Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g90 1/8 tsamba 14-16
  • Amai ndi Atate Ali Osaphunzira Kodi Ndingawalemekeze Bwanji?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Amai ndi Atate Ali Osaphunzira Kodi Ndingawalemekeze Bwanji?
  • Galamukani!—1990
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Chifukwa Chake Ulemu Uli Woyenera
  • Maphunziro Amene Makolo Ali nawo
  • Osaphunzira koma Achipambano
  • Khalani Thandizo kwa Makolo Anu!
  • Kodi Mwana Wanga Azipita ku Sukulu?
    Nsanja ya Olonda—2003
  • Kulemekeza Makolo Athu Okalamba
    Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja
  • Kodi Ndingatani Kuti Ndidziwane Bwino Ndi Makolo Anga?
    Galamukani!—2009
  • Achinyamata Mumasangalatsa Mtima wa Makolo Anu
    Nsanja ya Olonda—2007
Onani Zambiri
Galamukani!—1990
g90 1/8 tsamba 14-16

Achichepere Akufunsa Kuti . . .

Amai ndi Atate Ali Osaphunzira Kodi Ndingawalemekeze Bwanji?

THOMAS EDISON ali wodziwika dziko lonse kukhala amene anayamba kupanga gulobo ya nyali yamagetsi. Henry Ford mofananamo akudziŵika dziko lonse kukhala amene anayambitsa maluso opangila zinthu m’maunyinji okulira m’kapangidwe ka zinthu. Koma kodi munadziŵa kuti onse awiri Henry Ford ndi Thomas Edison anali ndi maphunziro ochepera?

Mtumwi Petro ndi Yohane anali mizati ya mpingo Wachikristu woyambilira. Iwo anali alankhuli olimba mtima ndi okhutiritsa a chowonadi. Komabe, iwo ananenedwa kukhala “osaphunzira ndi opulukira” ponena za maphunziro akudziko.—Machitidwe 4:13.

Inde, kupyola m’mbiri yonse pakhala amuna ndi akazi amene akwaniritsa zinthu zazikulu mosasamala kanthu za kukhala ndi maphunziro ochepera. Ndipo palibe munthu wolingalira amene akawasuliza iwo pambali imeneyo. Chotero, mowonekera, pali zambiri ku phindu la munthu ndi ulemu kuposa maphunziro.

Kumeneku sikunena kuti maphunziro ali osafunika kapena kuti kusaphunzira, kusakhoza kuwerenga ndi kulemba, sikuli chosowa. M’maiko ambiri, munthu wopanda dipuloma ya ku sukulu amakhala ndi vuto lalikulu kupeza ntchito. Wina wosakhoza kuŵerenga sangakhoze kudziŵa nzeru yotsekeredwa m’mabukhu ndi magazine. Munthu amene sakhoza kulemba angachititsidwe manyazi pamene afunsidwa kusaina dzina lake kapena kudzaza formu.

Ngakhale kuli tero, bwanji ngati makolo anu ali osaphunzira? Mu Africa ndi mbali zina za maiko otukuka kumene, sichiri chachilendo kwa achichepere ophunzira kukhala ndi makolo osakhoza kuŵerenga ndi kulemba. Ndipo ngakhale m’maiko otsungula, achichepere ena ali ndi mwaŵi wamaphunziro amene makolo awo sanasangalale nawo. Pa mlingo uliwonse, ngati zimenezi ziri zowona kwa inu, kodi mumadzimva motani ponena za makolo anu? Kodi inu mumachititsidwa manyazi ndi kusaphunzira kwawo? Kapena, choposa apo, kodi inu nthaŵi zina mumalingalira kuti iwo ali mbuli ndipo osayenerera ulemu?

Chifukwa Chake Ulemu Uli Woyenera

Ngati malingaliro oyipa oterowo akukanthani nthaŵi ndi nthaŵi, chingakuthandizeni kulingalira pa nsonga yakuti Mulungu amafuna kuti inu mulemekeze makolo anu. Aefeso 6:2, 3 imalamula kuti: “Lemekeza atate wako ndi amako (ndilo lamulo loyamba lokhala nalo lonjezano), kuti kukhale bwino ndi iwe, ndikuti ukhale wa nthaŵi yaikulu padziko.” Dikishonale ina imamasulira kulemekeza kukhala ‘kuchita mwaulemu.’ Ndiponso, dziŵani kuti, ziyembekezo za moyo wanu zakutsogolo zimadalira pa kusonyeza makolo anu ulemu. Kusawachitira ulemu makolo anu kumakhalanso kusam’chitira ulemu Mulungu.

Ndiiko nkomwe, muli athayo kwa makolo anu kaamba ka kukupatsani moyo. Kum’lingo umene angakhoze, iwo amakupezerani chakudya, zovala, ndi nyumba—ntchito yovuta kwenikweni m’maiko otukuka kumene—ndipo mosakaikira adzapitirizabe kutero ku zaka zirinkudza. Palibe malipiro angaikidwe pa nthaŵi yamtengo wake ya makolo anu, chisamaliro chabwino, ndi chilangizo chachikondi. Kodi iwo ayenera kusalemekezedwa chifukwa chakuti alibe ubwino winawake wamaphunziro? Akhale ophunzira kapena osaphunzira, iwo ali makolo anu.

Kumbukiraninso, kuti ali makolo anu amene anakulipilirani maphunziro alionse amene munakhala nawo, kaŵirikaŵiri akumataikiridwa iwo eni. Kodi chimenechi sichiyenera kusonkhezera chiyamikiro chanu?

Maphunziro Amene Makolo Ali nawo

Ndthudi, makolo anu mothekera ali ophunzira kuposa mmene inu muliri. Kuphunzira kwa kusukulu kumapereka maziko okulira pomwe munthu angayambire mu umoyo wake wonse. Koma samakuphunzitsani zonse zimene mufunikira kudziŵa m’moyo.

Mwambi wofala mu Ghana uli wakuti: “Mkulu panthaŵi ina anali mwana, koma mwana sanakhalepo mkulu.” Makolo anu ali ndi chinachake chimene inu simungachipeze m’bukhu: kuzoloŵera m’moyo. Kodi munagwirapo kale ntchito, kulipilira zogula, kusamalira ana aang’ono, kapena kusamalira banja? Makolo anu atha kale zaka zambiri za kuzolowera m’nkhani zimenezi.

Baibulo mowonjezereka limasonyeza pa Ahebri 5:14 kuti nzeru zamunthu zolingalira ‘zimaphunzitsidwa kusiyanitsa chabwino ndi choipa,’ osati kokha kupyolera m’kuŵerenga ndi kuphunzira, koma “mwakuchita nazo”! Chotero makolo anu ali m’malo abwino a kukupatsani chilangizo chamakhakidwe, kukhomereza makhalidwe abwino mwa inu. Izi ziri makamaka tero ngati makolo anu ali owopa Mulungu.

Mokondweretsa, chipambano chimene makolo anu ali nacho kuposa inu m’kuzolowera sichimatha ngakhale pamene nanunso mukhala wamkulu mokhoza kusamalira banja lanu! Miyambo 23:22 imati: “Tamvera atate wako anakubala, usapeputse amako atakalamba.” Chilangizo chimenechi chinalunjikitsidwa, osati kwa ana, koma kwa akulu okhala ndi makolo okalamba. Inde, ngakhale pamene wina ali mkulu, n’kwanzeru kumvetsera kwa makolo ake, akumalemekeza nzeru zimene iwo azipeza kupyolera m’kuzoloŵera. Makolo angakhale osaphunzira, koma chimenecho sichimatanthauza kuti uphungu wawo ulibe phindu.

Osaphunzira koma Achipambano

Zokumana nazo za moyo weniweni za achichepere oleredwa ndi makolo osaphunzira zimasonyeza kuwona kwake kwa zomwe zakambidwazo. Kwabena, wachichepere wa ku Ghana, akusimba za amake osaphunzira kuti: “Iwo anali opereka chilango olimba. Ine ndakula ndikuwakonda mokulira, chifukwa cha chiyamikiro cha mikhalidwe yabwino imene iwo anakhomereza mwa ine kaamba ka ubwino wanga. Alongo anga achikulire ali akazi okwatiwa achipambano, ndipo amayi anga angapange mbali yofunika kwambiri yachiyamikiro pa zimenezi.”

Reginald, kumbali ina, analeredwa ndi agogo wake aamuna nawonso osaphunzira. Reginald akukumbukira kuti: “Zitsogozo zawo zinali zofikapo ndi zosasintha, zothandizira kundikhozetsa kusenza mathayo aakulu pa msinkhu wachichepere m’moyo.”

Kwasi ali wachichepere wina wa ku Ghana amene amayi ake sanakhalepo konse ndi maphunziro akusukulu. Kodi chimenechi chinawayika iwo ku mbali yoipa kwenikweni pochita ndi mwana wawo wamwamunayo? Ayi. Kwasi akukumbukira kuti: “Nthaŵi zonse ndakhala ndikukhumbira amayi wanga kaamba ka luntha lawo lamaganizo. Iwo anali wogulitsa, ndipo m’zaka zanga zoyambilira ku sukulu ya sekondale, nthaŵi zonse pamene iwo anafuna kuŵerengera masamu, ndinafunikira kugwiritsira ntchito peni ndi pepala. Iwo anachita masamu am’maganizo. Kaŵirikaŵiri ndiwo anali kupeza mayankho olondola choyamba!”

Khalani Thandizo kwa Makolo Anu!

Zowona, kuphunzira kumakupatsani maubwino ena. Koma chimenechi sindicho chifukwa chodzitukumulira kwa makolo anu. Monga wachichepere, Yesu Kristu anali ndi chipambano chimodzi pa makolo ake. Iye anali wangwiro. Komabe, cholembedwa cha Baibulo chimasonyeza kuti “iye anawamvera iwo.”—Luka 2:51.

Pa mfundo imeneyi, kodi inu mwalingalirapo mmene mungagwiritsire ntchito maluso anu ku ubwino wa makolo anu? Mwachitsanzo, iwo mwinamwake angayamikire kuwaŵerengera makalata, nyuzipepala, Baibulo, ndi zofalitsidwa zozikidwa pa Baibulo. Kapena mwinamwake iwo angapindule mwakuwalembera makalata kapena kuwadzazira mafomu.

Kumbukirani, pamene Yehova Mulungu amathandiza anthu ake, “apatsa kwaonse modzala manja, niwosatonza.” (Yakobo 1:5) M’mawu ena, iye samatichititsa kudzimva opusa pokhala ofunikira thandizo lake. Chotero chitani ndi makolo anu mwanjira yodzichepetsa, yachisomo, ndipo iwo adzakhala othekera mokulira kulandira thandizo lanu.

Popeza kuti maluso a kuŵerenga ndi kulemba ali ogwira ntchito kwambiri motero mumpingo Wachikristu, inu mungapatsedi makolo anu chilimbikitso chofatsa kutenga mwaŵi wa maprogramu osiyanasiyana a kuŵerenga amene angakhaleko. Mokondweretsa, m’maiko ambiri kumene kusaphunzira kuli kofala, Nyumba Yaufumu ya Mboni za Yehova kaŵirikawiri imagwiritsiridwa ntchito monga malo ophunzilira. Mwinamwake liwu linalake lachilimbikitso lochokera kwa inu lingakhale kokha limene angofunikira kusonkhezeredwa kutenga mwaŵi wa programu ya maphunziro yoperekedwa kumeneko.

M’maiko ena a mu Africa, ana ena amayembekeza kufikira imfa ya makolo awo ndiyeno amawapatsa “ulemu womalizira” mwa kuwagulira bokosi lamaliro lamtengo wodula lowaikamo. Nkwabwinopo kwenikweni chotani nanga kusonyeza ulemu wakuya kwa makolo anu tsopano lino pamene adakali moyo! Musakhale konse amanyazi kuti iwo anamanidwa mwaŵi winawake pamene anali achichepere. Iwo ali ndi mikhalidwe imene imachita zokulira mokwaniritsa chosowa chawo cha maphunziro akudziko. Nthaŵi zonse sonyezani ulemu kwa iwo, ponse paŵiri m’mawu ndi m’kachitidwe. Khalani ‘wokonzekera kumvera,’ ngakhale pamene simuvomerezana nawo. (Yakobo 3:17) Tengeni ukoma, chikondi, ndi nzeru zimene makolo anu ali nazo kukhala zamtengo wapatali, mikhalidwe imene imatanthauza zochuruka kuposa luso la kuŵerenga ndi kulemba.

[Chithunzi patsamba 16]

Makolo angakhale magwero olemera a chilangizo ngakhale pamene alibe maluso akuŵerenga

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena