Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w96 2/1 tsamba 21-26
  • Khulupirirani Yehova ndi Mawu Ake

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Khulupirirani Yehova ndi Mawu Ake
  • Nsanja ya Olonda—1996
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Peŵani Kukhulupirira Nzeru Yadziko
  • Limbanani ndi Chikhoterero cha Kukayikira
  • Kutsatira Chitsogozo cha Yehova mu Ukwati
  • Achichepere​—Mvetserani Mawu a Mulungu
  • Achichepere—Kodi Mukulondola Chiyani?
    Nsanja ya Olonda—1993
  • Kodi Mwapanga Choonadi Kukhala Chanuchanu?
    Nsanja ya Olonda—2001
  • Musalole Kuti Kukayika Kuwononge Chikhulupiriro Chanu
    Nsanja ya Olonda—2001
  • Magwero Apamwamba Kwambiri a Nzeru
    Baibulo—Kodi Ndilo Mawu a Mulungu Kapena a Munthu?
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1996
w96 2/1 tsamba 21-26

Khulupirirani Yehova ndi Mawu Ake

“Iwo akudziŵa dzina lanu adzakhulupirira inu.”​—SALMO 9:10.

1. Kodi nchifukwa ninji tingadalirebe Yehova ndi Mawu ake m’tsiku lathuli?

M’DZIKO lamakonoli, chiitano cha kukhulupirira Mulungu ndi Mawu ake, Baibulo, chingaonekere kukhala chosapindulitsa ndi chosagwira ntchito. Komabe, nzeru ya Mulungu yakhala yoona kwanthaŵi yaitali. Mlengi wa mwamuna ndi mkazi ameneyo ndiye Woyambitsa ukwati ndi banja, ndipo amadziŵa bwino kwambiri zofunika zathu kuposa munthu wina aliyense. Monga momwe zofunika zazikulu za anthu sizinasinthire, moteronso njira zazikulu zopezera zofunika zimenezo sizinasinthe. Uphungu wa Baibulo wanzeru, ngakhale kuti unalembedwa zaka mazana ambiri zapitazo, umaperekabe chitsogozo chabwino koposa cha kupeza chipambano m’moyo ndi cha kuthetsera mavuto. Kuumvera kumabweretsa chimwemwe chambiri​—ngakhale m’dziko lopita patsogolo la sayansili limene tikukhalamo!

2. (a) Kodi ndi zipatso zabwino zotani zimene kumvera malamulo a Mulungu kwatulutsa m’moyo wa anthu a Yehova? (b) Kodi nchiyaninso chimene Yehova akulonjeza awo amene amamvera iye ndi Mawu ake?

2 Kukhulupirira Yehova ndi kugwiritsira ntchito mapulinsipulo a Baibulo kumadzetsa mapindu tsiku lililonse. Umboni wa zimenezi umasonyezedwa m’moyo wa mamiliyoni ambiri a Mboni za Yehova kuzungulira dziko lonse amene akhala ndi chikhulupiriro ndi kulimbika mtima pa kugwiritsira ntchito uphungu wa Baibulo. Iwo aikadi kukhulupirira Mlengi ndi Mawu ake pa malo oyenera. (Salmo 9:9, 10) Kumvera malamulo a Mulungu kwawapangitsa kukhala anthu abwino kwambiri ponena za ukhondo, kuona mtima, khama, kulemekeza moyo ndi katundu wa ena, ndiponso kudya ndi kumwa moyenera. Kwawachititsa kukhala ndi chikondi ndi maphunziro oyenera m’banja​—kukhala a ufulu, oleza mtima, achifundo, ndi okhululukira​—ndiponso zinthu zina zambiri. Iwo kwakukulukulu apeŵa zipatso zoipa za mkwiyo, udani, mbanda, kaduka, mantha, ulesi, kunyada, kunama, kuchita miseche, uchiwerewere, ndi chisembwere. (Salmo 32:10) Koma Mulungu amachita zambiri kuposa pa kungolonjeza zotulukapo zabwino kwa awo amene amasunga malamulo ake. Yesu anati awo amene amatsatira njira yachikristu adzalandira “makumi khumi tsopano nthaŵi ino, . . . amayi, ndi ana, ndi minda, pamodzi ndi mazunzo; ndipo nthaŵi ilinkudza, moyo wosatha.”​—Marko 10:29, 30.

Peŵani Kukhulupirira Nzeru Yadziko

3. Popitiriza kukhulupirira Yehova ndi Mawu ake, kodi Akristu nthaŵi zina amayang’anizana ndi mavuto otani?

3 Vuto la anthu opanda ungwiro nlakuti amakonda kuchepetsa kapena kuiŵala zimene Mulungu amafuna. Amayamba mosavuta kuganiza kuti amadziŵa bwino kwambiri kapena kuti nzeru yochokera kwa anthu ophunzira kwambiri a dzikoli njopambana ya Mulungu, kuti iyo njapanthaŵi yake. Atumiki a Mulungu angakhalenso ndi mkhalidwe umenewu, popeza akukhala pakati pa dzikoli. Motero, popereka chiitano cha kumvetsera uphungu wake, Atate wathu wakumwamba amaphatikizaponso machenjezo oyenera akuti: “Mwananga, usaiŵale malamulo anga, mtima wako usunge malangizo anga; pakuti adzakuonjezera masiku ambiri, ndi zaka za moyo ndi mtendere. Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse, osachirikizika pa luntha lako; umlemekeze m’njira zako zonse, ndipo iye adzawongola mayendedwe ako. Usadziyese wekha wanzeru; opa Yehova, nupatuke pazoipa.”​—Miyambo 3:1, 2, 5-7.

4. Kodi “nzeru ya dziko lino lapansi” njowanda motani, ndipo nchifukwa ninji “ili yopusa kwa Mulungu”?

4 Nzeru ya dziko lino ilipo yambiri ndipo imachokera kumbali zosiyanasiyana. Pali mabungwe ambiri a maphunziro, ndipo “saleka kulemba mabuku ambiri.” (Mlaliki 12:12) Tsopano yotchedwa kuti information superhighway m’zamakompyuta ikulonjeza kupereka chidziŵitso chopanda malire pafupifupi pankhani iliyonse. Koma kukhala ndi chidziŵitso chonsechi sikumapangitsa dzikoli kukhala lanzeru kwambiri kapena kuthetsa mavuto ake. M’malo mwake, mkhalidwe wa dziko ukuipiraipira tsiku lililonse. Nchifukwa chake, Baibulo limatiuza kuti “nzeru ya dziko lino lapansi ili yopusa kwa Mulungu.”​—1 Akorinto 3:19, 20.

5. Kodi ndi machenjezo otani amene Baibulo limapereka pa “nzeru ya dziko lino lapansi”?

5 Mkati mwa mbali ino yomaliza ya masiku otsiriza, tiyenera kuyembekezera kuti wonyenga wamkuluyo, Satana Mdyerekezi, adzatulutsa mabodza ochuluka poyesa kuwononga chidaliro pa kuona kwa Baibulo. Akatswiri a maphunziro apamwamba ofufuza Baibulo atulutsa mabuku ochuluka a malingaliro awo amene amatsutsa kutsimikizirika ndi kudalirika kwa Baibulo. Paulo anachenjeza Mkristu mnzake kuti: “Timoteo iwe, dikira chokusungitsa, ndi kulewa zokamba zopanda pake [zimene zimadetsa choyera, NW] ndi zotsutsana za ichi chitchedwa chizindikiritso [cho]nama; chimene ena pochivomereza adalakwa ndi kutaya chikhulupiriro.” (1 Timoteo 6:20, 21) Baibulo limapitiriza kuchenjeza kuti: “Penyani kuti pasakhale wina wakulanda inu ngati chuma, mwa kukonda nzeru kwake, ndi chinyengo chopanda pake, potsata mwambo wa anthu, potsata zoyamba za dziko lapansi, osati potsata Kristu.”​—Akolose 2:8.

Limbanani ndi Chikhoterero cha Kukayikira

6. Kodi nchifukwa ninji kukhala maso kuli kofunika kuti tiletse zikayikiro kuzikika mumtima mwathu?

6 Njira ina yamachenjera ya Mdyerekezi ndiyo kufesa zikayikiro m’maganizo. Amayang’anitsitsa nthaŵi zonse kuti aone chifooko china m’chikhulupiriro ndi kuchigwiritsira ntchito. Aliyense amene amakhala ndi zikayikiro zotero ayenera kukumbukira kuti munthu amene amachititsa zikayikirozo ndi uja amene anati kwa Hava: “Eya! kodi anatitu Mulungu, Usadye mitengo yonse ya m’mundamu?” Pamene Woyesayo anafesa chikayikiro m’maganizo mwa mkaziyo, chinthu chotsatira chinali cha kumuuza bodza, limene mkaziyo anakhulupirira. (Genesis 3:1, 4, 5) Kuti tipeŵe kuwonongedwa kwa chikhulupiriro chathu ndi chikayikiro monga momwe zinalili kwa Hava, tifunikira kukhala maso. Ngati chikayikiro chilichonse ponena za Yehova, Mawu ake, kapena gulu lake chiyamba kukhala mumtima mwanu, chitanipo kanthu mwamsanga kuchithetsa chisanakule kukhala chinthu chimene chingawononge chikhulupiriro chanu.​—Yerekezerani ndi 1 Akorinto 10:12.

7. Kodi nchiyani chimene tingachite kuti tichotse zikayikiro?

7 Kodi nchiyani chimene chingachitidwe? Kachiŵirinso, yankho lake ndilo kukhulupirira Yehova ndi Mawu ake. “Wina wa inu ikamsoŵa nzeru, apemphe kwa Mulungu, amene apatsa kwa onse modzala manja, niwosatonza; ndipo adzampatsa iye. Koma apemphe ndi chikhulupiriro, wosakayika konse; pakuti wokayikayo afanana ndi funde la nyanja lotengeka ndi mphepo ndi kuŵinduka nayo.” (Yakobo 1:5, 6; 2 Petro 3:17, 18) Chotero pemphero lakhama kwa Yehova ndilo sitepe yoyamba. (Salmo 62:8) Ndiyeno, musazengereze kupempha thandizo kwa oyang’anira achikondi mumpingo. (Machitidwe 20:28; Yakobo 5:14, 15; Yuda 22) Adzakuthandizani kudziŵa chochititsa zikayikiro zanu, chimene mwina chingakhale kunyada kapena kulingalira kwina kolakwika.

8. Kodi kuganiza kwampatuko kaŵirikaŵiri kumayamba motani, ndipo mankhwala ake nchiyani?

8 Kodi kuŵerenga kapena kumvetsera malingaliro a ampatuko kapena nzeru ya dziko ndiko kwaloŵetsa zikayikiro zoipa m’maganizo mwanu? Mwanzeru, Baibulo limalangiza kuti: “Uchite changu kudzionetsera kwa Mulungu wovomerezeka, wantchito wopanda chifukwa cha kuchita manyazi, wolunjika nawo bwino mawu a choonadi. Koma peŵa nkhani zopanda pake [zimene zimadetsa choyera, NW]; pakuti adzapitirira kutsata chisapembedzo, ndipo mawu awo adzanyeka chilonda.” (2 Timoteo 2:15-17) Ndi bwino kudziŵa kuti ambiri amene anakhala ampatuko anayamba mwa kutenga njira yolakwika, choyamba mwa kudandaula ponena za mmene anali kuchitiridwa m’gulu la Yehova. (Yuda 16) Kupeza zolakwa m’zikhulupiriro kunatsatira. Monga momwe dokotala wa opaleshoni amafulumirira kudula mbali yonyeka chilonda, fulumirani kudula chikhoterero chilichonse cha kudandaula m’maganizo mwanu, kusakhutira ndi mmene zinthu zikuyendera mumpingo wachikristu. (Akolose 3:13, 14) Dulani chilichonse chimene chimasonkhezera zikayikiro zimenezo.​—Marko 9:43.

9. Kodi ndi motani mmene chizoloŵezi chabwino cha teokrase chingatithandizire kukhala athanzi m’chikhulupiriro?

9 Mamatirani kwa Yehova ndi gulu lake. Tsanzirani Petro mokhulupirika, amene motsimikiza mtima anati: “Ambuye, tidzamuka kwa yani? Inu muli nawo mawu a moyo wosatha.” (Yohane 6:52, 60, 66-68) Khalani ndi programu yabwino ya kuphunzira Mawu a Yehova kuti chikhulupiriro chanu chikhale cholimba, monga chikopa chachikulu, chokhoza “kuzima nacho mivi yonse yoyaka moto ya woipayo.” (Aefeso 6:16) Khalani wokangalika mu utumiki wachikristu, mukumauza ena mwachikondi za uthenga wa Ufumu. Tsiku lililonse sinkhasinkhani moyamikira za mmene Yehova wakudalitsirani. Khalani wothokoza kuti muli ndi chidziŵitso cha choonadi. Kuchita zinthu zonsezi mwa chizoloŵezi chabwino chachikristu kudzakuthandizani kukhala wachimwemwe, kupirira, ndi kukhalabe wopanda zikayikiro.​—Salmo 40:4; Afilipi 3:15, 16; Ahebri 6:10-12.

Kutsatira Chitsogozo cha Yehova mu Ukwati

10. Kodi nchifukwa ninji makamaka kuli kofunika kuyang’ana kwa Yehova kaamba ka chitsogozo muukwati wachikristu?

10 Polinganiza kuti mwamuna ndi mkazi akhale pamodzi monga anthu okwatirana, Yehova sanangofuna kuti dziko lapansi lidzazidwe bwino komanso kuti awonjezere chimwemwe chawo. Komabe, uchimo ndi kupanda ungwiro zadzetsa mavuto aakulu muukwati. Nawonso Akristu amakhudzidwa nawo, popeza kuti nawonso ali opanda ungwiro ndipo amakumana ndi zitsenderezo za moyo watsiku ndi tsiku. Komabe, malinga ndi mlingo umene amakhulupirira Yehova ndi Mawu ake, Akristu angakhale ndi ukwati wopambana ndipo angapambane pa kulera ana awo. Muukwati wachikristu mulibe malo a machitachita ndi khalidwe lakudziko. Mawu a Mulungu amatilangiza kuti: “Ukwati uchitidwe ulemu ndi onse, ndi pogona pakhale posadetsedwa; pakuti adama ndi achigololo adzawaweruza Mulungu.”​—Ahebri 13:4.

11. Poyesayesa kuthetsa mavuto a ukwati, kodi nchiyani chimene okwatirana aŵiriwo ayenera kudziŵa?

11 Ukwati umene umagwirizana ndi uphungu wa Baibulo uli ndi mkhalidwe wachikondi, wathayo, ndi wachisungiko. Mwamuna ndi mkazi yemwe amamvetsa ndi kulemekeza pulinsipulo la umutu. Pamene mavuto abuka, amakhalapo kaŵirikaŵiri chifukwa cha kunyalanyaza kugwiritsira ntchito uphungu wa Baibulo. Poyesa kuthetsa vuto limene lilipo, nkofunika kuti okwatirana aŵiriwo akambirane moona mtima za chimene chili vutolo ndi kulimbana ndi zochititsa zake m’malo mwa zizindikiro zake. Ngati kukambirana kwaposachedwa kwachita zochepa kapena sanamvane, aŵiriwo angapemphe thandizo kwa mkulu wachikondi wosakhalira mbali ina.

12. (a) Kodi Baibulo limapereka uphungu pa mavuto ati ofala muukwati? (b) Kodi nchifukwa ninji okwatirana onse aŵiri afunikira kuchita zinthu m’njira ya Yehova?

12 Kodi vutolo likukhudza kulankhulana, kulemekeza malingaliro a mnzanu, kulemekeza umutu, kapena za mmene zosankha ziyenera kupangidwira? Kodi likukhudza za kulera ana, kapena kukhala osapambanitsa pankhani ya kugonana? Kapena kodi nlabajeti ya banja, kusanguluka, mayanjano, kapena kaya ngati mkazi ayenera kuloŵa ntchito yolembedwa kapena ayi, kapena kumene mudzakhala? Pavuto lililonse, Baibulo limapereka chilangizo chothandiza mwa malamulo achindunji kapena mwa njira ya mapulinsipulo. (Mateyu 19:4, 5, 9; 1 Akorinto 7:1-40; Aefeso 5:21-23, 28-33; 6:1-4; Akolose 3:18-21; Tito 2:4, 5; 1 Petro 3:1-7) Pamene aŵiriwo apeŵa kupanga mapempho adyera ndi kulola chikondi kukula muukwati wawo, pamakhala chimwemwe chachikulu kwambiri. Okwatirana onse aŵiri afunikira kukhala ndi chikhumbo chachikulu cha kupanga masinthidwe ofunika, kuti achite zinthu m’njira ya Yehova. “Wolabadira mawu adzapeza bwino; ndipo wokhulupirira Yehova adala.”​—Miyambo 16:20.

Achichepere​—Mvetserani Mawu a Mulungu

13. Kodi nchifukwa ninji kuli kovuta kwa achichepere achikristu kukula ndi chikhulupiriro cholimba mwa Yehova ndi m’Mawu ake?

13 Kuli kovuta kwa achichepere achikristu kukhala olimba m’chikhulupiriro pamene azingidwa ndi dziko loipa. Chifukwa chimodzi nchakuti “dziko lonse lapansi ligona mwa woipayo,” Satana Mdyerekezi. (1 Yohane 5:19) Achichepere akuukiridwa ndi mdani wankhanza ameneyu amene amapangitsa zoipa kuoneka ngati zabwino. Mzimu wakuti ine choyamba, zikhumbo zadyera, kulakalaka zinthu zoipa ndi zankhanza, ndi kulondola zikondwerero konyanyuka​—zonsezi zimapanga kaganizidwe kofala ndi kolamulira kolongosoledwa m’Baibulo kukhala “mzimu wakuchita tsopano mwa ana a kusamvera.” (Aefeso 2:1-3) Satana wachirikiza “mzimu” umenewu mwamachenjera m’mabuku ophunziridwa kusukulu, m’nyimbo zambiri zimene zilipo, m’maseŵero, ndi m’mitundu ina ya kusanguluka. Makolo afunikira kukhala maso kuletsa zisonkhezero zotero mwa kuthandiza ana awo kukula akumakhulupirira Yehova ndi Mawu ake.

14. Kodi achichepere ‘angathaŵe zilakolako za unyamata’ motani?

14 Paulo anapereka chilangizo chonga cha atate kwa bwenzi lake laling’onolo Timoteo kuti: “Thaŵa zilakolako za unyamata, nutsate chilungamo, chikhulupiriro, chikondi, mtendere, pamodzi ndi iwo akuitana pa Ambuye ndi mitima yoyera.” (2 Timoteo 2:22) Pamene kuli kwakuti si “zilakolako za unyamata” zonse zimene zili zoipa, achichepere ayenera ‘kuzithaŵa’ mwa njira yakuti sayenera kulola zinthu zimenezi kukhala zowatanganitsa, zikumawasiyira nthaŵi yochepa kwambiri, ngati imakhalapo nkomwe, ya kulondola zaumulungu. Kulimbitsa thupi, maseŵero, nyimbo, kusanguluka, zochita zapamtima, ndi maulendo, pamene kuli kwakuti sizili zoipa, zingakhale msampha ngati zikhala zinthu zazikulu m’moyo. Thaŵani kotheratu nkhani zopanda pake, kungoyendayenda, kukhala ndi chidwi chachikulu cha kugonana, kungokhala wopanda chochita ndi kunyong’onyeka, ndi kudandaula kuti makolo anu sakumvetsani.

15. Kodi ndi zinthu zotani zimene zingachitike kwa achichepere pamene ali okha kunyumba zimene zingawachititse kukhala ndi moyo wapaŵiri?

15 Achichepere angaloŵe m’ngozi ngakhale pamene ali okha kunyumba. Ngati aonerera mafilimu a pa TV ndi a mavidiyo oipa ndi achiwawa, chikhumbo cha kuchita zoipa chingafesedwe. (Yakobo 1:14, 15) Baibulo limalangiza kuti: “Inu okonda Yehova, danani nacho choipa.” (Sal. 97:10; 115:11) Yehova amadziŵa ngati munthu akuyesa kukhala ndi moyo wapaŵiri. (Miyambo 15:3) Achichepere achikristunu, yang’anani m’chipinda mwanu. Kodi mumapachika pakhoma zithunzithunzi za akatswiri amaseŵero kapena oimba nyimbo amakhalidwe oipa, kapena kodi mumapachika zinthu zabwino zimene zili zikumbutso zabwino? (Salmo 101:3) Kodi muli ndi zovala zoyenera mu wadirobu yanu, kapena kodi zovala zanu zina zili za masitayelo omkitsa a dzikoli? Mdyerekezi angakukoleni mochenjera kwambiri ngati mugonjera pa chiyeso cha kulaŵa zoipa. Baibulo limalangiza mwanzeru kuti: “Khalani odzisungira, dikirani; mdani wanu Mdyerekezi, monga mkango wobuma, ayendayenda ndi kufunafuna wina akamlikwire.”​—1 Petro 5:8.

16. Kodi uphungu wa Baibulo ungathandize motani wachichepere kupangitsa aliyense amene amamdera nkhaŵa kunyada chifukwa cha iye?

16 Baibulo limakuuzani kusamala pa mayanjano anu. (1 Akorinto 15:33) Mabwenzi anu ayenera kukhala aja amene amawopa Yehova. Musagonjere chitsenderezo cha ausinkhu wanu. (Salmo 56:11; Miyambo 29:25) Khalani omvera makolo anu owopa Mulungu. (Miyambo 6:20-22; Aefeso 6:1-3) Yang’anani kwa akulu kuti akutsogolereni ndi kukulimbikitsani. (Yesaya 32:1, 2) Sumikani maganizo anu ndi maso pa miyezo ndi zonulirapo zauzimu. Funani mipata imene ingakuchititseni kupita patsogolo mwauzimu ndi kukhala ndi phande mu ntchito za mpingo. Phunzirani mmene mungachitire zinthu ndi manja anu. Khalani ndi chikhulupiriro cholimba ndiponso chamoyo, ndipo pamenepo mudzasonyezadi kuti ndinu munthu wofunika​—munthu woyenera moyo m’dziko latsopano la Yehova! Atate wathu wakumwamba adzanyada chifukwa cha inu, makolo anu apadziko lapansi adzakondwera chifukwa cha inu, ndipo abale ndi alongo anu achikristu adzalimbikitsidwa chifukwa cha inu. Zimenezo nzimene zili zofunika!​—Miyambo 4:1, 2, 7, 8.

17. Kodi ndi mapindu otani amene amadza kwa awo amene amakhulupirira Yehova ndi Mawu ake?

17 Wamasalmo anauziridwa kulemba m’mawu andakatulo kuti: “Yehova . . . sadzakaniza chokoma iwo akuyenda angwiro. Yehova wamakamu, wodala munthu wakukhulupirira inu.” (Salmo 84:11, 12) Inde, chimwemwe ndi chipambano, osati kugwiritsidwa mwala ndi kulephera, nzimene zidzadza kwa awo onse amene amakhulupirira Yehova ndi Mawu ake, Baibulo.​—2 Timoteo 3:14, 16, 17.

Kodi Mungayankhe Motani?

◻ Kodi nchifukwa ninji Akristu sayenera kukhulupirira “nzeru ya dziko lino lapansi”?

◻ Kodi nchiyani chimene chiyenera kuchitidwa ngati munthu ali ndi zikayikiro?

◻ Kodi kuchita zinthu m’njira ya Yehova kumadzetsa motani chipambano ndi chimwemwe muukwati?

◻ Kodi Baibulo limathandiza motani achichepere ‘kuthaŵa zilakolako za unyamata’?

[Chithunzi patsamba 23]

Akristu amatembenukira kwa Yehova ndi Mawu ake, pamene akukana “nzeru ya dziko lino lapansi” kukhala yopusa

[Chithunzi patsamba 25]

Mabanja amene amakhulupirira Yehova ndi Mawu ake amakhala ndi chipambano chabwino ndi chimwemwe

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena