Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Kuzindikira “Munthu Wosayeruzika”
    Nsanja ya Olonda—1990 | February 1
    • Chiyambi cha Munthu Wosayeruzika

      4. Kodi ndani yemwe ali muyambitsi ndi m’chilikizi wa munthu wosayeruzikayu?

      4 Kodi ndani yemwe anayambitsa ndi kumachilikiza munthu wosayeruzika ameneyu? Paulo akuyankha kuti: “Kudza kwake kuli monga mwa machitidwe a Satana, mu mphamvu yonse, ndi zizindikiro ndi zozizwa zonama; ndi m’chinyengo chonse cha chosalungama kwa iwo akuwonongeka, popeza chikondi cha chowonadi sanachilandira, kuti akapulumutsidwe iwo.” (2 Atesalonika 2:9, 10) Chotero Satana ndiye atate ndi m’chilikizi wa munthu wosayeruzikayu. Ndipo mongadi mmene Satana amatsutsira Yehova, zifuno Zake, ndi anthu Ake, alinso tero munthu wosayeruzikayo, kaya akuchidziŵa chimenecho kapena ayi.

      5. Kodi ndi tsoka lotani limene likuyembekezera wosayeruzikayo ndi awo amene akumtsatira?

      5 Awo oyendera limodzi ndi munthu wosayeruzikayu adzavutika ndi tsoka lofananalo​—chiwonongeko: “Adzavumbulutsidwa wosayeruzikayo, amene Ambuye Yesu adzamthera . . . nadzamuwononga ndi mawonekedwe a kudza kwake.” (2 Atesalonika 2:8) Nthaŵi imeneyo ya kuwononga munthu wosayeruzika ndi achilikizi ake (‘awo akuwonongeka’) idzadza posachedwapa “pa vumbulutso la Ambuye Yesu wochokera kumwamba pamodzi ndi angelo a mphamvu yake, m’lawi lamoto, ndi kubwezera chilango kwa iwo osamdziŵa Mulungu, ndi iwo osamvera Uthenga Wabwino wa Ambuye wathu Yesu; amene adzamva chilango, ndicho chiwonongeko chosatha.”​—2 Atesalonika 1:6-9.

  • Kuzindikira “Munthu Wosayeruzika”
    Nsanja ya Olonda—1990 | February 1
    • Kuzindikira Wosayeruzikayo

      7. Kodi nchifukwa ninji tikumaliza kuti Paulo sanali kulankhula za munthu mmodzi, ndipo kodi nchiyani chimene munthu wosayeruzikayo amaimira?

      7 Kodi Paulo ankalankhula za munthu mmodzi? Ayi, popeza kuti iye akunena kuti “munthu” ameneyu analipo m’tsiku la Paulo ndipo akapitiriza kukhalapo kufikira Yehova akamuwononge iye pamapeto a dongosolo lino. Chotero, iye wakhalapo kwa zaka mazana ambiri. Ndithudi, palibe munthu weniweni yemwe wakhala kwa utali woterowo. Chotero mawu akuti “munthu wosayeruzika” ayenera kuimira bungwe, kapena gulu la anthu.

      8. Kodi munthu wosayeruzika ndani, ndipo kodi ndi ziti zimene ziri mbali zina zomzindikirira?

      8 Kodi iwo ndani? Umboni ukusonyeza kuti iwo ali bungwe la atsogoleri achipembedzo onyada, ofuna mapindu a Dziko Lachikristu, amene m’zaka mazanamazana adzikhazikira iwo eni malamulo awo. Izi zingawonedwe mwa nsonga yakuti pali zikwizikwi za zipembedzo ndi mipatuko yosiyanasiyana m’Dziko Lachikristu, chirichonse chikumakhala ndi atsogoleri ake, komabe chimodzi n’chimodzi chikumatsutsana ndi zinzake m’mbali inayake ya chiphunzitso kapena kachitidwe. Mkhalidwe wogawanikana umenewu uli umboni wowonekera wakuti iwo satsatira lamulo la Mulungu. Sangakhale ochokera kwa Mulungu. (Yerekezerani ndi Mika 2:12; Marko 3:24; Aroma 16:17; 1 Akorinto 1:10.) Chofanana chimene zipembedzo zonsezi ziri nacho n’chakuti izo sizimamatira ku ziphunzitso za Baibulo, popeza kuti adaswa lamulo lakuti: “Musapitirire zinthu zolembedwa.”​—1 Akorinto 4:6, NW; onaninso Mateyu 15:3, 9, 14.

      9. Kodi ndi zikhulupiriro zopanda malemba zotani zimene wosayeruzikayo waloŵetsa m’malo mwa zowonadi za Baibulo?

      9 Chotero, wosayeruzikayu ali munthu wokhalamo ambiri: atsogoleri achipembedzo a Dziko Lachikristu. Onsewo, kaya akhale apapa, ansembe, abambo, kapena alaliki Achiprotestanti, amakhalamo ndi phande m’machimo achipembedzo a Dziko Lachikristu. Iwo asinthanitsa chowonadi cha Mulungu ndi mabodza achikunja, akumaphunzitsa ziphunzitso zopanda malemba zonga ngati kusafa kwa moyo wa munthu, moto wa helo, purigatoriyo, ndi Utatu. Iwo ali ngati atsogoleri achipembedzo kwa amene Yesu ananena kuti: “Inu muli ochokera mwa atate wanu Mdyerekezi, ndipo zolakalaka zake za atate wanu mufuna kuchita. . . . Ali wabodza, ndi atate wake wa bodza.” (Yohane 8:44) Zochita zawo zimawavumbulanso kukhala osayeruzika, popeza kuti amagawanamo m’machitachita amene amaswa malamulo a Mulungu. Kwa oterowo Yesu akunena kuti: “Chokani kwa ine, inu akuchita kusayeruzika.”​—Mateyu 7:21-23.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena