Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
Ahebri 9:16 amanena kuti wochititsa pangano ayenera kufa kuti panganolo ligwire ntchito. Koma Mulungu anachita pangano latsopano, ndipo sanafe. Choncho tiyenera kulimva motani vesi lemeneli?
Pa Ahebri 9:15-17 timaŵerenga kuti: ‘Ndipo mwa ichi [Kristu] ali nkhoswe ya [pangano latsopano, NW], kotero kuti, popeza kudachitika imfa yakuwombola zolakwa za [pangano loyamba], oitanidwawo akalandire lonjezano la zoloŵa zosatha. Pakuti pamene pali [pangano] pafunika pafike imfa ya [wochititsa pangano (waumunthuyo), NW]. Pakuti [pangano] liwona mphamvu atafa mwini wake; popeza liribe mphamvu konse pokhala [wochititsa pangano (waumunthuyo), NW] ali ndi moyo.’a
Yehova ndiye Wopanga weniweni wa pangano latsopano. Pa Yeremiya 31:31-34, Mulungu ananeneratu mwachindunji kuti iye akapangana pangano limenelo ndi anthu ake. Mtumwi Paulo anagwira mawu a lembali pa Ahebri 8:8-13, amene amasonyeza kuti Paulo anazindikira kuti, kwenikweni, Mulungu anayambitsa pangano laumulungu limeneli.
Komabe, mu Ahebri mutu 9, Paulo anali kufotokoza ntchito zosiyanasiyana zimene Yesu anachita zokhudza pangano latsopano. Kristu anadza monga Mkulu Wansembe wa panganoli. M’lingaliro lina, Yesu anali nsembe ya pangano latsopano; “mwazi wa Kristu” wokha ukhoza ‘kuyeretsa chikumbumtima chanu kuchisiyanitsa ndi ntchito zakufa.’ Kristu analinso Nkhoswe ya pangano limeneli, monga momwedi Mose analiri nkhoswe ya pangano Lachilamulo.—Ahebri 9:11-15.
Paulo ananena kuti imfa inafunika kuti mapangano pakati pa Mulungu ndi anthu agwire ntchito. Mwachitsanzo, tinene pangano Lachilamulo. Mose anali nkhoswe yake, wochititsa kuvomerezana kumeneku pakati pa Mulungu ndi Israyeli wakuthupi. Motero Mose anachita mbali yofunika ndipo anali munthu amene anachita ndi Aisrayeli pamene anali kuloŵa m’panganolo. Motero Mose anawonedwa monga wochititsa pangano waumunthu wa pangano Lachilamulo limene Yehova anayamba. Koma kodi Mose anayenera kutaya mwazi wamoyo wake kuti pangano Lachilamulolo liyambe kugwira ntchito? Ayi. Mmalomwake nyama zinaperekedwa, mwazi wawo ukutenga malo a mwazi wa Mose.—Ahebri 9:18-22.
Nanga bwanji ponena za pangano latsopano pakati pa Yehova ndi mtundu wa Israyeli wauzimu? Yesu Kristu anali ndi thayo lalikulu la umkhala pakati, Unkhoswe pakati pa Yehova ndi Israyeli wauzimu. Ngakhale kuti Yehova anayambitsa pangano limeneli, linazikidwa pa Yesu Kristu. Pambali pokhala Nkhoswe yake, Yesu anachita mwachindunji m’thupi ndi amene akakhala oyamba kuloŵa m’panganolo. (Luka 22:20, 28, 29) Ndiponso, anayeneretsedwa kupereka nsembe yofunika kuti panganolo ligwire ntchito. Nsembe imeneyo sinali ya nyama koma ya moyo wangwiro waumunthu. Choncho Paulo anakhoza kutchula Kristu monga wochititsa pangano waumunthu wa pangano latsopano. Pamene ‘Kristu analoŵa . . . m’mwamba momwe, kuwonekera tsopano pamaso pa Mulungu chifukwa cha ife,’ pangano latsopano linayamba kugwira ntchito.—Ahebri 9:12-14, 24.
Polankhula za Mose ndi Yesu monga ochititsa mapangano aumunthu, Paulo sanali kunena kuti pali amene anayambitsa mapangano pakati pa aŵiriwo, amene kwenikweni anapangidwa ndi Mulungu. Mmalomwake, anthu aŵiriwo analoŵetsedwamo kwambiri monga nkhoswe m’kuchititsa mapangano amenewo. Ndipo pazochitika zonse ziŵirizo, panafunikiradi imfa—nyama mmalo mwa Mose, ndi Yesu akupereka nsembe mwazi wamoyo wakewo mmalo mwa awo okhala m’pangano latsopano.
[Mawu a M’munsi]
a Mawu aŵiri Achigiriki ogwiritsiridwa ntchito panopa a “ya wochititsa pangano” amamasuliridwa m’lingaliro lenileni kukhala “(amene) wadzipangira pangano” kapena “[iye] wopanga pangano.”—The Kingdom Interlinear Translation of the Greek Scriptures, yofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc., ndi The Interlinear Greek-English New Testament, yotembenuzidwa ndi Dr. Alfred Marshall.