Kumachita Mmene Tingathere Kulalikira Mbiri Yabwino
“Chita zimene ungathe kudziwonetsera wovomerezeka kwa Mulungu, wantchito wopanda kali konse kochita nako manyazi.”—2 TIMOTEO 2:15, NW.
1, 2. Kodi ndi kukula kotani mu mathayo a aminisitala anthawi zonse komwe mwawona? Kodi nchiyani chomwe chawonjezera ku icho?
“ZAKA PANG’ONO zapita, ambiri a ife tinali kuganiza kuti kokha awo amene ali ndi mikhalidwe yapadera angachite upainiya,” analemba motero mpainiya, kapena mtumiki wa nthawi zonse, mu Japani. “Chikuwoneka kuti tinali olakwa. Tikuphunzira kuti kokha awo amene ali ndi mikhalidwe yapadera sangachite upainiya.”
2 Kawonedwe kabwino kameneko katulukapo mu kukula kwa chibadwa kwa mathayo a aminisitala anthawi zonse pakati pa Mboni za Yehova mu zaka zaposachedwa. Lerolino mu Japani, awiri pa ofalitsa a Ufumu asanu alionse ali mu utumiki wa nthawi zonse. Koma mzimu wachangu umenewu siuli kokha mu Japani. Mu chaka chautumiki chapita, chiwerengero cha ofalitsa kuzungulira dziko lonse lapansi chinakula ndi 5 peresenti, pamene chiwerengero cha aminisitala a nthawi zonse chinawonjezeka ndi 22 peresenti. Mwachiwonekere, anthu a Yehova atenga mu mtima mawu a mtumwi Paulo: “Chita zimene ungathe kudziwonetsera wovomerezeka kwa Mulungu, wantchito wopanda kali konse kochita nako manyazi.” (2 Timoteo 2:15, NW) Kodi mmenemo ndimo momwe ziliri ndi inu?
“Ichi ndi Chikondi cha Mulungu”
3. Kodi nchiyani chimene chiri mphamvu yofulumiza kulinga ku kukula kumeneku?
3 Pamene apainiya anafunsidwa kuti nchifukwa ninji anatenga utumiki wa nthawi zonse, mosasiyana yankho lawo liri lakuti chiri chifukwa cha chikondi chawo kaamba ka Yehova Mulungu. (Mateyu 22:37, 38) Ichi, komabe, chiri monga mmene chiyenera kukhalira, popeza popanda chikondi monga chofulumiza chenicheni, unyinji wonse wa kuyesetsa ungakhale wopanda phindu. (1 Akorinto 13:1-3) Chiri choyamikirikadi kuti ambiri a Akristu anzathu—kwenikweni, avereji ya ofalitsa oposa asanu ndi awiri mu mpingo uli wonse kuzungulira dziko lonse—apanga malo mu miyoyo yawo kusonyeza chikondi chawo kaamba ka Mulungu mu njira iyi.
4. Ndi motani mmene tinakondera Mulungu? (Aroma 5:8)
4 Komabe, tonse a ife amene tinapereka miyoyo yathu kwa Yehova tinachita choncho chifukwa cha chikondi chathu kaamba ka iye. Pamene tinaphunzira za chikondi cha Yehova ndi Mwana wake, Yesu Kristu, kaamba ka ife, ndi za madalitso abwino kwambiri amene Ufumu wake udzabweretsa, mitima yathu inafulumizidwa kuvomereza ndi chikondi kaamba ka iye. Umo ndi mmene mtumwi Yohane anaikira icho: “Tikonda, chifukwa chakuti anayamba iye kutikonda.” (1 Yohane 4:19) Timavomereza mwa chibadwa mu njira imeneyo chifukwa chakuti mmenemo ndi mmene tinapangidwira. Koma kodi maganizo otentha amenewa mu mitima mwathu ndiwo kokha chimene chikondi cha Mulungu chimaphatikizamo?
5. Kodi chikondi cha Mulungu chimaphatikizamo chiyani? (1 Yohane 2:5)
5 Ayi, chikondi cha Mulungu chimatanthauza zochulukira. Mtumwi Yohane akutiuza ife: “Pakuti ichi ndi chikondi cha Mulungu, kuti tisunge malamulo ake; ndipo malamulo ake sali olemetsa.” (1 Yohane 5:3) Inde, chikondi chenicheni, monga chikhulupiriro chenicheni, chimasonyezedwa mwa ntchito. (Yerekezani ndi 2 Akorinto 8:24. ) Timafuna kusangalatsa ndi kupeza chivomerezo cha wokondedwa. Iri njira yabwino kwambiri chotani nanga imene awo amene ali mu utumiki wa nthawi zonse asankha kusonyeza chikondi chawo kaamba ka Yehova ndi Yesu Kristu!
6. (a) Kodi ndi anthu amtundu wanji amene akhoza kuchita upainiya? Kodi nchiyani chimene chachipangitsa icho kukhala chothekera kaamba ka iwo kuchita tero? (b) Kodi mumadziwa aliyense wa zitsanzo zimenezo?
6 Mikhalidwe ya aliyense payekha imasiyana, ndipo iyenera kulingaliridwa. Komabe, pamene tikuyang’ana kwa awo amene ali mu utumiki wa nthawi zonse, timapeza kuti amaphatikizapo anthu amene ali mu mkhalidwe uli wonse wothekera—aang’ono ndi a akulu, osakwatiwa ndi okwatiwa, okhala ndi thanzi labwino ndi loipa, okhala ndi mathayo abanja ndiponso opanda mathayo abanja, ndi zina zotero. Kusiyana kuli kwakuti, m’malo molola zinthu zimenezi kukhala zotsekereza njira, iwo, monga mtumwi Paulo, aphunzira kugwira ntchito mozungulira iyo kapena kukhala limodzi ndi iyo. (2 Akorinto 11:29, 30; 12:7) Talingalirani, mwachitsanzo, banja lachitsanzo.
Eiji ali mkulu mu mpingo wake. Iye ndi mkazi wake akhala akuchita upainiya limodzi kwa zaka 12 pamene anali kulera ana awo atatu. Ndi motani mmene iwo anachitira ichi? “Tinayenera kukhala mu mkhalidwe wokhweka kwambiri, anatero Eiji. Ndipo ana anayenera kuphunzira kulandira ayi kaamba ka zinthu zambiri zimene iwo anazifuna. “Angakhale kuti tinali ndi nthawi zina zovuta, Yehova nthawi zonse anapereka zomwe tinazifuna.”
Kodi kudzipereka kwakhala kuli koyenerera? “Usiku uli wonse tisanazimitse magetsi, ndimawona mkazi wanga akulemba ripoti lake laulaliki kaamba ka tsikulo,” anatero Eiji. “Pamene ndiwona banja langa likuika zikondwerero za Ufumu choyamba monga izi, ndimamvakuti chiri chonse chiri monga chiyenera kukhalira, ndipo ndimakhala ndi ganizo lakukwaniritsa. Sindingalingalire konse kusachita upainiya pamodzi.” Ndi motani mmene mkazi wake amamvera ponena za icho? “Eiji watisamalira ife bwino kwambiri,” iye anatero. “Pamene ndimuwona iye wotanganitsidwa ndi zinthu za uzimu, ndimamva kukwaniritsidwa kwa mkatikati. Ndikhulupirira kuti tidzapitiriza.”
Kukhala ndi atate ndi amayi akuwononga nthawi yambiri chotero mu ntchito ya kulalikira tsiku ndi tsiku, kodi ndi chiyambukiro chotani chomwe chakhala nacho pa ana? Mwana wamwamuna wa mkulu tsopano akugwira ntchito yomanga ya zaka zinayi pa nthambi ya Watch Tower Society. Mwana wa mkazi ndi mpainiya wokhazikika, ndipo mwana wamwamuna wa zaka zopita ku sukulu akulingalira za kudzakhala mpainiya wapadera. Iwo onse ali osangalala kuti makolo awo ali apainiya.
7. (a) Perekani zitsanzo kaamba ka awo amene mumadziwa omwe analaka zokhumudwitsa kuti alowe mu utumiki wa nthawi zonse. (b) Kodi ndi uphungu wa Baibulo wotani umene iwo analabadira?
7 Mabanja monga iri angapezeke pakati pa Mboni za Yehova mu maiko ambiri kuzungulira pa dziko lapansi. Iwo amaika patsogolo kuyesetsa kwenikweni kupanga kuthekera kwa mikhalidwe yawo ndi cholinga cholowa ndi kukhazikika mu utumiki wa nthawi zonse. Ndi ntchito zawo, iwo amasonyeza nchiyani chimene chikondi cha Mulungu chimatanthauza kwa iwo. Mofunitsitsa, iwo akulabadira ku chenjezo la Paulo: “Chita zimene ungathe kudziwonetsera wovomerezeka kwa Mulungu, wantchito wopanda kali konse kochita nako manyazi.”—2 Timoteo 2:15.
“Wantchito Wopanda Kali Konse Kochita nako Manyazi”
8. Kodi nchifukwa ninji Paulo anafulumiza Timoteo kuchita ‘zimene angathe’ ndipo kodi nchiyani chimene icho chimatanthauza?
8 Pamene Paulo analemba mawu amenewo kwa Timoteo, chifupifupi 65 C.E., Timoteo nkuti akutumikira kale m’malo athayo lofunika kwambiri mu mpingo wa Chikristu. Paulo anamutchula iye “msilikari wabwino wa Kristu Yesu” ndipo mobwerezabwereza anamukumbutsa iye za thayo lake mu kuphunzitsa ndi kulangiza ena. (2 Timoteo 2:3, 14, 25; 4:2) Pa nthawi imodzimodziyo, iye anafulumiza Timoteo: “Chita zimene ungathe kudziwonetsera wovomerezeka kwa Mulungu.” Mawu akuti “chita zimene ungathe” ali otembenuzidwa kuchokera ku mawu a Chigriki otanthauza “kukufulumiza.” (Onani Kingdom Interlinear Translation.) Mmawu ena, Paulo anali kuuza Timoteo kuti ndi cholinga chakuti iye akakhale wovomerezedwa ndi Mulungu anafunikira kupititsa patsogolo ntchito yake, angakhale kuti anali kutenga thayo lolemetsa. Nchifukwa ninji? Kotero kuti iye akakhale “wantchito wopanda kali konse kochita nako manyazi.”
9. Kodi ndi fanizo lotani la Yesu lomwe lingatithandize ife kumvetsetsa mawu a Paulo onena za “wantchito wopanda kali konse kochita nako manyazi”?
9 Mawu omalizirawo atikumbutsa ife za akapolo atatu a mu fanizo la Yesu la matalenti, monga lalembedwa pa Mateyu 25:14-30. Pamene mbuye wawo anabwerera, inali nthawi yawo yakupereka ntchito zawo kwa mbuye wawo kaamba ka chivomerezo. Akapolo amene anapatsidwa matalenti asanu ndi awiri anayamikiridwa ndi mbuye wawo kaamba ka zimene anachita ndi zinthu zomwe zinaperekedwa kwa iwo. Iwo anaitanidwa ‘kulowa mu chikondwerero cha mbuye wawo.’ Koma kapolo amene anapatsidwa talenti imodzi anapezedwa akufunafuna. Chimene anali nacho chinatengedwa, ndipo ku kuchititsidwa manyazi kwake, iye anatayidwa kunja “ku mdima wa kunja.”
10. Nchifukwa ninji kapolo amene anapatsidwa talenti imodzi anachititsidwa manyazi ndi kulangidwa?
10 Akapolo awiri oyambirira anagwira ntchito molimbika ndi kuchulukitsa zikondwerero za mbuye wawo. Iwo mowonadi anali ogwira ntchito “opanda kali konse kochita nako manyazi.” Koma nchifukwa ninji kapolo wachitatu anachititsidwa manyazi ndi kulangidwa ngakhale kuti iye sanataye chomwe chinapatsidwa kwa iye? Chinali chifukwa chakuti iye sanachite chiri chonse chomangirira ndi icho. Monga mmene mbuye wawo analozera, iye akanaika ndalamayo ku banki. Koma chomwe chinali cholakwa kwenikweni chinali chakuti iye analibe chikondi chenicheni kaamba ka mbuye wake. “Ndinawopa ine, ndinapita, ndinabisa pansi ndalama yanu,” iye anatero kwa mbuye wake. (Mateyu 25:25; yerekezani ndi 1 Yohane 4: 18. ) Iye anawona mbuye wake monga munthu wankhalwe, “munthu wolamulira” ndipo thayo lake monga cholemetsa. Iye anachita chochepera monga momwe kukanathekera ndi cholinga chofuna kupeza m’malo mwa kuchita “zimene angathe” kupeza chivomerezo cha mbuye wake.
11. Ndi motani mmene fanizo limenelo limatikhudzira ife lerolino?
11 Lerolino fanizo limenelo liri kukwaniritsidwa. Ambuye, Yesu Kristu, wabwerera ndipo akuyendera ntchito ya gulu la “kapolo” wake, limodzinso nda anzawo, a “khamu lalikulu” onga nkhosa. (Mateyu 24:45-47; Chivumbulutso 7:9, 15) Kodi ndi chiyani chimene Mbuye akupeza? Ngati tidzikwaniritsa ife eni ndi ntchito yachiphamaso ndi cholinga chofuna kupeza, ndiyeno chidzapezeka kuti tidzazipeza pakati pa awo ochititsidwa manyazi ndi kutaidwa “kumdima wa kunja.” Kumbali ina, ngati ife ‘tichita zimene tingathe,’ kunena kuti, ‘kufulumiza’ ntchito yathu mu chivomerezo cha kufulumira kwa nthawi, tidzapezeka ovomerezedwa monga ‘antchito opanda kali konse kochita nako manyazi’ ndipo tidzagawana mu ‘chimwemwe chambuye wathu.’
Chilango ndi Kudzipereka Kwaumwini Nkofunika
12. Kodi ndi zinthu ziti zimene zatheketsa peresenti yokulira ya ofalitsa mu Japani kulowa mu uminisitala wanthawi zonse?
12 Kufutukuka kopitirizabe kwa mathayo aupainiya mu dziko ndi dziko kuzungulira dziko lonse chiri chitsimikiziro chowonekera chakuti anthu a Yehova onse ‘akuchita zimene angathe’ kuzitsimikizira iwo eni ‘antchito opanda kali konse kochita nako manyazi.’ Koma kodi inu munayamba mwaganizirapo nchifukwa ninji mu maiko ena peresentenji ya abale okhoza kulowa mu utumiki wa nthawi zonse iri yokulira kuposa mu maiko ena? Funso losangalatsa limeneli linaperekedwa kwa apainiya ena a mu Japani. Lingalirani mayankho awa:
“Sindikuganiza kuti chimatanthauza kuti chikhulupiriro, kapena chikondi cha Mboni za Chijapani chiri chokulirapo kuposa chija cha abale awo mu maiko ena,” anatero wogwira ntchito pa Betele yemwe wakhala mu utumiki wa nthawi zonse kwa zaka 30. “Koma ndimakhulupirira kuti umunthu wa a Japani mwina mwake uyenera kulowetsedwamo. Monga onse, anthu a Chijapani ali omvera; amavomereza mwachangu ku chilimbikitso.”
“Popeza muli apainiya ambiri chifupifupi mu mpingo uli wonse,” mkulu anapereka ndemanga, “lingaliro lofala liri lakuti aliyense angachite iwo.” Anthu a Chijapani amakonda kuchita zinthu mu gulu. Iwo ali ndi mzimu wabwino kwambiri wa gulu.
Ndemanga zimenezi mowonadi ziri zokhudza maganizo, ndipo ngati ife tiri ofunitsitsa ponena za kuwongolera utumiki wathu kulinga kwa Yehova, pali mfundo zochuluka zowonekera bwino kwambiri zofunikira kulingalira kwathu kosamalitsa.
13. Kodi ndi motani mmene tingapindulire kuchokera ku nkhani yakukhala omvera ndi okonzekera kuvomereza ku chilimbikitso?
13 Choyambirira, pali kufunika kwa kukhala omvera ndi okonzekera kuvomereza ku chilimbikitso. Pamene chitsogozo ndi chilimbikitso chibwera kuchokera ku magwero oyenerera, chiri kokha cholondola kuti tiyenera kuvomereza mwachangu. Mwakutero, m’malo mwakuwona mikhalidwe imeneyi monga zizolowezi za mtundu, tisunge m’maganizo mawu a Yesu: “Nkhosa zanga zimva mawu anga, ndipo ine ndizizindikira, ndipo zinditsata ine.” (Yohane 10:27) Timakumbukiranso kuti njira imodzi ya “nzeru yochokera kumwamba” iri “yomvera bwino”. (Yakobo 3:17) Awa ali makhalidwe omwe Akristu onse akulimbikitsidwa kukhala nawo. Kaamba ka mayambidwe ndi maleredwe, ena angakhale operekedwa kwambiri ku kulingalira kodzikhalira pawokha ndi chifuno chaumwini kuposa ena Mwina mwake iri liri dera limene tikafunikira kudzilanga ife eni ndi ‘kusintha maganizo athu’ kotero kuti tikawonetsetse bwino chimene chiri “chifuniro cha Mulungu.”—Aroma 12:2.
14. Kodi ndi chiitano chotani chimene Akristu onse odzipereka achilandira, ndipo kodi icho chimaphatikizamo chiyani?
14 Monga Akristu odzipereka, talandira chiitano cha Yesu: “Ngati munthu afuna kudza pambuyo panga, adzikane yekha natenge [mtengo wake wozunzirapo, NW] nanditsate ine.” (Mateyu 16:24) “Kudzikana” iwe mwini kumatanthauza ‘kudzikana iwe mwini kotheratu’ ndipo pambuyo pake mofunitsitsa kuvomereza kukhala wotengedwa ndi Yehova Mulungu ndi Yesu Kristu, kuwalola iwo kulamulira miyoyo yathu ndi kutiuza ife chimene tiyenera ndi chimene sitiyenera kuchita. Kodi ndi njira yabwinopo yotani yosonyezera kuti tadzikana ife eni koposa kutsatira mapazi a Yesu mu utumiki wa nthawi zonse?
15. (a) Kodi ndi motani mmene kukhala wokwanira ndi zochepa mwa kuthupi kumagwirizanira ndi kutsatira Yesu? (b) Kodi ndi motani mmene otsatira oyambirira anavomerezera ku chiitano cha Yesu cha kumutsatira iye?
15 Kenaka pali nkhani ya kukhala wokwanira ndi zinthu zochepa mwakuthupi. Ichi mwachiwonekere chiri chotsutsana ndi lingaliro lofala la dziko, limene limapititsa patsogolo “chilakolako chathupi ndi chilakolako cha maso ndi matamandidwe a moyo.” (1 Yohane 2:16) Koma Yesu ananena mogogomezera: “Chifukwa chache tsono yense wa inu amene sakaniza zonse ali nazo sakhoza kukhala wophunzira wanga.” (Luka 14:33) Nchifukwa ninji ichi chiri tero? Chifukwa chakuti kukhala wophunzira wa Yesu kumatanthauza koposa kungokhala mkhulupiriri. Pamene Yesu anaitana Andreya, Petro, Yakobo ndi Yohane, ndi ena kukhala otsatira ake, mu chaka chachiwiri cha utumiki wake iye sanaleke kuwafunsa iwo kukhulupirira mwa iye monga Mesiya. Iye pambuyo pache anawaitana iwo kumutsatira iye ndi kuchita ntchito imene iye anali kuchita, kunena kuti, kukhala mu ntchito yolalikira ya nthawi zonse. Kodi nchiyani chimene chinali chivomerezo chawo? “Ndipo pomwepo anasiya makoka awo, namutsata iye.” Yakobo ndi Yohane “anasiya atate wawo Zebedayo m’chombo pamodzi ndi antchito olembedwa namutsata iye.” (Marko 1:16-20) Iwo anasiya m’mbuyo malonda awo ndi ogwirizana nawo akale, ndipo anatenga ntchito yolalikira ya nthawi zonse.
16. Monga Akristu odzipereka, ndi mu chiyani mmene tiyenera kusunga nthawi yathu ndi mphamvu zathu? (Miyambo 3:9)
16 Chiri chapafupi kuwona, chotero, nchifukwa ninji kukhala wokwanira ndi zochepa kuli kofunika kwambiri mkuchita zimene tingathe mu utumiki wa Yehova. Ngati tiri olemetsedwa ndi zinthu zambiri zakuthupi kapena mathayo ena ali onse, tingakhale ngati wolamulira wachichepere wachuma yemwe sanavomereze chiitano cha Yesu chakukhala wotsatira wake, osati chifukwa chakuti sakanakhoza kutero, koma chifukwa chakuti sanali wovomereza kusiya m’mbuyo “chuma chambiri.” (Mateyu 19:16-22; Luka 18:18-23) Chotero m’malo mwakuwononga nthawi yathu ndi mphamvu yathu kulondola zinthu zomwe posachedwapa ‘zidzataika’ tifuna kusunga zinthu za mtengo wapatali kwambiri zimenezi kaamba ka moyo wathu wosatha.—1 Yohane 2:16, 17.
17. Ndi kumlingo wotani kumene mzimu wagulu ungakhale ndi chotulukapo chabwino?
17 Pomalizira, pali nkhani ya mzimu wa gulu. Andreya, Petro, Yakobo, ndi Yohane mosakaikira anafulumizana wina ndi mnzake mu chosankha chawo chakulandira chiitano cha Yesu cha kumutsatira iye. (Yohane 1:40, 41) Mofananamo, chenicheni chakuti ambiri a abale athu ali okhoza kupanga malo mu miyoyo yawo yotanganitsidwa kulowa mu utumiki wa nthawi zonse chiyenera kutifulumiza ife kulingalira mkhalidwe wathu mosamalitsa. Kumbali ina, awo pakati pa ife amene akusangalala ndi mwawi umenewu angagawane zokumana nazo zawo zosangalatsa ndi ena, mwakutero kulimbikitsa awanso kulowa mu mathayo awo. Ndipo, komabe, aminisitala anthawi zonse angathandizane wina ndi mnzake ku phindu laonse.—Aroma 1:12.
18. Ndi motani mmene tonse a ife tingaperekere ku mzimu wa upainiya?
18 Angakhale awo amene mikhalidwe yawo pa nthawi ino siwalola iwo kutenga utumiki wa nthawi zonse angachite zambiri kuwonjezera mzimu waupainiya. Motani? Mwakuchirikiza ndi kulimbikitsa awo amene akuchita upainiya, mwa kusonyeza chikondwerero cha changu mu awo amene ali ndi mphamvu yakuchita tero, mwa kukonzekeretsa kaamba ka chifupifupi m’modzi wa membala wa banja lawo kuchita upainiya, mwakukhala mu ntchito ya upainiya wothandizira ngati kungatheke, ndi mwakugwira ntchito kulinga ku kulowa mu utumiki wanthawi zonse mwamsanga. Kuchita tero, tonse a ife tingasonyeze kuti ‘tikuchita zimene tingathe’ kutumikira Yehova kaya talembetsa kale mu utumiki wanthawi zonse kapena ayi.
Kuchita Khama M’kuchita Kuthekera Kwathu
19. Ndi chiyani chimene tiyenera kugamula kuchita m’chiyang’aniro chanthawi?
19 Indedi, pamene Yehova akufulumiza ntchito, tsopano iri nthawi kaamba ka ife ‘kuchita zimene tingathe’ ndi cholinga chofuna kukhala ‘antchito opanda kali konse kochita nako manyazi.’ Monga msilikari wabwino wa Yesu Kristu, ifenso tikafunikira kuika pambali zolemetsa zosayenera kotero kuti tikatumikire mokhutiritsa ndi kulandira chivomerezo. (2 Timoteo 2:3-5) Pamene tikugwira ntchito molimbika kufutukula kugawana kwathu mu utumiki wa Ufumu, tingatsimikiziridwe kuti zoyesayesa zathu zidzafupidwa molemerera. (Ahebri 6:10; 2 Akorinto 9:6) Mwakutero, m’malo mwakuima mphepete mwanjira, monga mmene tinganenere, tiyeni tichite khama mkuchita zimene tingathe m’kulalikira mbiri yabwino, m’kupereka yankho ku chiitano cha wa masalmo: “Tumikirani Yehova ndi chikondwerero. Idzani pamaso pake ndi kumuyimbira mokondwera.”—Masalmo 100:2.
Bokosi Lakubwereramo
◻ Kodi chikondi cha Mulungu chimaphatikizamo chiyani?
◻ Kodi nchiyani chimene chinali vuto lenileni la kapolo wachitatu mu fanizo la Yesu la matalenti?
◻ Kodi kudzikana ife eni kumatanthauzanji?
◻ Nchifuka ninji otsatira a Yesu ayenera ‘kutsazikana ndi chuma chawo chakuthupi’?
◻ Ndi motani mmene tonse a ife tingaperekere ku mzimu wa upainiya?
[Chithunzi pa tsamba 28]
‘Ponyani kapoloyo wopanda pake kunja’