Kutengapo Phunziro pa Zolakwa Zakale
MALAMULO a Mlengi wathu onena za makhalidwe abwino adzakhalapo kosatha ndipo ngosasinthika. Nchifukwa chake pulinsipulo lopezeka pa Agalatiya 6:7 limagwiranso ntchito lerolino, ndipo limati: “Chimene munthu achifesa, chimenenso adzachituta.” Zoonadi, munthu angakane kuti sadzadziŵerengera mlandu kwa Mulungu pazimene anachita, koma lamulo la Mulungu limeneli silisintha. Ndithudi, palibe munthu amene angathe kupeŵa zotsatirapo za zochita zake.
Nanga bwanji ponena za munthu amene anali kuchita zoipa ndipo kenaka wasintha, nakhala mtumiki wa Mulungu? Iye angayang’anizanebe ndi zotsatirapo za moyo wake wakale. Komabe, zimenezi sizitanthauza kuti Mulungu sanamkhululukire ayi. Chigololo cha Mfumu Davide ndi Bateseba chinadzetsa mavuto ambiri pamoyo wa Davideyo. Iye sanathe kuwapeŵa. Komatu anali atalapa, ndipo Mulungu anali atamkhululukira.—2 Samueli 12:13-19; 13:1-31.
Kodi munamvapo chisoni pamene munayang’anizana ndi zotsatirapo za zolakwa zanu? Kumva chisoni chifukwa cha zolakwa zathu, ngati tikuona moyenerera, kungatikumbutse kuti ‘tizichenjera, tisalunjike kumphulupulu.’ (Yobu 36:21) Inde, kumva chisoni kungatithandizire kupeŵa kubwereza kuchita choipa. Chosangalatsa nchakuti Davide anagwiritsira ntchito phunziro limene anatengapo pa tchimo lake kuti limthandize komanso kuthandiza ena. Iye anati: “Ndidzalangiza ochimwa njira zanu; ndipo olakwa adzabwera kwa Inu.”—Salmo 51:13.
[Zithunzi patsamba 7]
Davide anatengapo phunziro pa tchimo lake ndi Bateseba