Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Chipambano—Pa Mtengo Wonse?
    Nsanja ya Olonda—1988 | August 15
    • Ndi kufalikira kwa umphawi, anthu ambiri alondola chipambano cha chuma kupatulapo china chirichonse. Ena amakhoterera ku kusawona mtima kotero kuti afikire chimenechi. Pa kukhala Akristu owona, ngakhale ndi tero, iwo ayenera kukhala anasiya kotheratu mkhalidwe umenewo kumbuyo ndi cholinga chofuna kugwirizana ndi miyezo yolungama ya Baibulo.

      Ngakhale kuli tero, ngakhale Akristu ena amagwidwa kachiŵirinso m’kulunjikitsa chidwi pa zonulirapo zakudziko. Iwo angagwere mu mkhalidwe wosakhala Wachikristu ndi cholinga chofuna kupeza chipambano. Makolo amanyalanyaza mabanja awo. Aliyense payekha amanyalanyaza utumiki wawo kwa Mulungu. Nchiyani chomwe mukulingalira kuti chidzakhala chotulukapo ponena za chokwaniritsa m’moyo ndi chimwemwe?

      Likumatigalamutsa ife ku chotulukapocho, Baibulo likuchenjeza kuti: “Koma iwo akufuna kukhala ahuma amagwa m’chiyesero ndi mumsampha ndi m’zilakolako zambiri zoposa ndi zopweteka . . . Pakuti muzu wa zoipa zonse ndiwo chikondi cha pa ndalama, chimene ena pochikhumba anasokera nataya chikhulupiriro nadzipyoza ndi zowawa zambiri.”​—1 Timoteo 6:9, 10.

  • Chipambano—Pa Mtengo Wonse?
    Nsanja ya Olonda—1988 | August 15
    • Chikondi cha chuma chiri mbuye wolamulira. Icho chimatha nthaŵi ya anthu, mphamvu, ndi kuthekera; ndipo chimatsamwitsa kudzipereka kwaumulungu. Icho kaŵirikaŵiri chimawanyenga anthu kufunafuna ngakhale chuma chokulira ndi kunyada kwa kudziko, motero kuwakokera iwo kutali ndi chikhulupiriro. Baibulo molondola limanena kuti: “Wokonda siliva sadzakhuta siliva, ngakhale wokonda chuma sadzakhuta phindu.”​—Mlaliki 5:10.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena