsidwa pa kusangalatsa Atate wake wa kumwamba, ngakhale pamene Yesu anali wachichepere. (Luka 2:42-49) Iye pambuyo pake ananena kuti: “Kundiyenera ine ndilalikire mbiri yabwino ya ufumu wa Mulungu, chifukwa ndinatumidwa kudzatero.” (Luka 4:43) Chirimwe chapita mu kalata ya magazini ya tchalitchi Ministry inalongosola kuti: “Mpulumutsi wathu anakonda kuchoka pa khamu, ndipo kenaka Anapita kunyumba ndi nyumba​—kusaka moyo. Khamu la moyo umodzi linamusangalatsa. Kenaka Iye anatsanula chowonadi​—chikondi cha Mulungu.”​—Luka 10:1-16.

15. (a) Kodi nchifukwa ninji kulalikira kwa kunyumba ndi nyumba kuli chitokoso? (b) Kodi nchiyani chimene chimasonyeza kuti utumiki wa ku nyumba ndi nyumba wa achichepere uli wokhutiritsa?

15 Chitalingaliridwa, kulalikira kwa kunyumba ndi nyumba sikuli kopepuka. Kumafunikira phunziro losamalitsa kuti mumvetsetse mbiri yabwino ya Ufumu ndi ntchito yochuluka ya kukonzekera kaperekedwe katanthauzo. Ndiponso, utumiki umenewu umafunikira kulimba mtima, popeza eninyumba ambiri sali osangalatsidwa, ndipo ena amakhala ankhalwe. Komabe, utumiki wa kunyumba ndi nyumba wa inu achichepere ukukhala ndi zotulukapo zosangalatsa, monga momwe chinawonedwera mu magazini ya tchalitchi ya ku Italy La Voce. Mlembiyo ananena kuti: “Mwaumwini, ndimakonda Mboni za Yehova,” zimene, iye akulongosola kuti, “zimabwera ndi kukuchezerani panyumba yanu.” Iye anachitira ndemanga: “Zimene ndimazidziwa ziri mopanda china zamakhalidwe abwino, zolankhula bwino; anthu okongolanso ndipo mochulukira achichepere. Kukongola ndi uchichepere pamene zisonyezedwa, zimakhala zokakamiza kwambiri.”

16. (a) Ndi kaamba ka ntchito iti imene achichepere afunikira kuyamikiridwa? (b) Kodi ndimotani mmene gulu la Mboni za Yehova limayerekezedwera ndi matchalitchi m’kuchita ntchito yofunika kwambiri padziko lapansi?

16 Ndithudi, inu achichepere amene mukulandira Kristu monga chitsanzo chanu muyenera kuyamikiridwa! Achichepere oposa 12, 000, a zaka 25 ndi kutsika pansi, ali mu ntchito ya upainiya mu United States, ndipo makumi a zikwi zowonjezereka ali kuchita upainiya kwina kwake. (Masalmo 110:3) Khalani otsimikizirika kuti kulibe ntchito iriyonse imene mungachite imene iri yabwino koposa! Ngakhale wolemba wotchulidwa pamwambapo m’magazini ya tchalitchi ananena kuti: “Mulungu amanena kuti ntchito yabwino kwambiri iri ya kuchezera kunyumba ndi nyumba​—kusaka moyo,” koma anapitiriza, “Kodi nchiyani chimene munganene ponena za funso limeneli? Kodi ndi kuchezera kochulukira kotani kumene inu ndi ine tikuchita? Sindinawonepo kutchulidwa kochulukira kwa mtundu wa ntchito mu MINISTRY.” Kodi sitingakhale oyamikira kuti timayanjana ndi gulu limene limagogomezera kufunika kwa kutsanzira chitsanzo cha Yesu cha kulalikira?

17. Kodi nchiyani chimene Timoteo anakwaniritsa pamene mwinamwake anali adakali wachichepere wa zaka za pakati pa 13 ndi 19, ndipo nchiyani chimene chimasonyeza kuti iye angakhale anali wachichepere panthawi imeneyo?

17 Popeza chimene mudzachita ndi moyo wanu mokulira chidzasonkhezeredwa ndi awo amene mumakhumbira, kulitsani kusiriranso kaamba ka chitsanzo choperekedwa ndi Timoteo wachichepere. Atabadwa mwamsanga isanafike imfa ya Yesu, Timoteo monga mwamuna wachichepere anachoka ku banja lake ndi kugwirizana ndi mtumwi Paulo pa ulendo wake wachiwiri wa umishonale. Miyezi yochepa pambuyo pake khamu la anthu linakakamiza Paulo ndi Silasi kuthawa ku Tesalonika, koma osati asanapange ophunzira ena. (Machitidwe 16:1-3; 17:1-10, 13-15) Mwamsanga pambuyo pake Paulo anatumiza Timoteo mu gawo lowopsya limenelo kukawatonthoza ophunzira amenewa mu ziyeso zawo. (1 Atesalonika 3:1-3) Timoteo mwinamwake anali kumapeto kwa zaka zake za pakati pa 13 ndi 19 panthawiyo, popeza kuti zaka zina 12 mpaka 14 pambuyo pake Paulo anali kulankhulabe ponena za “uchichepere” wake. (1 Timoteo 4:12) Kodi simumasirira wachichepere wolimba mtima, wodzipereka woteroyo?

18. Kodi nchifukwa ninji Paulo anafunikira kumutumiza Timoteo ku Akorinto?

18 Zaka zisanu pambuyo pa kugawiridwa gawo kwa Timoteo la kulimbikitsa abale mu Tesalonika, Paulo analemba kwa abale a ku Akorinto kuchokera ku Efeso: “Khalani akutsanza ine. Chifukwa cha ichi ndatuma kwa inu Timoteo, . . . amene adzakumbutsa njira zanga za mwa Kristu, monga ndiphunzitsa ponsepo mu mipingo yonse.” (1 Akorinto 4:16, 17) Timoteo wachichepere, pokhala atagwira kale ntchito zaka zisanu ndi Paulo, anali wozolowe- rana ndi njira za kuphunzitsira za Paulo. Iye anadziwa mmene Paulo anaperekera uthenga kwa Aefeso, kuphatikizapo ndi mmene iye anaphunzitsira “pabwalo ndi kunyumba ndi nyumba.” (Machitidwe 20:20, 21) Pokhala ataphunzitsidwa bwino chotero mu njira zolalikira, Timoteo anali thandizo labwino chotani nanga ku mipingo!

19. Kodi nchiyani chimene Paulo ananena ponena za Timoteo patapita zaka zoposa khumi pambuyo pa kuyamba kutumikira pamodzi?

19 Zaka zina zisanu kapena zisanu ndi chimodzi zinapita, ndipo Paulo anali m’ndende ku Roma. Timoteo, amene iyemwini posachedwapa anali atatulutsidwa m’ndende, ali ndi iye. (Ahebri 13:23) Tangolingalirani chochitikacho: Mwinamwake akugwiritsira ntchito Timoteo monga mlembi, Paulo akulemba kalata ku Afilipi. Akulankhula mwadala, Paulo akupitiriza: “Koma ndiyembekeza mwa Ambuye Yesu kuti tidzatumiza Timoteo kwa inu msanga . . . Pakuti ndiribe wina wa mtima womwewo, ye- mwe adzasamalira za kwa inu ndi mtima wowona . . . Koma muzindikira matsimikizidwe ake, kuti monga mwana achitira atate wake, anatumikira pamodzi ndi ine uthenga wabwino.”​—Afilipi 1:1; 2:19-22.

20. Kodi nchiyani chimene chinapanga Timoteo kukhala chitsanzo choyenera kuchitsanzira chokhumbirika kwa achichepere?

20 Ndithudi, Timoteo wachichepere ali chitsanzo chokhumbirika! Iye anali mnzake wa Paulo wodalirika, wokhulupirika, womamatira kwa iye kupyolera m’nsautso, nachirikiza iye mu ntchito yolalikira, ndi kukhala wofunitsitsa kutumikira kuli konse kumene anatumizidwa. Iye anapereka chomwe chitchedwa moyo wake wachibadwa wa panyumba, koma ndi chikhutiritso ndi chikwaniritso chotani nanga chimene moyo wake mu utumiki wa Mulungu unabweretsa kwa iye! Timoteo mowonadi ‘sanali kukhalira moyo kwa iye yekha, koma kwa Kristu amene anali atafa kaamba ka iye.’ (2 Akorinto 5:15) Kodi inu mwafulumizidwa kutsanzira chitsanzo chake?

Khalani ndi Moyo Kaamba ka Dziko Latsopano la Mulungu

21. Kodi nchifukwa ninji tinganene kuti Timoteo anali ndi malingaliro auzimu?

21 Timoteo, m’chenicheni, anali kukhala ndi moyo kaamba ka dziko latsopano la Mulungu. Iye sanali kulingalira kokha zatsopano koma anali kugwiritsira ntchito moyo wake kubweretsa zotulukapo zosatha. (Mateyu 6:19-21) Popeza atate wake a Timoteo anali m’Griki ndipo mwachiwonekere wosakhulupirira, iye angakhale anafulumiza Timoteo kulondola maphunziro apamwamba ndi ntchito ya kudziko. Koma monga chotulukapo cha malangizo aumulungu ochokera kwa amayi wake ndi agogo wake, moyo wa Timoteo unakutidwa ndi mpingo Wachikristu. Iye analondola zikondwerero zauzimu, ndipo mwachiwonekere anakhala wosakwatira kwa chifupifupi nthawi yotalikirapo, ndipo woyenerera kutumikira ndi mtumwi Paulo.​—2 Timoteo 1:5.

22. Kodi ndimotani mmene kabroshuwa ka School kamawunikirira kwa achichepere lerolino njira ya moyo yofanana ndi ya Timoteo?

22 Bwanji ponena za inu? Kodi mudzagwiritsira ntchito uchichepere wanu mu njira imene Timoteo anachitira? Kabroshuwa ka School and Jehovah’s Witnesses kanali kulozera ku njira imeneyo ya moyo pamene kanalongosola ponena za Mboni zachichepere: “Chonulirapo chawo chachikulu mu moyo chiri kutumikira mokhutiritsa monga aminisitala a Mulungu, ndipo iwo amayamikira sukulu monga thandizo ku mapeto ameneo. Chotero iwo mwachisawawa amasankha kosi imene iri yogwirira ntchito kaamba ka kuchirikiza iwo eni mu dziko lamakono. Chotero, ambiri angatenge ntchito ya utumiki kapena kukapezeka pa sukulu ya ntchito ya utumiki. Pamene achokapa sukulu amakhumba kupeza ntchito imene idzawatheketsa iwo kumamatira ku ntchito yawo ya utumiki yeniyeni, utumiki Wachikristu.”

23. Kodi nchifukwa ninji sichiyenera kukhala cholimba kwa achichepere Achikristu kuyankha funso ili, Kodi nchiyani chimene ndidzachita ndi moyo wanga?

23 Kwa inu amene mowonadi mumayamikira zimene Yehova Mulungu ndi Mwana wake achita kaamba ka inu, sichiyenera kukhala chovuta kuyankha funso ili: Kodi nchiyani chimene ndidzachita ndi moyo wanga? M’malo mwa kudzikhalira ndi moyo kwa inumwini ndi zosangalatsa zaumwini, mudzagwiritsira ntchito moyo wanu kuchita chifuno cha Mulungu. Mudzakhala ndi moyo, monga momwe anachitira Timoteo, monga munthu wauzimu.

Mafunso Akubwereramo

◻ Kodi nchifukwa ninji Akristu owona sayenera kuika ntchito za kudziko patsogolo m’moyo?

◻ Kodi ndi thandizo lolakwika lotani limene ena apereka, koma kodi nchiyani chimene tingaphunzire kuchokera ku yankho la Yesu kwa Petro?

◻ Ndi mu njira zotani mmene Yesu ndi Timoteo anaperekera zitsanzo zabwino zoyenera kuzitsanzira kwa achichepere?

◻ Kodi nchiyani chimene chikuphatikizidwapo m’kukhala ndi malingaliro auzimu?

[Chithunzi patsamba 12]

Luka, ngakhale anali sing’anga wophunzitsidwa, anaika zoyambirira za Chikristu poyamba m’moyo

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena