Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w92 7/1 tsamba 4-7
  • Chiyembekezo Chimagonjetsa Kutaya Mtima!

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chiyembekezo Chimagonjetsa Kutaya Mtima!
  • Nsanja ya Olonda—1992
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Maziko a Chiyembekezo
  • Chiyembekezo​—“Chokhazikika ndi Cholimbanso”
  • Chiyembekezo​—“Nangula wa Moyo”
  • ‘Gwiritsani Zolimba’!
  • Pitirizani Kulimbitsa Chiyembekezo Chanu
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2022
  • Tili ndi Chiyembekezo Chomwe Sichitikhumudwitsa
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2023
  • Kodi Chiyembekezo Chodalirika Mungachipeze Kuti?
    Galamukani!—2004
  • Yembekezani Yehova Kuti Mukhale Olimba Mtima
    Nsanja ya Olonda—2006
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1992
w92 7/1 tsamba 4-7

Chiyembekezo Chimagonjetsa Kutaya Mtima!

MU Webster’s Ninth New Collegiate Dictionary, kutaya mtima kwalongosoledwa kukhala “kutaikiridwa chiyembekezo kotheratu.” Chotero, nkowonekeratu kuti kuti tigonjetse kutaya mtima, timafunikira chiyembekezo!

Munthu wosauka wokakamizika kukhala m’mphepete mwakhwalala sangataye mtima kotheratu ngati ali nacho chiyembekezo. Chiyembekezo chikhoza kupereka kulimba mtima ndi nyonga yakupirira kwa awo amene amavutika ndi kuchita tondovi. Koma chiyembekezocho chiyenera kukhala chodalirika! Kodi zimenezi zimatanthauzanji?

Maziko a Chiyembekezo

Talingalirani zimene zinachitika kwa Sara, mkazi wa kholo Abrahamu. Pofikira zaka 90, iye adakali woumabe ndipo atataya kale chiyembekezo chakubala mwana. Chikhalirechobe, pamene mwamuna wake anali wazaka 99, Yehova anabwereza lonjezo limene adalipereka zaka zambiri kalelo​—Abrahamu akakhaladi ndi “mbewu,” kapena woloŵa nyumba. Abrahamu anadziŵa kuti limeneli linali lonjezo lodalirika. Tangoyerekezerani chimwemwe chimene Sara ayenera kukhala anali nacho pamene, mozizwitsa, chochitika chosangalatsacho chinachitika, ndipo anabala Isake! (Genesis 12:2, 3; 17:1-4, 19; 21:2) Chidaliro cha Abrahamu mwa Mulungu sichinali cholakwika, monga momwedi mtumwi Paulo anafotokozera kuti: “Poyang’anira lonjezo la Mulungu [Abrahamu] sanagwedezeka chifukwa cha kusakhulupirira, koma analimbika m’chikhulupiriro, napatsa Mulungu ulemu.”​—Aroma 4:20.

Polembera Ayuda omwe anakhala Akristu m’tsiku lake, Paulo anadziŵa kuti anakhoza kudalira palonjezo la Mulungu la chipulumutso kupyolera mwa Yesu kaamba ka zifukwa zazikulu ziŵiri. Akumatchula lonjezo limene Mulungu anapereka kwa Abrahamu ndi lumbiro Lake lotsagana, mtumwiyo ananenetsa kuti: “Pakuti anthu amalumbira pa wamkulu; ndipo m’chitsutsano chawo chiri chonse lumbiro litsiriza kutsimikiza. Momwemo Mulungu, pofuna kuwonetsera mochulukira kwa oloŵa a lonjezano kuti chifuniro chake sichisinthika, analoŵa pakati ndi lumbiro; kuti mwa zinthu ziŵiri zosasinthika, mmene Mulungu sakhoza kunama, tikakhale nacho chotichenjeza cholimba, ife amene tidathaŵira kuchigwira chiyembekezo choikika pamaso pathu.” (Ahebri 6:16-18) Inde, malonjezo a Mulungu ali owona ndi odalirika. Yehova ngwamphamvu yonse ndipo amakhoza mwapadera kutsimikizira kukwaniritsidwa kwa mawu ake.

Chiyembekezo​—“Chokhazikika ndi Cholimbanso”

Paulo analemba kuti chiyembekezo Chachikristu chiri “chokhazikika ndi cholimbanso.” (Ahebri 6:19) Paulo anadziŵa pamene anazika chiyembekezo chake. Akufotokoza kuti: “[Chiyembekezo] chakuloŵa m’kati mwa chophimba.” Kodi zimenezi zimatanthauzanji? Paulo analikupereka chitsanzo chodziŵika bwino lomwe cha kachisi wakale m’Yerusalemu. M’kati mwake munali chipinda Chopatulikitsa, cholekanitsidwa ku mbali zina zonse za kachisi ndi chinsalu chochinga. (Eksodo 26:31, 33; Mateyu 27:51) Ndithudi, kachisi weniweniyo m’Yerusalemu anawonongedwa kalekale. Chotero, kodi malo Opatulikitsa amenewo nchiyani lerolino?

Ndiwo kumwamba kwenikweniko, kumene kuli mpando wachifumu wa Mulungu! Paulo anafotokoza zimenezi pamene ananena kuti Yesu atakwera kumwamba “sanaloŵa m’malo opatulika omangika ndi manja [m’kachisi mu Yerusalemu], akutsanza owonawo; komatu m’mwamba momwe, kuwonekera tsopano pamaso pa Mulungu chifukwa cha ife.” (Ahebri 9:24) Chotero chiyembekezo Chachikristu, chimene chimatithandiza kulimbana ndi kutaya mtima, sichimadalira pa anthu andale zadziko koma pakakonzedwe kakumwamba. Chimadalira pa Uyo amene Mulungu anamuika, Yesu Kristu, amene anapereka moyo wake kaamba ka machimo athu ndi amene tsopano akuwonekera pamaso pa Mulungu mmalo mwa ife. (1 Yohane 2:1, 2) Ndiponso, monga momwe magazini ano amasonyezera kaŵirikaŵiri, Yesu mmodzimodziyo ndiye anaikidwa ndi Mulungu kulamulira monga Mfumu ya Ufumu wakumwamba wa Mulungu ndipo watero chiyambire 1914. Ufumu wakumwamba umenewu posachedwapa udzachotsa zinthu zimene zimataitsa mtima anthu ambiri.

Chiyembekezo​—“Nangula wa Moyo”

Kuti akhutiritse oŵerenga kalata yake kuti chiyembekezo chawo cha chipulumutso chodzera mwa Yesu chinali ndi maziko olimba, paulo anagwiritsira ntchito mawu ofananitsa. ‘Chiyembekezochi’ iye anafotokoza, ‘tiri nacho [ngati] nangula wa moyo.’​—Ahebri 6:19.

Anangula anali odziŵika bwino kwambiri kwa anthu apaulendo onga Paulo. Anangula akale anali ofananako ndi amakono, kaŵirikaŵiri opangidwa ndi chitsulo okhala ndi nsonga ziŵiri zimene zimakazika zolimba pansi panyanja. Ali paulendo wopita ku Roma pafupifupi chaka cha 58 C.E., ngalawa imene Paulo analimo inali pafupi kumira. Koma pamene bwatolo linayenda pamadzi osaya kwambiri, amalinyerowo “anaponya anangula anayi kumakaliro.” Chifukwa cha anangula amenewo, chombocho sichinasweke ndi mkunthowo.​—Machitidwe 27:29, 39, 40, 44.

Pamenepo, kodi muyenera kuchitanji kupangitsa chiyembekezo chanu kuti chikhale cholimba monga nangula kotero kuti musasweke ndi mavuto achuma, matenda, kupanda chimwemwe, kapena “mikuntho” iriyonse imene mungayang’anizane nayo? Choyamba, dzitsimikizireni kuti malonjezo a Baibulo ali okhulupiririka. “Tsimikizirani zinthu zonse.” (1 Atesalonika 5:21) Mwachitsanzo, nthaŵi yotsatira imene Mboni za Yehova zidzalankhula nanu, mvetserani zimene zidzanena. Ngati sizimafika kaŵirikaŵiri kwanuko, kazifuneni ku Nyumba Yaufumu yapafupi. Simudzakakamizidwa kugwirizana nazo, koma mudzapemphedwa kuvomereza kosi yaulere ya phunziro la Baibulo, imene idzalinganizidwa kuchitidwira kulikonse ndi panthaŵi iriyonse yokukomerani.

Phunziro loterolo lidzakutsimikizirani kuti Mulungu “ali wobwezera mphotho iwo akumfuna iye.” (Ahebri 11:6) Mudzaphunzira kuti posachedwapa Ufumu wa Mulungu m’manja mwa Mfumu, Kristu Yesu, udzachotsa chinyengo ndi chisalungamo chonse zimene zimapangitsa ambiri kukhala otaya mtima lerolino. Mu Ufumu umenewo, dziko lapansili lidzabwezeretsedwa kukhala paradaiso, ndipo Mulungu adzapereka moyo wamuyaya kwa awo amene amamkonda. (Salmo 37:29; Chivumbulutso 21:4) Nchiyembekezo chaulemerero chotani nanga!

Ŵerengani Baibulo mosamalitsa kuti muwone kuti chiyembekezo chimenechi nchowona. Ndiyeno gwirirani ntchito pakukulitsa unansi wanu ndi Mulungu, mukumakhala bwenzi lake monga momwe Abrahamu analiri. (Yakobo 2:23) Popeza kuti Yehova ndiye “Wakumva pemphero,” muuzeni nkhaŵa zanu. Pamene mumfikira mowona mtima, pemphero lanu lidzakuthandizani kutula katundu wothodwetsa wa mavuto anu ndi kugonjetsa kutaya mtima. Mzimu wa Mulungu ungakutsegulireni njira yosinthira mkhalidwe umene umakupsinjani.​—Salmo 55:22; 65:2; 1 Yohane 5:14, 15.

‘Gwiritsani Zolimba’!

Atalimbikitsa ophunzira anzake “kutsimikizira zinthu zonse,” Paulo anawonjezera kuti: “Gwiritsani zolimba chokomacho.” (1 Atesalonika 5:21, NW) Njira imodzi yochitira zimenezi ndiyo kugwirizana ndi anthu amene nawonso amagwiritsa zolimba chiyembekezo Chachikristu. Solomo Mfumu yanzeru anachenjeza kuti: “Ukayenda ndi wanzeru udzakhala wanzeru: Koma mnzawo wa opusa adzapwetekedwa.” (Miyambo 13:20) Musalole tsankho kapena malingaliro oipa kukulepheretsani kufunafuna mayanjano abwino. Mwachitsanzo, pakati pa Mboni za Yehova, pali anthu amene kale analibe chiyembekezo. Koma kuphunzira kwawo Baibulo, limodzi ndi mayanjano achimwemwe ndi okhulupirira anzawo, zimalimbitsa unansi wawo ndi Yehova ndi kuwapatsa chiyembekezo chodalirika chonga nangula. Kodi zimenezi zimagonjetsadi kutaya mtima? Inde zimatero.

Talingalirani chitsanzo cha Annmarie, yemwe analoŵetsedwa mumkhalidwe wakutaya mtima chifukwa chakuchitiridwa nkhanza ndi mwamuna wake. “Ndinasankha kudzipha,” iye anatero, “koma kaamba ka chifukwa china ndinati choyamba ndipemphere kwa Mulungu. Ndikukumbukirabe kukhala ndikunena kuti, ‘Kodi simungandithandize? Ndayembekezera mwa inuyo kwa nthaŵi yaitali, koma mosaphula kanthu.’ Ndinamaliza pemphero langa ndikulingalira kuti moyo unalibe chifuno chirichonse, choncho ndibwino kuti ndingofa. Pamphindi yomweyo ndinamva kugogoda pachitseko. Ndinangonyalanyaza, ndikuyembekezera kuti aliyense amene alipo, akachoka.

“Kugogodako kunapitirizabe, ndipo ndinakwiya. Ndinapukuta misozi ndikupita kukawona amene anali pakhomopo, ndikumalingalira kuti ndikadziwonjole mofulumira kotero kuti ndikwaniritse cholinga changa. Koma,” akutero Annmarie, “ndiyamika Yehova, sizinachitike mwanjirayo, popeza kuti pamene ndinatsegula chitseko, ndinapeza akazi aŵiri ali chiliri pomwepo. Ndithudi, ndinasokonezeka maganizo kwambiri, ndipo sindinamvetsetsedi zimene anali kunena. Koma anandigaŵira bukhu limene linafotokoza kuti moyo uli ndi chifuno. Ndilo limene ndinafunikira kutsitsimula chikondwerero changa m’moyo.” Alendo akewo analinganiza kuchita naye phunziro Labaibulo lokhazikika. Annmarie anaphunzira kukhala bwenzi la Mulungu. Atatero, anapeza chifuno m’moyo. Tsopano iye amathandiza ena kukhala ndi chidaliro mwa Mulungu.

Mwinamwake inuyo mwakhala mukuyembekezera kutha kwa kutaya mtima popanda kudziŵa kwenikweni zimene zimaloŵetsedwamo. Koma ngati munapempherapo kuti: “Ufumu wanu udze. Kufuna kwanu kuchitidwe, monga kumwamba chomwecho pansi pano,” pamenepo munapempherera kudza kwa Ufumu wa Mulungu mwa Yesu Kristu, umene udzachotsa zinthuzo zimene zimachititsa anthu amaganizo olama kutaya mtima. (Mateyu 6:10) Phunziro laumwini la Baibulo ndi kusonkhana nthaŵi zonse ndi ena amene ali ndi chidaliro chofananacho zidzalimbikitsa kugwiritsa kwanu zolimba chiyembekezo cha Ufumu wa Yehova umene udzabweretsa Paradaiso padziko lapansi. (1 Timoteo 6:12, 19) Chimenechi ndicho chiyembekezo chaulemerero chimene magazini ano amalengeza m’kope lirilonse. Gwiritsani chiyembekezocho ndi mtima wonse kuti mulimbane nako kutaya mtima. Ndithudi, chiyembekezo “sichigwiritsa mwala.”​—Aroma 5:5, NW.

[Chithunzi patsamba 7]

Kuphunzira Baibulo kumatipatsa chiyembekezo chonga “nangula wa moyo”

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena