Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g89 8/8 tsamba 28-29
  • Kodi Wochita Kugonana kwa Ofanana Ziŵalo Angakhale Mtumiki wa Mulungu?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Wochita Kugonana kwa Ofanana Ziŵalo Angakhale Mtumiki wa Mulungu?
  • Galamukani!—1989
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Ansembe mu Israyeli
  • Muyezo Wachikristu
  • ‘Inenso Ndikukaniza’
  • Kodi Tiyenera Kuyamba Kuvomereza Khalidwe Logonana Amuna Kapena Akazi Okhaokha?
    Galamukani!—2012
  • Umathanyula—Kodi Ngwoipa Kwambiridi?
    Galamukani!—1995
  • Kugonana kwa Ofanana Ziŵalo—Kodi Nchiyani Chimene Chiri Thayo la Atsogoleri Achipembedzo?
    Galamukani!—1989
  • Kodi Baibulo Limalola kuti Akazi Kapena Amuna Okhaokha Azigonana?
    Galamukani!—2016
Onani Zambiri
Galamukani!—1989
g89 8/8 tsamba 28-29

Lingaliro la Baibulo

Kodi Wochita Kugonana kwa Ofanana Ziŵalo Angakhale Mtumiki wa Mulungu?

MUNALI mu January 1987, ndipo Robert Arpin anali kufa ndi AIDS. Chimenecho, mwa icho chokha, sichinalinso chofunikira kusimbidwa. Koma Robert Arpin anali wansembe, mmodzi wa chiŵerengero chomakulakula cha atsogoleri achipembedzo ochita kugonana kwa ofanana ziŵalo olengezedwa mwapoyera.

M’zaka za posachedwapa osati kokha kuti ogonana ofanana ziŵalo “akuwonekera poyera” koma akutulukanso mu maseminale. Munthu wosatchuka pa Catholic University Theological College mu United States anawuza National Catholic Reporter kuti: “Ndingakhoze kuyerekeza maperesenti 60 kufika ku 70 a kalasi langa kukhala ogonana ofanana ziŵalo ndipo chiŵerengero chofananacho kaamba ka seminaleyo.” Kuchitira ndemanga pa chikhoterero cha kugonana kwa ofanana ziŵalo mu maseminale, Anthony Kosnick, mkonzi wa Human Sexuality, ananena kuti: “Chiri chofala mokulira kuposa ndi mmene ndakhala ndikuchilingalira.”

Zipembedzo zosiyanasiyana zafuula kufalikira kokulira kwa malingaliro a kaya wochita kugonana kwa ofanana ziŵalo akayenera kukhala mtumiki kapena ayi. Anthu ambiri, ngakhale ndi tero, sali okondweretsedwa m’malingaliro opangidwa ndi zikhoterero zamakono koma, m’malomwake, m’chimene Baibulo limanena. Nchiyani, kenaka, chomwe chiri muyezo wa Mulungu kaamba ka atumiki? Kodi wochita kugonana kwa ofanana ziŵalo amayenerera?

Ansembe mu Israyeli

Mu Israyeli wakale muyezo kaamba ka ansembe a Yehova Mulungu unali wapamwamba kwenikweni. (Levitiko, mutu 21) Popeza kuti iwo anaimira Wokhalako Woyera Koposatu, iwo anafunikira kukhala oyera mwauzimu, kuthupi, ndi makhalidwe. “Chirichonse chokhudza guwa la nsembelo chikhale chopatulika,” Mulungu analamula tero. Chotero, pamene mkulu wansembe woyambirira wa Israyeli, Aroni, ndi ana ake aamuna anakhazikitsidwa kukhala ansembe, phwando la masiku asanu ndi aŵiri linachitidwa kuwayeretsa iwo kaamba ka ntchito zawo zopatulika.—Eksodo 29:37.

Ansembewo analinso athayo la kuphunzitsa Lamulo la Mulungu ndipo, limodzi ndi oweruza, kuwona kuti ilo linatsatiridwa. (Malaki 2:7) Chophatikizidwa mu Lamulo limenelo chinali kuletsedwa kowonekera kwa kugonana kwa ofanana ziŵalo. Mulungu analamulira kuti: “Munthu akagonana ndi mwamuna mnzake, monga amagonana ndi mkazi, achita chonyansa onse aŵiri; awaphe ndithu; mwazi wawo ukhale pamtu pawo.” (Levitiko 20:13) Mosasinthika, ansembe anafunikira kukhala ndi moyo molingana ndi Lamulo limodzimodzilo.

Pamene ansembewo analephera kusungirira lamulo laumulungu, iwo anaweruzidwa, monga m’nkhani ya mkulu wansembe wina, Eli, ndi ana ake aamuna aŵiri achisembwere. (1 Samueli 2:12-35; 4:17, 18) Pambuyo pake, m’tsiku la mneneri Ezekieli, Yehova ananena kuti: “Ansembe ake [a Israyeli] achitira choipa chilamulo changa, nadetsa zopatulika zanga.” Chifukwa cha chimenechi, Mulungu anawakana iwo.—Ezekieli 22:26, 31.

Muyezo Wachikristu

Muyezo kaamba ka awo otsogolera m’kulambira mu mpingo Wachikristu ulinso wapamwamba. Pakati pa ziyeneretso zondandalitsidwa m’Baibulo, onani izi: “wopanda chirema,” “wodzisunga,” “wodziletsa,” “woyeneretsedwa kuphunzitsa,” “[wokhala] ndi umboni wabwino kwa anthu akunja.” (1 Timoteo 3:1-7) Chotero, woyang’anira Wachikristu ayenera kukhala wopanda banga. Kawonedwe kake ka machitidwe amene ali olondola ndi osalondola kayenera kuzikidwa pa Baibulo, ndipo mkhalidwe wake suyenera kutseka maganizo a awo omwe iye akufuna kuphunzitsa. Kodi wochita kugonana kwa ofanana ziŵalo amafikira miyezo ya m’Malemba imeneyo?

Asanalembe zitsogozo zomwe ziri pamwambazo, mtumwi Paulo anachenjeza Timoteo ponena za ziŵalo zina zimene zinakhumba “kukhala aphunzitsi a lamulo.” Timoteo anafunikira kulamulira osokoneza a chikhulupiriro amenewa kuti “asaphunzitse kanthu kena.” Chotsatira, iye anachenjeza Timoteo za “anthu osayeruzika ndi osamvera lamulo, osapembedza, ndi ochimwa,” ndipo kenaka iye anazindikiritsa mwachindunji “amuna omwe amagonana ndi amuna” (NW) kukhala “akutsutsana nacho chiphunzitso cholamitsa.” (1 Timoteo 1:3-11) Motsimikizirika, yemwe amatsogolera mpingo m’kulambira sayenera kutsekereza ziphunzitso zopindulitsa za Baibulo kaya m’mawu kapena m’kakhalidwe ka moyo.—Yerekezani ndi Aroma 2:21.

Mphamvu ya kulangiza kumeneku ikuwonedwanso m’chimene Paulo analembera Tito m’Krete. M’kukhazikitsa zofunika za “akulu oikidwa” (King James Version), iye analongosola kukhala kwawo “opanda chirema,” “olungama,” “odziletsa,” “ogwira mawu okhulupirika monga mwa chiphunzitso.” (Tito 1:5-9) Yophatikizidwa mu “mawu okhulupirika” amenewo inali kalata ya Paulo yoyambirirayo kwa Akristu okhala mu Korinto, yomwe inanena kuti “amuna ogonana ndi amuna” sakaloŵa Ufumu wa Mulungu. (1 Akorinto 6:9, 10, NW) Kugwiririra ku “mawu okhulupirika” kukatheketsa mtumiki “kutsutsa otsutsana naye.” (Tito 1:9) Ndimotani mmene mtumiki wochita kugonana kwa ofanana ziŵalo angatsutsire ena pamene mkhalidwe wake wa moyo umatsutsa “mawu okhulupirika”? Mosiyanako, mtumwi Petro ananena za “aphunzitsi onama” kuti “ambiri adzatsata zonyansa zawo.”—2 Petro 2:1, 2.

‘Inenso Ndikukaniza’

Lingaliraninso ichi: M’masomphenya, mneneri Zekariya wa m’zana lachisanu ndi chiŵiri B.C.E. anawona mkulu wansembe Yoswa wovala zovala zodetsedwa. Ndimotani mmene iye akayeretsera izo kotero kuti apitirizebe kukhala wansembe? “Utamvera malamulo anga ndi kusamalira ntchito yomwe ndakugawira,” Mulungu anatero, “kenaka udzapitiriza kukhala wolamulira Kachisi yanga.” (Zekariya 3:7, Today’s English Version) Kwa aliyense pa yekha yemwe alephera kumvera malamulo aumulungu, kuphatikizapo malamulo aja oletsa kachitidwe ka kugonana kwa ofanana ziŵalo, Mulungu akunena kuti: “Popeza unakana kudziŵa, inenso ndikukaniza, kuti usakhale wansembe wanga.”—Hoseya 4:6.

Chotero, kodi wochita kugonana kwa ofanana ziŵalo angakhale mtumiki wa Yehova Mulungu? Ayi. Anthu omwe sayenerera mogwirizana ndi “ziphunzitso zamoyo” zopezeka m’Baibulo sali atumiki owona a Mulungu.—Tito 2:1; 1 Timoteo 1:10; onaninso Aroma 1:24-27, 32.

[Chithunzi patsamba 29]

Ndimotani mmene mtumiki angaphunzitsire ena molongosoka pamene mkhalidwe yake wa moyo umatsutsa “mawu okhulupirika”?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena