-
Kukoma Mtima Ndi Khalidwe Lofunika Kwambiri kwa MulunguNsanja ya Olonda—2012 | September 1
-
-
Popeza anthufe timatha kusonyeza khalidweli mwachibadwa komanso kuti Mulungu amaliona kukhala lofunika kwambiri, ndiye n’zomveka kuti Mulungu amatiuza kuti: “Khalani okomerana mtima.” (Aefeso 4:32) Komanso timakumbutsidwa kuti: “Musaiwale kuchereza alendo” kapena kuti anthu osawadziwa.—Aheberi 13:2.
-
-
Kukoma Mtima Ndi Khalidwe Lofunika Kwambiri kwa MulunguNsanja ya Olonda—2012 | September 1
-
-
N’zochititsa chidwi kuti mtumwi Paulo atanena za kufunika kokomera mtima alendo, anapitiriza kunena kuti: “Pakuti potero, ena anachereza angelo mosadziwa.” Kodi inuyo mungamve bwanji mutapatsidwa mwayi wochereza angelo? Taonani kuti Paulo anagwiritsira ntchito mawu akuti “mosadziwa.” M’mawu ena tinganene kuti mfundo yake inali yakuti ngati titamakomera mtima anthu ena, kuphatikizapo amene sitikuwadziwa, tikhoza kupeza madalitso amene mwina sitinkawayembekezera.
Mabaibulo ambiri amene ali ndi malifalensi amagwirizanitsa mawu a Paulo amenewa ndi nkhani zonena za Abulahamu ndi Loti zimene zikupezeka m’chaputala 18 ndi 19 m’buku la Genesis. M’nkhani zimenezi, timawerenga kuti angelo anaonekera kwa Abulahamu komanso kwa Loti monga alendo ndipo anabweretsa mauthenga ofunika kwambiri. Uthenga umene Abulahamu anauzidwa unali wonena za lonjezo la Mulungu lakuti Abulahamuyo adzakhala ndi mwana wamwamuna. Koma uthenga wopita kwa Loti unali wonena kuti adzapulumutsidwa pamene Sodomu ndi Gomora azidzawonongedwa.—Genesis 18:1-10; 19:1-3, 15-17.
Ngati mutawerenga malemba amene ali pamwambapa, muona kuti Abulahamu ndi Loti anakomera mtima anthu amene ankangodutsa m’njira omwe sankawadziwa n’komwe. M’nthawi ya Abulahamu anthu ankakonda kuchereza anthu apaulendo, kaya anthuwo anali anzawo, achibale, kapena osawadziwa. Chimenechi chinali chikhalidwe cha pa nthawi imeneyo. Ndipotu Chilamulo cha Mose chinkanena kuti Aisiraeli azisamaliranso anthu amene sanali amtundu wawo amene ankakhala m’dziko lawo. (Deuteronomo 10:17-19) Ngakhale zinali choncho, n’zodziwikiratu kuti Abulahamu ndi Loti anachita zinthu zambiri zimene zinaposa ngakhale zimene Chilamulo chomwe chinakhazikitsidwa pambuyo pake, chinkafuna. Iwo anakomera mtima alendo amene sankawadziwa, ndipo anadalitsidwa chifukwa chochita zimenezi.
Sikuti Abulahamu yekha ndi amene anapindula n’zimene anachitazi. Ifenso timapindula chifukwa cha kukoma mtima kwake. Motani? Abulahamu ndi mwana wake Isake anathandizira kuti cholinga cha Mulungu chikwaniritsidwe. Iwotu anali m’gulu la makolo a Yesu yemwe ndi Mesiya. Ndipotu kukhulupirika kwawo kunachitira chithunzi zimene Mulungu adzachita populumutsa anthu chifukwa cha chikondi komanso kukoma mtima kwake kwakukulu.—Genesis 22:1-18; Mateyu 1:1, 2; Yohane 3:16.
-