Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g92 11/8 tsamba 20-21
  • Kodi Mapwando Achipembedzo Onse Amakondweretsa Mulungu?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mapwando Achipembedzo Onse Amakondweretsa Mulungu?
  • Galamukani!—1992
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Amadzetsa Chiyanjo cha Mulungu?
  • Kanthu Kena Kabwinopo Koposa Maligubo
  • Kodi Madyerero A Kututa Amakondweretsa Mulungu?
    Nsanja ya Olonda—1997
  • Krisimasi—kodi Ndiyo Njira Yolandirira Yesu?
    Nsanja ya Olonda—1991
  • N’chifukwa Chiyani a Mboni za Yehova Sachita Nawo Maholide Ena?
    Mafunso Ofunsidwa Kawirikawiri
  • Miyambo Yofala Yosamkondweretsa Mulungu
    Coonadi Cimene Cimatsogolera ku Moyo Wamuyaya
Onani Zambiri
Galamukani!—1992
g92 11/8 tsamba 20-21

Lingaliro la Baibulo

Kodi Mapwando Achipembedzo Onse Amakondweretsa Mulungu?

Okhulupirika, ofikira ku 20,000, akuchita phwando la Misa yapadera m’malo apakati amzinda. Pamene chochitikacho chitha, dzoma liyamba. Khamu la olambiralo tsopano likukula kufikira anthu 60,000, amene akuchita piringupiringu m’makwalala, onsewo akumatsatira fano la Nossa Senhora Aparecida, “woyera mtima” amene ali mchirikizi wa Brazil. Masana, mfuwu yogonthetsa ikumvedwa pafupi ndi kachisi pamene ocheza kumalo oyera ayamba kuphulitsa zinthu zowalazo.

MAPWANDO achipembedzo oterowo limodzi ndi kuguba kwawo ngofala m’maiko ambiri. Koma kodi nchiyani chimene chimasonkhezera makamu kugwirizana m’kuguba koteroko? Kusunga mwambo ndi kudzipereka ndizo ziŵiri za zisonkhezero zazikulu za Akatolika, Abhudha, ndi awo okhala ndi zisonkhezero zina zachipembedzo. Ndiponso, monga m’nthaŵi zakale, kusanguluka kungakhale chifukwa chachikulu. The World Book Encyclopedia likufotokoza kuti m’nthaŵi zapakati “mapwando achipembedzo ambiri anagogomezera kusanguluka. Analola anthu kuiŵala mavuto a moyo wawo watsiku ndi tsiku.” Ndimo mmene kaŵirikaŵiri ziliri lerolino. Mwachitsanzo, Salvador, Brazil, ngwodziŵika chifukwa cha mapwando ake achipembedzo ndi otchuka, kusanganiza zamatsenga ndi kukondwera m’mapwando osiyanasiyana ndi michezo zimene chitsiriziro chake chimakhala kuchita mapwando. Komabe, pamene kuli kwakuti kuguba kwina kwachipembedzo kungakhale phwando, kwina kumakhala kwadzoma.

“Akumatsagana ndi fano ndi ansembe, ochepekera anali kuimba nyimbo zatchalitchi pamene ena anatsatira mwakachetechete,” akutero mlendo wina padzoma la m’Brazil. “Koma mkhalidwe waukulu pachochitikacho unali kusaseka, kapena tinene kuti chisoni, monga ngati kuti khamulo linali pamaliro.” Ndipo Lúcio, wa kumpoto kwa Brazil, akuti: “Monga momwe panthaŵi ina ndinachitira, anthu amafuna kwambiri mankhwala kapena chothetsera mavuto abanja kapena andalama. Kaŵirikaŵiri kudzipereka kwa mchirikizi ‘woyera mtima’ kumaphatikizapo kupsopsona fano, kukwera makwerero ndi mawondo, kapena kuyenda maulendo aatali utasenza chimwala pamutu.”

Kudzimana kodzichitira koteroko kungawonekere kukhala kwachilendo kwa osakhulupirira. Komabe, okhala ndi phande amalingalira kuti akukondweretsa Mulungu. Koma kodi akutero? Baibulo limatithandiza kuwona ngati mapwando ndi maligubo oterowo amakondweretsa Mulungu kapena ayi.

Kodi Amadzetsa Chiyanjo cha Mulungu?

Mbiri yakale imatiuza kuti Israyeli wakale anachita ponse paŵiri mapwando achaka ndi chaka ndi apanthaŵi ndi nthaŵi mosangalala. Mapwando oterowo analemekeza Yehova Mulungu. (Deuteronomo 16:14, 15) Ponena za mapwando a m’Baibulo, The Illustrated Bible Dictionary imati: “Chisangalalo chosonyezedwa chinali chochokera pansi pamtima. Kudzipereka kwachipembedzo sikunali kosagwirizana ndi kusangalala ndi zinthu zakanthaŵi zowonedwa monga mphatso za Mulungu.” Mosasamala kanthu za mapwando achipembedzowo, ansembe ndi anthu a Israyeli ananyalanyaza mkhalidwe wawo wauzimu. (Yesaya 1:15-17; Mateyu 23:23) Komabe, funso tsopano nlakuti, Kodi maligubo achipembedzo anali mbali ya Chikristu cha m’zaka za zana loyamba?

Ngakhale kuti Yesu Kristu anachita mapwando ena Achiyuda, Yesu kapena atumwi ake sanayambitse maligubo achipembedzo. The Encyclopædia Britannica limati: “Maligubo akuwonekera kukhala atayamba kutchuka mwamsanga pambuyo pa kuzindikiridwa kwa Chikristu monga chipembedzo chaboma ndi Constantine m’zaka za zana la 4.” Ndipo The World Book Encyclopedia ikufotokoza kuti: “Mapwando atchalitchi [limodzi ndi maligubo awo] anatenga miyambo yachikunja yambiri, akumaipatsa matanthauzo atsopano.”

Akristu alibe thayo la kugwirizana ndi mapwando ndi maligubo achipembedzo oterowo. Posonya kumapwando amene anali ofunika ndi Chilamulo cha Mulungu kwa Israyeli wakale, mtumwi Paulo analemba kuti: “Munthu ali yense asakuweruzeni inu m’chakudya, kapena chakumwa, kapena m’kunena tsiku la phwando, kapena tsiku lokhala mwezi, kapena la Sabata; ndizo mthunzi wa zirinkudzazo; koma thupi [chenicheni, NW] ndi la Kristu.” (Akolose 2:16, 17) Akristu a m’Kolose sanali kudzalola aliyense kuweruza mkhalidwe wawo pamaso pa Mulungu pamaziko a kusungidwa kwa mapwando a Chilamulo cha Mose.

Kanthu Kena Kabwinopo Koposa Maligubo

Kwa Akolose kugwirizanitsa chiphunzitso chawo Chachikristu ndi dzoma kukakhala kubwevuka pachikhulupiriro chawo. Lingaliro la Paulo linali lakuti, Kodi nkutsatiliranji mthunzi chabe wa chowonadi? Chowonadi chenicheni chiri mwa Kristu. Chifukwa chake, kumamatira kumthunzi waulosi ndiko kuzimbaitsa chenicheni chauzimu kumene zinthu zimenezo zinasonya? Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti, monga momwe Paulo ananenera, ‘[Chenicheni] ncha Kristu.’ Chotero, kuchita mapwando achipembedzo oterowo lerolino sikuli mbali ya kulambira kwa Chikristu chowona.

Pamenepa, Akristuwo, safunikiranso kusunga miyambo yokhala ndi chiyambi chaumulungu imeneyi, ndipo ndithudi iwo ayenera kupewa mapwando okhala ndi chiyambi chachikunja, amene angaphatikizepo kugwiritsira ntchito mafano ndi michezo. (Salmo 115:4-8) Mtumwi Paulo anachenjeza kuti: “Musakhale omangidwa m’goli ndi osakhulupira osiyana; pakuti chilungamo chigawana bwanji ndi chosalungama? Kapena wokhulupira ali nalo gawo lanji pamodzi ndi wosakhulupira? Ndipo Kristu avomerezana bwanji ndi Beliyali?” (2 Akorinto 6:14, 15) Mwamawu ena, ngati tifuna kukondweretsa Mulungu, sitingasanganize kulambira kowona ndi konama. Kodi tinganyalanyaze chifuniro cha Mulungu motani ndi kumkondweretsabe?—Mateyu 7:21.

Ayi, Mulungu samavomereza mapwando achipembedzo achikunja limodzi ndi maligubo awo. Kunena zowona, adzazimiririkira limodzi ndi miyambo yonse imene imaluluza Yehova, monga momwe kunanenedweratu m’Mawu a Mulungu. Pa Chivumbulutso 18:21, 22, chipembedzo chonama limodzi ndi zizolowezi zake zikugwirizanitsidwa ndi mzinda wachikunja wa Babulo. Pamati: “Ndipo mngelo wolimba ananyamula mwala, ngati mphero yaikulu, naiponya m’nyanja, nanena, Chotero Babulo, mudzi waukulu, udzapasulidwa kolimba, ndipo sudzapezedwanso konse. Ndipo mawu a anthu oyimba zeze, ndi a oyimba, ndi a oliza zitoliro, ndi a owomba malipenga sadzamvekanso konse mwa iwe.” Popeza mwazindikira kuti mapwando achipembdzo Achibabulo samakondweretsa Mulungu, kodi mudzachitanji?

Tayerekezerani kuti muli paulendo womka kumalo ofunika ndipo mwasokera. Ngati munthu wina mokoma mtima akusonyezani mmene mungafikire motetezereka kumene mukupita, kodi simukakhala woyamikira kukhala mutapeza njira yolondola? Mofananamo, pokhala mutadziŵa mmene Mulungu amalingalilira madzoma achipembedzo, kodi mulekeranji kupenda mowonjezereka Mawu a Mulungu kuti muwone zimene zimamkondweretsa? Kuchitapo kanthu pa zimene mukuphunzira m’Baibulo kudzawonjezera kuunansi wabwino ndi Mulungu—umene uli wapamwamba kwambiri kuposa kusunga mapwando ndi maligubo achipembedzo.—Yohane 17:3.

[Mawu a Chithunzi patsamba 20]

Ligubo la Isitala wa Dutch, Harper’s, m’zaka za zana la 19

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena