-
“Kumbukirani Amene Akutsogolera Pakati Panu”Gulu Lochita Chifuniro cha Mulungu
-
-
N’CHIFUKWA CHIYANI TIYENERA ‘KUKUMBUKIRA AMENE AKUTSOGOLERA PAKATI PATHU’?
9 Pali zifukwa zambiri zotichititsa ‘kukumbukira amene akutsogolera pakati pathu’ ndiponso kusonyeza kuti timawakhulupirira. N’chifukwa chiyani kuchita zimenezi n’kothandiza? Mtumwi Paulo ananena kuti: “Iwo amayang’anira miyoyo yanu monga anthu amene adzayankhe mlandu. Muziwamvera ndi kuwagonjera kuti agwire ntchito yawo mwachimwemwe, osati modandaula, pakuti akatero zingakhale zokuvulazani.” (Aheb. 13:17) Choncho tiyenera kumvera ndi kugonjera malangizo a anthu amene akutitsogolera chifukwa amatiyang’anira kuti tikhale otetezeka komanso kuti zinthu zizitiyendera bwino mwauzimu.
10 Palemba la 1 Akorinto 16:14, Paulo anati: “Zonse zimene mukuchita, muzichite mwachikondi.” Choncho, zilizonse zimene abale amene amatitsogolera amasankha kuti tizitsatira, amazichita chifukwa cha khalidwe lapadera limeneli la chikondi. Lemba la 1 Akorinto 13:4-8 limanena kuti: “Chikondi n’choleza mtima ndiponso n’chokoma mtima. Chikondi sichichita nsanje, sichidzitama, sichidzikuza, sichichita zosayenera, sichisamala zofuna zake zokha, sichikwiya. Sichisunga zifukwa. Sichikondwera ndi zosalungama, koma chimakondwera ndi choonadi. Chimakwirira zinthu zonse, chimakhulupirira zinthu zonse, chimayembekezera zinthu zonse, chimapirira zinthu zonse. Chikondi sichitha.” Popeza anthu amene amatitsogolera amatikonda ndipo amasankha zinthu zonse n’cholinga choti zitiyendere bwino, sitikayikira kuti kutsatira malangizo amene amatipatsa n’kothandiza kwambiri. Zimene abalewa amachita zimasonyezanso kuti Yehova amatikonda.
Kumvera anthu amene amatiyang’anira n’kofunika kwambiri kuti zinthu zitiyendere bwino mwauzimu
11 Mofanana ndi mmene zinalili m’nthawi ya atumwi, anthu amene Yehova akuwagwiritsa ntchito potsogolera anthu ake ndi opanda ungwiro. Komabe Yehova wakhala akugwiritsa ntchito anthu opanda ungwiro kuti akwaniritse cholinga chake. Mwachitsanzo, Nowa anamanga chingalawa komanso analalikira zoti Mulungu akufuna kuwononga anthu oipa. (Gen. 6:13, 14, 22; 2 Pet. 2:5) Mose anasankhidwa kuti atsogolere anthu a Mulungu kutuluka ku Iguputo. (Eks. 3:10) Ndiponso Mulungu anagwiritsa ntchito anthu opanda ungwiro kuti alembe Baibulo. (2 Tim. 3:16; 2 Pet. 1:21) Choncho, timakhulupirirabe gulu la Mulungu ngakhale kuti Yehova akugwiritsa ntchito anthu opanda ungwiro kuti azitsogolera ntchito yolalikira ndi kuphunzitsa anthu. Timachita zimenezi chifukwa timadziwa kuti gululi silingakwanitse kuchita zimene limachita popanda kuthandizidwa ndi Yehova. Kapolo wasonyeza kuti amatsogoleredwa ndi mzimu wa Mulungu chifukwa chopirira mavuto amene wakhala akukumana nawo. Yehova wadalitsa kwambiri mbali ya padziko lapansi ya gulu lake, choncho tiyenera kuchita zinthu mogwirizana ndi gululi komanso kulikhulupirira ndi mtima wonse.
-
-
“Kumbukirani Amene Akutsogolera Pakati Panu”Gulu Lochita Chifuniro cha Mulungu
-
-
14 Njira ina imene timasonyezera kuti timakhulupirira kapolo ndi kugwirizana ndi zimene wasankha. Zimenezi zikuphatikizapo kumvera modzichepetsa malangizo omwe timapatsidwa ndi abale amene ali ndi udindo woyang’anira, monga oyang’anira madera komanso akulu mumpingo. Abale amenewa ali m’gulu la anthu ‘amene amatitsogolera,’ omwe tiyenera kuwamvera ndi kuwagonjera. (Aheb. 13:7, 17) Ngakhale kuti sitingamvetse zifukwa zimene asankhira kuchita zinazake, koma tiyenera kumverabe chifukwa timadziwa kuti tikamawamvera zinthu zidzatiyendera bwino. Ndipo Yehova amatidalitsa chifukwa chomvera Mawu ake komanso gulu lake. Timasonyezanso kuti timagonjera Ambuye wathu, Yesu Khristu.
-