Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w96 5/1 tsamba 21-24
  • Sungani Chidaliro Chanu Chili Cholimba Kufikira Mapeto

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Sungani Chidaliro Chanu Chili Cholimba Kufikira Mapeto
  • Nsanja ya Olonda—1996
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Sonyezani Chikhulupiriro Chanu
  • Kukulitsa Chidaliro mwa Kukhala Wozoloŵera
  • Mayanjano Angatitayitse Njira
  • Chinyengo cha Chuma
  • Chikhulupiriro Chimadalira Pamtima Wotseguka
  • Kuyang’ana kwa Mulungu wa Chipulumutso Chathu
  • Kodi Mumakhulupiriradi Uthenga Wabwino?
    Nsanja ya Olonda—2003
  • Muzisonyeza Kuti Mumakhulupirira Malonjezo a Yehova
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2016
  • “Tiwonjezereni Chikhulupiriro”
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
  • Labadirani Malonjezo a Mulungu mwa Kusonyeza Chikhulupiriro
    Nsanja ya Olonda—1993
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1996
w96 5/1 tsamba 21-24

Sungani Chidaliro Chanu Chili Cholimba Kufikira Mapeto

TALINGALIRANI za ndege yaing’ono imene ili kuuluka m’mphepo yovuta. Woyendetsa wake satha kuonanso zizindikiro pansi. Wakutidwa ndi mitambo yochindikala. Satha kuona zakunja, komabe akumva kukhala wotsimikizira kuti angamalize bwino ulendo wake. Kodi nchifukwa ninji ali ndi chidaliro chotero?

Ali ndi ziŵiya zolongosoka zimene zimamtheketsa kuuluka m’mitambo ndi kutera mumdima. Pamene ali paulendo wake, makamaka pafupi ndi bwalo la ndege, zizindikiro zamagetsi zapawailesi zimamtsogolera, ndipo amalankhula pawailesi ndi olangiza olamulira kayendedwe ka ndege amene amakhala pansi.

Mwa njira yofananayo, tingayang’ane mtsogolo ndi chidaliro, ngakhale kuti mikhalidwe yadziko ikuvundiravundirabe tsiku lililonse. Ulendo wathu wopyola m’dongosolo lino loipa ungaoneke kukhala wautali kuposa ndi mmene ena anaganizira, koma tingakhale ndi chidaliro chakuti tili panjira yake ndipo tikuyenda ndi nthaŵi yake. Nchifukwa ninji tingakhalire otsimikiza motero? Chifukwa chakuti tili ndi chitsogozo chimene chimatitheketsa kuona zimene munthu sangaone.

Mawu a Mulungu ali ‘kuunika kwa panjira pathu,’ ndipo ali ‘okhazikika, akuwapatsa opusa nzeru.’ (Salmo 19:7; 119:105) Monga zizindikiro zapawailesi zimene zimaonetsa woyendetsa ndege mmene ayenera kupita, Baibulo limafotokoza mosaphonya zochitika zamtsogolo ndipo limatipatsa malangizo omvekera bwino potsimikizira kuti tifike bwino kumene tikupita. Komabe, kuti tipindule ndi chitsogozo chaumulungu, tiyenera kuchidalira.

M’kalata yake kwa Ahebri, Paulo analimbikitsa Akristu achiyuda ‘kugwiritsa chiyambi cha kutama kwawo kuchigwira kufikira chitsiriziro.’ (Ahebri 3:14) Chidaliro chingagwedere ngati ‘sichigwiritsidwa’ mmene tikuchigwirira. Motero funso likubuka, Kodi ndi motani mmene tingachititsire chidaliro chathu mwa Yehova kukhala cholimba kufikira mapeto?

Sonyezani Chikhulupiriro Chanu

Woyendetsa ndege asanayambe kuyendetsa mosagwiritsira ntchito maso ake, akumadalira kokha pa ziŵiya zake ndi omlangiza amene ali pansi, amafunikira kuphunzira mokwana ndi kuuluka kwa maola ambiri. Mofananamo, Mkristu ayenera kusonyeza chikhulupiriro chake nthaŵi zonse kotero kuti asungebe chidaliro chake pa chitsogozo cha Yehova, makamaka pamene mavuto abuka. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Pokhala nawo mzimu womwewo wa chikhulupiriro, monga mwa cholembedwacho, ndinakhulupira, chifukwa chake ndinalankhula; ifenso tikhulupira, chifukwa chake tilankhula.” (2 Akorinto 4:13) Motero pamene tilankhula za uthenga wabwino wa Mulungu, tikusonyeza ndi kulimbitsa chikhulupiriro chathu.

Magdalena, amene anathera zaka zinayi m’ndende yachibalo m’nkhondo yachiŵiri yadziko, akufotokoza kufunika kwa ntchito yolalikira: “Amayi anandiphunzitsa kuti ngati ukufuna kusungabe chikhulupiriro cholimba, nkofunika kudera nkhaŵa za mkhalidwe wauzimu wa ena. Ndikukumbukira chochitika china chimene chimasonyeza mmene tinalingalirira. Tinamasulidwa kundende yachibalo ya Ravensbrück, ineyo ndi amayi tinafika kunyumba pa Lachisanu. Masiku aŵiri pambuyo pake, pa Sande, tinagwirizana ndi abale mu ulaliki wa kunyumba ndi nyumba. Ndimakhulupiriradi kuti ngati tisumika maganizo pakuthandiza ena kudalira malonjezo a Mulungu, malonjezo amenewowo amakhalanso enieni kwambiri kwa ife.”​—Yerekezerani ndi Machitidwe 5:42.

Kusunga chidaliro chathu chili cholimba kufikira mapeto kumafuna ntchito yauzimu m’mbali zina. Phunziro laumwini lili mbali ina yabwino kwambiri yolimbitsa chikhulupiriro. Ngati titsanzira Abereya ndi kusanthula Malemba mwakhama tsiku ndi tsiku, zidzatithandiza ‘kulinga ku chiyembekezo chokwanira kufikira chitsiriziro.’ (Ahebri 6:11; Machitidwe 17:11) Zoona, phunziro laumwini limafuna nthaŵi ndi kutsimikiza mtima. Mwachionekere, nchifukwa chake Paulo anachenjeza Ahebri za ngozi ya kukhala “aulesi,” kapena amphwayi, m’nkhani zotere.​—Ahebri 6:12.

Malingaliro amphwayi angakhale ndi zotulukapo zoipa m’mbali zambiri zamoyo. Solomo ananena kuti “nyumba idontha ndi ulesi wa manja.” (Mlaliki 10:18) Posakhalitsa denga losafoleredwa bwino limayamba kudontha. Ngati tichita ulesi mwauzimu ndi kulephera kusungabe chikhulupiriro chathu, zikayikiro zimaloŵa mwakachetechete. Mosiyana ndi zimenezo, kusinkhasinkha nthaŵi zonse ndi kuphunzira Mawu a Mulungu kudzalimbitsa ndi kutetezera chikhulupiriro chathu.​—Salmo 1:2, 3.

Kukulitsa Chidaliro mwa Kukhala Wozoloŵera

Zoonadi, woyendetsa ndege amadziŵa mwa kuzoloŵera ndiponso mwa kupenda ngati ziŵiya zake zili zodalirika. Momwemonso, chidaliro chathu mwa Yehova chimakula pamene ifeyo m’moyo wathu tiona umboni wachisamaliro chake chachikondi. Zimenezo zinamchitikirapo Yoswa, ndipo anakumbutsa Aisrayeli anzake kuti: “Mudziŵa m’mitima yanu yonse, ndi m’moyo mwa inu nonse, kuti pamawu okoma onse Yehova Mulungu wanu anawanena za inu sanagwa padera mawu amodzi; onse anachitikira inu.”​—Yoswa 23:14.

Josefina, mlongo wokwatiwa wa ku Philippines, anaphunzira phunziro limodzimodzilo. Akufotokoza mmene moyo unalili asanadziŵe choonadi kuti: “Mwamuna wanga anali kumwa kwambiri, ndipo ataledzera, ankakwiya ndi kundimenya. Ukwati wathu wopanda chimwemwe unali kuyambukiranso mwana wathu wamwamuna. Ineyo ndi mwamuna wanga tinali kugwira ntchito, tikumalandira ndalama zambiri, koma zambiri za izo tinazithera pa kutchova juga. Mwamuna wanga anali ndi mabwenzi ambiri, komabe ambiri a iwo ankafuna kuchita naye ubwenzi kuti awagulire moŵa, ndipo ena ankamledzeretsadi kungoti amseke.

“Zinthu zinasintha pamene tinadzadziŵa Yehova ndi kumvetseradi uphungu wake. Mwamuna wanga sakumwanso, tinaleka kutchova juga, ndipo tili ndi mabwenzi oona amene amatikonda ndi kutithandiza. Ukwati wathu ngwachimwemwe, ndipo mwana wathu wamwamuna akukula kukhala mnyamata wabwino. Timagwira ntchito kwa maola ochepa, koma tili ndi ndalama zambiri. Zochitika zatiphunzitsa kuti Yehova ali ngati Atate wachikondi, amene amatipatsa chitsogozo choyenera nthaŵi zonse.”

Chifukwa cha malangizo apawailesi kapena mwa kuyang’ana pa chiŵiya choonerapo, nthaŵi zina oyendetsa ndege amadziŵa kuti ayenera kuwongolera njira yawo. Momwemonso tingafunikire kusintha njira malinga ndi malangizo a Yehova. “Makutu ako adzamva mawu kumbuyo kwa iwe akuti, Njira ndi iyi, yendani inu mmenemo: potembenukira inu kulamanja, ndi potembenukira inu kulamanzere.” (Yesaya 30:21) Mwa Mawu ake ndi mwa gulu lake, timalandira uphungu wotichenjeza za ngozi zauzimu. Imodzi ya zimenezi imakhudza mayanjano.

Mayanjano Angatitayitse Njira

Ndege yaing’ono ingatayike pa njira yake mosavuta ngati kuwongolera kofunika sikupangidwa. Momwemonso, chisonkhezero cha ena chimawomba pa Akristu nthaŵi zonse lerolino. Tikukhala m’dziko lokondetsa zinthu zakuthupi mmene ambiri amanyoza mkhalidwe wauzimu, akumaona ndalama ndi kusanguluka kukhala zofunika kwambiri. Paulo anachenjeza Timoteo kuti masiku otsiriza adzakhala “oŵaŵitsa.” (2 Timoteo 3:1-5) Achichepere, amene amafunitsitsa kulandiridwa ndi anzawo ndi kutchuka, ndiwo makamaka amakhala pangozi ya mayanjano oipa.​—2 Timoteo 2:22.

Amanda, wazaka 17, akufotokoza kuti: “Kwakanthaŵi anzanga am’kalasi anafooketsa chikhulupiriro changa pamlingo wakutiwakuti. Nthaŵi zonse ankanena kuti chipembedzo changa chinali cholanda ufulu ndipo chosalolera, ndipo zimenezi zinayamba kundilefula. Komabe, makolo anga anandithandiza kumvetsetsa kuti zitsogozo zachikristu zimatetezera m’malo molanda ufulu. Tsopano ndazindikira kuti mapulinsipulo ameneŵa akundithandiza kukhala ndi moyo wokhutiritsa kwambiri kuposa uja wa amene kale anali anzanga akusukulu. Ndaphunzira kudalira amene amandisamaliradi​—makolo anga ndi Yehova​—ndipo ndikusangalala ndi utumiki waupainiya.”

Kaya ndife amsinkhu wanji, tidzakumana ndi anthu amene amanyoza zikhulupiriro zathu. Angaoneke kukhala ngati odziŵa zinthu, koma kwa Mulungu ngachibadwidwe, opanda mkhalidwe wauzimu. (1 Akorinto 2:14) Gulu losonkhezera ku Korinto wa m’nthaŵi ya Paulo linali la a Skepitiki anzeru za kudziko. Ziphunzitso za a filosofi ameneŵa mwachionekere zinachititsanso Akristu ena a ku Korinto kutaya chikhulupiriro m’chiyembekezo chachiukiriro. (1 Corinthians 15:12) “Musanyengedwe,” anachenjeza motero mtumwi Paulo. “Mayanjano oipa aipsa makhalidwe okoma.”​—1 Akorinto 15:33.

Kumbali ina, mayanjano abwino amatilimbitsa mwauzimu. Mumpingo wachikristu, tili ndi mwaŵi wa kuyanjana ndi anthu amene ali ndi moyo wachikhulupiriro. Norman, mbale amene anaphunzira choonadi mu 1939, adakali wolimbikitsa kwambiri kwa onse. Kodi nchiyani chimene chasungabe maso ake auzimu kukhala akuthwa? “Misonkhano ndi maubwenzi athithithi ndi abale okhulupirika nzofunika kwambiri,” akuyankha motero. “Mtundu wa mayanjano umenewu wandithandiza kuona bwinobwino kusiyana pakati pa gulu la Mulungu ndi la Satana.”

Chinyengo cha Chuma

Brian, woyendetsa ndege wachidziŵitso, akufotokoza kuti “nthaŵi zina woyendetsa ndege angaone kukhala kovuta kukhulupirira ziŵiya zake​—chabe chifukwa chakuti nzeru zake zachibadwa sizikuvomereza. Oyendetsa ndege zankhondo ena achidziŵitso auluka chagada chifukwa chakuti magetsi apansi amaoneka ngati nyenyezi​—ngakhale kuti ziŵiya zawo sizinawauze zimenezo.”

Mofananamo, nzeru zathu zachibadwa zadyera zingatisokeretse m’lingaliro lauzimu. Yesu ananena kuti chuma chili ndi “chinyengo,” ndipo Paulo anachenjeza kuti ‘chikondi cha pa ndalama chatayitsa ambiri chikhulupiriro.’​—Marko 4:19; 1 Timoteo 6:10.

Monga magetsi onyenga onyezimira, zonulirapo zakuthupi zoonekera bwino zingatisonyeze njira yolakwika. M’malo mosangalala ndi “zinthu zoyembekezeka,” tingakopedwe ndi matamandidwe a dziko limene likupita. (Ahebri 11:1; 1 Yohane 2:16, 17) Ngati tili “otsimikiza mtima” kukhala ndi moyo wapamwamba, mwachionekere tidzakhala ndi nthaŵi yochepa ya kukula kwauzimu.​—1 Timoteo 6:9, NW; Mateyu 6:24; Ahebri 13:5.

Mnyamata wina wokwatira wotchedwa Patrick anavomereza kuti iyeyo ndi mkazi wake anakana zonulirapo zauzimu kaamba ka kukhala ndi moyo wabwinopo. Akufotokoza kuti: “Tinasonkhezeredwa ndi aja a mumpingo a galimoto zodula ndi nyumba zapamwamba. Ngakhale kuti sitinataye chiyembekezo cha Ufumu, tinalingalira kuti tingakhalenso ndi moyo wabwino panthaŵi ino. Komabe, m’kupita kwanthaŵi tinazindikira kuti chimwemwe chenicheni chimadza mwa kutumikira Yehova ndi mwa kukula mwauzimu. Tsopano moyo wathu siwapamwambanso. Tachepetsa maola athu antchito, ndipo takhala apainiya okhazikika.”

Chikhulupiriro Chimadalira Pamtima Wotseguka

Mtima wotseguka ulinso ndi mbali yofunika pa kukulitsa chidaliro mwa Yehova. Zoona, “chikhulupiriro ndicho chikhazikitso cha zinthu zoyembekezeka, chiyesero [kapena, “umboni wokhutiritsa,” NW, mawu amtsinde] cha zinthu zosapenyeka.” (Ahebri 11:1) Koma mwachionekere sitingakhutiritsidwe pokhapokhapo titakhala ndi mtima wotseguka. (Miyambo 18:15; Mateyu 5:6) Pa chifukwa chimenechi mtumwi Paulo anati “si onse ali nacho chikhulupiriro.”​—2 Atesalonika 3:2.

Motero, kodi ndi motani mmene tingachititsire mitima yathu kuvomereza maumboni okhutiritsa onse amene alipo? Mwa kukulitsa mikhalidwe yaumulungu, mikhalidwe imene imalemeretsa ndi kusonkhezera chikhulupiriro. Petro akutilimbikitsa kuti ‘pachikhulupiriro chathu tiwonjezerepo ukoma, chizindikiritso, chodziletsa, chipiriro, chipembedzo, chikondi cha pa abale, ndi chikondi.’ (2 Petro 1:5-7; Agalatiya 5:22, 23) Kumbali ina, ngati tili ndi moyo wokonda za ife eni kapena kupatsa Yehova utumiki wochepa, moyenera sitingayembekezere chikhulupiriro chathu kukula.

Ezara “adaikiratu mtima wake” kuŵerenga Mawu a Yehova ndi kuwachita. (Ezara 7:10) Momwemonso Mika anali ndi mtima wotseguka. “Koma ine, ndidzadikira Yehova; ndidzalindirira Mulungu wa chipulumutso changa; Mulungu wanga adzandimvera.”​—Mika 7:7.

Magdalena, wogwidwa mawu pachiyambi, amalindiriranso Yehova modekha. (Habakuku 2:3) Iye akuti: “Tili kale ndi paradaiso wauzimu. Sitepe lachiŵiri, Paradaiso wakuthupi, adzadza posachedwapa. Pakali pano anthu zikwi mazana ambiri akugwirizana ndi khamu lalikulu. Zimandisangalatsa kuona ochuluka motero alinkudza kugulu la Mulungu.”

Kuyang’ana kwa Mulungu wa Chipulumutso Chathu

Kusunga chidaliro chathu chili cholimba kufikira mapeto kumafuna kusonyeza chikhulupiriro chathu ndi kumvetsera mosamalitsa ku chitsogozo chimene timalandira kuchokera kwa Yehova ndi gulu lake. Iko nkoyenereradi kumenyera nkhondo. Woyendetsa ndege amakhala ndi chikhutiro chachikulu pamene atsika ndi kutuluka mumtambo wochindikalawo pomalizira pake, pambuyo pa ulendo wautali ndi wovuta. Patsogolo pakepo pamakhala dziko lapansi​—lobiriŵira ndipo likumlandira. Njira ya ndege pabwalo la ndege imaoneka munsi, ikumyembekezera kumlandira.

Ifenso tikuyembekezera chokumana nacho chokondweretsa. Dziko lovunda ndi loipali lidzaloŵedwa m’malo ndi dziko lapansi latsopano lachilungamo. Mulungu akuyembekezera kutilandira. Tingafike kumeneko ngati tilabadira mawu a wamasalmo akuti: “Inu ndinu chiyembekezo changa, Ambuye Yehova; mwandikhalira wokhulupirika kuyambira ubwana wanga. . . . Ndidzakulemekezani kosalekeza.”​—Salmo 71:5, 6.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena