-
Yehova Akusonkhanitsa Banja LakeNsanja ya Olonda—2012 | July 15
-
-
7. Kodi tingatani kuti ‘tisunge umodzi wathu mwa mzimu’?
7 Popeza kuti timakhulupirira nsembe ya dipo ya Khristu, Yehova amationa kuti ndife olungama. Iye amaona kuti odzozedwa ndi ana ake ndipo nkhosa zina ndi mabwenzi ake. Ngakhale zili choncho, m’dziko loipali nthawi zina timasemphana maganizo. (Aroma 5:9; Yak. 2:23) N’chifukwa chake Baibulo limatiuza kuti tiyenera kupitiriza ‘kulolerana.’ Kodi tingatani kuti tizigwirizana ndi Akhristu anzathu? Tiyenera kuyesetsa kukhala ‘odzichepetsa nthawi zonse ndiponso ofatsa.’ Paulo anatilimbikitsa kuti ‘tiziyesetsa ndi mtima wonse kusunga umodzi wathu mwa mzimu, ndi mwamtendere monga chomangira chotigwirizanitsa.’ (Werengani Aefeso 4:1-3.) Kuti zimenezi zitheke, tiyenera kulola mzimu wa Mulungu kutitsogolera ndiponso kutithandiza kukhala ndi makhalidwe amene mzimuwu umatulutsa. Makhalidwe amenewa amatigwirizanitsa koma ntchito za thupi zimasokoneza mgwirizano.
-
-
Yehova Akusonkhanitsa Banja LakeNsanja ya Olonda—2012 | July 15
-
-
9. Kodi tingadzifunse mafunso ati kuti tione ngati tikuyesetsa ‘ndi mtima wonse kusunga umodzi wathu mwa mzimu’?
9 Tonsefe tiyenera kudzifunsa kuti: ‘Kodi ndimayesetsa ndi mtima wonse “kusunga umodzi wathu mwa mzimu, ndi mwamtendere monga chomangira chotigwirizanitsa”? Kodi ndimatani pakakhala mavuto? Kodi ndimakonda kuuza anthu ambiri n’cholinga choti andiikire kumbuyo? Kodi ndimafuna kuti akulu andithetsere mavuto anga ndikasemphana maganizo ndi munthu wina m’malo moyesetsa pandekha kukhazikitsa mtendere? Kodi ndimapewa anthu amene amaona kuti ndawalakwira n’cholinga choti tisakambirane?’ Kodi kuchita zinthu zimenezi kungasonyeze kuti tikugwirizana ndi cholinga cha Yehova chosonkhanitsa anthu kuti akhale banja limodzi lolamuliridwa ndi Khristu?
10, 11. (a) Kodi kukhala pa mtendere ndi abale athu n’kofunika bwanji? (b) Kodi tingachite chiyani kuti tilimbikitse mtendere ndiponso kuti Yehova atidalitse?
10 Yesu anati: “Ngati wabweretsa mphatso yako paguwa lansembe, ndipo uli pomwepo wakumbukira kuti m’bale wako ali nawe chifukwa, siya mphatso yako patsogolo pa guwa lansembe pomwepo. Pita ukayanjane ndi m’bale wako choyamba, ndipo ukabwerako, pereka mphatso yako. Thetsa nkhani mofulumira.” (Mat. 5:23-25) Yakobo analemba kuti: “Chilungamo ndicho chipatso cha mbewu zimene anthu odzetsa mtendere amafesa mu mtendere.” (Yak. 3:17, 18) Choncho sitingapitirize kuchita chilungamo ngati sitili pa mtendere ndi anthu ena.
11 Mwachitsanzo, m’madera amene kunkachitika nkhondo, malo ambiri salimidwa chifukwa choti anthu amaopa mabomba amene anakwiriridwa. Bomba likaphulika, anthu amasiya kulima dera lonselo. Izi zimachititsa kuti anthu a m’midzi asowe ntchito ndipo m’mizinda anthu amasowanso chakudya. Ifenso tikhoza kukhala ngati mabombawa ngati timavutika kukhala mwamtendere ndi anthu ena. Izi zingatilepheretse kukhala ndi makhalidwe abwino. Ngati zili choncho, tiyenera kusintha. Tikamafulumira kukhululuka ndiponso kuchitira ena zabwino, tingakhale pa mtendere ndiponso Yehova adzatidalitsa.
-