Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Muzisankha Mwanzeru Anthu Ocheza Nawo
    Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
    • 1. Kodi zochita za anthu amene mungasankhe kucheza nawo zingakukhudzeni bwanji?

      Anthufe timatengera zochita za anthu amene timacheza nawo. Zimenezi zikutanthauza kuti tikhoza kutengera makhalidwe abwino kapena oipa a anthu amene timacheza nawo pamasom’pamaso kapena pa intaneti. Mpake kuti Baibulo limati: “Munthu woyenda ndi anthu anzeru adzakhala wanzeru, koma wochita zinthu ndi anthu opusa [anthu omwe sakonda Yehova] adzapeza mavuto.” (Miyambo 13:20) Mukamacheza ndi anthu omwe amakonda komanso kulambira Yehova, angakuthandizeni kuti nanunso mukhale pa ubwenzi ndi Yehova komanso kuti muzisankha zinthu mwanzeru. Koma kucheza kwambiri ndi anthu amene sakonda Yehova, kungachititse kuti tisiye kumukonda. N’chifukwa chake Baibulo limatilimbikitsa kuti tizisankha mwanzeru anthu ocheza nawo. Tikamacheza ndi anthu omwe amakonda Mulungu, timatengera zochita zawo zabwino ndipo nawonso amatengera zochita zathu zabwino. Choncho, ‘timapitiriza kutonthozana ndi kulimbikitsana.’​—1 Atesalonika 5:11.

  • Mungatani Kuti Zimene Mumalankhula Zizisangalatsa Yehova?
    Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
    • Yehova anatilenga m’njira yakuti tizitha kulankhula ndipo imeneyi ndi mphatso yapadera. Kodi zimamukhudza akamaona mmene timagwiritsira ntchito mphatsoyi? Inde. (Werengani Yakobo 1:​26.) Ndiye kodi tingatani kuti zolankhula zathu zizisangalatsa Yehova?

      1. Kodi tizigwiritsa ntchito bwanji mphatso ya kulankhula?

      Baibulo limatiuza kuti ‘tipitirize kutonthozana ndi kulimbikitsana.’ (1 Atesalonika 5:11) Kodi mukuona kuti pali anthu ena amene mukufunika kuwalimbikitsa? Ndiye mungatani kuti muwalimbikitse? Muziwatsimikizira kuti ndi ofunika kwambiri. Mwinanso mungawauze makhalidwe abwino omwe ali nawo amene amakusangalatsani. Kodi mungaganizire lemba linalake lomwe mungalimbikitse nalo munthu wina? Pali malemba ambiri ndipo mungathe kusankha limodzi n’kuligwiritsa ntchito. Musaiwalenso kuti mungathe kulimbikitsa munthu chifukwa cha mawu amene mwasankha kuwagwiritsa ntchito komanso mmene mwawalankhulira. Choncho nthawi zonse muzilankhula mokoma mtima komanso modekha.​—Miyambo 15:1.

      2. Kodi tiyenera kupewa kulankhula zinthu zotani?

      Baibulo limati: “Mawu alionse owola asatuluke pakamwa panu.” (Werengani Aefeso 4:29.) Zimenezi zikutanthauza kuti tiyenera kupewa kulankhula mawu otukwana kapena achipongwe, ndiponso tisamanene zinthu n’cholinga chofuna kupsetsa mtima munthu wina. Tizipewanso miseche komanso kunena zinthu zoipa zokhudza anthu ena.​—Werengani Miyambo 16:28.

      3. N’chiyani chimene chingatithandize kuti tizilankhula zinthu zolimbikitsa?

      Nthawi zambiri zinthu zimene timalankhula zimasonyeza zimene zili mumtima mwathu kapenanso zimene tikuganiza. (Luka 6:​45) Choncho tiziyesetsa kudziphunzitsa kuti tiziganizira zinthu zabwino zomwe ndi zolungama, zoyera, zachikondi ndi zoyamikirika. (Afilipi 4:8) Kuti zimenezi zitheke, tizisamala posankha zosangalatsa komanso anthu ocheza nawo. (Miyambo 13:20) Tingachitenso bwino kumaganizira kaye zomwe tikufuna kulankhula tisanazilankhule. Tiziganiziranso mmene zonena zathuzo zingakhudzire anthu ena. Baibulo limati: “Pali munthu amene amalankhula mosaganizira ndi mawu olasa ngati lupanga, koma lilime la anthu anzeru limachiritsa.”​—Miyambo 12:18.

      FUFUZANI MOZAMA

      Onani zimene mungachite kuti muzilankhula zinthu zomwe zingasangalatse Yehova ndi kulimbikitsa anthu ena.

      4. Muzisamala ndi zimene mumalankhula

      Tonsefe nthawi zina timalankhula zinthu zimene timadzanong’oneza nazo bondo pambuyo pake. (Yakobo 3:2) Werengani Agalatiya 5:22, 23, kenako mukambirane mafunso awa:

      • Kodi muyenera kupempha Yehova kuti akuthandizeni kukhala ndi makhalidwe ati n’cholinga choti muzisamala ndi zimene mumalankhula? Kodi makhalidwe amenewa angakuthandizeni bwanji?

      Werengani 1 Akorinto 15:33, kenako mukambirane funso ili:

      • Kodi anzanu ndiponso zosangalatsa zomwe mumasankha zingakhudze bwanji mmene mumalankhulira?

      Zithunzi: Zinthu zimene zikuchititsa kuti mwamuna azilankhula mkazi wake mwaukali. 1. Akumvetsera nyimbo zolimbikitsa chiwawa. 2. Akuchemerera masewera ankhonya amene akuonera pa TV ndi mnzake. Zithunzi: Zinthu zomwe zikuchititsa mwamuna yemwe uja kuti azilankhula mkazi wake mwachikondi. 1. Akuwerenga Baibulo. 2. Iye ndi mkazi wake akucheza ndi mnzawo ku Nyumba ya Ufumu.

      Ndi zinthu ziti zomwe zingachititse kuti muzilankhula bwino kapenanso kuti musamalankhule bwino?

      Werengani Mlaliki 3:1, 7, kenako mukambirane funso ili:

      • Kodi ndi pa nthawi iti imene muyenera kukhala chete kapena kudikira kaye nthawi yabwino yoti mulankhule?

      5. Muzilankhula zinthu zabwino zokhudza ena

      Kodi tingapewe bwanji kulankhula mawu omwe angakhumudwitse anthu ena? Onerani VIDIYO, kenako mukambirane mafunso otsatirawa.

      VIDIYO: Muzilankhula Mawu “Olimbikitsa” (4:07)

      • N’chifukwa chiyani m’bale wamuvidiyoyi ankafunika kusintha mmene amalankhulira zokhudza anthu ena?

      • Nanga anachita chiyani kuti asinthe?

      Werengani Mlaliki 7:16, kenako mukambirane funso ili:

      • Kodi tizikumbukira mfundo iti kuti tipewe kulankhula zinthu zoipa zokhudza munthu winawake?

      Werengani Mlaliki 7:21, 22, kenako mukambirane funso ili:

      • Kodi mavesiwa angakuthandizeni bwanji kuti musamafulumire kupsa mtima munthu wina akalankhula zoipa zokhudza inuyo?

      6. Muzilankhula bwino ndi anthu am’banja lanu

      Yehova amafuna kuti tizilankhula mwachikondi komanso mokoma mtima ndi anthu am’banja lathu. Onerani VIDIYO, kenako mukambirane funso lotsatirali.

      VIDIYO: Chikondi ndi Ulemu Zimachititsa Banja Kukhala Logwirizana (3:08)

      • N’chiyani chingakuthandizeni kuti muzilankhulana mokoma mtima m’banja lanu?

      Werengani Aefeso 4:31, 32, kenako mukambirane funso ili:

      • Kodi tizilankhula mawu otani kwa anthu am’banja lathu kuti azimva kuti timawakonda?

      Yehova anafotokoza mmene amakondera Mwana wake Yesu. Werengani Mateyu 17:5, kenako mukambirane funso ili:

      • Kodi mungatsanzire bwanji Yehova polankhula ndi anthu am’banja lanu?

      Mayi akuyamikira mwana wake wamkazi yemwe wangomaliza kumene kujambula.

      Muzichita chidwi ndi zimene ena amachita n’kumawayamikira

      ZIMENE ENA AMANENA: “Ine ndimalankhula zimene zabwera m’mutu mwanga. Ndiye kaya anthu akhumudwa, izo n’zawo.”

      • Kodi inunso mumaona choncho? N’chifukwa chiyani mukutero?

      ZOMWE TAPHUNZIRA

      Zimene timalankhula zingakhumudwitse kapena kulimbikitsa anthu ena. Choncho tiyenera kusamala ndi zimene timalankhula, mmene timazilankhulira komanso nthawi imene tingalankhule.

      Kubwereza

      • Kodi ndi zinthu ziti zimene mungachite kuti muzilimbikitsa ena ndi zimene mumalankhula?

      • Kodi ndi zinthu ziti zimene mukufuna kupewa kumazilankhula?

      • Kodi n’chiyani chingatithandize kuti nthawi zonse tizilankhula zinthu zabwino komanso zolimbikitsa?

      Zolinga

      ONANI ZINANSO

      N’chiyani chingatithandize kuti tizilankhula zinthu zanzeru?

      Khalani Ndi Lilime la Anthu Anzeru 8:04

      Onani chimene chingakuthandizeni kuti musamalankhule mawu oipa.

      “Kodi Kutukwana N’koipadi?” (Nkhani yapawebusaiti)

      Onani zimene mungachite kuti mupewe miseche.

      Kodi Ndingatani Kuti Ndithetse Miseche? 2:36

      Onani mmene Yehova anathandizira munthu wina yemwe ankavutika kusiya kutukwana.

      “Ndinayamba Kuganizira Kwambiri za Moyo Wanga” (Nsanja ya Olonda, August 1, 2013)

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena