-
Kodi Baibulo Limanena Zotani pa Nkhani ya Kugonana?Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
-
-
4. Yesetsani kuti musagonje pa mayesero
N’chiyani chingapangitse kuti munthu agonje mosavuta akamayesedwa kuti achite chiwerewere? Onerani VIDIYO, kenako mukambirane mafunso otsatirawa.
Kodi m’bale wamuvidiyoyi anachita chiyani atazindikira kuti zinthu zina zimene amaganiza ndi kuchita zikanachititsa kuti asiye kukhala wokhulupirika kwa mkazi wake?
Ngakhale Akhristu okhulupirika amafunika kuchita khama kuti asamaganizire zinthu zoipa. Kodi mungatani kuti musamaganizire zinthu zachiwerewere? Werengani Afilipi 4:8, kenako mukambirane mafunso awa:
Kodi ndi zinthu ziti zimene tiyenera kumaziganizira?
Kodi kuwerenga Baibulo komanso kukhala ndi zochita zambiri potumikira Yehova kungatithandize bwanji kuti tipewe mayesero?
-
-
Mungatani Kuti Zimene Mumalankhula Zizisangalatsa Yehova?Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
-
-
3. N’chiyani chimene chingatithandize kuti tizilankhula zinthu zolimbikitsa?
Nthawi zambiri zinthu zimene timalankhula zimasonyeza zimene zili mumtima mwathu kapenanso zimene tikuganiza. (Luka 6:45) Choncho tiziyesetsa kudziphunzitsa kuti tiziganizira zinthu zabwino zomwe ndi zolungama, zoyera, zachikondi ndi zoyamikirika. (Afilipi 4:8) Kuti zimenezi zitheke, tizisamala posankha zosangalatsa komanso anthu ocheza nawo. (Miyambo 13:20) Tingachitenso bwino kumaganizira kaye zomwe tikufuna kulankhula tisanazilankhule. Tiziganiziranso mmene zonena zathuzo zingakhudzire anthu ena. Baibulo limati: “Pali munthu amene amalankhula mosaganizira ndi mawu olasa ngati lupanga, koma lilime la anthu anzeru limachiritsa.”—Miyambo 12:18.
-