Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Utumiki Wothandiza Anthu pa Nthawi ya Mavuto
    Ufumu wa Mulungu Ukulamulira
    • 6. (a) Malinga ndi zimene Paulo ananena, n’chifukwa chiyani tinganene kuti ntchito yothandiza anthu ndi mbali ya kulambira kwathu? (b) Fotokozani mmene ntchito yothandiza anthu pa mavuto ikuchitikira padziko lonse lapansi. (Onani bokosi lakuti “Kukonzekera Masoka a Chilengedwe” patsamba 214.)

      6 Paulo anathandiza Akorinto kuti adziwe chifukwa chake ntchito yothandiza anthu inali mbali ya utumiki komanso kulambira kwawo Yehova. Iye ananena kuti: Akhristu amene amathandiza Akhristu anzawo amachita zimenezo chifukwa ‘chogonjera uthenga wabwino wonena za Khristu.’ (2 Akor. 9:13) Choncho, pofuna kutsatira zimene Khristu anaphunzitsa, Akhristu amathandiza okhulupirira anzawo. Paulo ananenanso kuti zinthu zabwino zimene amachitira abale awo ndi ‘kukoma mtima kwakukulu kumene Mulungu wawasonyeza.’ (2 Akor. 9:14; 1 Pet. 4:10) Posonyeza kufunika kotumikira abale athu amene ali pa mavuto, Nsanja ya Olonda ya December 1, 1975, inanena kuti: “Tisamakayikire kuti Yehova Mulungu ndi Mwana wake Yesu Khristu amaona kuti utumiki umenewu ndi wofunika kwambiri.” Izi zikusonyeza kuti kuthandiza anthu amene ali pa mavuto ndi mbali yofunika kwambiri ya utumiki wopatulika.​—Aroma 12:1, 7; 2 Akor. 8:7; Aheb. 13:16.

  • Utumiki Wothandiza Anthu pa Nthawi ya Mavuto
    Ufumu wa Mulungu Ukulamulira
    • 7, 8. Kodi cholinga chathu choyamba pothandiza anthu amene ali pa mavuto ndi chiyani? Fotokozani.

      7 Kodi zolinga zathu pogwira ntchitoyi ndi zotani? Paulo anayankha funso limeneli m’kalata yake yachiwiri yopita kwa Akorinto. (Werengani 2 Akorinto 9:11-15.) M’mavesi amenewa, Paulo anafotokoza zifukwa zitatu, kapena kuti zolinga, zimene timakwaniritsa tikamachita nawo “utumiki wothandiza anthu umenewu.” Tiyeni tikambirane zolinga zimenezi chimodzi ndi chimodzi.

      8 Choyamba, utumiki wothandiza anthu amene ali pa mavuto umalemekeza Yehova. Onani kuti m’mavesi 5 amene tawerenga pamwambawa, Paulo analimbikitsa abale kuganizira kwambiri za Yehova Mulungu. Mtumwiyu anawakumbutsa “kuyamika Mulunguyo” ndiponso “kupereka mapemphero ochuluka oyamika Mulungu.” (Vesi 11, 12) Anafotokoza mmene ntchito yothandiza anthu amene ali pa mavuto imachititsira Akhristu ‘kulemekeza Mulungu’ ndiponso kuyamikira “kukoma mtima kwakukulu [kwa] Mulungu.” (Vesi 13, 14) Paulo anamaliza nkhaniyi ndi mawu akuti: “Tikuyamika Mulungu.”​—Vesi 15; 1 Pet. 4:11.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena