Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Tizigonjera Abusa Achikondi Modzichepetsa
    Nsanja ya Olonda—2007 | April 1
    • 7. Kodi mtumwi Paulo anapereka malangizo otani a mmene tiyenera kuonera oyang’anira achikhristu?

      7 Yehova Mulungu ndi Yesu Khristu, Abusa athu akumwamba, amafuna kuti tizimvera ndi kugonjera abusa aang’ono amene apatsidwa udindo mumpingo. (1 Petulo 5:5) Mouziridwa ndi Mulungu, mtumwi Paulo analemba kuti: “Kumbukirani amene akutsogolera pakati panu, amene alankhula mawu a Mulungu kwa inu, ndipo poonetsetsa mmene khalidwe lawo likukhalira, tsanzirani chikhulupiriro chawo. Muzimvera amene akutsogolera pakati panu ndipo muziwagonjera. Iwo amayang’anira miyoyo yanu monga anthu amene adzayankha mlandu. Teroni kuti achite ntchito yawo mwachimwemwe, osati modandaula, pakuti akatero zingakhale zokuwonongani.”​—Aheberi 13:7, 17.

      8. Kodi Paulo akutiuza ‘kuonetsetsa’ chiyani, ndipo tiyenera ‘kumvera’ motani?

      8 Onani kuti Paulo akutiuza ‘kuonetsetsa’ mmene khalidwe labwino la akulu likukhalira ndi kutsanzira chitsanzo chawo cha chikhulupiriro. Kenako akutilangiza kumvera ndi kugonjera zimene amuna amenewa akutiuza. Katswiri wa Baibulo R. T. France anafotokoza kuti m’Chigiriki choyambirira, mawu amene pano anawamasulira kuti “muzimvera” si mawu amene nthawi zonse amatanthauza “kumvera, koma ndi mawu otanthauza ‘kutsimikiza,’ kusonyeza kuti munthu akuvomereza ndi mtima wonse utsogoleri wawo.” Sikuti timamvera akulu chabe chifukwa chakuti Mawu a Mulungu amatiuza kutero koma chifukwa chakuti tatsimikiza kuti iwo amakonda zinthu za Ufumu ndiponso kuti amatifunira zabwino. Tikavomereza ndi mtima wonse utsogoleri wawo, timakhaladi osangalala.

      9. Kuwonjezera pa kukhala omvera, n’chifukwa chiyani tiyenera kukhala ‘ogonjera’?

      9 Nanga bwanji ngati sitili otsimikiza kuti njira imene akulu akutiuza kutsatira pankhani inayake, si njira yabwino kwenikweni? Apa ndiye pofunika kugonjera. N’zosavuta kumvera malangizo amene tapatsidwa ngati tikuwamvetsa bwino ndi kuwavomereza. Koma timasonyezadi kuti ndife ogonjera ngati tilolera kuchita zimene atiuzazo ngakhale kuti sitikuzimvetsa bwino. Petulo, yemwe kenako anadzakhala mtumwi, anagonjera mwanjira imeneyi.​—Luka 5:4, 5.

  • Tizigonjera Abusa Achikondi Modzichepetsa
    Nsanja ya Olonda—2007 | April 1
    • 12. Kodi akulu “amayang’anira miyoyo” yathu motani?

      12 Chifukwa chachiwiri chogonjera oyang’anira achikhristu ndi chakuti “iwo amayang’anira miyoyo” yathu. Akaona kuti penapake mtima wathu kapena khalidwe lathu lingaike moyo wathu wauzimu pachiswe, mwachangu amatilangiza pofuna kutiwongolera. (Agalatiya 6:1) Mawu achigiriki amene anawamasulira kuti “amayang’anira” amatanthauza “kusagona tulo.” Katswiri wina wa Baibulo anati mawuwo “amanena za m’busa amene amakhala tcheru nthawi zonse.” Kuwonjezera pa kuyesetsa kwawo kukhala atcheru mwauzimu, akulu nthawi zina sagona tulo chifukwa chodera nkhawa moyo wathu wauzimu. Kodi simukuona kuti n’koyenera kukhala ndi mtima wogonjera abusa aang’ono achikondi, amene amayesetsa kusamalira nkhosa mwachikondi ngati Yesu Khristu, “m’busa wa nkhosa wamkuluyo”?​—Aheberi 13:20.

      13. Kodi oyang’anira ndi Akhristu onse adzayankha mlandu kwa ndani, ndipo n’chifukwa chiyani?

      13 Chifukwa chachitatu chokhalira ndi mtima wogonjera oyang’anira ndi chakuti iwo amatiyang’anira “monga anthu amene adzayankha mlandu.” Oyang’anirawo amakumbukira kuti iwo ndi abusa aang’ono, amene akutumikira pansi pa Yehova Mulungu ndi Yesu Khristu, Abusa akumwamba. (Ezekieli 34:22-24) Yehova ndiye Mwini nkhosa zimene ‘anazigula ndi magazi a Mwana wake wa iye mwini,’ ndipo amafuna kuti zizisamaliridwa “mwachikondi.” N’chifukwa chake oyang’anira adzayankha mlandu kwa Iye wokhudza mmene iwo akusamalira nkhosa Zake. (Machitidwe 20:28, 29) Choncho, tonsefe tidzayankha mlandu kwa Yehova chifukwa cha mmene timalabadirira malangizo ake. (Aroma 14:10-12) Tikamamvera akulu, timapereka umboni wakuti timagonjera Khristu, Mutu wa mpingo.​—Akolose 2:19.

      14. N’chiyani chimene chingachititse oyang’anira achikhristu kutumikira “modandaula,” ndipo zotsatira zake zingakhale zotani?

      14 Paulo anapereka chifukwa chachinayi chogonjera oyang’anira achikhristu modzichepetsa. Analemba kuti: “Teroni kuti achite ntchito yawo mwachimwemwe, osati modandaula, pakuti akatero zingakhale zokuwonongani.” (Aheberi 13:17) Akulu achikhristu amasenza mtolo wolemera chifukwa cha udindo waukulu umene ali nawo wophunzitsa, kuweta, kutsogolera ntchito yolalikira, kusamalira banja ndiponso mavuto mumpingo. (2 Akorinto 11:28, 29) Tikapanda kuwagonjera, timangowawonjezera mtolo. Mapeto ake, iwo angayambe ‘kudandaula.’ Tikakhala ndi mtima wosagonjera, Yehova sasangalala ndipo zimenezi zingatiwononge. Koma tikamawapatsa ulemu woyenera ndi kuwagonjera, akulu amachita ntchito yawo mwachimwemwe, ndipo zimenezi zimalimbikitsa umodzi komanso anthu amasangalala kuchita ntchito yolalikira Ufumu.​—Aroma 15:5, 6.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena