Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Kuyamikira Kaamba ka Abale Athu
    Nsanja ya Olonda—1988 | October 1
    • 10 Mu Linguistic Key to the Greek New Testament, Fritz Rienecker akuchitira ndemanga pa liwu lotembenuzidwa “kwenikweni,” kapena “motambasuka,” mu 1 Petro 1:22. Iye akulmeba kuti: “lingaliro lokulira liri lija la kufunitsitsa, changu (kuchita chinthu osati mopepuka . . . koma monga mmene zinaliri ndi kuvutikira) (Hort).” Kuvutikira kumatanthauza, pakati pa zinthu zina, “kutambasuka ku mlingo wokulira.” Chotero kukondana wina ndi mnzake kwenikweni kuchokera mu mtima kumatanthauza kudziikizako ife eni mokwanira m’kuyesayesa kwathu kwa kukhala ndi chiyanjo chaubale kaamba ka anzathu Achikirstu onse. Kodi ena a abale ndi alongo athu ali opsyinjika m’chiyanjo chathu chachikondi? Ngati ndi tero, tifunikira kukulitsa.

  • Kuyamikira Kaamba ka Abale Athu
    Nsanja ya Olonda—1988 | October 1
    • 11, 12. (a) Ndi uphungu wotani umene mtumwi Paulo anapereka kwa Akristu mu Korinto? (b) Ndimotani mmene Pualo anakhazikitsira chitsanzo chabwino m’mbaliyi?

      11 Mtumwi Paulo mwachiwonekere anamva kufunika kaamba ka ichi mu mpingo wa ku Korinto. Iye analembera Akristu kumeneko kuti: “Mkamwa mwathu m’motseguka kwa inu, Akorinto, mtima wathu wakulitsidwa. Simupsyinjika mwa ife, koma mupsyinjika mumtima mwanu. Ndipo kukhale chibwezero chomwechi​—ndinena monga ndi ana anga​—mukulitsidwe inunso.”​—2 Akorinto 6:11-13.

      12 Kodi ndimotani mmene tingakulitsire mitima yathu kuti tiphatikize abale ndi along athu onse? Paulo anakhazikitsa chitsanzo chabwino m’mbaliyi. Iye m’chenicheni anafunafuna zabwino mwa abale ake, ndipo anawakumbukira iwo osati kaamba ka zolephera zawo koma kaamba ka mikhalidwe yawo yabwino. Mutu wotsirizira wa kalata yake kwa Akristu mu Roma umasonyeza chimenechi. Tiyeni tisanthule Aroma mutu 16 ndi kuwona mmene umwunikirira mkhalidwe weniweni wa Paulo kulinga kwa abale ndi alongo ake.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena