Chidziŵitso pa Nyuzi
Chizindikiro Chochenjeza
December watha chivomezi cha mlingo wa 6.9 pa muyezo wa Richter chinakantha Soviet Armenia ndi mkuntho wosakaza. Cholongosoledwa kukhala “chimodzi cha zoipitsitsa m’mbiri yakale ya Soviet,” chivomezicho chinatenga chifupifupi miyoyo 25,000 ndi kusiya 500,000 opanda nyumba. Icho chinawononga magawo aŵiri mwa atatu a mzinda wachiŵiri pa waukulu koposa mu Armenia, Leninakan, wokhala ndi chiŵerengero cha anthu 290,000 ndipo chinawononga Spitak kotheratu, tauni yokhala ndi chifupifupi nzika 30,000. Midzi yosiyanasiyana yaing’ono inathetsedwanso ndi chivomezicho. Chifupifupi 5,400 a opulumuka anakokedwa kuchokera mu miyulu ya zidutswa zophwanyika ndi gulu la mitundu yonse la antchito opulumutsa, ndipo mogwirizana ndi maulamuliro a Soviet, chiŵerengero cha ovulazidwa chinafikira 13,000.
Ngakhale kuti asayansi ali ndi lingaliro linalake la zochititsa za magwero a pansi pa nthaka za zivomezi zochulukira, iwo sangakhoze kuneneratu molondola pamene izi zidzachitika. Ngakhale ndi tero, kubwerezabwereza kwa kusakaza kwa zivomezi m’zana lino sikumadza monga chozizwitsa kwa ophunzira a Baibulo ozoloŵerana ndi “chizindikiro” chonenedweratu ndi Yesu Kristu chozindikiritsa “kukhalapo” kwake kosawoneka ndi “mathedwe a dongosolo la zinthu.” Nchifukwa ninji ziri tero? Chifukwa chakuti ngakhale kuti Yesu sanalongosole chochititsa cha zochitika zogwedeza dzikozi, iye anachenjeza kuti monga mbali ya “chizindikiro” chokhala ndi zambiri chimenecho, padzakhala “zivomezi m’malo akuti akuti.”—Mateyu 24:3, 7.
“Boma la Dziko”
Njira yokha ya kulimbanira ndi ziyambukiro za zomera zobiriŵira ndi matsoka ena otulukapo m’malo ozungulira iri boma la dziko, akutero Dr. Kenneth Hare, katswiri wa sayansi ya chikhalidwe cha dziko lapansi wotchuka ndi katswiri wa kusintha kwa kutentha kapena kuzizira. Anthu akuwunjika kusakaza kwakupha pa chilengedwe, Hare anachenjeza tero. Pulaneti ikuwopsyezedwa osati kokha ndi chipululutso cha nyukliya “komanso ndi kusagwiritsira ntchito bwino kwa malo ozungulira,” yasimba tero Calgary Herald, nyuzipepala ya ku Canada. Hare wadzinenera kuti matani mabiliyoni atatu a mpweya wa carbon amathiridwa mu mlengalenga chaka chirichonse ndi utsi wa magalimoto ndi wa mu maindastri. Maphunziro a kompyuta amasonyeza kuti ngakhale ndi kukula kwa pang’onopang’ono kwa zachuma, mlingo wa mpweya wa carbon-dioxide ukawirikiza kaŵiri podzafika chaka cha 2075. “Tapanga vuto la dziko lonse,” ndipo popanda malamulo a malo otizungulira pa mlingo wa dziko lonse, “tidzakhala m’vuto,” anatero Hare.
Chimene Dr. Hare akuyamikira ndithudi chiri chanzeru. Chikhalirechobe, kodi munthu angakhoze kuyembekezera kukhazikitsa boma la dziko lonse lomwe likakhoza kuchita zinthu zoterozo monga kulamulira kakulidwe ka zachuma, kuyambitsa magwero a mphamvu osaipitsa, ndi kukhutiritsa mtundu wa anthu pa kuyamba programu ya kusamalira kwa malo ozungulira a dziko lonse?
Kutalitali! Mawu a Mulungu amanena momvekera kuti: “Njira ya munthu siri mwa iyemwini; sikuli kwa munthu woyenda kulongosola mapazi ake.” (Yeremiya 10:23) Ngakhale kuli tero, ichi chiri m’manja a Mulungu. Monga “Kalonga wa Mtendere,” Mwana wake, Yesu Kristu, adzalamulira boma la dziko lomwe lidzalamulira m’chilungamo ndi m’chilunjiko. Pansi pa ulamuliro wake wa kumwamba, mtundu wa anthu sudzaipitsa malo ozungulira.—Yesaya 9:6, 7; 11:9; Danieli 2:44.
Langizo Loipa
Kodi chiri chinthu choipa kaamba ka mwana kusamvera makolo ake? Osati kwenekweni, akudzinenera tero Leon Kuczynski, profesa wa kakulidwe ka zamalingaliro pa Yunivesite ya Guelph mu Ontario, Canada. M’chenicheni, The Toronto Star yasimba kuti pambuyo pa kuphunzira amayi 70 ndi ana awo, Kuczynski wakhulupirira kuti “machenjera amene mwana amagwiritsira ntchito kusamvera makolo ake ali ofunika m’kakulidwe kake ka mayanjano.” Mogwirizana ndi nkhaniyo, ngati ana alephera kuchita chomwe awuzidwa, makolo sayenera kudera nkhaŵa. Chifukwa chake? Kuczynski wanena kuti mkhalidwe woterowo uli wachibadwa. Profesayo akudzimvanso kuti “kukana kwa mwana kumvera makolo ake kungakhale chizindikiro cha kudziimira payekha ndi kukula.”
Kulephera kwa ana kumvera makolo awo sikuli chizindikiro cha kukula. Mosiyanako, Mfumu yanzeru Solomo analemba kuti: “Utsiru umangidwa mu mtima mwa mwana.” (Miyambo 22:15) Pamene kuli kwakuti ena angakhoze ngakhale kumaliza kuti kusamvera kwa mwana kumatulutsa zotulukapo zabwino, Mawu a Mulungu samavomereza tero. Mazana angapo apita mtumwi Paulo analemba kuti: “Ana inu, mverani akubala inu m’zonse, pakuti ichi Ambuye akondwera nacho.” (Akolose 3:20) Makolo anzeru adzayang’ana kwa Yehova Mulungu monga wolamulira wawo kaamba ka kuphunzitsa mwana.—Miyambo 19:18; 29:15.