Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Chitirani Umboni Yehova Ndipo Musaleme
    Nsanja ya Olonda—1989 | December 15
    • 8. (a) Kodi nchiyani chimene chinafulumiza Paulo kulemba kalata yake kwa Ahebri? (b) Kodi ndi pa mbali iti ya kalata yake pamene tidzalunjikitsa chisamaliro chathu, ndipo nchifukwa ninji?

      8 Podzafika 61 C.E., Paulo anali ataikidwa m’ndende mu Roma, koma anadziŵa za chimene chinali kuchitika kwa abale ake m’Yerusalemu. Chotero, pansi pa chitsogozo cha mzimu wa Yehova, iye analemba kalata yake ya panthaŵi yake kwa Ahebri. Iyo iri yodzala ndi kudera nkhaŵa kwachikondi kaamba ka abale ndi alongo ake Achihebri. Paulo anadziŵa chimene iwo anafunikira kuti amangirire chikhulupiriro ndi chidaliro chawo mwa Yehova monga Mthandizi wawo. Pamenepo akakhoza ‘kuthamanga mwachipiriro makaniwo oikidwa pamaso pawo’ ndi kunena modalirika kuti: “Yehova ndiye mthandizi wanga; sindidzawopa. Kodi munthu angandichitenji?” (Ahebri 12:1; 13:6, NW) Ndi pa nsonga imeneyi ya kalata ya Paulo kwa Ahebri (mitu 11-13) pamene tsopano tikufuna kulunjikitsa chisamaliro chathu. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti mkhalidwe umene Akristu oyambirirawo anakumana nawo uli wofanana ndi umene ukukumanidwa ndi Mboni za Yehova lerolino.

  • Chitirani Umboni Yehova Ndipo Musaleme
    Nsanja ya Olonda—1989 | December 15
    • 11. Kodi ndimotani mmene tingapindulire lerolino ku ‘mtambo waukulu wa mboni zotizinga’?

      11 Kutsatira cholembedwa cha amuna ndi akazi okhulupirika amenewo, Paulo akunena kuti: “Chifukwa chake ifenso, popeza tizingidwa nawo mtambo waukulu wotere wa mboni, titaye cholemetsa chirichonse, ndi chimoli limangotizinga, ndipo tithamange mwachipiriro makaniwo adatiikira.” (Ahebri 12:1) Ngakhale kuti iwo tsopano aligone m’manda, kodi mboni zokhulupirika zachitsanzo chabwino zimenezi ziri zamoyo m’maganizo athu? Kodi mumazidziŵa izo mokwanira limodzi ndi zokumana nazo zawo kotero kuti mungakhoze kuyankha kuti inde? Iyi iri imodzi ya mphotho zochulukira za phunziro la Baibulo lokhazikika, kugwiritsira ntchito maganizo athu onse kukhalitsa ndi moyo zokumana nazo zosangalatsa za “mtambo wa mboni” umenewu. Zowonadi, kuphunzira zitsanzo zawo zokhulupirika kudzatithandiza ife mokulira kulaka kusoŵeka kwa chikhulupiriro kulikonse. Pambuyo pake, ichi chidzatithandiza kupereka umboni wolimba mtima ndi wopanda mantha wa chowonadi pansi pa mikhalidwe iriyonse.​—Aroma 15:4.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena