Lingaliro la Baibulo
Kodi Muyenera Kulola Chikumbumtima Chanu Kukhala Mtsogoleri Wanu?
PAMENE muyenda mumsewu wa piringupiringu, mupitana ndi mkazi wovala bwino amene mosazindikira ataya chikwama cha ndalama. Pamene mukuwerama kutola ndalamazo, muwona mwamsanga mkaziyo akukwera galimoto lambambande. Kodi mudzachitanji? Mudzamuitana mofuula kapena kodi mudzangoika ndalamazo m’nthumba mwanu mofulumira?
Yankho lidzadalira pachikumbumtima chanu. Kodi chidzakuuzani kuchita chiyani? Chofunika kwambiri, kodi mumakhulupirira zimene chimakuuzani? Kodi modalirika mungalole chikumbumtima chanu kukhala mtsogoleri wanu?
Chimene Chikumbumtima Chili
Chikumbumtima chafotokozedwa kukhala lingaliro lachibadwa la chimene chili chabwino ndi choipa, cholungama ndi chosalungama, makhalidwe abwino ndi oipa. Baibulo limafotokoza kagwiridwe ka ntchito ka chikumbumtima pa Aroma 2:14, 15 kuti: “Pakuti pamene anthu a mitundu akukhala opanda lamulo, amachita mwa okha za lamulo, omwewo angakhale alibe lamulo, adzikhalira okha ngati lamulo; popeza iwo awonetsa ntchito ya lamulo yolembedwa m’mitima yawo, ndipo chikumbumtima chawo chichitiranso umboni pamodzi nawo, ndipo maganizo awo wina ndi mnzake anenezana kapena akanirana.” Motero, chikumbumtima chanu ncholinganizidwa kukukhozetsani kusiyanitsa mikhalidwe, kupanga zosankha zabwino, ndi kudziweruza nokha pa zosankha zimene mwapanga. Koma kodi mungachidalire?
Zimenezo zimadalira pamikhalidwe ina yake. Komabe, pali umboni wochuluka wakutsimikizira kuti chikumbumtima cholakwa chingatsogolere munthu kuchita zoipa. Chenicheni chakuti chikumbumtima cha munthu chimalolera khalidwe linalake sindicho chilolezo chakuti Mulungu amakhululukira khalidwe limenelo. Mwachitsanzo, Saulo wa ku Tariso asanakhale Mkristu, anatsogolera kuzunza Akristu. Iye anavomereza ndi kutenga mbali m’chochitika choipa chakupha mwambanda Mkristu wofera chikhulupiriro Stefano. M’zimenezi, chikumbumtima chake sichinamtsutse.—Machitidwe 7:58, 59; Agalatiya 1:13, 14; 1 Timoteo 1:12-16.
Mu Germany wa Nazi mkati mwa Nkhondo Yadziko II, asilikali ambiri a SS ananena kuti iwo anali kungotsatira chabe malamulo pamene anazunza mwankhanza ndi kupha mamiliyoni ambiri pa misasa ya chibalo ya Hitler. Zikumbumtima zawo zinawalola kutero. Koma chiweruzo chadziko—ndipo chofunika kwambiri, chiweruzo cha Mulungu—sichinakhululukire zochita zawo. Iwo anatsutsidwa moyenera.
Kodi Nchifukwa Ninji Sichigwira Ntchito Moyenerera?
Kodi nchifukwa ninji chinthu cholengedwa ndi Mulungu sichimagwira ntchito moyenerera nthaŵi zina? Baibulo limapereka yankho. Chifukwa cha kuchimwa kwa munthu kupyolera mwa kusamvera kwa Adamu, uchimo ukunenedwa kukhala ‘ukuchita ufumu,’ kukakamiza anthu kumvera zikhumbo zake. (Aroma 5:12; 6:12) Chikumbumtima cha munthu, chimene chinali changwiro pachiyambi, chinakhotetsedwa; mphamvu ya uchimo tsopano imalimbana ndi chikumbumtima. (Aroma 7:18-20) Zimenezi zinayambitsa kulimbana kumene timadziŵa: “Ndipo chotero ndipeza lamulo ili, kuti, pamene ndifuna chabwino, choipa chiliko. . . . Koma ndiona lamulo lina m’ziŵalo zanga, lilikulimbana ndi lamulo la mtima wanga, ndi kundigonjetsa kapolo wa lamulo la m’ziŵalo zanga.”—Aroma 7:21-23.
Kuwonjezera pa kufooka kobadwa nako kumeneku, zikumbumtima zathu zimayambukiridwa ndi chisonkhezero chakunja. Mwachitsanzo, chitsenderezo cha anzawo mwachiwonekere chinakhotetsa kapena kugonjetsa zikumbumtima za asilikali a SS a Nazi amene atchulidwa poyambapo. (Yerekezerani ndi Miyambo 29:25.) Ndiponso, kudyetsa malingaliro athu zinthu zosakhala zabwino, monga ngati chisembwere ndi chiwawa pa TV ndi akanema, ndi mabuku, zingatiyambukire mofananamo. Ngati nthaŵi zonse tiona zinthu zoterozo, pomalizira pake sizidzaoneka kukhala zoipa, ndipo chikumbumtima chathu chidzafoketsedwa. Kunena kwina tingati, “mayanjano oipa aipsa makhalidwe abwino.”—1 Akorinto 15:33.
Ngati munthu aphunzitsidwa kudziŵa ndi kulemekeza malamulo a Mulungu, mwachiwonekere chikumbumtima chake chidzakhala chitsogozo chodalirika kusiyana ndi mmene akanakhalira wosaphunzitsidwa. Komabe, ngakhale munthu womvetsetsa ndi wozindikira kwambiri njira za Mulungu nthaŵi zina angapezebe kuti chikumbumtima chake sichili mtsogoleri wodalirika, chifukwa cha choloŵa cha uchimo ndi kupanda ungwiro, ndipo mwinamwake chisonkhezero chakunja.
Kodi Tingachite Chiyani?
Kodi chikumbumtima chingasinthidwe, kupangidwa kukhala chozindikira malamulo oyenera? Inde. Paulo analangiza Akristu kuti akanatha ‘mwakuzigwiritsira ntchito, kuphunzitsa mphamvu zawozo zakuzindikira kusiyanitsa zonse ziŵiri chabwino ndi choipa.’ (Ahebri 5:11-14, NW) Kugwiritsira ntchito ndi kuphunzitsa koteroko kumaphatikizapo kuphunzira Baibulo, kusumika maganizo mosamalitsa pa chitsanzo changwiro chosiyidwa ndi Yesu Kristu. (1 Petro 2:21, 22) Pambuyo pake, pamene tigwiritsira ntchito mphamvu zathu zakuzindikira popanga zosankha, zikumbumtima zathu zidzatitsogolera kusiya malingaliro ndi ntchito zoipa ndi kutisonkhezera kuchita chimene chili cholemekezeka ndi cholungama.
Ngakhale ndichoncho, sitiyenera kukhala odzilungamitsa kapena kunena kuti ngati kanthu kena “sikavutitsana ndi chikumbumtima changa,” pamenepo zili bwino. Kagwiritsidwe koyenera ndi kotetezereka ka chikumbumtima mwa anthu opanda ungwiro kangafaniziridwe ndi woyendetsa galimoto wosamala. Pamene woyendetsa galimoto akufuna kusintha njira, choyamba mwanzeru amayang’ana pa galasi lake lowonera m’mbuyo. Ngati awona galimoto, amadziŵa kuti sikuli bwino kuti asinthe njira. Komabe, ngati sawona kanthu, woyendetsa wanzeru amazindikira kuti pali zinthu zina zimene sangathe kuwona—sizonse zimene zingaonedwe pagalasi nthaŵi zonse. Chifukwa chake, samangoyang’ana chabe pagalasi. Amatulutsa mutu wake kuti awone, akumatsimikizira kuti njira ili yabwino asanasinthe. Zimenezi nzofanana ndi chikumbumtima. Ngati chikuchenjezani, mverani! Koma ngakhale ngati sichimagunda pachiyambi, khalani wofanana ndi woyendetsa galimoto wanzeru—yang’anitsitsani kutsimikizira kuti kulibe ngozi.
Pendani maganizo anu kuwona ngati amagwirizana ndi kalingaliridwe ka Mulungu. Gwiritsirani ntchito Mawu ake monga chopimira chikumbumtima chanu. Pa Miyambo 3:5, 6 mwanzeru pamati: “Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse, osachirikizika pa luntha lako; umlemekeze m’njira zako zonse, ndipo iye adzaongola mayendedwe ako.”
Chotero nkwanzeru kumvera chikumbumtima chanu. Komanso nkwanzeru koposa kuyerekezera zonse zimene timachita ndi chifuno cha Mulungu monga momwe chavumbulidwira m’Mawu ake. Mpokhapo pamene tinganene mwachitsimikizo kuti, “Takopeka mtima kuti tili nacho chikumbumtima chokoma m’zonse.”—Ahebri 13:18; 2 Akorinto 1:12.
[Chithunzi patsamba 27]
“Kutembenuzidwa kwa St. Paul”
[Mawu a Chithunzi]
Chithunzi ndi Caravaggio: Scala/Art Resource, N.Y.