-
Muzikhulupirira Kwambiri Zinthu Zimene MukuyembekezeraNsanja ya Olonda (Yophunzira)—2016 | October
-
-
2 Anthu a m’dzikoli amayembekezeranso zinthu zosiyanasiyana koma sakhala otsimikiza ngati zingachitikedi. Mwachitsanzo, amene amatchova juga amayembekezera kuti awina koma sangatsimikize zoti awinadi. Koma Akhristufe timatsimikizira ndi mtima wonse kuti zimene tikuyembekezera zidzachitikadi. (Aheb. 11:1) Koma kodi tingatani kuti tizikhulupirira kwambiri zinthu zimene tikuyembekezera? Nanga kuchita zimenezi kungatithandize bwanji?
3. N’chifukwa chiyani timakhulupirira kwambiri zimene Mulungu watilonjeza?
3 Munthu sabadwa ndi chikhulupiriro ndipo sichibwera chokha. Mkhristu amakhala ndi chikhulupiriro chifukwa choti mzimu woyera ukumuthandiza. (Agal. 5:22) Baibulo silinena kuti Yehova ali ndi chikhulupiriro kapena kuti amafunika chikhulupiriro. Iye ndi Wamphamvuyonse ndipo ali ndi nzeru zopanda malire choncho sangalephere kukwaniritsa cholinga chake. Sakayikira zoti adzakwaniritsa lonjezo lakuti adzadalitsa anthu ake. Kwa iye zili ngati “zakwaniritsidwa” kale. (Werengani Chivumbulutso 21:3-6.) Akhristufe timakhala ndi chikhulupiriro chifukwa chodziwa kuti Yehova ndi Mulungu wokhulupirika ndipo amakwaniritsa chilichonse chimene walonjeza.—Deut. 7:9.
TIZITSANZIRA CHIKHULUPIRIRO CHA ANTHU AKALE
4. Kodi anthu amene anamwalira Yesu asanabwere padzikoli akuyembekezera chiyani?
4 Chaputala 11 cha buku la Aheberi chimatchula za amuna ndi akazi okwana 16 amene anali ndi chikhulupiriro. Paulo anatchula za anthuwa komanso za ena ambiri amene “anachitiridwa umboni chifukwa cha chikhulupiriro chawo.” (Aheb. 11:39) Onsewa anali ndi “chiyembekezo chotsimikizika” choti Mulungu adzatumiza “mbewu” imene idzaphwanye mutu wa Satana n’kukwaniritsa cholinga cha Mulungu choyambirira. (Gen. 3:15) Koma anthu okhulupirika amenewa anamwalira Yesu Khristu yemwe ndi “mbewu,” asanatsegule njira yoti anthu ena adzapite kumwamba. (Agal. 3:16) Komabe popeza Yehova amakwaniritsa malonjezo ake, anthuwa adzaukitsidwa ndipo adzakhala m’paradaiso.—Sal. 37:11; Yes. 26:19; Hos. 13:14.
-
-
Muzikhulupirira Kwambiri Zinthu Zimene MukuyembekezeraNsanja ya Olonda (Yophunzira)—2016 | October
-
-
7. Kodi Yehova watipatsa zinthu ziti kuti tikhalebe ndi chikhulupiriro cholimba, nanga ifeyo tiyenera kuchita chiyani?
7 Yehova watipatsa Baibulo lathunthu kuti litithandize kukhala ndi chikhulupiriro cholimba. M’Baibulo muli malangizo amene angatithandize kuti tizisangalala. Choncho ndi bwino kuyesetsa kuti tiziwerenga Mawu a Mulungu tsiku lililonse. (Sal. 1:1-3; werengani Machitidwe 17:11.) Mofanana ndi atumiki a Mulungu akale, tiyenera kuganizira kwambiri malonjezo a Yehova komanso kumvera malangizo ake. Yehova amagwiritsanso ntchito “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” kuti azitipatsa chakudya chauzimu pa nthawi yoyenera. (Mat. 24:45) Tiyeni tizigwiritsa ntchito zinthu zonse zimene Yehova amatipatsa. Tikatero tidzafanana ndi atumiki akale okhulupirika omwe ankayembekezera Ufumu wa Mulungu ndipo sankakayikira malonjezo ake.
-