-
Kuzindikira “Munthu Wosayeruzika”Nsanja ya Olonda—1990 | February 1
-
-
3. Kodi ndimotani mmene Baibulo limakokera chisamaliro chathu kwa wosayeruzikayu?
3 Baibulo limatiwuza za munthu wosayeruzika ameneyu pa 2 Atesalonika 2:3. Mowuziridwa ndi mzimu wa Mulungu, mtumwi Paulo analemba kuti: “Munthu asakunyengeni konseko; kuti [tsiku la Yehova la kuwononga dongosolo loipa iri la zinthu] silifika, koma chiyambe chikife chipatukocho, navumbulutsike munthu wosayeruzika.” Panopa Paulo analosera kuti mpatuko ukabuka ndipo munthu wosayeruzika akawonekera dongosolo lino la zinthu lisanathe. M’chenicheni, Paulo analongosola m’vesi 7 (NW) kuti: “Chinsinsi cha kusayeruzika kumeneku chikugwira kale ntchito.” Chotero m’zaka za zana loyamba, munthu wosayeruzika ameneyu adayamba kudziwonetsera iyemwini.
Chiyambi cha Munthu Wosayeruzika
4. Kodi ndani yemwe ali muyambitsi ndi m’chilikizi wa munthu wosayeruzikayu?
4 Kodi ndani yemwe anayambitsa ndi kumachilikiza munthu wosayeruzika ameneyu? Paulo akuyankha kuti: “Kudza kwake kuli monga mwa machitidwe a Satana, mu mphamvu yonse, ndi zizindikiro ndi zozizwa zonama; ndi m’chinyengo chonse cha chosalungama kwa iwo akuwonongeka, popeza chikondi cha chowonadi sanachilandira, kuti akapulumutsidwe iwo.” (2 Atesalonika 2:9, 10) Chotero Satana ndiye atate ndi m’chilikizi wa munthu wosayeruzikayu. Ndipo mongadi mmene Satana amatsutsira Yehova, zifuno Zake, ndi anthu Ake, alinso tero munthu wosayeruzikayo, kaya akuchidziŵa chimenecho kapena ayi.
5. Kodi ndi tsoka lotani limene likuyembekezera wosayeruzikayo ndi awo amene akumtsatira?
5 Awo oyendera limodzi ndi munthu wosayeruzikayu adzavutika ndi tsoka lofananalo—chiwonongeko: “Adzavumbulutsidwa wosayeruzikayo, amene Ambuye Yesu adzamthera . . . nadzamuwononga ndi mawonekedwe a kudza kwake.” (2 Atesalonika 2:8) Nthaŵi imeneyo ya kuwononga munthu wosayeruzika ndi achilikizi ake (‘awo akuwonongeka’) idzadza posachedwapa “pa vumbulutso la Ambuye Yesu wochokera kumwamba pamodzi ndi angelo a mphamvu yake, m’lawi lamoto, ndi kubwezera chilango kwa iwo osamdziŵa Mulungu, ndi iwo osamvera Uthenga Wabwino wa Ambuye wathu Yesu; amene adzamva chilango, ndicho chiwonongeko chosatha.”—2 Atesalonika 1:6-9.
6. Kodi ndi chidziŵitso chowonjezereka chotani chimene Paulo akupereka ponena za wosayeruzikayo?
6 Paulo akulongosola mowonjezereka munthu wosayeruzikayu, akumanena kuti: “Amene atsutsana nazo, nadzikuza pa zonse zotchedwa mulungu, kapena zopembedzeka; kotero kuti iye wakhala pansi ku kachisi wa Mulungu, nadziwonetsera yekha kuti ali mulungu.” (2 Atesalonika 2:4) Chotero Paulo akuchenjeza kuti Satana akadzutsa wosayeruzikayo, chinthu chonyenga cholambiridwa, yemwe akadzikwezadi iyemwini pamwamba pa lamulo la Mulungu.
Kuzindikira Wosayeruzikayo
7. Kodi nchifukwa ninji tikumaliza kuti Paulo sanali kulankhula za munthu mmodzi, ndipo kodi nchiyani chimene munthu wosayeruzikayo amaimira?
7 Kodi Paulo ankalankhula za munthu mmodzi? Ayi, popeza kuti iye akunena kuti “munthu” ameneyu analipo m’tsiku la Paulo ndipo akapitiriza kukhalapo kufikira Yehova akamuwononge iye pamapeto a dongosolo lino. Chotero, iye wakhalapo kwa zaka mazana ambiri. Ndithudi, palibe munthu weniweni yemwe wakhala kwa utali woterowo. Chotero mawu akuti “munthu wosayeruzika” ayenera kuimira bungwe, kapena gulu la anthu.
8. Kodi munthu wosayeruzika ndani, ndipo kodi ndi ziti zimene ziri mbali zina zomzindikirira?
8 Kodi iwo ndani? Umboni ukusonyeza kuti iwo ali bungwe la atsogoleri achipembedzo onyada, ofuna mapindu a Dziko Lachikristu, amene m’zaka mazanamazana adzikhazikira iwo eni malamulo awo. Izi zingawonedwe mwa nsonga yakuti pali zikwizikwi za zipembedzo ndi mipatuko yosiyanasiyana m’Dziko Lachikristu, chirichonse chikumakhala ndi atsogoleri ake, komabe chimodzi n’chimodzi chikumatsutsana ndi zinzake m’mbali inayake ya chiphunzitso kapena kachitidwe. Mkhalidwe wogawanikana umenewu uli umboni wowonekera wakuti iwo satsatira lamulo la Mulungu. Sangakhale ochokera kwa Mulungu. (Yerekezerani ndi Mika 2:12; Marko 3:24; Aroma 16:17; 1 Akorinto 1:10.) Chofanana chimene zipembedzo zonsezi ziri nacho n’chakuti izo sizimamatira ku ziphunzitso za Baibulo, popeza kuti adaswa lamulo lakuti: “Musapitirire zinthu zolembedwa.”—1 Akorinto 4:6, NW; onaninso Mateyu 15:3, 9, 14.
9. Kodi ndi zikhulupiriro zopanda malemba zotani zimene wosayeruzikayo waloŵetsa m’malo mwa zowonadi za Baibulo?
9 Chotero, wosayeruzikayu ali munthu wokhalamo ambiri: atsogoleri achipembedzo a Dziko Lachikristu. Onsewo, kaya akhale apapa, ansembe, abambo, kapena alaliki Achiprotestanti, amakhalamo ndi phande m’machimo achipembedzo a Dziko Lachikristu. Iwo asinthanitsa chowonadi cha Mulungu ndi mabodza achikunja, akumaphunzitsa ziphunzitso zopanda malemba zonga ngati kusafa kwa moyo wa munthu, moto wa helo, purigatoriyo, ndi Utatu. Iwo ali ngati atsogoleri achipembedzo kwa amene Yesu ananena kuti: “Inu muli ochokera mwa atate wanu Mdyerekezi, ndipo zolakalaka zake za atate wanu mufuna kuchita. . . . Ali wabodza, ndi atate wake wa bodza.” (Yohane 8:44) Zochita zawo zimawavumbulanso kukhala osayeruzika, popeza kuti amagawanamo m’machitachita amene amaswa malamulo a Mulungu. Kwa oterowo Yesu akunena kuti: “Chokani kwa ine, inu akuchita kusayeruzika.”—Mateyu 7:21-23.
Kudzikweza Iwo Eni
10. Kodi ndi unansi wotani umene wosayeruzikayo wakhala nawo ndi olamulira a ndale zadziko?
10 Mbiri yakale ikusonyeza kuti awo okhala m’gulu la munthu wosayeruzikayu asonyeza kunyada ndi kudzitama kotero kuti iwo aperekadi malingaliro kwa olamulira a dziko. Pansi pa kunamizira chiphunzitso cha ‘kuyenerera kwaumulungu kwa mafumu,’ atsogoleri achipembedzo adzinenera kukhala nkhoswe zofunikira pakati pa olamulira ndi Mulungu. Iwo ayika ndi kugwetsa mafumu ndi olamulira ndipo akhala okhoza kutembenuza unyinji kuyanja kapena kutsutsa olamulira. Mwakutero, iwo anena, monga mmene ananenera ansembe aakulu Achiyuda amene anakana Yesu kuti: “Tiribe Mfumu koma Kaisara.” (Yohane 19:15) Komabe, Yesu anaphunzitsa momvekera kuti: “Ufumu wanga suli wa dziko lino lapansi.”—Yohane 18:36.
11. Kodi ndimotani mmene atsogoleri achipembedzo adzikwezera iwo eni?
11 Kuti adzikwezedi iwo eni pamwamba pa anthu wamba, gulu losayeruzikali latenga kavalidwe kosiyana, kaŵirikaŵiri zovala zakuda. Kuwonjezerapo, iwo adzikometsera iwo eni ndi mitundu yonse ya zokometsera zokhumbirika, limodzi ndi zisoti zachifumu, mitanda, ndi zisoti za papa. (Yerekezerani ndi Mateyu 23:5, 6.) Koma Yesu ndi atsatiri ake analibe zovala zoterozo; iwo anavala monga mmene anachitira anthu wamba. Atsogoleri achipembedzo adzipatsanso maina aulemu onga ngati “Bambo,” “Bambo Woyera,” “Revulande,” “Revulande Wamkulukulu,” “Wolemekezeka,” ndi “Wopambana Onse,” omwe amawonjezera ‘kudzikweza kwawo pamwamba pa aliyense.’ Komabe, ponena za maina aulemu achipembedzo Yesu anaphunzitsa kuti: “Ndipo inu musatchule wina atate wanu pansi pano.” (Mateyu 23:9) Mofananamo, Elihu, podzudzula otonthoza Yobu achinyengo, ananena kuti: “Ndisati ndisamalire nkhope ya munthu, kapena kumtchula munthu maina omdyola nawo.”—Yobu 32:21.
12. Kodi ndani yemwe Paulo ananena kuti ndi amene atsogoleri achipembedzo ankamtumikiradi?
12 Pamene Paulo kumbuyoko m’tsiku lake ananena kuti munthu wosayeruzikayo adali atayamba kale ntchito zake, iye adanenanso za awo amene akawunikira mkhalidwe wa wosayeruzikayo kuti: “Pakuti otere ali atumwi onyenga, ochita ochenjerera, odziwonetsa ngati atumwi a Kristu. Ndipo kulibe kudabwa, pakuti Satana yemwe adziwonetsa ngati mngelo wa kuunika. Chifukwa chake sikuli kanthu kwakukulu ngatinso atumiki ake adziwonetsa monga atumiki achilungamo; amene chimaliziro chawo chidzakhala monga ntchito zawo.”—2 Akorinto 11:13-15.
Kupandukira Kulambira Kowona
13. Kodi nchiyani chimene chiri chipatuko chimene Paulo ananeneratu?
13 Paulo ananena kuti munthu wosayeruzika ameneyu akayamba limodzi ndi mpatuko. M’chenicheni, mfungulo yoyamba imene Paulo anapereka yozindikirira gulu losayeruzika limeneli ndiyakuti “tsiku la Yehova [pamene Yehova adzawononga dongosolo loipa iri la zinthu] . . . silifika koma chiyambe chifike chipatukocho.” (2 Atesalonika 2:2, 3, NW) Koma kodi nchiyani chimene “chipatuko” chimenechi chikutanthauza? M’mawu ozungulira lembali, icho sichikutanthauza kungolefuka kapena kugwa chifukwa cha kufooka kwauzimu. Liwu Lachigriki logwiritsiridwa ntchito pano kaamba ka “chipatuko” linatanthauza, pakati pa zinthu zina, “kupatuka” kapena “kuwukira.” Matembenuzidwe osiyanasiyana amalimasulira ilo kukhala “chipanduko.” Matembenuzidwe a William Barclay amanena kuti: “Tsiku limenelo silingadze kufikira Chipanduko Chachikulu chitachitika.” The Jerusalem Bible imakutcha iko kukhala “Kuwukira Kwakukulu.” Chotero, m’mawu ozungulira lemba a chimene Paulo akulankhula, “chipatuko” chimatanthauza kuwukira kulambira kowona.
14. Kodi ndiliti pamene chipatuko chinayambadi?
14 Kodi ndimotani mmene chipatuko chimenechi, chipanduko chimenechi chinayambira? Pa 2 Atesalonika 2:6, (NW), Paulo analemba, ponena za m’tsiku lake, za “chomletsa” wosayeruzikayo. Kodi icho chinali chiyani? Inali mphamvu yoletsa ya atumwi. Kukhalapo kwawo, ndi mphatso zawo zamphamvu zopatsidwa ndi mzimu woyera, kunaletsa chipatuko panthaŵiyo kukhala mliri. (Machitidwe 2:1-4; 1 Akorinto 12:28) Koma pamene atumwiwo anamwalira, chifupifupi kumapeto kwa zaka za zana loyamba, magwero oletsawo anachotsedwa.
Gulu Losakhala Lamalemba la Atsogoleri Achipembedzo Liyambika
15. Kodi ndi makonzedwe otani amene Yesu anakhazikitsa kaamba ka mpingo Wachikristu?
15 Mpingo umene Yesu anakhazikitsa unayambika mkati mwa zaka za zana loyamba pansi pa chitsogozo cha akulu (oyang’anira) ndi atumiki otumikira. (Mateyu 20:25-27; 1 Timoteo 3:1-13; Tito 1:5-9) Iwowa anatengedwa kuchokera mumpingomo. Iwo anali amuna auzimu ofikapo opanda maphunziro apadera a ukatswiri wa zaumulungu, mongadi mmene Yesu sanakhalire ndi maphunziro oterowo. Ndithudi, adani ake anazizwa kuti: “Ameneyu adziwa bwanji zolemba, wosaphunzira?” (Yohane 7:15) Ndipo ponena za atumwi, olamulira achipembedzo anawona zofananazo: “Koma pakuwona kulimbika mtima kwa Petro ndi Yohane, ndipo pozindikira kuti ndiwo anthu osaphunzira ndi opulukira, anazizwa ndipo anawazindikira, kuti adakhala pamodzi ndi Yesu.”—Machitidwe 4:13.
16. Kodi ndimotani mmene chipatuko chinapangitsira kupatuka kuchoka pa chitsanzo Chachikristu m’zaka za zana loyamba kaamba ka kakonzedwe ka mpingo?
16 Komabe, chipatuko chinabweretsa mfundo zotengedwa kuchokera kwa atsogoleri achipembedzo Achiyuda ndipo pomalizira pake kuchokera ku kakhazikitsidwe kachipembedzo kachikunja ka ku Roma. Pamene nthaŵi inapitapo ndipo kupatuka kuchoka pa chowonadi kutachitika, gulu losakhala lamalemba la atsogoleri achipembedzo linayambika. Papa woikidwa ufumu anayamba kulamulira bungwe la akadinala, amene pambuyo pake anatengedwa kuchokera kwa abishopu ndi aarkibishopu mazanamazana, amene pambuyo pake anakwezedwa kuchokera pa udindo wa ansembe ophunzitsidwa ku seminale. Chotero, sipanapite nthaŵi yaitali pambuyo pa zaka za zana loyamba, pamene gulu lokhulupirira m’zinsinsi la atsogoleri achipembedzo linatenga mphamvu m’Dziko Lachikristu. Gulu limeneli silinatsanzire akulu Achikristu ndi atumiki otumikira a m’zaka za zana loyamba koma linatsanzira dongosolo lachipembedzo chachikunja.
17. Kodi ndiliti makamaka, pamene mphamvu ya wosayeruzikayo inalimbitsidwa?
17 Kuchiyambiyambi m’zaka za zana lachitatu C.E., akhulupiriri wamba adatsitsidwira ku malo a gulu lachiŵiri la Akristu wamba. Munthu wosayeruzika wa chipatukoyo pang’onopang’ono anayambitsa mphamvu ya kulamulira. Mphamvu imeneyi inalimbitsidwa mkati mwa kulamulira kwa wolamulira Wachiroma Constantine, makamaka pambuyo pa Bungwe la pa Nicaea mu 325 C.E. Pambuyo pake Tchalitchi ndi Boma zinagwirizana pamodzi. Chotero, munthu wosayeruzika—atsogoleri achipembedzo a Dziko Lachikristu—anakhala mzere wautali wa m’zaka za mazanamazana wa ampatuko amene awukira Mulungu wowona, Yehova. Malamulo ndi makonzedwe amene iwo atsatira ali awo ndipo osati a Mulungu.
Ziphunzitso Zachikunja
18. Kodi ndi ziphunzitso zachikunja zamwano zotani zimene wosayeruzikayo anatenga?
18 Munthu wosayeruzika woyambitsidwayo anabwerekanso ziphunzitso zachikunja. Mwachitsanzo, mulungu wachinsinsi wa Utatu, wosakhoza kumvetsetseka anaikidwa m’malo mwa Yemwe ananena kuti: “Ine ndine Yehova; dzina langa ndi lomweli; ndipo ulemerero wanga Ine sindidzapereka kwa wina.” “Ine ndiri Yehova, ndipo palibe winanso; popanda Ine palibe Mulungu.” (Yesaya 42:8; 45:5) Kuloŵetsa mfundo za munthu kumeneku, zachikunja, m’malo mwa zowonadi za Mulungu kunafutukulidwa kuphatikizamo mwano winanso: kupatulikitsa Mariya wodzichepetsa wa m’Baibulo kukhala “Amayi a Mulungu” wa Dziko Lachikristu. Chotero, achilikizi a ziphunzitso zonyenga zoterozo, gulu la atsogoleri achipembedzo, anakhala m’malo apamwamba a “namsongole” wofesedwa ndi Satana kuyesera kupha mbewu zabwino zofesedwa ndi Kristu.—Mateyu 13:36-39.
19. Kodi ndimotani mmene Dziko Lachikristu lagaŵanikira m’zaka mazanamazana, koma kodi nchiyani chimene chinapitirizidwabe?
19 Pamene kusagwirizana ndi kusamvana kunabuka, Dziko Lachikristu linagaŵikana m’mazanamazana a zipembedzo ndi mipatuko. Koma chipembedzo kapena mpatuko watsopano uliwonse, kusiyapo yoŵerengeka yokha, inasungabe kupatula atsogoleri achipembedzo ndi anthu wamba. Chotero, gulu la munthu wosayeruzika lapitirizidwabe kufikira lerolino. Ndipo lidakapitirizabe kudzikweza pamwamba pa anthu wamba ndi zovala zake zosiyanitsa ndi maina aulemu apamwamba. Momvekera, Paulo sanangosinjirira pamene ananena kuti gulu la munthu wosayeruzika likadzilemekeza lokha ndi kudzikweza ku udindo waumulungu.
Upapa
20. Kodi ndimotani mmene magwero Achikatolika akulongosolera papa?
20 Chitsanzo cha ulemerero woterowo ndi chija cha upapa wa Roma. Dikishonale yatchalitchi yolembedwa ndi Lucio Ferraris, yofalitsidwira mu Italy, imalongosola papa kukhala “wolemekezekadi ndi wapamwamba kotero kuti iye sali kokha munthu koma, Mulungu, kunena kwake titero, ndi Woimira Mulungu.” Korona wake wachifumu ngwa mbali zitatu “monga mfumu ya kumwamba, ya dziko lapansi ndi ya helo.” Dikishonale imodzimodziyo ikupitiriza kuti: “Papa ndiye Mulungu padziko lapansi, kunena kwake titero, kalonga yekha wa okhulupirika a Kristu, mfumu yaikulu kuposa mafumu onse.” Iyo ikuwonjezera kuti: “Papa nthaŵi zina angaletse lamulo laumulungu.” Ndiponso, The New Catholic Dictionary ikunena za papa kuti: “Akazembe ake ali m’malo oyamba kwa ziŵalo zina za bungwe la oimira.”
21. Siyanitsani machitidwe a papa ndi aja a Petro ndi mngelo.
21 Mosiyana ndi atumwi a Yesu, papa kaŵirikaŵiri amavala chovala chokometseredwa kwambiri ndipo amalandira kulambiridwa ndi anthu. Papa amalola anthu kumgwadira, kupsompsona mphete yake, ndi kum’nyamula pamapewa awo pa mpando wapadera. Ndi uchabe wotani nanga umene apapa asonyeza kwa zaka mazanamazana! Kosiyanadi ndi kudzichepetsa kwa Petro, yemwe ananena kwa Korneliyo, mdindo Wachiroma yemwe anagwada pamapazi a Petro kuti amulambire: “Taima, . . . Ine ndinetu munthu”! (Machitidwe 10:25, 26, Jerusalem Bible Yachikatolika) Ndipo ndi kusiyana kotani nanga ndi mngelo amene anapatsa Chivumbulutso kwa mtumwi Yohane! Yohane anayesera kugwada pansi molambira mngelo ameneyo, koma mngeloyo analengeza kuti: “Tapenya, usachite; ndine kapolo mnzako, ndi mnzawo wa abale ako aneneri, ndi wa iwo akusunga mawu a bukhu ili; lambira Mulungu.”—Chibvumbulutso 22:8, 9.
22. Kodi wosayerukizayo angazindikiridwe ndi lamulo Lamalemba lotani?
22 Kodi kupenda gulu la atsogoleri achipembedzo kumeneku nkopambanitsa? Tingadziŵe chimenechi mwa kugwiritsira ntchito lamulo limene Yesu anapereka la kuzindikirira aneneri onyenga lakuti: “Mudzawazindikira ndi zipatso zawo.” (Mateyu 7:15, 16) Pamenepa, kodi nchiyani chimene chakhala zipatso za atsogoleri achipembedzo kwa zaka mazanamazana ndi m’zaka zathu za zana la 20? Kodi nchiyani chidzakhala chimaliziro cha tsoka cha munthu wosayeruzika ameneyu, ndipo kodi ndani amene adzagawanako m’tsoka limenelo? Kodi ndi thayo lotani limene awo amene amawopadi Mulungu ali nalo m’chigwirizano ndi wosayeruzikayu? M’nkhani zotsatira zidzalongosola nsongazi.
-
-
Chiweruzo cha Mulungu Motsutsana ndi “Munthu Wosayeruzika”Nsanja ya Olonda—1990 | February 1
-
-
Chiweruzo cha Mulungu Motsutsana ndi “Munthu Wosayeruzika”
“Mtengo uliwonse wosapatsa chipatso chokoma, audula, nautaya kumoto.”—MATEYU 7:19.
1, 2. Kodi nchiyani chimene chiri munthu wosayeruzika, ndipo kodi anayamba motani?
PAMENE mtumwi Paulo anawuziridwa ndi Mulungu kuneneratu za kudza kwa “munthu wosayeruzika,” iye ananena kuti akayamba kuwoneka m’tsiku lake. Monga mmene nkhani yapitayo yalongosolera, Paulo ankalankhula za gulu la anthu omwe akatsogolera m’kupatuka kuchoka pa Chikristu chowona. Kupatuka kumeneko kuchoka pa chowonadi kunayambika kumapeto kwa zaka za zana loyamba, makamaka pambuyo pa imfa ya atumwi omalizira. Gulu la wosayeruzikayo linayambitsa ziphunzitso ndi machitachita omwe adatsutsana ndi Mawu a Mulungu.—2 Atesalonika 2:3, 7; Machitidwe 20:29, 30; 2 Timoteo 3:16, 17; 4:3, 4.
-