Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w20 July tsamba 31
  • Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mafunso Ochokera kwa Owerenga
  • Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2020
  • Nkhani Yofanana
  • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
    Nsanja ya Olonda—1989
  • ‘Mudzakhala Ufumu wa Ansembe’
    Nsanja ya Olonda—2014
  • Yehova Ananeneratu za Pangano Latsopano
    Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2017
  • Pangano Latsopano la Mulungu Liyandikira Kukwaniritsidwa Kwake
    Chisungiko cha Padziko Lonse mu Ulamuliro wa “Kalonga wa Mtendere”
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2020
w20 July tsamba 31

Mafunso Ochokera Kwa Owerenga

Kodi ndi liti pamene Yesu anakhala mkulu wa ansembe, nanga kodi pali kusiyana pakati pa nthawi imene pangano latsopano linakhazikitsidwa komanso nthawi imene linayamba kugwira ntchito?

Pali umboni wosonyeza kuti Yesu anakhala mkulu wa ansembe mu 29 C.E., pamene anabatizidwa. Kodi tikudziwa bwanji zimenezi? Pamene Yesu ankabatizidwa, anasonyeza kuti ankafunitsitsa kupereka moyo wake paguwa lansembe lophiphiritsira lomwe likuimira “chifuniro” cha Mulungu. (Agal. 1:4; Aheb. 10:5-10) Popeza guwa lansembe linali lofunika kwambiri pakachisi, kachisi wauzimu ayenera kuti anakhazikitsidwa pa nthawi imene Yesu anabatizidwa. Kachisi wamkulu wauzimu wa Yehova amaimira zimene Mulungu wachita kuti tizimulambira m’njira yoyenera, zomwe zimatheka chifukwa cha nsembe ya Yesu.​—Mat. 3:16, 17; Aheb. 5:4-6.

Kachisi wamkulu wauzimu ankafunika kukhala ndi wansembe. Choncho Yehova anasankha Yesu kuti akhale mkulu wa ansembe ndipo anamudzoza ndi “mzimu woyera ndi mphamvu.” (Mac. 10:37, 38; Maliko 1:9-11) Komano kodi tingatsimikize bwanji kuti Yesu anasankhidwa kukhala mkulu wa ansembe asanaphedwe komanso kuukitsidwa? Chitsanzo cha Aroni komanso akulu a ansembe omwe anasankhidwa pambuyo pake, chingatithandize kupeza yankho la funso limeneli.

Chilamulo chimene Yehova anapereka kwa Mose chinkanena kuti mkulu wa ansembe yekha ndi amene ankayenera kulowa m’Malo Oyera Koposa a chihema ndipo kachisi atamangidwa ankalowa m’Malo Oyera Koposa a kachisi. Katani ndi yomwe inkalekanitsa Malo Oyera Koposa ndi Malo Oyera. Mkulu wa ansembe ankadutsa katani imeneyi kamodzi pachaka pa Tsiku la Mwambo Wophimba Machimo. (Aheb. 9:1-3, 6, 7) Aroni komanso akulu a ansembe omwe anabwera pambuyo pake ankadzozedwa asanadutse katani imeneyi n’kukafika m’Malo Oyera Koposa. Choncho, nayenso Yesu ayenera kuti anadzozedwa kukhala mkulu wa ansembe asanaphedwe n’kudutsa “nsalu yotchinga, imene ndi thupi lake” kuti apite kumwamba. (Aheb. 10:20) Chimenechi n’chifukwa chake Paulo ananena kuti Yesu anabwera “monga mkulu wa ansembe” ndipo anadutsa “kudzera m’chihema chachikulu ndi changwiro kwambiri chimene sichinapangidwe ndi manja a anthu,” n’kukalowa “kumwamba kwenikweniko.”​—Aheb. 9:11, 24.

Palibe kusiyana pakati pa nthawi imene pangano latsopano linakhazikitsidwa komanso nthawi imene linayamba kugwira ntchito. N’chifukwa chiyani tikutero? Pamene Yesu anapita kumwamba n’kukapereka mtengo wa nsembe yomwe anapereka m’malo mwa ife, anachita chinthu choyamba pa zinthu zitatu zomwe zinachititsa kuti mwalamulo pangano latsopano likhazikitsidwe. Zinthu zitatu zimenezi ndi zomwe zinachititsanso kuti liyambe kugwira ntchito. Kodi zinthu zitatuzi ndi ziti?

Choyamba, Yesu anakaonekera pamaso pa Yehova. Chachiwiri, anapereka mtengo wa nsembe yake kwa Yehova. Ndipo chachitatu, Yehova anavomereza mtengo wa nsembe ya magazi omwe Yesu anakhetsa. Zinthu zitatu zimenezi zinkayenera kuchitika kaye kuti pangano latsopano liyambe kugwira ntchito.

Baibulo silinena nthawi yeniyeni imene Yehova anavomereza mtengo wa nsembe ya Yesu. Choncho sitinganene nthawi yeniyeni imene pangano latsopano linakhazikitsidwa komanso imene linayamba kugwira ntchito. Komabe, timadziwa kuti Yesu anapita kumwamba kutatsala masiku 10 kuti chikondwerero cha Pentekosite chichitike. (Mac. 1:3) Nthawi inayake pakati pa kanthawi kakafupi kameneka, Yesu anapereka mtengo wa nsembe yake ndipo Yehova analandira. (Aheb. 9:12) Tikudziwa zimenezi chifukwa cha zomwe zinachitika pa Pentekosite mu 33 C.E. (Mac. 2:1-4, 32, 33) Zomwe zinachitika pa tsikuli zinasonyezeratu kuti pangano latsopano linali litakhazikitsidwa komanso linali litayamba kugwira ntchito.

Mwachidule, pangano latsopano linakhazikitsidwa komanso linayamba kugwira ntchito pamene Yehova analandira mtengo wansembe ya magazi omwe Yesu anakhetsa. Pa nthawiyi, panganoli linayamba kugwira ntchito ndipo Yesu yemwe ndi mkulu wa ansembe ndi amene ali mkhalapakati wake.​—Aheb. 7:25; 8:1-3, 6; 9:13-15.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena