Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w90 11/15 tsamba 27-28
  • “Ligubo Lachigonjetso”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Ligubo Lachigonjetso”
  • Nsanja ya Olonda​—1990
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Mukudziwa?
    Nsanja ya Olonda—2010
  • Kuwanditsa Fungo Lokoma la Chidziŵitso Chonena za Mulungu
    Nsanja ya Olonda​—1990
Nsanja ya Olonda​—1990
w90 11/15 tsamba 27-28

“Ligubo Lachigonjetso”

LIGUBO lachigonjetso linali phwando lachilakiko pa mdani lochititsa chidwi. Umodzi wa ulemu waukulu womwe Bungwe Landuna Lachiroma linkapereka kwa kazembe wolakika unali kumlola iye kusangalalira chilakiko chake mwakulinganiza ligubo lalamulo, lodya ndalama zochuluka. Mtumwi Paulo anatchula ligubo lachigonjetso kaŵiri m’zolemba zake. Komabe, tisanakambitsirane mawu ake, yesani kuwona m’diso lamaganizo ligubo loterolo. Yerekezerani magulu a anthu akufola pamakwalala namayenda pang’onopang’ono motsatira Via Triumphalis namakwera kudzera njira yokhwetakhweta yonka ku kachisi wa Jupiter pamwamba pa Phiri la Capitoline.

“Fungo lokoma lochokera ku zonunkhiritsa zotenthedwa linafalitsidwa mu akachisi ndi m’makwalala, kudzaza mpweya ndi kununkhira kwawo,” analemba motero katswiri James M. Freeman. “M’ligubomo munali bungwe landuna ndi nzika zotchuka zaboma, omwe kupezekapo kwawo kunalemekeza wolakikayo. Zofunkha pankhondo zamtengo koposa, zonga golidi, siliva, zida zamtundu ndi muyezo uliwonse, zopangapanga zaluso zosawonekawoneka ndi zodula, ndi zirizonse zimene zinawonedwa kukhala zamtengo koposa kaya ndi wogonjetsa kapena wogonjetsedwa, zinanyamulidwa poyera mumzinda wodzaza anthuwo. Andende ankhondo nawonso anakakamizidwa kufola m’ligubolo. Kazembe, wochitiridwa ulemu ndi ligubolo, anayendera m’gareta lopangidwa mwapadera ndipo linakokedwa ndi akavalo anayi. Mwinjiro wake unapetedwa ndi golidi, ndipo malaya ake ndi maluŵa. M’dzanja lake lamanja munali nthambi yamlombwa, ndi m’lamanzere ndodo yachifumu; pamene chapamphumi pake anali ndi chizindikiro chamlombwa cha Delphi. Mkati mwakufuula kwa asirikali ndi kuwomba m’manja kwa anthu, wolakikayo ananyamulidwa kupyola m’makwalala kunka ku kachisi wa Jupiter, kumene nsembe zinaperekedwa, pambuyo pake nakhala ndi phwando la anthu onse m’kachisimo.”

Paulo anagwiritsira ntchito ligubo lachigonjetso kufotokoza mwafanizo pamene analemba kalata yake yachiŵiri kwa Akristu a ku Korinto m’chaka cha 55 cha Nyengo yathu Ino. Iye anati: ‘Koma ayamikike Mulungu, amene atitsogolera m’chigonjetso mwa Kristu, namveketsa fungo la chidziŵitso chake mwa ife pamalo ponse. Pakuti ife ndife fungo labwino la Kristu, kwa Mulungu, mwa iwo akupulumutsidwa, ndi mwa iwo akuwonongeka; kwa ena fungo la imfa kuimfa; koma kwa ena fungo la moyo kumoyo.’​—2 Akorinto 2:14-16.

Panopa Paulo ndi Akristu ena odzozedwa akuimiridwa monga nzika zodzipereka za Mulungu, “mwa Kristu.” Iwo akusonyezedwa kukhala ana, maofisala, ndi asirikali kutsatira mzera wa Yehova natsogoleredwa naye m’ligubo lachigonjetso panjira yoikidwa mankhwala onunkhiritsa. (Onani Nsanja ya Olonda ya July 15, 1990, masamba 10-15.) Kugwiritsira ntchito kochitira fanizoku kwa ligubo loteroli kumasonyezanso kuti awo okana mbiri yabwino ya Ufumu wa Mulungu ali ndi chiyembekezo cha imfa chokha. Koma nzosiyana chotani nanga ndi otsatira odzozedwa a Yesu! Iwo ali ndi chiyembekezo cha chipulumutso chakukhala ndi moyo wosakhoza kufa pamodzi ndi Kristu. Ndipo bwanji ponena za atsamwali awo okhulupirika, nawonso odzipereka kwa Mulungu? Iwo ali ndi chiyembekezo chosangalatsa cha moyo m’paradaiso wa padziko lapansi, kumene Mulungu ‘adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena chowawitsa.’ (Chibvumbulutso 21:1-4; Luka 23:43) Kodi inuyo muli mbali ya khamu lachimwemwe limeneli?

Chithunzi chosiyana chikuperekedwa pa Akolose 2:15, (NW) pamene Paulo analemba kuti: “Atavula maboma ndi maulamuliro, [Mulungu] anawawonetsera poyera monga ogonjetsedwa, nawatsogolera m’ligubo lachigonjetso ndi iwo.” Panopa maboma ndi maulamuliro audani okhala pansi pa Satana Mdyerekezi akusonyezedwa kukhala ogwidwa ukapolo ndi andende m’ligubo lachigonjetso. Yehova Wogonjetsayo akuwavula nawasiya maliseche ndikuwawonetsera poyera monga ogonjetsedwa. Iwo anagonjetsedwa “ndi iwo” ndiwo, ‘mtengo wozunzirapo’ wa Yesu. Imfa yake pamtengowo inapereka maziko ochotserako ‘cholembedwa’ (pangano la Lamulo) ndikutheketsa Akristu kumasuka ku ukapolo wa mphamvu zamdima zausatana. (Akolose 2:13, 14) Tiyenera kuuyamikira chotani nanga ufulu Wachikristu woterowu!

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena