-
Kodi Baibulo Limanena Zotani pa Nkhani ya Kugonana?Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
-
-
PHUNZIRO 41
Kodi Baibulo Limanena Zotani pa Nkhani ya Kugonana?
Anthu ambiri amaona kuti nkhani zokhudza kugonana ndi zoumitsa pakamwa. Komabe, Baibulo likamanena zokhudza kugonana, limanena zinthu mosapita m’mbali, koma mwaulemu. Ndipo zimene limanena n’zothandiza kwambiri. Zimenezi ndi zomveka chifukwa Yehova ndi amene anatilenga. Choncho amadziwa bwino zimene zingatithandize kuti tizikhala ndi moyo wabwino. Iye amatiuza zimene tiyenera kuchita kuti tizimusangalatsa ndiponso zimene zingatithandize kuti tizisangalala ndi moyo kuyambira panopa mpaka kalekale.
1. Kodi maganizo a Yehova ndi otani pa nkhani ya kugonana?
Kugonana ndi mphatso yochokera kwa Yehova yomwe anapereka kwa anthu okwatirana kuti azisangalala nayo. Mphatsoyi simangothandiza anthu kuti azibereka ana basi, koma imawathandizanso kuti azisonyezana chikondi n’kumasangalala. N’chifukwa chake Mawu a Mulungu amati: “Uzisangalala ndi mkazi amene unamukwatira udakali wachinyamata.” (Miyambo 5:18, 19) Yehova amayembekezera kuti Akhristu okwatirana azikhala okhulupirika m’banja, ndipo zimenezi zimawathandiza kuti asachite chigololo.—Werengani Aheberi 13:4.
2. Kodi chiwerewere n’chiyani?
Baibulo limatiuza kuti “achiwerewere . . . sadzalowa mu Ufumu wa Mulungu.” (1 Akorinto 6:9, 10) Olemba Baibulo ena amene analilemba m’Chigiriki anagwiritsa ntchito mawu akuti por·neiʹa ponena za chiwerewere. Mawuwa amanena za (1) kugonanaa kwa anthu amene sali pabanja, (2) kugonana kwa amuna kapena akazi okhaokha, komanso (3) kugonana ndi nyama. Timasangalatsa Yehova komanso timakhala ndi moyo wabwino tikamayesetsa ‘kupewa chiwerewere.’—1 Atesalonika 4:3.
FUFUZANI MOZAMA
Onani zimene mungachite kuti mupewe chiwerewere komanso phindu limene mungapeze ngati mutayesetsa kukhalabe ndi makhalidwe oyera.
3. Muziyesetsa kupewa chiwerewere
Yosefe, yemwe anali munthu wokhulupirika, anakana kugonana ndi mzimayi yemwe ankamunyengerera kuti achite naye zachiwerewere. Werengani Genesis 39:1-12, kenako mukambirane mafunso awa:
N’chifukwa chiyani Yosefe anakana kuchita chiwerewere?—Onani vesi 9.
Kodi mukuganiza kuti Yosefe anachita zinthu mwanzeru? N’chifukwa chiyani mukutero?
Kodi masiku ano achinyamata angatsanzire bwanji Yosefe pa nkhani yokana kuchita chiwerewere? Onerani VIDIYO.
Yehova amafuna kuti tonsefe tiziyesetsa kupewa chiwerewere. Werengani 1 Akorinto 6:18, kenako mukambirane mafunso awa:
Kodi ndi zinthu ziti zimene zingapangitse munthu kuti achite chiwerewere?
Kodi mungatani kuti mupewe kuchita chiwerewere?
4. Yesetsani kuti musagonje pa mayesero
N’chiyani chingapangitse kuti munthu agonje mosavuta akamayesedwa kuti achite chiwerewere? Onerani VIDIYO, kenako mukambirane mafunso otsatirawa.
Kodi m’bale wamuvidiyoyi anachita chiyani atazindikira kuti zinthu zina zimene amaganiza ndi kuchita zikanachititsa kuti asiye kukhala wokhulupirika kwa mkazi wake?
Ngakhale Akhristu okhulupirika amafunika kuchita khama kuti asamaganizire zinthu zoipa. Kodi mungatani kuti musamaganizire zinthu zachiwerewere? Werengani Afilipi 4:8, kenako mukambirane mafunso awa:
Kodi ndi zinthu ziti zimene tiyenera kumaziganizira?
Kodi kuwerenga Baibulo komanso kukhala ndi zochita zambiri potumikira Yehova kungatithandize bwanji kuti tipewe mayesero?
5. Mfundo za Yehova zimatithandiza kukhala ndi moyo wabwino
Yehova amafuna kuti zinthu zizitiyendera bwino. Iye amatiuza zimene tingachite kuti tikhale ndi makhalidwe oyera komanso ubwino wochita zimenezi. Werengani Miyambo 7:7-27 kapena onerani VIDIYO, kenako mukambirane mafunso otsatirawa.
Kodi mnyamatayu anachita chiyani chimene chinamulowetsa m’mayesero?—Onani Miyambo 7:8, 9.
Lemba la Miyambo 7:23, 26, limasonyeza kuti kuchita chiwerewere kukhoza kutibweretsera mavuto aakulu. Ndiye kodi tingapewe mavuto ati tikamayesetsa kukhala ndi makhalidwe oyera?
Kodi kukhala ndi makhalidwe oyera kungatithandize bwanji kuti tizisangalala ndi moyo mpaka kalekale?
Anthu ena amaona kuti zimene Baibulo limanena pa nkhani ya kugonana kwa amuna komanso akazi okhaokha, ndi kukhwimitsa zinthu. Koma zimenezi si zoona chifukwa Yehova amatikonda ndipo amafuna kuti tonse tizisangalala ndi moyo mpaka kalekale. Kuti zimenezi zitheke, tiziyesetsa kutsatira mfundo zake. Werengani 1 Akorinto 6:9-11, kenako mukambirane funso ili:
Kodi kugonana kwa amuna kapena akazi okhaokha ndi khalidwe lokhalo limene Mulungu amadana nalo?
Kuti tizisangalatsa Mulungu, tonsefe tiyenera kuyesetsa kusintha moyo wathu. Kodi kuchita zimenezi n’kothandizadi? Werengani Salimo 19:8, 11, kenako mukambirane mafunso awa:
Kodi Yehova anachita bwino kutipatsa mfundo zamakhalidwe abwino kapena anangokhwimitsa zinthu? N’chifukwa chiyani mukutero?
Yehova wathandiza anthu ambiri kuti asiye makhalidwe oipa. Inunso angakuthandizeni
ANTHU ENA AMANENA KUTI: “Palibe vuto kugonana ndi wina aliyense amene ukufuna, bola ngati mukukondana.”
Kodi inuyo mungamuthandize bwanji munthu wotereyu?
ZOMWE TAPHUNZIRA
Kugonana ndi mphatso yochokera kwa Yehova ndipo imathandiza kuti mwamuna ndi mkazi wake azisangalala.
Kubwereza
Kodi kuchita chiwerewere kumaphatikizaponso kuchita zinthu ziti?
N’chiyani chingatithandize kuti tipewe kuchita chiwerewere?
Kodi timapindula bwanji tikamatsatira mfundo za Yehova zamakhalidwe abwino?
ONANI ZINANSO
Onani chifukwa chake Yehova amafuna kuti mwamuna ndi mkazi azikwatirana kaye asanayambe kukhala limodzi.
Baibulo limaphunzitsa kuti kugonana kwa amuna kapena akazi okhaokha n’kulakwa, koma silitanthauza kuti tizidana ndi anthu amene amachita zimenezi. Onani chifukwa chake tikutero.
“Kodi Kugonana Kwa Amuna Kapena Akazi Okhaokha N’kolakwika?” (Nkhani yapawebusaiti)
Onani mmene malamulo a Mulungu pa nkhani zokhudza kugonana amatitetezera.
“Kodi Kugonana M’kamwa Kumakhaladi Kugonana?” (Nkhani yapawebusaiti)
Munkhani yakuti, “Anandilandira Mwaulemu Kwambiri,” onani zimene zinathandiza munthu wina kusiya khalidwe logonana ndi amuna anzake n’cholinga choti azisangalatsa Mulungu.
“Baibulo Limasintha Anthu” (Nsanja ya Olonda, April 1, 2011)
a Zimenezi zikuphatikizapo kuchita zinthu monga chiwerewere, kugonana m’kamwa, kugonana kobibira komanso kuseweretsa maliseche a munthu wina ndi cholinga chofuna kudzutsa kapena kukhutiritsa chilakolako cha kugonana.
-
-
Kodi Baibulo Limanena Zotani pa Nkhani Yokhala Pabanja Ndi Kusakhala Pabanja?Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
-
-
PHUNZIRO 42
Kodi Baibulo Limanena Zotani pa Nkhani Yokhala Pabanja Ndi Kusakhala Pabanja?
Anthu azikhalidwe zina amakhulupirira kuti munthu sangakhale wosangalala pokhapokha akhale pabanja. Komabe, si anthu onse omwe ali pabanja amene amasangalala. Komanso si anthu onse amene sali pabanja amene sasangalala. Baibulo limanena kuti kukhala pabanja komanso kusakhala pabanja, zonse ndi mphatso zochokera kwa Yehova.
1. Kodi kusakhala pabanja kuli ndi ubwino wotani?
Baibulo limati: “Amenenso wasiyana ndi moyo wokhala yekha n’kulowa m’banja wachita bwino, koma amene sanalowe m’banja wachita bwino kwambiri.” (Werengani 1 Akorinto 7:32, 33, 38.) N’chifukwa chiyani tinganene kuti munthu amene wasankha kusakhala pabanja “wachita bwino kwambiri”? Popeza kuti Mkhristu amene sali pabanja sakhala ndi udindo wosamalira mwamuna kapena mkazi wake, iye amakhala ndi ufulu wambiri. Anthu amene sali pabanja akhoza kuwonjezera utumiki wawo m’njira zambiri. Mwachitsanzo, angapite kudziko lina kuti akalalikire uthenga wabwino. Komanso chofunika kwambiri, amakhala ndi nthawi yambiri yolimbitsa ubwenzi wawo ndi Yehova.
2. Kodi kupanga ukwati wovomerezeka ndi boma kuli ndi ubwino wotani?
Mofanana ndi kusakhala pabanja, kukhala pabanja nakonso kuli ndi ubwino wake. Baibulo limanena kuti “awiri amaposa mmodzi.” (Mlaliki 4:9) Zimenezi ndi zimene zimachitika kwa Akhristu amene amatsatira mfundo za m’Baibulo m’banja mwawo. Anthu amene amapanga ukwati wovomerezeka ndi boma, amalonjeza kuti azikonda ndi kulemekeza mnzawoyo komanso kumuona kuti ndi wofunika kwambiri. Anthu amene ali m’banja lovomerezeka ndi boma amaona kuti ndi otetezeka kwambiri kusiyana ndi anthu amene amangotengana n’kumakhala limodzi. Ubwino winanso ndi wakuti ana amene abadwira m’banja limene makolo awo anapanga ukwati wovomerezeka ndi boma amakhala otetezeka.
3. Kodi maganizo a Yehova ndi otani pa nkhani ya banja?
Pamene Yehova ankayambitsa banja ananena kuti: “Mwamuna adzasiya bambo ake ndi mayi ake, n’kudziphatika kwa mkazi wake.” (Genesis 2:24) Yehova amafuna kuti mwamuna ndi mkazi amene akwatirana azikondana n’kumakhala limodzi kwa moyo wawo wonse. Iye amalola munthu kuti athetse banja pokhapokha ngati mnzake wachita chigololo. Zikatere, Yehova amapereka mwayi kwa munthu wosalakwayo kuti asankhe kuthetsa banja kapena ayi.a (Mateyu 19:9) Yehova safuna kuti Akhristu azikhala pa mitala.—1 Timoteyo 3:2.
FUFUZANI MOZAMA
Onani zimene mungachite kuti muzisangalala komanso kusangalatsa Yehova kaya muli pabanja kapena ayi.
4. Muzigwiritsa ntchito bwino mphatso ya kusakhala pabanja
Yesu ankaona kuti kusakhala pabanja ndi mphatso. (Mateyu 19:11, 12) Werengani Mateyu 4:23, kenako mukambirane funso ili:
Kodi Yesu anagwiritsa ntchito bwanji mphatso ya kusakhala pabanja potumikira Atate ake komanso kuthandiza anthu ena?
Akhristu akhoza kumasangalala pogwiritsa ntchito mphatso yawo ya kusakhala pabanja ngati mmene Yesu ankachitira. Onerani VIDIYO, kenako mukambirane funso ili:
Kodi Akhristu angagwiritse ntchito bwanji mphatso yawo ya kusakhala pabanja?
Kodi mukudziwa?
Baibulo silinena kuti munthu ayenera kukwatira kapena kukwatiwa ali ndi zaka zingati. Komabe, limalimbikitsa kuti munthu ayenera kudikira mpaka ‘atapitirira pachimake pa unyamata.’ Pa nthawi imeneyi, wachinyamata amakhala ndi chilakolako champhamvu kwambiri cha kugonana zomwe zingachititse kuti alephere kusankha zinthu moyenera.—1 Akorinto 7:36.
5. Sankhani mwanzeru munthu amene mukufuna kukwatirana naye
Kusankha munthu yemwe mukufuna kukwatirana naye ndi nkhani yaikulu. Werengani Mateyu 19:4-6, 9, kenako mukambirane funso ili:
N’chifukwa chiyani Mkhristu sayenera kuthamangira kulowa m’banja?
Baibulo lingakuthandizeni kuti musankhe bwino munthu yemwe mungakhale naye pabanja. Koma chofunika kwambiri ndi kusankha munthu yemwe amakonda Yehova.b Werengani 1 Akorinto 7:39 ndi 2 Akorinto 6:14. Kenako mukambirane mafunso awa:
N’chifukwa chiyani Mkhristu ayenera kukwatirana ndi Mkhristu mnzake?
Kodi mukuganiza kuti Yehova angamve bwanji ngati Mkhristu atakwatirana ndi munthu yemwe samutumikira?
Nyama zomwe ndi zosiyana zikamangidwa limodzi pagoli zingavutike kuchitira zinthu limodzi. Mofanana ndi zimenezi, Mkhristu amene wakwatirana ndi munthu wosakhulupirira angakumane ndi mavuto ambiri
6. Muziona ukwati mmene Yehova amauonera
Kale ku Isiraeli, amuna ena ankasiya akazi awo pa zifukwa zosamveka. Werengani Malaki 2:13, 14, 16, kenako mukambirane funso ili:
N’chifukwa chiyani Yehova amadana ndi kuthetsa banja pa zifukwa zosagwirizana ndi mfundo za m’Baibulo?
Wina akachita chigololo kapenanso banja likatha zimabweretsa mavuto kwa munthu amene sanalakweyo komanso ana
Onerani VIDIYO, kenako mukambirane funso lotsatirali.
Ngati munakwatirana ndi munthu yemwe satumikira Yehova, kodi mungatani kuti banja lanu liziyenda bwino?
7. Muzigwiritsa ntchito mfundo za Yehova zokhudza ukwati
Munthu angafunike kuchita khama kuti azigwiritsa ntchito mfundo za Yehova zokhudza ukwati.c Komabe Yehova amadalitsa anthu amene amayesetsa kuchita zimenezi. Onerani VIDIYO.
Werengani Aheberi 13:4, kenako mukambirane mafunso awa:
Kodi inuyo mukuona kuti mungakwanitse kutsatira mfundo zokhudza banja zimene Yehova anatipatsa? N’chifukwa chiyani mukutero?
Yehova amafuna kuti Akhristu amene akufuna kukwatirana azikalembetsa ukwati wawo kuboma komanso Akhristu amene akufuna kuthetsa banja, azikatenga chikalata chothetsera ukwati kuboma. Chifukwa zimenezi ndi zimene maboma amafuna kuti nzika zawo zizichita. Werengani Tito 3:1, kenako mukambirane funso ili:
Ngati muli pabanja, kodi munalembetsa ukwati wanu kuboma?
MUNTHU WINA ATAKUFUNSANI KUTI: “Kodi pali chifukwa chokalembetsera ukwati wanga kuboma? Si bola ngati tikukondana basi?”
Kodi munthu wotereyu mungamuyankhe bwanji?
ZOMWE TAPHUNZIRA
Kukhala pabanja kapena kusakhala pabanja, zonse ndi mphatso zochokera kwa Yehova. Zonse zingathandize munthu amene akuchita zimene Yehova amafuna kukhala wosangalala.
Kubwereza
Kodi munthu angatani kuti azigwiritsa ntchito bwino mphatso yake ya kusakhala pabanja?
N’chifukwa chiyani Baibulo limanena kuti Mkhristu azikwatirana ndi Mkhristu mnzake?
Kodi Baibulo limanena kuti munthu akhoza kuthetsa banja pa chifukwa chiti?
ONANI ZINANSO
Kodi kukwatira kapena kukwatiwa “mwa Ambuye” kumatanthauza chiyani?
“Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga” (Nsanja ya Olonda, July 1, 2004)
“Onerani vidiyo ya mbali ziwiri yomwe ingakuthandizeni kusankha zochita mwanzeru pa nkhani zokhudza chibwenzi komanso kukhala pabanja.
Onani chifukwa chake m’bale wina amaona kuti zimene Yehova wamupatsa ndi zamtengo wapatali kwambiri kuposa zinthu zonse zimene anasiya.
Ndinkakhulupirira Kuti Nayenso Akhoza Kuphunzira Choonadi 1:56
Kodi munthu ayenera kuganizira mfundo ziti akamafuna kupatukana kapena kuthetsa ukwati?
“Tizilemekeza ‘Chimene Mulungu Wachimanga Pamodzi’” (Nsanja ya Olonda, December 2018)
a Onani Mawu Akumapeto 4, pa nkhani ya kupatukana ngati wina sanachite chigololo.
b M’zikhalidwe zina, makolo amatha kusankhira mwana wawo munthu woti adzakwatirane naye. M’zikhalidwe zoterozo, makolo achikondi amaganizira zosankha munthu amene amakonda Yehova osati chuma chimene munthuyo ali nacho.
c Ngati mukukhala ndi munthu amene simunakwatirane naye, zili ndi inu kusankha kumusiya kapena kukwatirana naye.
-