-
Anadedwa Chifukwa cha Chikhulupiriro ChawoNsanja ya Olonda—1998 | December 1
-
-
17. Kodi nchiyani chikusonyeza kuti ntchito yolalikira ya Akristu a m’zaka za zana loyamba inali yogwira mtima?
17 Akristu a m’zaka za zana loyamba analalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu ndi changu chosaneneka. (Mateyu 24:14) Pofika cha m’ma 60 C.E., Paulo anatha kunena kuti uthenga wabwino ‘unalalikidwa cholengedwa chonse cha pansi pa thambo.’ (Akolose 1:23) Pofika kumapeto kwa zaka za zana loyamba, otsatira a Yesu anali atapanga ophunzira mu Ufumu wonse wa Roma—ku Asia, ku Ulaya, ndi ku Afirika! Ngakhale anthu ena “a banja la Kaisara” anakhala Akristu.a (Afilipi 4:22) Kulalikira mwachangu kumeneku kunadzutsa mkwiyo. Neander anati: “Chikristu chinafalikira bwino pakati pa anthu a udindo uliwonsewo, ndipo chinaoneka kuti chidzaposa chipembedzo cha m’dzikomo.”
-
-
Anadedwa Chifukwa cha Chikhulupiriro ChawoNsanja ya Olonda—1998 | December 1
-
-
a Mawu akuti “banja la Kaisara” sanena kwenikweni za anthu amene anali abale ake enieni a Nero, yemwe anali kulamulira panthaŵiyo. M’malo mwake, anganene za antchito ake a panyumba ndi maofesala ang’onoang’ono, amene mwinamwake anali kugwira ntchito zonga ngati kuphika ndi kusamalira panyumba m’malo mwa banja lachifumulo ndi antchito awo ena.
-