-
Tsanzirani Chikhulupiriro cha MoseNsanja ya Olonda—2014 | April 15
-
-
1, 2. (a) Kodi Mose ali ndi zaka 40 anasankha kuchita chiyani? (Onani chithunzi pamwambapa.) (b) N’chifukwa chiyani Mose anasankha kuvutikira limodzi ndi anthu a Mulungu?
MOSE analeredwa m’banja lachifumu ndipo ankadziwa zinthu zabwino zimene zinali ku Iguputo. Iye ankaona nyumba zikuluzikulu za anthu olemera komanso “anaphunzira nzeru zonse za Aiguputo” monga luso losiyanasiyana, masamu ndi maphunziro ena a sayansi. (Mac. 7:22) Iye akanatha kukhala ndi chuma, udindo komanso zinthu zina zimene Aiguputo ena sakanazipeza.
2 Koma ali ndi zaka 40, Mose anachita zinthu zimene zinadabwitsa kwambiri banja lachifumu limene linkamulera. Iye anasankha kuchoka m’banja lachifumu. Kodi anangokhala ngati munthu wamba wa ku Iguputo? Ayi. Iye anasankha kukhala ndi anthu a mtundu wake amene anali akapolo. N’chifukwa chiyani anachita zimenezi? Mose anali ndi chikhulupiriro. (Werengani Aheberi 11:24-26.) Chifukwa cha chikhulupiriro, Mose sankangoona zinthu zooneka. Iye ankakhulupirira Yehova “Wosaonekayo” ndipo ankadziwa kuti malonjezo ake onse adzakwaniritsidwa.—Aheb. 11:27.
-
-
Tsanzirani Chikhulupiriro cha MoseNsanja ya Olonda—2014 | April 15
-
-
6. (a) N’chifukwa chiyani Mose anakana “kutchedwa mwana wa mwana wamkazi wa Farao”? (b) N’chifukwa chiyani tinganene kuti Mose anasankha bwino?
6 Chikhulupiriro chimene Mose anali nacho chinamuthandizanso posankha zochita pa moyo wake. Baibulo limati: “Mwa chikhulupiriro, Mose atakula anakana kutchedwa mwana wa mwana wamkazi wa Farao.” (Aheb. 11:24) Mose sanaganize kuti angathe kutumikira Mulungu kunyumba yachifumu komweko ndi kumagwiritsa ntchito chuma chake komanso udindo womwe akanakhala nawo kuthandiza Aisiraeli anzake. M’malomwake, Mose ankakonda Yehova ndi mtima wake wonse, moyo wake wonse, ndi mphamvu zake zonse. (Deut. 6:5) Zimene Mose anasankhazi zinamuthandiza kupewa mavuto aakulu. Chuma chambiri cha Aiguputo chimene Mose anachisiya chinadzatengedwa ndi Aisiraeli. (Eks. 12:35, 36) Farao anachititsidwa manyazi kenako anaphedwa. (Sal. 136:15) Koma Mose sanaphedwe ndipo Mulungu anamugwiritsa ntchito kutsogolera anthu ake kuti atuluke mu Iguputo. Iye anachita zaphindu pa moyo wake.
-