Yehova Akhoza Kukulimbikitsani
“Iye alimbitsa olefuka, nawonjezera mphamvu iye amene alibe mphamvu.”—YESAYA 40:29.
1, 2. Kodi maumboni ena a mphamvu zambiri za Yehova ndi ati?
YEHOVA ali Mulungu “wa mphamvu zambiri.” Tingaone umboni wa ‘mphamvu yosatha ndi Umulungu’ wa Mulungu m’chilengedwe chake chokongola kwambiri chooneka. Awo amene amakana kuvomereza umboni wotero wa kukhala kwake Mlengi sangaŵiringule.—Salmo 147:5; Aroma 1:19, 20.
2 Mphamvu ya Yehova imaonekera kwambiri pamene asayansi afufuza patali m’chilengedwe, chokhala ndi milalang’amba yake yosaŵerengeka yokhala pamtunda wa zaka za kuunika mamiliyoni ambiri. Pa usiku wa mdima koma wopanda mitambo, yang’anani kuthambo ndi kuona ngati simudzalingalira monga momwe wamasalmo anachitira: “Pakuona ine thambo la kumwamba lanu, ntchito ya zala zanu, mwezi ndi nyenyezi, zimene munazikhazika, munthu ndani kuti mumkumbukira? Ndi mwana wa munthu kuti mucheza naye?” (Salmo 8:3, 4) Ha, Yehova wasamalira anthufe bwino chotani nanga! Iye anapereka kwa mwamuna ndi mkazi woyamba malo okhala okongola apadziko lapansi. Ngakhale nthaka yake inali ndi mphamvu—yomerapo therere, kutulutsa chakudya chomanga thupi ndi chosaipitsidwa. Munthu ndi zinyama zimapeza mphamvu yakuthupi mu umboni umenewu wa mphamvu ya Mulungu.—Genesis 1:12; 4:12; 1 Samueli 28:22.
3. Kuwonjezera pa zinthu zooneka za m’chilengedwe, kodi nchiyani china chimene chimasonyeza mphamvu ya Mulungu?
3 Kuwonjezera pa mfundo yakuti thambo lili lochititsa chidwi ndi kuti zomera ndi zinyama zili zosangalatsa kuona, izo zimatisonyezanso mphamvu ya Mulungu. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Chilengedwere dziko lapansi zaoneka bwino zosaoneka zake ndizo mphamvu yake yosatha ndi umulungu wake; popeza zazindikirika ndi zinthu zolengedwa.” (Aroma 1:20) Koma pali umboni wina wa mphamvu yake umene tiyenera kuupenda ndi kuumvetsetsa. Mungadabwe kuti, ‘Kodi nchiyani chimene chimasonyeza kwambiri mphamvu ya Mulungu koposa chilengedwe chonse?’ Yankho lake ndiye Yesu Kristu. Kwenikweni, mtumwi Paulo akunena mouziridwa kuti Kristu wopachikidwa ndiye “mphamvu ya Mulungu, ndi nzeru ya Mulungu.” (1 Akorinto 1:24) ‘Nchifukwa ninji zili choncho?’ mungafunse motero, ‘Ndipo kodi zimenezo zikugwirizana bwanji ndi moyo wanga tsopano lino?’
Mphamvu mwa Mwana Wake
4. Kodi mphamvu ya Mulungu inasonyezedwa motani mogwirizana ndi Mwana wake?
4 Mphamvu ya Mulungu choyamba inasonyezedwa pamene analenga Mwana wake wobadwa yekha, wopangidwa m’chifanizo chake. Mwana wauzimu ameneyu anatumikira Yehova monga “mmisiri” mwa kugwiritsira ntchito mphamvu zambiri za Mulungu kulengera zinthu zina zonse. (Miyambo 8:22, 30) Paulo analembera abale ake Achikristu ku Kolose kuti: “Mwa Iye, zinalengedwa zonse za m’mwamba, ndi za padziko, zooneka ndi zosaonekazo . . . zinthu zonse zinalengedwa mwa Iye ndi kwa Iye.”—Akolose 1:15, 16.
5-7. (a) Kale, kodi anthu anaphatikizidwa motani m’kusonyezedwa kwa mphamvu ya Mulungu? (b) Kodi pali chifukwa chotani chokhulupirira kuti mphamvu ya Mulungu ingasonyezedwe kwa Akristu lerolino?
5 Ife ndife mbali ya zimene ‘zinalengedwa padziko.’ Chotero kodi Mulungu akakhoza kupatsa anthufe mphamvu yake? Eya, m’zochita zonse za Mulungu ndi anthu opanda ungwiro, Yehova nthaŵi ndi nthaŵi wapereka mphamvu zowonjezera kwa atumiki ake kuti iwo achite zifuno zake. Mose anadziŵa kuti nthaŵi zambiri anthu opanda ungwiro amakhala ndi moyo zaka 70 kapena 80. (Salmo 90:10) Bwanji nanga za Mose mwiniyo? Anakhala ndi moyo zaka 120, komabe “diso lake silinachita mdima, ndi mphamvu yake siidaleka.” (Deuteronomo 34:7) Pamene kuli kwakuti zimenezo sizikutanthauza kuti Mulungu amatheketsa aliyense wa atumiki ake kukhala ndi moyo zaka zofananazo kapena kukhala ndi nyonga yotero, zimasonyezabe kuti Yehova akhoza kupatsa anthu mphamvu.
6 Zimene Mulungu anachitira mkazi wa Abrahamu zimasonyezanso kukhoza kwake kwa kupatsa mphamvu amuna ndi akazi. “Sara yemwe analandira mphamvu yakukhala ndi pakati, patapita nthaŵi yake, popeza anamŵerengera wokhulupirika Iye amene adalonjeza.” Kapena talingalirani mmene Mulungu anapatsira mphamvu oweruza ndi anthu ena m’Israyeli: “Gideoni, Baraki, Samsoni, Yefita; za Davide, ndi Samueli ndi aneneri; amene . . . analimbikitsidwa pokhala ofooka.”—Ahebri 11:11, 32-34.
7 Mphamvu yotero ingagwirenso ntchito pa ife. Ayi, lerolino sitingayembekezere kukhala ndi ana mwa chozizwitsa, kapena sitingasonyeze mphamvu yonga ya Samsoni. Koma tingakhalebe amphamvu, monga momwe Paulo anauzira anthu wamba ku Kolose. Inde, Paulo analembera amuna, akazi, ndi ana, onga amene timaona m’mipingo lerolino, ndipo ananena kuti iwo anali ‘kulimbikitsidwa m’chilimbiko chonse.’—Akolose 1:11.
8, 9. M’zaka za zana loyamba, kodi mphamvu ya Yehova inasonyezedwa motani pa anthu onga ife?
8 Mu utumiki wa Yesu wa padziko lapansi, Yehova anasonyeza bwino lomwe kuti mphamvu yake inali kugwira ntchito mwa Mwana wake. Mwachitsanzo, pamene makamu a anthu anapita kwa Yesu ku Kapernao, “mphamvu ya [Yehova, NW] inali ndi Iye ya kuwachiritsa.”—Luka 5:17.
9 Pambuyo pa kuuka kwake, Yesu analonjeza otsatira ake kuti ‘akalandira mphamvu, mzimu woyera utadza pa iwo.’ (Machitidwe 1:8) Zimenezi zinali zoona chotani nanga! Wolemba mbiri wina akusimba zimene zinachitika masiku angapo pambuyo pa Pentekoste wa 33 C.E.: “Atumwi anachita umboni ndi mphamvu yaikulu za kuuka kwa Ambuye Yesu.” (Machitidwe 4:33) Paulo mwiniyo anali wina wa amene analimbikitsidwa kaamba ka ntchito imene Mulungu anamtuma kuchita. Atatembenuka nayamba kuona, “anakula makamaka mumphamvu, nadodometsa Ayuda akukhala m’Damasiko, nawatsimikizira kuti ameneyo ndi Kristu.”—Machitidwe 9:22.
10. Kodi mphamvu yochokera kwa Mulungu inamthandiza motani Paulo?
10 Pamene tilingalira za nyonga yauzimu ndi yamaganizo yofunikira popanga maulendo atatu aumishonale oyenda mtunda wa makilomita zikwizikwi, ndithudi Paulo anafunikira mphamvu yowonjezereka. Anapiriranso zovuta za mtundu uliwonse, kuponyedwa m’ndende ndi kuyang’anizana ndi kuphedwera chikhulupiriro. Motani? Iye anayankha kuti: “Ambuye anaima nane nandipatsa mphamvu; kuti mwa ine chilalikiro chimveke konsekonse.”—2 Timoteo 4:6-8, 17; 2 Akorinto 11:23-27.
11. Ponena za mphamvu ya Mulungu, kodi ndi chiyembekezo chotani cha atumiki anzake m’Kolose chimene Paulo anatchula?
11 Pamenepa, mposadabwitsa kuti polembera ‘abale ake mwa Kristu’ m’Kolose, Paulo anawatsimikizira kuti iwo ‘akalimbikitsidwa m’chilimbiko chonse, monga mwa mphamvu ya ulemerero wa [Yehova] kuchitira chipiriro chonse ndi kuleza mtima konse pamodzi ndi chimwemwe.’ (Akolose 1:2, 11) Ngakhale kuti mawu amenewo analembedwa makamaka kwa Akristu odzozedwa, onse amene amatsatira mapazi a Kristu angapindule kwambiri ndi zimene Paulo analemba.
Alimbikitsidwa m’Kolose
12, 13. Kodi nchiyani chimene chinachititsa kuti kalata ya kwa Akolose ilembedwe, ndipo kodi iyenera kukhala itawayambukira motani?
12 Mpingo wa m’Kolose, wa m’chigawo cha Roma cha Asia, mwinamwake unapangidwa mwa kulalikira kwa Mkristu wokhulupirika wotchedwa Epafra. Zikuchita ngati kuti pamene iye anamva za kuponyedwa m’ndende kwa Paulo m’Roma pafupifupi 58 C.E., Epafra analinganiza kukachezera mtumwiyo ndi kumlimbikitsa ndi lipoti labwino la chikondi ndi chipiriro cha abale ake m’Kolose. Mwinamwakenso Epafra anapereka lipoti loona la zovuta zina zimene zinali mumpingo wa ku Kolose zimene zinafunikira kuwongoleredwa. Paulo nayenso anakakamizika kulembera mpingowo kalata yachilimbikitso ndi chilangizo. Nanunso mungapeze chilimbikitso chachikulu m’chaputala 1 cha kalata imeneyo, pakuti chimasonyeza bwino lomwe mmene Yehova angalimbikitsire atumiki ake.
13 Mungathe kulingalira mmene abale ndi alongowo m’Kolose ayenera kukhala atachitira pamene Paulo anawatcha “abale okhulupirika mwa Kristu.” Iwo anafunikiradi kuyamikiridwa kaamba ka ‘chikondi chawo kwa oyera mtima’ ndi kaamba ka ‘kubala kwawo zipatso za uthenga wabwino’ kuyambira pamene anakhala Akristu! Kodi mawu amodzimodziwa anganenedwe ponena za mpingo wathu ndi ife patokha?—Akolose 1:2-8.
14. Kodi nchiyani chimene chinali chikhumbo cha Paulo kwa Akolose?
14 Lipotilo linamsonkhezera kwambiri Paulo kwakuti anauza Akolose kuti sanasiye kuwapembedzera ndi kuwapempherera kuti ‘akadzazidwe ndi chizindikiritso cha chifuniro [cha Mulungu] mu nzeru zonse ndi chidziŵitso cha mzimu, kuti akayende koyenera [Yehova, NW].’ Iye anapemphera kuti iwo ‘abale zipatso mu ntchito yonse yabwino, ndi kukula m’chizindikiritso cha Mulungu; olimbikitsidwa m’chilimbiko chonse, monga mwa mphamvu ya ulemerero wake, kuchitira chipiriro chonse ndi kuleza mtima konse pamodzi ndi chimwemwe.’—Akolose 1:9-11.
Kulimbikitsidwa Lerolinonso
15. Kodi tingasonyeze motani mkhalidwe wa maganizo umodzimodziwo umene unasonyezedwa ndi zimene Paulo analembera Akolose?
15 Ha, Paulo anaika chitsanzo chabwino chotani nanga! Abale athu padziko lonse afunikira mapemphero athu kuti apirire ndi kusunga chimwemwe chawo mosasamala kanthu za kuvutika kwawo. Monga Paulo, tiyenera kukhala olunjika m’mapemphero athu pamene tilandira lipoti lakuti abale athu mumpingo wina, kapena kudziko lina, akuvutika. Nthaŵi zina zingachitike kuti mpingo wapafupi wakanthidwa ndi tsoka lachilengedwe kapena vuto lina lauzimu. Kapena zingachitike kuti Akristu akupirira m’dziko losakazidwa ndi nkhondo yachiweniweni kapena kuphana kwa mafuko. M’pemphero, tiyenera kupempha Mulungu kuthandiza abale athu ‘kuyenda koyenera Yehova,’ kupitiriza kubala zipatso za Ufumu pamene akupirira, ndi kukula m’chizindikiritso. M’njira imeneyi atumiki a Mulungu amalandira mphamvu ya mzimu wake, ‘akumalimbikitsidwa m’chilimbiko chonse.’ Kunena zoona, Atate wanu adzamva ndi kukuyankhani.—1 Yohane 5:14, 15.
16, 17. (a) Malinga ndi zimene Paulo analemba, kodi tiyenera kuyamikira chiyani? (b) Kodi ndi m’lingaliro lotani limene anthu a Mulungu amasulidwira ndi kukhululukidwa?
16 Paulo analemba kuti Akolose anayenera ‘kuyamika Atate, amene anawayeneretsa iwo kulandirana nawo choloŵa cha oyera mtima m’kuunika.’ Tiyeni nafenso tiyamike Atate wathu wakumwamba kaamba ka malo athu m’kakonzedwe kake, akhale m’gawo la kumwamba kapena la padziko lapansi la Ufumu wake. Kodi ndimotani mmene Mulungu anayeneretsera anthu opanda ungwiro m’maso mwake? Paulo analembera abale ake odzozedwa kuti: “Anatilanditsa ife ku ulamuliro wa mdima, natisunthitsa kutiloŵetsa m[u] ufumu wa Mwana wa chikondi chake; amene tili nawo maomboledwe mwa Iye, m’kukhululukidwa kwa zochimwa zathu.”—Akolose 1:12-14.
17 Mosasamala kanthu za chiyembekezo chimene tili nacho, cha kumwamba kapena cha padziko lapansi, tiyamika Mulungu tsiku ndi tsiku kaamba ka kutilanditsa ku dongosolo ili loipa la mdima chifukwa cha chikhulupiriro chathu m’makonzedwe amtengo wapatali a nsembe ya dipo ya Mwana wokondedwa wa Yehova. (Mateyu 20:28) Akristu odzozedwa ndi mzimu apindula ndi dipo limene likugwira ntchito pa iwo m’njira yapadera kuti iwo ‘asunthitsidwe kuloŵa mu ufumu wa Mwana wa chikondi cha Mulungu.’ (Luka 22:20, 29, 30) Komanso “nkhosa zina” zimapindula ndi dipolo ngakhale tsopano. (Yohane 10:16) Izo zingakhululukidwe ndi Mulungu kuti zikhale ndi kaimidwe kolungama pamaso pake monga mabwenzi ake. Zili ndi phande lalikulu m’kulengeza “uthenga uwu wabwino wa Ufumu” m’nthaŵi ino ya mapeto. (Mateyu 24:14) Ndiponso, zili ndi chiyembekezo chabwino koposa cha kukhaliratu zolungama ndi zangwiro mwa kuthupi, kumapeto kwa Ulamuliro wa Zaka Chikwi wa Kristu. Pamene muŵerenga zolongosoledwa pa Chivumbulutso 7:13-17, onani ngati simungavomereze kuti zimenezo zidzakhala umboni wa kulanditsidwa ndi kudalitsidwa kwawo.
18. Kodi ndi kuyanjanitsa kotani kotchulidwa mu Akolose kumene Mulungu akali kuchita?
18 Kalata ya Paulo imatithandiza kuzindikira kukula kwa mangawa amene tili nawo kwa munthu wamkulu woposa onse amene anakhalako. Kodi Mulungu anali kuchita chiyani mwa Kristu? Anali “kuyanjanitsa zinthu zonse kwa Iye mwini, atachita mtendere mwa mwazi [umene anakhetsa pa mtengo wozunzirapo, NW]; . . . kapena za padziko, kapena za m’mwamba.” Chifuno cha Mulungu nchakuti chilengedwe chonse chigwirizanitsidwenso ndi iye kotheratu, monga momwe zinalili chisanachitike chipanduko m’Edene. Amene anagwiritsiridwa ntchito kulenga zinthu zonse ndi Munthu mmodzimodziyo amene akugwiritsiridwanso ntchito tsopano kuchita kuyanjanitsa kumeneku.—Akolose 1:20.
Olimbitsidwa ndi Cholinga Chotani?
19, 20. Kodi kukhala kwathu oyera ndi opanda chilema kumadalira pa chiyani?
19 Ife amene tili oyanjanitsidwa kwa Mulungu tili ndi mathayo. Panthaŵi ina tinali ochimwa ndi alendo kwa Mulungu. Koma tsopano, pokhala taika chikhulupiriro m’nsembe ya Yesu ndipo maganizo athu salinso pa ntchito zoipa, kwenikweni tili mumkhalidwe ‘woyera, ndi wopanda chilema,’ “osatsutsika pamaso pa [Mulungu].” (Akolose 1:21, 22) Tangolingalirani, monga momwedi Mulungu sanachitire manyazi ndi mboni zokhulupirika zakale, sachitanso nafe manyazi potchedwa Mulungu wathu. (Ahebri 11:16) Lerolino, palibe aliyense amene angatitsutse potchedwa ndi dzina lake lalikulu, kapena amene anganene kuti tili amantha kulengeza dzinalo kumalekezero a dziko lapansi!
20 Komabe taonani chenjezo limene Paulo anawonjezera pa Akolose 1:23: “Ngatitu mukhalabe m’chikhulupiriro, ochirimika ndi okhazikika ndi osasunthika kulekana nacho chiyembekezo cha Uthenga Wabwino umene mudaumva, wolalikidwa cholengedwa chonse cha pansi pa thambo.” Chotero zambiri zimadalira pa kukhalabe kwathu okhulupirika kwa Yehova, tikumatsatira mapazi a Mwana wake wokondedwa. Yehova ndi Yesu atichitira zambiri! Tiyeni tisonyeze chikondi chathu pa iwo mwa kutsatira uphungu wa Paulo.
21. Kodi nchifukwa ninji tili ndi chifukwa chachikulu chosangalalira lerolino?
21 Akristu a ku Kolose ayenera kukhala atasangalala kumva kuti ‘uthenga wabwino umene adaumva’ unali ‘utalalikidwa kale cholengedwa chonse cha pansi pa thambo.’ Lerolino kuli kosangalatsa kwambiri kumva za mlingo umene mbiri yabwino ya Ufumu ikulengezedwako ndi Mboni zoposa mamiliyoni anayi ndi theka m’maiko oposa 230. Eya, pafupifupi anthu 300,000 a m’mitundu yonse akuyanjanitsidwa kwa Mulungu chaka chilichonse!—Mateyu 24:14; 28:19, 20.
22. Ngakhale ngati tikuvutika, kodi nchiyani chimene Mulungu angatichitire?
22 Ngakhale kuti Paulo, malinga ndi umboni umene ulipo, anali m’ndende pamene analemba kalatayo kwa Akolose, sanachite chisoni mwanjira iliyonse ndi zomgwerazo. M’malo mwake, anati: “Ndikondwera nazo zoŵaŵazo chifukwa cha inu.” Paulo anadziŵa tanthauzo la “chipiriro chonse ndi kuleza mtima konse pamodzi ndi chimwemwe.” (Akolose 1:11, 24) Koma anadziŵa kuti anachita zimenezi osati mwa mphamvu yake. Yehova anali atamlimbikitsa! Ndimmenenso zilili lerolino. Mboni zikwi zambiri zimene zaponyedwa m’ndende ndi kuzunzidwa sizinataye chimwemwe chawo cha kutumikira Yehova. M’malo mwake, zafika pa kuzindikira choonadi cha mawu a Mulungu opezeka pa Yesaya 40:29-31: “Iye alimbitsa olefuka . . . Iwo amene alindira Yehova adzatenganso mphamvu.”
23, 24. Kodi chinsinsi chopatulika chotchulidwa pa Akolose 1:26 nchiyani?
23 Utumiki wa mbiri yabwino yonena za Kristu unali wofunika kwambiri kwa Paulo. Iye anafuna ena kuzindikira kufunika kwake kwa ntchito ya Kristu m’chifuno cha Mulungu, chotero anautcha “chinsinsicho [chopatulika chimene, NW] chinabisika kuyambira pa nthaŵizo, ndi kuyambira pa mibadwoyo.” Komabe, sichinali kudzakhala chinsinsi nthaŵi zonse. Paulo anawonjezera kuti: “Anachionetsa tsopano kwa oyera mtima ake.” (Akolose 1:26) Pamene chipanduko chinabuka m’Edene, Yehova analonjeza kuti kukakhala zinthu zabwino, akumalosera kuti ‘mbewu ya mkazi ikalalira mutu wa chinjoka.’ (Genesis 3:15) Kodi zimenezi zinatanthauzanji? Kwa mibadwo yambiri, kwa zaka mazana ambiri, zimenezi zinali chinsinsi. Ndiyeno Yesu anadza, “naonetsera poyera moyo ndi chosavunda mwa Uthenga Wabwino.”—2 Timoteo 1:10.
24 Inde, “chinsinsi chopatulika” chimanena za Kristu ndi Ufumu wa Mesiya. Paulo anatchula “za m’mwamba,” kunena za amene adzalamulira ndi Kristu mu Ufumu. Ameneŵa adzakhala njira yodzetsera madalitso ochuluka kwa zonse “za padziko,” awo amene adzasangalala ndi paradaiso wosatha pompano. Mungathe kuona tsopano chifukwa chake kunali koyenera kwambiri kwa Paulo kutchula za “chuma cha ulemerero wa chinsinsi [chopatulika, NW].”—Akolose 1:20, 27.
25. Malinga ndi zimene Akolose 1:29 akusonyeza, kodi mkhalidwe wathu wa maganizo uyenera kukhala wotani tsopano?
25 Paulo anayembekezera mwachidwi malo ake mu Ufumuwo. Komabe anazindikira kuti sichinali chinthu chimene anafunikira kungokhala ndi kuyembekezera popanda kuchitapo kanthu. “Kuchita ichi ndidzivutitsa ndi kuyesetsa monga mwa machitidwe ake akuchita mwa ine ndi mphamvu.” (Akolose 1:29) Onani kuti Yehova, kupyolera mwa Kristu, analimbikitsa Paulo kuti achite utumiki wopulumutsa moyo. Yehova akhoza kuchitanso zimenezo kwa ife lerolino. Koma tiyenera kudzifunsa kuti, ‘Kodi ndili ndi mzimu wa kulengeza umene ndinali nawo pamene ndinangodziŵa choonadi?’ Kodi yankho lanu nlotani? Kodi nchiyani chimene chingathandize aliyense wa ife kupitiriza ‘kudzivutitsa ndi kuyesetsa monga mwa machitidwe a mphamvu ya Yehova’? Nkhani yotsatira ikufotokoza zimenezi kumene.
Kodi Mwazindikira?
◻ Kodi nchifukwa ninji tingakhale otsimikizira kuti Yehova akhoza kusonyeza mphamvu yake m’malo mwa anthu?
◻ Kodi nchiyani chimene chinachititsa kuti Paulo alembe mawu ake m’chaputala 1 cha Akolose?
◻ Kodi ndimotani mmene Mulungu akuchitira kuyanjanitsa kotchulidwa pa Akolose 1:20?
◻ Kodi nchiyani chimene Yehova angachite mwa ife ndi mphamvu yake?
[Mapu/Chithunzi patsamba 8]
(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)
KOLOSE